Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndani Amene Akutsatira Ziphunzitso za Kristu Masiku Ano?

Kodi Ndani Amene Akutsatira Ziphunzitso za Kristu Masiku Ano?

Kodi Ndani Amene Akutsatira Ziphunzitso za Kristu Masiku Ano?

ANTHU ambiri amakhulupirira kuti mwa anthu onse otchuka kwambiri amene anakhalako, Yesu Kristu anali mmodzi wa iwo. Enanso ambiri amakhulupirira kuti iyeyo ndiye amawaposa onsewo kutchuka kwake. Kwa zaka pafupifupi 2,000, ziphunzitso zake zakhudza kwambiri moyo wa anthu. Munthu winawake wa ku England wolemba nkhani, dzina lake Melvyn Bragg, analemba kuti ziphunzitso zakezo zakhudza “moyo wa anthu abwino ndi okoma mtima osadziwika n’komwe ndiponso zalimbikitsa ntchito zazikulu zachifundo.”

Nanga Chikristu Anthu Amachiona Bwanji?

Nangano Chikristu anthu amachiona bwanji? Anthu anenapo zoti Chikristu ndi “chimodzi mwa zinthu zotsogola kwambiri pa zauzimu zimene anthu akhala nazo.” Wina amene ananenapo maganizo ake ndi David Kelso wa pa Yunivesite ya Glasgow Caledonian, ku Scotland. Iyeyu analemba kuti: “Pa zaka zake 2,000 zimene [Chikristu] chakhalapo chachita zinthu zazikulu kwambiri pa luso losiyanasiyana monga la zojambulajambula ndi zoumbaumba, zomangamanga, maphunziro, nyimbo ndi chikhalidwe cha anthu.”

Ngakhale zili choncho, alipo anthu ena ambiri amene sagwirizana ndi zimenezo. Sikuti vuto lawo ndi mmene dikishonale ina imamasulira mawu akuti Chikristu, kuti ndi “chipembedzo chimene chimatsatira ziphunzitso za Yesu Kristu ndi chikhulupiriro chakuti iye anali mwana wa Mulungu.” (Collins Cobuild) Koma kuti iwo amaipidwa ndi khalidwe la mabungwe a zipembedzo amene amati chipembedzo chawo ndi Chikristu.

Mwachitsanzo, munthu winawake wa ku Germany wofufuza nzeru zapamwamba, dzina lake Friedrich Nietzsche, anafotokoza maganizo ake pa Chikristu. Analemba kuti Chikristu chili ngati “chilema chachikhalire pa anthu. Ndi temberero lalikulu, n’champhulupulu zokhazokha, . . . ndipo chimatha kuchita china chilichonse monga nkhanza, chinyengo, machenjera ndi chidani pofuna kukwanitsa zolinga zake.” Kunena zoona, Nietzsche ananyanyira ndi maganizo akewo, koma anthu ena osatengeka maganizo ngati iyeyo anenapo zofanana ndi zimenezi. Chifukwa chake n’chiyani? N’chifukwa chakuti kwa zaka zambiri makhalidwe amene anthu amene amati ndi Akristu adziwika nawo, si makhalidwe a Yesu Kristu ayi. M’malo mwake, adziwika kwambiri ndi “makhalidwe otayirira, nkhanza zosaneneka ndi ntchito zonyoza Mulungu.”

Kodi Kristu Adakali Pakati pa Akristu?

Ndiye m’pake kufunsa kuti, “Kodi Kristu adakali pakati pa Akristu?” Ambiri sazengereza kuyankha funso limeneli kuti, “N’zosachita kufunsa! Si nanga analonjeza otsatira ake kuti adzakhala nawo ‘kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano’?” (Mateyu 28:20) Ee, Yesu ananenadi zimenezo. Koma kodi iye anatanthauza kuti adzakhala ndi munthu wina aliyense wonena kuti ndi wotsatira wake, kaya khalidwe la munthuyo ndi lotani?

Kumbukirani kuti m’masiku a Yesu panali atsogoleri ena achipembedzo amene ankaganiza kuti, mulimonsemo, Mulungu anali nawo basi. Popeza kuti Mulungu anali atasankha Israyeli kuti achite ntchito yapadera, atsogoleri ena achipembedzo ankaganiza kuti Mulungu sangawasiye​—kaya achite zotani. (Mika 3:11) Koma patapita nthawi, iwo anaphwanya malamulo ndi mfundo za Mulungu mopitirira muyeso. Mapeto ake, Yesu Kristu sanawabisire koma anawauza kuti: “Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.” (Mateyu 23:38) Chipembedzo chawo chonsecho Mulungu anachikana ndipo analola asilikali a Roma kuwononga Yerusalemu, limene linali likulu lake, ndi kachisi wake mu 70 C.E.

Kodi zimenezi zingachitikirenso Chikristu? Tiyeni tione mfundo zina zofunika zimene Yesu anaphatikiza pa lonjezo lake lakuti adzakhala ndi otsatira ake mpaka “chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.”

[Zithunzi pamasamba 2, 3]

Ziphunzitso za Yesu Kristu zikukhudza anthu mamiliyoni padziko lonse lapansi