Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Imfa Siona Nkhope

Imfa Siona Nkhope

Imfa Siona Nkhope

WOLEMBA mbiri wina wa ku Britain, dzina lake Arnold Toynbee, analemba kuti: “Munthu akangobadwa, imfa imayamba kum’dikira. Ndipo mulimonsemo imadzam’tenga basi.” Imfa ikatenga mbale wathu kapena mnzathu wapamtima, chisoni chathu chimakhala chosaneneka.

Imfa yakhala ikuzunza anthu kwa zakazaka. Munthu amene timam’konda akamwalira, timasowa mtengo wogwira. Imfa sithawika ndipo siona nkhope. Wolemba nkhani wina wa m’zaka za m’ma 1800 analemba kuti: “Tonsefe maliro amatisandutsa ana, ndipo saona maphunziro a munthu. Maliro amaimitsa mutu ngakhale anthu anzeru zogometsa zedi.” N’zoona kuti maliro amatisandutsa ana, chifukwa sitidziwa chochita. Chuma kapena mphamvu sizingaukitse wakufayo. Anthu anzeru ndi ophunzira omwe amaima mutu. Amphamvu ndi ofooka omwe amangogwetsa misozi pa maliro.

Mfumu Davide ya ku Israyeli, nayo inathedwa nzeru mwana wake Abisalomu atamwalira. Davide atamva za malirowo, analira n’kunena kuti: “Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!” (2 Samueli 18:33) Davide anali mfumu yoopeka ndipo anali atagonjetsa adani amphamvu ambiri, koma panthawiyi anafika poona kuti zikanakhala bwino kuti iyeyo, osati mwana wake, ndiye agonjetsedwe ndi “mdani wotsiriza” ameneyu, “imfa.”​—1 Akorinto 15:26.

Kodi pali njira yothetsera imfa? Ngati ilipo kodi tingayembekeze zotani pankhani ya anthu akufa? Kodi anzathu ndiponso abale athu amene anafa tidzawaonanso? Nkhani yotsatirayi ikuyankha mafunso amenewa mogwiritsira ntchito Malemba.