Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dzasonkhaneni Nafe Lachitatu, pa April 12

Dzasonkhaneni Nafe Lachitatu, pa April 12

Dzasonkhaneni Nafe Lachitatu, pa April 12

Tsiku Lofunika Kulikumbukira

Usiku, patsiku lomwe anaphedwa, Yesu Kristu anakhazikitsa Chikumbutso cha imfa yake. Yesu anagwiritsira ntchito vinyo ndi mkate wopanda chotupitsa m’njira yophiphiritsira ndipo analamula kuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.”​—Luka 22:19.

Pomvera lamulo la Yesuli, Mboni za Yehova zikukuitanani kuti mukakhale nawo pa mwambo wa chaka n’chaka umenewu. Onani kuseri kwa kapepalaka kapena funsani Mboni za Yehova kwanuko kuti mudziwe malo, tsiku ndi nthawi ya msonkhanowu.