Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tapitiriza!”

“Tapitiriza!”

“Tapitiriza!”

MU MZINDA wa Nezlobnaya, m’dziko la Russia, kalasi ina yophunzira za mabuku pasukulu ina ya sekondale, inkafufuza za mlembi wina wa mabuku wa ku Russia dzina lake Mikhail Bulgakov. Mwa mabuku amene iye analemba panali buku lina limene linkalongosola za Yesu Kristu monyoza, ndipo linkalongosolanso za Satana kuti ndi ngwazi. Atamaliza kukambirana m’kalasimo, mphunzitsi anauza ophunzira onse kuti alembe mayeso ochokera m’buku limenelo. Komabe, mmodzi wa ophunzirawo, yemwe anali ndi zaka 16 wa Mboni za Yehova, ndipo dzina lake ndi Andrey, anapempha mwaulemu kuti asalembe nawo mayesowo chifukwa chikumbumtima chake sichimulola kuphunzira mabuku oterowo. Ndipo anapempha mphunzitsiyo kuti alembe nkhani imene imafotokoza mmene iye amaonera Yesu Kristu m’malo mwa zimene ankaphunzirazo. Mphunzitsiyo anavomera.

M’nkhani yakeyo, Andrey anafotokoza kuti, ngakhale kuti iye amalemekeza maganizo a ena, amaona kuti njira yabwino kwambiri yophunzirira za Yesu n’kuwerenga imodzi mwa nkhani zinayi zolembedwa m’Mauthenga Abwino. Potero, “mudzaphunzira za moyo wa Yesu ndi ziphunzitso zimene zinalembedwa ndi anthu amene anali mboni zoona ndi maso.” Andrey anawonjezera kuti: “Nkhani ina ndi ya mmene Satana akumufotokozera. Ena angaone kukhala zoseketsa kuwerenga buku limene lamulongosola Satana kuti ndi ngwazi, koma kwa ine si zinthu zoseketsa m’pang’ono pomwe.” Andrey anafotokoza kuti Satana kwenikweni ndi cholengedwa champhamvu chauzimu chomwe ndi choipa ndipo chinapandukira Mulungu, n’kuyambitsa kuipa ndi mavuto pa anthu. Andrey anamaliza nkhani yake ndi kuti: “Sindikukhulupirira kuti kuwerenga buku limeneli kungandipindulitse ayi. Komabe, Sikuti ndikumuda Bulgakov. Koma ineyo, ndingakonde kuwerenga Baibulo kuti ndiphunzire mbiri yoona yonena za Yesu Kristu.”

Mphunzitsi wa Andrey anasangalala kwambiri ndi nkhaniyo moti anauza Andrey kuti akakambe nkhani yokhudza Yesu Kristu. Andrey anavomera ndi mtima wonse. Panthawi imene anali ndi phunziro lina m’kalasi mwawo, Andrey anawerengera nkhaniyo ophunzira anzake. Analongosola chifukwa chimene amaonera kuti Yesu ndi munthu woposa onse amene anakhalako. Ndipo anawerenga chaputala chonena za imfa ya Yesu kuchokera m’buku la Mateyu m’Baibulo. Popeza kuti nthawi imene anakonza kuti awerenge nkhaniyo inali itatsala pang’ono kutha, Andrey ankafuna kuti amalize nkhaniyo, koma anzakewo anamulimbikitsa kuti: “Tapitiriza! Kenako chinachitika n’chiyani?” Anapitiriza kuwerenga nkhani ya m’buku la Mateyu yonena za kuuka kwa Yesu.

Andrey atamaliza kuwerenga, anzake a m’kalasiwo anamufunsa mafunso ambiri onena za Yesu ndi Yehova. Andrey anati: “Ndinapemphera kwa Yehova kuti andipatse nzeru, ndipo anandiyankha pemphero langa, ndinatha kuyankha mafunso onse!” Ataweruka, Andrey anapatsa mphunzitsi wakeyo buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, * ndipo mphunzitsiyo analilandira mwachidwi. Andrey anati: “Anandipatsa malikisi apamwamba chifukwa cha nkhani yangayo ndipo anandiyamikira chifukwa chokhala ndi mfundo zimene ndimakhulupirira ndi kusachita nazo manyazi. Ananenanso kuti akugwirizana ndi zina za zimene ndimakhulupirira.”

Andrey akusangalala kuti anasankha kutsatira chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo pokana kuwerenga zinthu zimene sizilemekeza Yehova ndi Mwana wake, Yesu Kristu. Pochita zimenezo Andrey sanangodziteteza chabe ku mfundo zomwe sizigwirizana ndi Malemba ayi koma anatsegulanso mwayi wouza ena choonadi chofunika cha m’Baibulo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.