Kodi Mukufuna Kukhala ndi Anzanu Enieni?
Kodi Mukufuna Kukhala ndi Anzanu Enieni?
ANTHU ambiri amafuna kukhala ndi anzawo enieni. Moyo umakhala wosangalatsa kwambiri ukakhala ndi mnzako amene ungathe kumuuza nkhani zakukhosi. Koma kodi mungapeze bwanji anzanu enieni? Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, Yesu anasonyeza kuti chinthu chofunika kwambiri kuti anthu akhale paubwenzi wopambana, ndicho kukhala ndi chikondi chopanda dyera. Iye anaphunzitsa kuti: “Monga mufuna inu kuti anthu adzakuchitirani inu, muwachitire iwo motero inu momwe.” (Luka 6:31) Mawu amenewa amasonyeza kuti muyenera kukhala munthu wosadzikonda, ndiponso wopatsa kuti mupeze anzanu. Kunena kwina tingati, kuti mupeze mnzanu muyambe inuyo kukhala waubwenzi. Motani?
Ubwenzi wolimba ndi wosangalatsa sumangoyamba mwadzidzidzi. Ndipotu, mabwenzi amaposa anthu ongodziwana nawo. Iwo ndi anthu omwe umafika powakonda kwambiri. Kuti munthu upeze mnzako ndi kupitiriza kugwirizana naye pamafunika khama. Ubwenzi kawirikawiri umafuna kuti uziika zofuna za mnzako patsogolo pa zofuna zako. Mabwenzi samangaouzana chabe zinthu zomwe zawasangalatsa ayi koma amauzananso zinthu zomwe zawakhumudwitsa.
Mumaonetsa kuti ndinu bwenzi lenileni polimbikitsa ndi kuthandiza anthu omwe akuyenerera thandizo. Lemba la Miyambo 17:17 limati: “Bwenzi limakonda nthawi zonse; ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.” Inde ubwenzi ungakhale wolimba kuposa chibale. Lemba la Miyambo 18:24 limati: “[“Alipo mabwenzi omwe amangokhalira kupwetekana,” NW], koma lilipo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira.” Kodi mungakonde kudziwa zambiri za mmene mungapezere anzanu enieni? Kodi mukufuna kukhala m’gulu la anthu amene amadziwika chifukwa chokhala ndi chikondi pa wina ndi mnzake? (Yohane 13:35) Ngati ndi choncho, Mboni za Yehova za m’dera lanu zidzasangalala kukusonyezani mmene mungapezere anzanu enieni.