Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zosangalatsa Zomwe Zimatsitsimula

Zosangalatsa Zomwe Zimatsitsimula

Zosangalatsa Zomwe Zimatsitsimula

“Mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.”​—1 AKORINTO 10:31.

1, 2. Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti zosangalatsa ndi “mtulo wa Mulungu,” komano Baibulo limachenjeza za chiyani?

KULAKALAKA kuchita zinthu zosangalatsa n’kwachibadwa. Mulungu wathu wachisangalalo, Yehova, amafuna kuti tisangalale ndi moyo, ndipo pofuna kuti zimenezi zitheke iye watipatsa zinthu zambiri. (1 Timoteo 1:11; 6:17) Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: ‘Ndadziwa kuti . . . palibe chabwino, koma kukondwa . . . ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.’​—Mlaliki 3:12, 13.

2 Munthu akamakondwera chonchi poganizira ntchito zabwino zomwe wachita, zimakhala zotsitsimula kwambiri, makamaka akamasangalala ndi banja lake kapena anzake. Moti sitingalakwe kunena kuti umakhala “mtulo wa Mulungu.” Ndi zoona kuti ngakhale kuti Mlengi watipatsa mphatso zochuluka, sizikutanthauza kuti tizingosangalala popanda kudziletsa. Baibulo limaletsa kuledzera, kususuka, ndi chiwerewere, ndipo limachenjeza kuti anthu ochita zimenezi “sadzalowa Ufumu wa Mulungu.”​—1 Akorinto 6:9, 10; Miyambo 23:20, 21; 1 Petro 4:1-4.

3. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhala odikira mwauzimu ndi kumakumbukira tsiku lalikulu la Yehova?

3 Kusiyana ndi kale lonseli, m’masiku omaliza owawitsa ano, Akristu akufunika kuyesetsa kukhala mosamala m’dziko loipali, osatengera makhalidwe ake. (Yohane 17:15, 16) Mogwirizana ndi zomwe zinanenedwa kale, mbadwo wa masiku ano ndi ‘wokonda zokondweretsa munthu, osati wokonda Mulungu’ moti ‘sudziwa’ umboni wosonyeza kuti ‘chisautso chachikulu’ chili pafupi. (2 Timoteo 3:4, 5; Mateyu 24:21, 37-39) Yesu anachenjeza otsatira ake kuti: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha.” (Luka 21:34) Popeza ndife atumiki a Mulungu, timafuna kumvera chenjezo la Yesu limeneli. Mosiyana ndi anthu a m’dziko losaopa Mulunguli, timayesetsa kukhala odikira mwauzimu ndi kumakumbukira tsiku lalikulu la Yehova.​—Zefaniya 3:8; Luka 21:36.

4. (a) N’chifukwa chiyani kupeza zosangalatsa zoyenera n’kovuta? (b) Kodi ndi malangizo otani opezeka pa Aefeso 5:15, 16 omwe tiyenera kuwagwiritsa ntchito?

4 Kupewa makhalidwe oipa a m’dzikoli si nkhani yophweka, chifukwa chakuti Mdyerekezi wakometsera ndi kuwafalitsa kwambiri makhalidwe amenewa. Zimakhala zovuta kwambiri makamaka tikamafuna zosangalatsa. Zosangalatsa zambiri za m’dzikoli zimakonzedwa n’cholinga chokhutiritsa “zilakolako za thupi.” (1 Petro 2:11) Zosangalatsa zosayenera zimapezeka m’malo achisangalalo ndipo zingathenso kupezeka m’nyumba zathu kudzera m’mabuku ndi magazini, wailesi za kanema, Intaneti, ndiponso mavidiyo. N’chifukwa chaketu Mawu a Mulungu amapatsa Akristu malangizo anzeru awa, akuti: “Penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.” (Aefeso 5:15, 16) Kutsatira mosamala malangizo amenewa ndi njira yokhayo yotsimikizira kuti sitikukopeka ndiponso sitikutaya nthawi ndi zosangalatsa zosayenera, komanso kuti sizikutiwonongetsa ubwenzi wathu ndi Yehova, zomwe mapeto ake ndi chiwonongeko.​—Yakobo 1:14, 15.

5. Kodi n’chiyani chimene chimatitsitsimula kwambiri?

5 Popeza kuti Akristu amakhala otanganidwa, m’pomveka kuti nthawi zina amafuna kusangalalako. Ndipo lemba la Mlaliki 3:4 limati pali “mphindi yakuseka” ndi “mphindi yakuvina.” Motero Baibulo silinena kuti kusangalala n’kungowononga nthawi. Koma kusangalalako kuyenera kutitsitsimula, osati kutilowetsa m’mavuto mwauzimu kapena kusokoneza zochita zathu zauzimu. Akristu okhwima maganizo adzionera okha kuti kupatsa ndiko kumabweretsa chimwemwe chachikulu. Kuchita chifuniro cha Yehova kumakhala patsogolo pa zonse m’moyo wawo ndipo amapeza ‘mpumulo [weniweni] wa miyoyo yawo’ chifukwa chovomera kusenza goli labwino la Yesu.​—Mateyu 11:29, 30; Machitidwe 20:35.

Kusankha Zosangalatsa Zoyenera

6, 7. N’chiyani chingakuthandizeni kudziwa zosangalatsa zoyenera ndi zosayenera?

6 Kodi tingatsimikize bwanji kuti zosangalatsa zinazake ndi zoyenera kwa Mkristu? Makolo amafunika kulangiza ana awo, ndipo akulu amathandiza pakafunika kutero. Komabe, sitiyenera kumachita kuuzidwa kuti buku, vidiyo, masewera, gule kapena nyimbo inayake si yoyenera. Paulo ananena kuti “anthu akulu misinkhu . . . mwa kuchita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zawo kusiyanitsa chabwino ndi choipa.” (Ahebri 5:14; 1 Akorinto 14:20) Baibulo lili ndi mfundo zomwe zingatithandize. Chikumbumtima chanu, chophunzitsidwa Mawu a Mulungu, chingakuthandizeni ngati muchimvera.​—1 Timoteo 1:19.

7 Yesu ananena kuti “ndi chipatso chake mtengo udziwika.” (Mateyu 12:33) Ngati zosangalatsa zinazake zimabala zipatso zovunda zolimbikitsa chiwawa, chiwerewere, kapena kukhulupirira zamizimu, sitiyenera kuchita nawo. Komanso zosangalatsa sizingakhale zoyenera ngati zili zoti zingaike moyo kapena thanzi lathu pa chiswe, ngati zingatibweretsere mavuto a za chuma kapena ngati zimalefula munthu, kapenanso ngati zimakhumudwitsa anthu ena. Mtumwi Paulo anatichenjeza kuti ndi tchimo ngati tilasa chikumbumtima cha mbale wathu. Paulo analemba kuti: ‘Pakuchimwira abale, ndi kulasa chikumbumtima chawo chofooka, muchimwira kotero Kristu. Chifukwa chake, ngati chakudya chikhumudwitsa mbale wanga, sindidzadya nyama ku nthawi yonse, kuti ndingakhumudwitse mbale wanga.’​—1 Akorinto 8:12, 13.

8. Kodi kusewera masewera a pakompyuta ndi m’mavidiyo kungagwetse munthu m’mavuto otani?

8 M’masitolo masiku ano mwadzaza makompyuta ndi mavidiyo okhala ndi zinthu zoseweretsa. Zina mwa zosangalatsa zimenezi zingakhale zopanda vuto, koma nthawi zambiri zosangalatsa zimenezi zikumasonyeza zinthu zomwe Baibulo limaletsa. Kunena zoona masewera amene amafuna kuti osewerawo avulaze ndi kupha kapena kukhala ndi khalidwe loipa kwambiri, si abwino ayi. Yehova amadana ndi anthu ‘okonda chiwawa.’ (Salmo 11:5; Miyambo 3:31; Akolose 3:5, 6) Ndipo ngati kusewera masewera enaake kumalimbikitsa mtima wadyera kapena waukali, kumakusiyani wachisoni, kapena kukutayirani nthawi yanu yochuluka ya mtengo wapatali, ndiye kuti muyenera kusamala ndi mavuto auzimu omwe mungagweremo ndipo sinthani mwamsangamsanga.​—Mateyu 18:8, 9.

Kupeza Zosangalatsa Zokhutiritsadi

9, 10. Kodi anthu osamala angatani kuti apeze zosangalatsa zokhutiritsa?

9 Nthawi zina Akristu amafunsa kuti: “Kodi zosangalatsa zoyenera ndi zotani? Zosangalatsa zambiri zopezeka m’dzikoli zimatsutsana ndi mfundo za m’Baibulo.” Tikufuna kukutsimikizirani kuti n’zotheka kupeza zosangalatsa zotsitsimula, koma kuti m’pofunika khama. Pamafunika kukonzekera bwino, makamaka makolo. Ambiri amakhutira ndi zosangalala zochitika pabanja ndiponso mu mpingo. Kudyera limodzi chakudya mwachifatse ndi kumakambirana zomwe zinachitika patsikulo kapena nkhani ya m’Baibulo kumakhala kosangalatsa ndiponso kolimbikitsa. Mungathe kukonza zosewera masewera oyenera kapena kuyenda ulendo. Zosangalatsa zimenezi n’zabwino ndiponso zotsitsimula.

10 Mkulu wina wachikristu limodzi ndi mkazi wake, amene alera ana atatu anati: “Kuyambira ali aang’ono, ana athu ankasankha nawo koti tipite patchuthi. Nthawi zina tinkalola mwana aliyense kuitana mnzake wapamtima, zomwe zinkapangitsa tchuthicho kukhala chosangalatsa kwambiri. Tinkakonza zochita zinthu zina zapadera m’moyo wawo. Nthawi zina tinkapempha mabanja ndiponso mabwenzi athu a mu mpingo kuti abwere kunyumba kwathu. Nthawi zina tinkakonza chakudya ndi kudyera panja komanso kusewera masewera osiyanasiyana. Nthawi zinanso tinkayenda pagalimoto komanso pansi m’mapiri, ndipo nthawi zoterozo tinkaphunzira za chilengedwe cha Yehova.”

11, 12. (a) Kodi mungatani kuti muphatikize ena pa zosangalatsa zomwe mukukonza? (b) Kodi ndi kucheza kotani komwe ambiri saiwala?

11 Kodi panokha kapena monga banja mungakonze zoitana anthu ena kuti adzakhale nanu pa zosangalatsa? Anthu monga mkazi wamasiye, munthu wosakwatira, kholo lomwe likulera lokha ana, angafune kulimbikitsidwa. (Luka 14:12-14) Mungaphatikizeponso anthu angapo amene angoyamba kumene kusonkhana ndi mpingo, komabe muyenera kusamala kuti ena asacheze ndi anthu omwe angawasokoneze. (2 Timoteo 2:20, 21) Ngati anthu achikulire amavutika kuchoka panyumba pawo, mwina mungakonze zopita ndi chakudya ku nyumba kwawoko n’kukadya nawo limodzi.​—Ahebri 13:1, 2.

12 Ambiri saiwala mmene anachezera atasonkhana ndi anzawo ndi kudya chakudya chomwe amadya nthawi zonse, kumva mmene ena anakhalira Akristu, ndiponso kuphunzira zimene zawathandiza kukhala okhulupirika kwa Mulungu. Mungathe kuyambitsa nkhani za m’Baibulo zoti mukambirane ndi onse amene alipo, kuphatikizapo ana. Zimakhala zolimbikitsa kwambiri kukambirana nkhani ngati zimenezi ndipo palibe amene amachita manyazi kapena kuona kuti sangachitepo kalikonse.

13. Kodi Yesu ndi Paulo anasonyeza motani chitsanzo pankhani yochereza anthu komanso kucherezedwa?

13 Yesu anasonyeza chitsanzo chabwino pankhani yochereza anthu komanso kucherezedwa. Chinali chizolowezi chake kugwiritsa ntchito nthawi yoteroyo kuthandizira anthu mwauzimu. (Luka 5:27-39; 10:42; 19:1-10; 24:28-32) Ophunzira ake oyambirira anatengera chitsanzo chake. (Machitidwe 2:46, 47) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndilakalaka kuonana ndinu, kuti ndikagawire kwa inu mtulo wina wauzimu, kuti inu mukhazikike; ndiko, kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa chikhulupiriro cha ife tonse awiri, chanu ndi changa.” (Aroma 1:11, 12) Nafenso, kucheza kwathu kuyenera kupereka mpata woti tilimbikitsane.​—Aroma 12:13; 15:1, 2.

Zofunika Kukumbukira ndi Kusamala Nazo

14. Kodi n’chifukwa chiyani si bwino kuitana gulu lalikulu ku phwando?

14 Si bwino kuitana gulu lalikulu paphwando chifukwa nthawi zambiri limavuta kuliyang’anira. Mabanja angapo angakonze zopita kokayenda kapena kusewera masewera osalimbikitsa mpikisano, ndipo angakonze kuti achite zimenezi nthawi yomwe sikusokoneza zochita zauzimu. Ngati paphwando pali ena mwa akulu, atumiki othandiza, kapena anthu ena okhwima maganizo mwauzimu zingathandize kuti phwandolo liyende bwino komanso likhale lotsitsimula kwambiri.

15. Kodi n’chifukwa chiyani pokonza phwando m’pofunikanso kuganizira zodzaliyang’anira bwino?

15 Anthu amene akukonza phwando sayenera kunyalanyaza kufunika koyang’anira bwino zochitika paphwandopo. Ngakhale kuti mumakonda kuchereza alendo, kodi simungakhumudwe kumva kuti chifukwa cha kusasamala kwanu, munthu wina wakhumudwa ndi zomwe zinachitika m’nyumba mwanu? Taganizirani mfundo yomwe ili pa Deuteronomo 22:8. Mwisrayeli amene wamanga nyumba yatsopano ankafunika kumanga kampanda pa tsindwi lathyathyathya la nyumbayo, pomwe ankakonda kucherezerapo alendo. Chifukwa chiyani ankatero? ‘Kuti angatengere nyumba yawo mwazi, akagwako munthu.’ Mofanana ndi zimenezi, zomwe mungachite, popanda kuika malire onyanyira, pofuna kuteteza alendo anu paphwando zizikhala ndi cholinga chofunira zabwino anthuwo mwakuthupi ndi mwauzimu.

16. Ngati paphwando pali mowa, kodi m’pofunika kusamala ndi chiyani?

16 Ngati paphwando pangakhale mowa, m’pofunika kusamala kwambiri. Akristu ambiri akamachereza alendo amakonza zopatsa alendowo mowa pokhapokha ngati iwo eniakewo ndiwo ayang’anire za mowa womwe alendowo apatsidwe kapena kumwa. Osalola kuti pakhale chinthu chomwe chingakhumudwitse ena kapena kuwaika pachiyeso chofuna kumwa kwambiri. (Aefeso 5:18, 19) Alendo ena sangafune kumwa mowa pa zifukwa zosiyanasiyana. Madera ambiri ali ndi malamulo oletsa anthu osakwanitsa zaka zinazake kumwa mowa, ndipo Akristu amamvera malamulo a Kaisara ngakhale malamulowo aoneke kuti ndi okhwimitsa zinthu monyanyira.​—Aroma 13:5.

17. (a) Ngati paphwando pali nyimbo, n’chifukwa chiyani wokonza phwandolo ayenera kusankha bwino nyimbozo? (b) Ngati paphwando pakhale kuvina, kodi tingasonyeze motani kudziletsa?

17 Wokonza phwandolo ayenera kuonetsetsa kuti nyimbo, kuvina, kapena zosangalatsa zilizonse zikhale zogwirizana ndi mfundo zachikristu. Anthufe timakonda nyimbo zosiyanasiyana ndipo nazonso nyimbo zilipo mitundumitundu. Koma nyimbo zambiri masiku ano zimalimbikitsa mtima wopanduka, wachiwerewere, ndi wachiwawa. Motero, m’pofunika kuti tizisankha nyimbo zomwe tikufuna kumvera. Sikuti nyimbo zabwino ndi zokhazo zoimbidwa mwachifatse ayi, komanso nyimbo zolimbikitsa kugonana kapena zotukwana, zaphokoso kwambiri si zabwino. Onetsetsani kuti munthu amene akusankha nyimbo amadziwa bwino kuti nyimbo zimafunika kukhala zosakwera kwambiri. N’zodziwikiratu kuti kuvina mwa dama, mokonda kudukula ndi kuvinitsa mawere, n’kosayenera kwa Akristu.​—1 Timoteo 2:8-10.

18. Kodi makolo angateteze motani ana awo ngati akusamala ndi kumene anawo amakacheza?

18 Makolo achikristu ayenera kudziwa zimene zakonzedwa paphwando lomwe ana awo aitanidwa, ndipo nthawi zambiri n’chinthu chanzeru kupita nawo pamodzi. N’zomvetsa chisoni kuti makolo ena alola ana awo kupita ku mapwando opanda munthu woyang’anira, komwe anthu ena amakopeka ndi kuchita zachiwerewere kapena makhalidwe ena oipa. (Aefeso 6:1-4) Ngakhale achinyamata omwe akuyandikira zaka za m’ma 20 ndipo amasonyeza kuti akhoza kuchita zinthu mosamala, m’pofunikabe kuwathandiza ‘kuthawa zilakolako za unyamata.’​—2 Timoteo 2:22.

19. Kodi n’chiyani chingatithandize kuika maganizo athu pa zinthu zofunika kuzifunafuna choyamba?

19 Kukhala ndi zoyenera ndiponso zotsitsimula nthawi zina kungapangitse moyo kukhala wosangalatsa. Yehova satiletsa kusangalala kumeneku, koma timadziwa kuti zochita zoterozo sikuti pazokha zimatithandiza kukundika chuma chauzimu m’mwamba. (Mateyu 6:19-21) Yesu anathandiza ophunzira ake kumvetsetsa kuti ‘kuthanga tafuna Ufumu . . . ndi chilungamo’ cha Mulungu n’kofunika kwambiri m’moyo, osati zimene timadya, kumwa kapena kuvala, zinthu zimene ‘anthu akunja akuzifunitsitsa.’​—Mateyu 6:31-34.

20. Kodi atumiki okhulupirika a Yehova angayembekezere zinthu zabwino zotani kuchokera kwa iye amene amatipatsa zonse?

20 Zoonadi, kaya ‘tikudya, ngakhale kumwa, ngakhale kuchita kanthu kena,’ tingachite “zonse ku ulemerero wa Mulungu,” kuthokoza Mlengi amene amatipatsa zinthu zabwino zoti tisangalale nazo pamlingo wabwino. (1 Akorinto 10:31) M’dziko lake lapansi laparadaiso lomwe layandikira, padzakhala nthawi zambiri zosangalala kwambiri ndi kuwolowa manja kwa Yehova, limodzi ndi kucheza ndi anthu omwe azikwaniritsa zofuna zake zolungama.​—Salmo 145:16; Yesaya 25:6; 2 Akorinto 7:1.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi n’chifukwa chiyani masiku ano Akristu amavutika kupeza zosangalatsa zoyenera?

• Kodi ndi zosangalatsa zotani zomwe zimatsitsimula mabanja achikristu?

• Munthu akakhala pa zosangalatsa, kodi ayenera kukumbukira ndi kusamala ndi zinthu zotani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 18]

Sankhani zosangalatsa zomwe zimabala zipatso zabwino

[Zithunzi patsamba 19]

Kodi ndi zosangalatsa zotani zimene Akristu amakana?