Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muziganiza Bwino Kwambiri

Muziganiza Bwino Kwambiri

Muziganiza Bwino Kwambiri

“Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.”​—MIYAMBO 14:15.

1, 2. (a) Kodi zomwe zinachitikira Loti ku Sodomu zikutiphunzitsa chiyani? (b) Kodi mawu akuti “mukhale odzisunga” amatanthauza chiyani?

ABRAHAMU atapatsa Loti mwayi woti ayambe ndi iye kusankha dziko lomwe akufuna, Loti anakopeka ndi dera la madzi ambiri looneka “monga munda wa Yehova.” N’kutheka kuti deralo linkaoneka labwino kwambiri kukhalamo ndi banja lake, popeza kuti “Loti anasankha chigwa chonse cha Yordano” ndi kukamanga mahema ake kufupi ndi Sodomu. Koma maonekedwe anam’pusitsa, chifukwa kufupi ndi derali kunali “anthu a ku Sodomu [omwe] anali oipa ndi ochimwa kwambiri pamaso pa Yehova.” (Genesis 13:7-13) M’kupita kwa nthawi, Loti ndi banja lake anavutika kwambiri. Mapeto ake, iye ndi ana ake aakazi anakakhala m’phanga. (Genesis 19:17, 23-26, 30) Dera lomwe poyamba analiona kukhala labwino kwambiri linapezeka kuti ndiye dera loipitsitsa.

2 Nkhani ya zomwe zinachitikira Loti ili ndi phunziro kwa atumiki a Mulungu masiku ano. Tikamafuna kusankha zochita, tiyenera kusamala ndi mavuto amene angabwere pambuyo pake ndipo tiyenera kusamala kuti tisanyengedwe ndi zomwe taona poyamba. M’paketu kuti Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti: “Mukhale odzisunga.” (1 Petro 1:13) Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “mukhale odzisunga” kwenikweni amatanthauza “kukhala oganiza bwino.” Malinga ndi zomwe ananena katswiri wina wamaphunziro a Baibulo, R. C. H. Lenski, kuganiza bwino kumeneku ndiko “kukhala ndi maganizo osapupuluma, osinkhasinkha bwino zinthu; maganizo omwe amam’thandiza munthu kusankha bwino zochita.” Tiyeni tione nkhani zina zimene zimafuna kuti tiganize bwino.

Kuganizira Bwino Mwayi wa Malonda

3. N’chifukwa chiyani pamafunika kusamala ngati munthu wina watipatsa mwayi wochita nawo malonda?

3 Tiyerekeze kuti munthu wina waulemu wake, mwina yemwe mumapembedzera naye limodzi Yehova, wakupatsani mwayi woti muchite malonda. Iye ali ndi chikhulupiriro chonse kuti malondawo adzayenda bwino kwambiri ndipo akukulimbikitsani kuchita zinthu mwamsanga kuti musaphonye mwayi umenewo. Mwina mungayambe kuganizira moyo wabwino womwe inu ndi banja lanu mugadzakhale nawo chifukwa cha malondawo, mwinanso n’kumaganiza kuti izi zidzakuthandizani kupeza nthawi yambiri yochita zinthu zauzimu. Komatu, lemba la Miyambo 14:15 limachenjeza kuti: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.” Chifukwa cha chisangalalo chomwe nthawi zambiri chimakhalapo poganizira zoyamba malonda atsopano, munthu angathe kunyalanyaza mfundo yakuti n’zotheka kuti ndalama zilowe m’madzi, ndiponso sangaganizire bwinobwino kuti tsogolo la malondawo lidzakhala lotani. (Yakobo 4:13, 14) Zikatero, m’pofunikatu kuganiza bwino kwambiri.

4. Kodi ‘tingasamalire mayendedwe athu’ motani tikaganizira mofatsa za mwayi wa malonda womwe tapatsidwa?

4 Munthu wanzeru amaganizira mofatsa za malondawo kuti aone zochita. (Miyambo 21:5) Nthawi zambiri munthu amatha kuona mavuto omwe angadzakhalepo akaganizira mofatsa chonchi. Taganizirani izi: Munthu wina akufuna kubwereka ndalama zoti agwiritse ntchito pa malonda ake omwe akuwaganizira ndipo akulonjeza kuti adzakupatsani phindu lalikulu ngati mutam’bwereka ndalamazo. Mungathe kukopeka ndi lonjezo lakelo, komano kodi pangakhale mavuto otani? Kodi wobwereka ndalamayo wavomera kudzabweza ngongoleyo kaya malondawo adzayende bwino kapena ayi? Kapena kubweza ngongoleyo kukudalira mmene malondawo adzayendere? M’mawu ena, kodi ndinu wokonzeka kuluza ndalama zanu malondawo atalephereka? Mungathenso kufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani akufuna ngongole kwa anthu? Kodi mabanki akuona kuti zimene iye akufuna kuchitazo zingathe kuwonongetsa ndalama?” Kuyamba mwaganizira za mavuto omwe angakhalepo kungakuthandizeni kuganizira bwino mwayi womwe mwapatsidwawo.​—Miyambo 13:16; 22:3.

5. (a) Kodi n’chinthu chanzeru chiti chimene Yeremiya anachita atagula munda? (b) N’chifukwa chiyani ndi bwino kumalemba nkhani zonse zokhudza malonda m’chikalata cholembedwa bwino cha mapangano?

5 Mneneri Yeremiya atagula munda kwa msuweni wake, yemwenso anali kupembedzera naye limodzi Yehova, analemberana za malondawo pamaso pa mboni. (Yeremiya 32:9-12) Masiku ano, munthu wanzeru amaonetsetsa kuti nkhani zonse za malonda amene akuchita ndi anzake, kuphatikizapo amene akuchita ndi achibale ake kapena okhulupirira anzake, akulemberana m’chikalata chosonyeza mfundo za mapangano awowo. * Kukhala ndi chikalata cholembedwa bwino cha mapanganowo kumathandiza kupewa mikangano ndiponso kumalimbikitsa umodzi. Koma nthawi zambiri, kulephera kulemberana mapangano n’kumene kumathandizira kuti pakati pa atumiki a Yehova pakhale mavuto. N’zomvetsa chisoni kuti anthu amasautsidwa, kusungirana udani, ndipo mwinanso kufa mwauzimu chifukwa cha mavuto oterowo.

6. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kusamala ndi dyera?

6 Tiyeneranso kusamala ndi dyera. (Luka 12:15) Kulonjezedwa phindu lalikulu kungalepheretse munthu kuganizira za mavuto omwe angathe kudzabuka pa malonda osadalirika. Ngakhale ena amene ali ndi maudindo akuluakulu potumikira Yehova akodwa mumsampha umenewu. Mawu a Mulungu amatichenjeza kuti: “Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni.” (Ahebri 13:5) Polingalira za mwayi wa malonda womwe wapatsidwa, Mkristu ayenera kuganizira kuti, ‘Kodi m’pofunikadi kuti ndichite nawo malonda amenewa?’ Kukhala moyo wosalira zambiri, wolimbikira pa kulambira kwathu Yehova kungatiteteze ku “zoipa zonse.”​—1 Timoteo 6:6-10.

Mavuto Amene Akristu Osakwatira Amakumana Nawo

7. (a) Kodi ndi mavuto otani amene Akristu ambiri osakwatira amakumana nawo? (b) Kodi mmene tasankhira munthu womanga naye banja zimakhudza motani kukhulupirika kwathu kwa Mulungu?

7 Atumiki ambiri a Yehova amafuna kukwatira kapena kukwatiwa koma sanapezebe munthu wowayenera. M’mayiko ena, chikhalidwe chimakakamiza anthu kulowa m’banja. Ngakhale zili choncho, mwayi woti n’kupeza mwamuna kapena mkazi pakati pa okhulupirira ungakhale wochepa. (Miyambo 13:12) Komabe, Akristu amadziwa kuti kumvera lamulo lokwatira “mwa Ambuye” ndi nkhani imene imasonyeza kukhulupirika kwawo kwa Yehova. (1 Akorinto 7:39) Kuti Akristu osakwatira athe kulimbana ndi mavuto ndiponso mayesero omwe amakumana nawo, ayenera kukhala oganiza bwino.

8. Kodi Msulami anakumana ndi vuto lotani, ndipo akazi achikristu angakumane motani ndi vuto ngati limeneli masiku ano?

8 M’buku la Nyimbo ya Solomo, mfumu inakopeka ndi mtsikana wina wosauka wakumudzi, Msulami. Mfumuyo inayesa kukopa mtsikanayo ndi chuma chambiri, ulemu, ndiponso kukongola kwake, ngakhale kuti mtsikanayo anali kale pachibwenzi ndi mnyamata wina. (Nyimbo ya Solomo 1:9-11; 3:7-10; 6:8-10, 13) Ngati ndinu mkazi wachikristu, n’kutheka kuti inunso anthu ena akopeka nanu mosayenerera. Munthu wina kuntchito kwanu, mwinamwake bwana wanu, angayambe kumakuyamikirani, kukuchitirani zinthu zina, ndiponso kufufuza mipata yoti acheze nanu. Chenjerani ndi chidwi chopanda pake choterocho. Ngakhale kuti si nthawi zonse pamene maganizo a anthu oterowo amakhala oipa, koma nthawi zambiri maganizo awo amakhala oipa. Mofanana ndi mtsikana uja, Msulami, khalani “khoma.” (Nyimbo ya Solomo 8:4, 10) Kanani kwamtuwagalu zokhala nawo pachibwenzi. Poyambirira pomwe, dziwitsani anthu amene mukugwira nawo ntchito kuti ndinu wa Mboni za Yehova, ndipo alalikireni nthawi iliyonse yomwe mwapeza mpata. Zimenezi zidzakutetezani.

9. Kodi ena mwa mavuto omwe munthu angakumane nawo chifukwa choyamba chibwenzi pa cha Intaneti ndi munthu wosam’dziwa ndi otani? (Onaninso bokosi patsamba 25.)

9 Pa Intaneti pamapezeka malo ena amene munthu wosakwatira amatha kupezerapo munthu womanga naye banja, ndipo malo oterewa akuchuluka kwambiri. Ena amaona kuti malo amenewa ndi njira yodziwanirana ndi anthu amene sakanadziwana nawo. Komabe, kuyamba chibwenzi mwachimbulimbuli ndi munthu amene simukum’dziwa n’koopsa kwambiri. Pa Intaneti n’zovuta kutha kusiyanitsa zoona ndi zabodza. (Salmo 26:4) Si aliyense amene anganene zoona kuti ndi mtumiki wa Yehova. Komanso, pa chibwenzi cha pa Intaneti, chikondi chimakula mwamsanga, ndipo zimenezi zingalepheretse munthu kuganiza bwino. (Miyambo 28:26) Kaya ndi kudzera pa Intaneti kapena njira ina iliyonse, n’kupanda nzeru kuyamba kugwirizana ndi munthu amene simukum’dziwa bwino.​—1 Akorinto 15:33.

10. Kodi Akristu osakwatira angalimbikitsidwe motani ndi okhulupirira anzawo?

10 Yehova ‘amawakonda’ kwambiri atumiki ake. (Yakobo 5:11) Iye amadziwa kuti mavuto omwe Akristu amene sali pabanja osati mwa kufuna kwawo amakumana nawo nthawi zina ndi olefula kwambiri, ndipo iye amasangalala kwambiri ndi kukhulupirika kwawo. Kodi anthu ena angawalimbikitse motani Akristu amenewa? Tiyenera kumawayamikira nthawi zonse chifukwa choti ndi omvera ndiponso ali ndi mtima wodzipereka. (Oweruza 11:39, 40) Tingathenso kuwaitana kuti akhale nafe pa macheza omwe takonza. Kodi mwachitapo zimenezi posachedwapa? Komanso, tingathe kuwapempherera, ndi kupempha Yehova kuti awathandize kukhalabe olimba mwauzimu ndiponso kukhala osangalala pamene akum’tumikira. Tiyeni tisonyeze kuti timaona anthu okhulupirikawa kuti ndi ofunika monganso mmene Yehova amawaonera ndipo tichite zimenezo mwa kukhala nawo chidwi.​—Salmo 37:28.

Nkhani Zokhudza Umoyo

11. Kodi munthu akadwala matenda aakulu pamakhala mavuto otani?

11 Kunena zoona, timathedwa nzeru kwambiri tikadwala matenda aakulu kapena vutoli likagwera munthu wina amene timam’konda. (Yesaya 38:1-3) Ngakhale kuti timayesetsa kupeza chithandizo chabwino, koma m’pofunika kuti tizitsatira mfundo za m’Malemba. Mwachitsanzo, Akristu amaonetsetsa kuti akumvera lamulo la m’Baibulo lopewa magazi, ndipo amakana chithandizo chilichonse chokhudzana ndi kukhulupirira mizimu. (Machitidwe 15:28, 29; Agalatiya 5:19-21) Komabe, kwa anthu amene sanaphunzirepo zachipatala, kungakhale kovuta kuganizira mofatsa za chithandizo chomwe angalandire. Kodi n’chiyani chingatithandize kuganiza bwino za nkhaniyi?

12. Kodi Mkristu angatani kuti aganize bwino pamene akulingalira za chithandizo choti alandire?

12 “Wochenjera asamalira mayendedwe ake” mwa kufufuza nkhani m’Baibulo ndi m’mabuku achikristu. (Miyambo 14:15) M’madera ena kumene madokotala ndiponso zipatala ndi zochepa, chithandizo chomwe anthu amachidalira akadwala chingakhale mankhwala azitsamba. Ngati tikulingalira zopeza chithandizo choterocho, tingapeze mfundo zabwino kwambiri mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1987 masamba 21 mpaka 24. Nkhani yomwe ili m’masamba amenewa imatithandiza kusamala ndi mavuto omwe angakhalepo. Mwachitsanzo, tingafunike kudziwa zinthu zotsatirazi: Kodi munthu wodziwa za mankhwalayo amadziwika kuti amachita zamizimu? Kodi chithandizocho n’chogwirizana ndi chikhulupiriro chakuti matenda ndi imfa zimachitika mwina ndi milungu (kapena mizimu ya makolo) yomwe yakwiya kapena ndi adani omwe achita zaufiti? Kodi pokonza kapena kugwiritsa ntchito mankhwalawo pamafunika kuthira nsembe, kulankhula mawu a matsenga, kapena kuchita miyambo ina yokhudzana ndi kukhulupirira mizimu? (Deuteronomo 18:10-12) Kufufuza zimenezi kungatithandize kutsatira malangizo ouziridwa akuti: “Yesani zonse; sungani chokomacho.” * (1 Atesalonika 5:21) Zingatithandize kuti tiganize bwino.

13, 14. (a) Kodi tingasonyeze motani kuti tikuganiza bwino pankhani yosamalira umoyo wathu? (b) Kodi n’chifukwa chiyani kuganiza bwino n’kofunika tikamakambirana ndi anzathu nkhani za umoyo ndi zamankhwala?

13 “Kufatsa,” kapena kuti kuchita zinthu mosamala n’kofunika pankhani zonse zokhudza moyo, kuphatikizapo za umoyo wathu. (Afilipi 4:5) Kusamalira bwino moyo wathu kumasonyeza kuti timayamikira mphatso yamtengo wapatali imeneyi. Pamene sitikupeza bwino, tiyenera kufunafuna chithandizo. Komabe, panopa n’zosatheka kukhala moyo wangwiro mpaka itakwana nthawi ya Mulungu ‘yochiritsa . . . amitundu.’ (Chivumbulutso 22:1, 2) Tisamale kuti tisatanganidwe kwambiri ndi umoyo wathu mpaka kufika polephera kuchita zinthu zofunika kwambiri zauzimu.​—Mateyu 5:3; Afilipi 1:10.

14 Komanso tikamakambirana ndi anzathu nkhani za umoyo ndi zamankhwala tikufunika kusamala. Nkhani zimenezi siziyenera kutenga mbali yaikulu ya macheza athu tikakumana kuti tilimbikitsane mwauzimu pa misonkhano ya mpingo ndiponso misonkhano ikuluikulu. Komanso, zosankha za munthu pankhani za mankhwala nthawi zambiri zimakhudza mfundo za m’Baibulo, chikumbumtima chake, ndiponso ubwenzi wake ndi Yehova. Motero, kungakhale kupanda chikondi kukakamiza wokhulupirira mnzathu kuti atsatire maganizo athu kapena kuti anyalanyaze zimene chikumbumtima chake chikumuuza. Ngakhale kuti munthu angapemphe thandizo pankhanizi kwa anthu okhwima maganizo mu mpingo, Mkristu aliyense ayenera ‘kusenza katundu wake wa iye mwini’ pa zomwe wasankha kuchita, ndipo “aliyense wa ife adzadziwerengera mlandu wake kwa Mulungu.”​—Agalatiya 6:5; Aroma 14:12, 22, 23.

Tikapanikizika Maganizo

15. Kodi zinthu zopanikiza maganizo zingatisokoneze motani?

15 Zinthu zopanikiza maganizo zingapangitse munthu ngakhale amene amatumikira Yehova kulankhula kapena kuchita zinthu mopanda nzeru. (Mlaliki 7:7) Atakumana ndi mayesero aakulu, Yobu anasokonezeka maganizo pang’ono ndipo anafunika kulangizidwa. (Yobu 35:2, 3; 40:6-8) Ngakhale kuti “Mose [anali] wofatsa woposa anthu onse a pa dziko lapansi,” nthawi ina anakwiya n’kulankhula mokalipa. (Numeri 12:3; 20:7-12; Salmo 106:32, 33) Davide anali atadziletsa kwambiri kuti asaphe Mfumu Sauli, koma Nabala atam’tukwana ndiponso kum’nyozera anyamata ake, Davide anakwiya kwambiri ndipo sanathe kuganiza bwino. Abigayeli atalowererapo pankhaniyi, m’pamene Davide anayambiranso kuganiza bwino, moti anangotsala pang’onong’ono kuchita zinthu zoopsa kwambiri.​—1 Samueli 24:2-7; 25:9-13, 32, 33.

16. N’chiyani chingatithandize kuti tisapupulume pochita zinthu?

16 Nafenso tingathe kupanikizika maganizo moti tingalephere kuganiza bwino. Kulingalira mofatsa maganizo a ena, ngati mmene Davide anachitira, kungatithandize kuti tisachite zinthu mopupuluma ndi kuthamangira m’tchimo. (Miyambo 19:2) Komanso, Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti: “Chitani chinthenthe [kapena kuti kwiyani], ndipo musachimwe: Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete.” (Salmo 4:4) Ngati ndi zotheka, n’chinthu chanzeru kudikira mpaka maganizo atakhala m’malo tisanachitepo chilichonse kapena kusankha chochita chilichonse. (Miyambo 14:17, 29) Tingapemphere kwa Yehova n’kumuuza zakukhosi kwathu, “ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima [yathu] ndi maganizo [athu] mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Mtendere wa Mulungu umenewu ungatithandize kukhazika mtima m’malo ndiponso kuti tiganize bwino kwambiri.

17. N’chifukwa chiyani tiyenera kudalira Yehova kuti tikhale anthu oganiza bwino kwambiri?

17 Ngakhale titayesetsa motani kuti tipewe mavuto ndiponso kuti tichite zinthu mwanzeru, tonsefe timaphonyetsa zinthu nthawi zina. (Yakobo 3:2) Nthawi zina tingafike poti tatsala pang’ono kuchita cholakwa choopsa kwambiri, popanda kudziwa chilichonse. (Salmo 19:12, 13) Kuwonjezera pamenepo, popeza ndife anthu, sitingathe ndiponso si udindo wathu kulongosola mapazi athu, ndipo Yehova ndi amene angachite zimenezo. (Yeremiya 10:23) Timayamikira kwambiri lonjezo lake lakuti: “Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.” (Salmo 32:8) Inde, mothandizidwa ndi Yehova, zingatheke kuti tikhale oganiza bwino kwambiri.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Kuti mumve zambiri pankhani yolemberana chikalata cha mapangano a malondayi, onani Nsanja ya Olonda ya August 1, 1997, masamba 30 ndi 31; Nsanja ya Olonda ya November 15, 1986, masamba 16 ndi 17; ndiponso Galamukani! ya Chingelezi ya February 8, 1983, masamba 13 mpaka 15. Magaziniwa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 12 Kuchita zimenezi kungathandizenso anthu amene akuganizira zolandira chithandizo chomwe anthu sakugwirizana chimodzi.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi tingachite chiyani kuti tiganize bwino

• tikapatsidwa mwayi wochita nawo malonda?

• pofufuza munthu womanga naye banja?

• tikakumana ndi mavuto a umoyo?

• tikapanikizika maganizo?

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 25]

Kodi Mungadalire za pa Intaneti?

Posafuna kuimbidwa mlandu, alangizi a pa Intaneti a anthu ofuna mabanja amanena mawu otsatirawa:

“Ngakhale kuti tayesetsa kudziwa khalidwe la munthu aliyense, koma sitingam’tsimikizire munthu kuti amenewa ndi makhalidwe awo enieni.”

“Sitingam’tsimikizire munthu kuti zomwe tafotokoza zokhudza munthu winawake ndi zoona, zokwanira, kapena zothandiza.”

“Maganizo, malangizo, mawu, malonjezo, kapena zinthu zina zopezeka [pano] n’za eniake amene alemba zimenezi . . . ndipo si zoti n’kuzidalira kwenikweni.”

[Chithunzi patsamba 23]

“Wochenjera asamalira mayendedwe ake”

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Kodi akazi achikristu angatsanzire motani Msulami?

[Chithunzi patsamba 26]

“Yesani zonse; sungani chokomacho”