Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Abale Atsopano a M’bungwe Lolamulira

Abale Atsopano a M’bungwe Lolamulira

Abale Atsopano a M’bungwe Lolamulira

LACHITATU m’mawa, pa August 24, 2005, mabanja a Beteli a ku United States ndi ku Canada, anamva chilengezo chochititsa chidwi kwambiri atalumikizidwa pa vidiyo. Chilengezocho chinali chakuti kuyambira pa September 1, 2005, Bungwe Lolamulira lidzakhala ndi abale awiri atsopano: Geoffrey W. Jackson ndi Anthony Morris III.

Mbale Jackson anayamba upainiya mu February 1971 ku Tasmania, chilumba cha ku Australia. Mu June 1974, iye anakwatira Jeanette (Jenny). Pambuyo pake iwowa anaikidwa kukhala apainiya apadera. Kuchokera mu 1979 mpaka 2003, anali amishonale ku zilumba za ku South Pacific zotchedwa Tuvalu, Samoa, ndi Fiji. Ali pa zilumbazi, Mbale ndi Mlongo Jackson anathandizanso kwambiri pa ntchito yomasulira mabuku ofotokoza za m’Baibulo. Kuyambira mu 1992, Mbale Jackson anali mu Komiti ya Nthambi ya ku Samoa, ndipo kuyambira mu 1996, anali mu Komiti ya Nthambi ya ku Fiji. Mu April 2003, mbaleyu ndi mkazi wake Jenny anayamba kutumikira pa banja la Beteli la ku United States mu Dipatimenti Yothandiza Otembenuza. Posakhalitsa Mbale Jackson anaikidwa kukhala wothandizira Komiti Yophunzitsa ya Bungwe Lolamulira.

Mbale Morris anayamba utumiki wa upainiya mu 1971 ku United States. Mu December chaka chomwecho anakwatira Susan, ndipo anapitiriza kuchita upainiya kwa zaka pafupifupi zinayi mpaka pamene anadzakhala ndi mwana wawo woyamba Jesse, yemwe anali wamwamuna. Kenaka, anadzakhalanso ndi mwana wina wamwamuna dzina lake Paul. Mbale Morris anayambiranso utumiki wa nthawi zonse mu 1979 monga mpainiya wokhazikika. Ana awo aja atayamba sukulu mkazi wawo anayambanso utumikiwu. Banjali linkatumikira ku Rhode Island ndi ku North Carolina, m’dziko la United States, komwe kunalibe alaliki okwanira. Ku North Carolina, Mbale Morris anali woyang’anira dera wogwirizira, ndipo ana awo aja anayamba upainiya wokhazikika. Anyamata awiri onsewa anaitanidwa kukatumikira ku ofesi ya nthambi ya United States ali ndi zaka 19. Apa n’kuti Mbale Morris atayamba ntchito yoyang’anira dera. Kenaka, mu 2002 iwo ndi mkazi wawo Susan anaitanidwa ku Beteli, ndipo utumiki wawo anauyamba pa August 1. Mbale Morris ankagwira ntchito mu Dipatimenti ya Utumiki ku Patterson ndipo kenaka ankagwira ntchito yothandiza Komiti ya Utumiki ya Bungwe Lolamulira.

Kuphatikiza pa abale awiriwa, m’Bungwe Lolamulira muli mbale C. W. Barber; J. E. Barr; S. F. Herd; M. S. Lett; G. Lösch; T. Jaracz; G. H. Pierce; A. D. Schroeder; D. H. Splane; ndi D. Sydlik. Abale onse a m’Bungwe Lolamulira ndi Akristu odzozedwa.