Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kutumikira Mumpingo wa Chinenero China

Kutumikira Mumpingo wa Chinenero China

Kutumikira Mumpingo wa Chinenero China

MTUMWI Yohane analemba kuti: “Ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nawo Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.” (Chivumbulutso 14:6) Pokwaniritsa masomphenya a ulosi amenewa, uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ukulalikidwa padziko lonse m’zinenero zosiyanasiyana. Anthu ambiri olankhula zinenero zimenezi ndi anthu oti asamukira kumayiko ena akutali ndi kwawo. Anthu amenewanso akumva uthenga wabwino womwe Mboni za Yehova zimene zaphunzira chinenero china zikulalikira mwakhama.

Kodi inuyo muli m’gulu la Mboni zimene zikutumikira mumpingo wa chinenero china? Kapena kodi mukuganiza zochita zimenezi? Kuti khama lanu lipindule, musakhale ndi zifukwa zongokomera inuyo ndipo pewani maganizo osalimbikitsa. Popeza mukufuna kuthandiza ena kuphunzira choonadi cha Mawu a Mulungu, ndiye kuti muli n’chifukwa chabwino kwambiri, chomwe ndi kukonda Mulungu ndi anansi anu. (Mateyu 22:37-39; 1 Akorinto 13:1) Kufuna kuthandiza ena kudziwa Mulungu kumalimbikitsa kwambiri kuposa kungofuna kukhalako ndi anthu achikhalidwe china kapenanso kulawa zakudya zawo. Kodi mumaopa kuphunzira chinenero china? Ngati n’choncho ndibwino kuiona bwino nkhaniyi. James, amene anaphunzirapo Chijapanizi anati: “Musaope kuphunzira chinenero china.” Kuzindikira kuti pali anthu ena ambiri amene anaphunzirapo chinenerocho bwinobwino kungakuthandizeni kulimbikirabe ndi kusafooka. Ndiyeno kodi mungaphunzire bwanji chinenero china? N’chiyani chingakuthandizeni kuzolowera mpingo wa chinenerocho? Ndipo mungatani kuti mukhalebe munthu wauzimu?

Kuyamba Kuphunzira Chinenerocho

Pali njira zosiyanasiyana zophunzirira chinenero. Ophunzira ndiponso ophunzitsa amakonda njira zosiyanasiyana. Koma ophunzira ambiri amaphunzira msanga ndiponso mosavuta akamaphunzitsidwa kwa nthawi zingapo ndi mphunzitsi wodziwa bwino ntchito yake. Kuwerenga Baibulo ndiponso mabuku ofokokoza Baibulo m’chinenerocho, ndi kumvetsera matepi kapena ma CD a m’chinenerocho kungakuthandizeni kudziwa mawu osiyanasiyana ndiponso kudziwa mawu ambiri okhudza zinthu zauzimu. Mapulogalamu abwino a pa wailesi ndi pa TV ndi mavidiyo angakuthandizeni kudziwa bwino chinenerocho ndi chikhalidwe cha anthu ake. Ndi bwino kuti tsiku lililonse muziphunzira pang’ono kusiyana ndi kuti muziphunzira modukizadukiza zinthu zambirimbiri nthawi imodzi.

Kuphunzira chinenero china kuli ngati kusambira. Simungaphunzire kusambira powerenga m’buku basi. Muyenera kulowa m’madzi n’kuyamba kudampira. N’chimodzimodzinso ndi kuphunzira chinenero china. M’povuta kuchiphunzira powerenga basi. Muyenera kumachita zinthu ndi anthu paliponse pamene mungathe, muzimvetsera mmene akulankhulira, muzicheza nawo, ndipo chachikulu yesetsani kumalankhula nawo! Zochitika zachikristu zimatipatsa mwayi wabwino kwambiri wochitira zimenezi. Nthawi zambiri, zimene mwaphunzira mungathe kuzigwiritsa ntchito nthawi yomweyo mukalowa muutumiki wa m’munda. Midori yemwe akuphunzira Chitchainizi anati: “Zimachititsa mantha, koma eninyumba amaona kuti a Mbonife timayesetsa. Motero angathe kukhudzidwa nazo mtima. Amasangalala kwambiri tikangowauza m’chinenero chawo kuti, ‘Ndasangalala kuti tadziwana.’”

Misonkhano yachikristu imathandizanso kwambiri. Pa msonkhano uliwonse yesetsani kuyankhapo ngakhale kamodzi kokha. Poyamba mungachite mantha kwambiri, koma musadandaule. Mpingo wonsewo ukufuna kuti muphunzire chinenerocho. Monifa, yemwe akuphunzira Chikoleya anati: “Ndimayamikira kwambiri mlongo amene ndimayandikana naye kumisonkhano, yemwe amandilembera matanthauzo a mawu osiyanasiyana. Ndimathandizidwa kwambiri chifukwa cha chikondi ndi kuleza mtima kwake.” Mukayamba kudziwa mawu ambiri, mungathe kuyamba kuganiza m’chinenero chatsopanocho, motero mumaganizira za mawu a chinenerocho mogwirizana ndi matanthauzo ake m’chinenerocho osati kumachita kumasulira liwu lililonse kuchokera ku chinenero chanu.

Cholinga chanu choyamba pophunzira chinenerocho chizikhala kulankhula “mawu omveka bwino.” (1 Akorinto 14:8-11) Ngakhale kuti anthu amatha kudziwa zimene mukutanthauza, kulankhula chinenero chothyokathyoka kapena kulankhula mochita kumvekeratu kuti si chinenero chanu kungathe kuchititsa kuti anthuwo asamve bwino uthenga wanu. Mukangoyamba kuphunzira chinenerocho, yesetsani kukhala osamala pa katchulidwe ka mawu ndiponso pa malamulo a chinenerocho. Zimenezi zimathandiza kuti musadzavutike m’tsogolo poyesa kusiya zizolowezi zoipa. Mark, yemwe anaphunzira Chiswahili anati: “Funsani anthu amene amalankhula bwino chinenerocho kuti azikukonzani zinthu zimene mukulakwitsa kwambiri, ndipo pambuyo pake muziwathokoza!” Koma ndi bwinonso kuganizira nthawi ndiponso mphamvu zimene iwo akuwononga. Ngakhale kuti mungathe kufunsa ena kuti akuonereni zimene mwakonzekera, yesetsani kukonzekera nkhani ndiponso mayankho anu pogwiritsa ntchito mawu amene mukudziwa kale kapena amene mwaona matanthauzo ake. Zimenezi zimakuthandizani kuphunzira mwamsanga ndipo mumalankhula molimba mtima.

Pitirizanibe Kulimbikira

Monifa anati: “Chinthu chovuta kwambiri chimene ndachitapo m’moyo wanga ndicho kuphunzira chinenero china. Nthawi zina ndimaganiza zongosiya basi. Koma ndimaganizira chidwi chofuna kuphunzira choonadi chimene anthu amene ndikuphunzira nawo Baibulo amaonetsa ngakhale kuti Chikoleya changa n’cholumira. Ndimaganiziranso chisangalalo chimene abale amakhala nacho ngakhale ndikamachita bwino pang’ono chabe.” Pamenepa mfundo n’njakuti, osafulumira kusiya ayi. Cholinga chanu ndicho kuphunzitsa anthu choonadi chopulumutsa moyo. (1 Akorinto 2:10) Motero, kuphunzira chinenero china n’kumaphunzitsa anthu Baibulo m’chinenerocho kumafunika khama ndipo kumatenga nthawi. Musamadziyekezere ndi anzanu n’kumaona ngati kuti inuyo sizikukuyenderani bwino. Pophunzira chinenero china anthu amapita patsogolo pa liwiro losiyana ndiponso m’njira zosiyanasiyana. Komabe, zimathandiza kudziwa mmene inuyo panokha mukupitira patsogolo. (Agalatiya 6:4) Joon, amene akuphunzira Chitchainizi anati: “Kuphunzira chinenero kuli ngati kukwera masitepesi, umati kukwera n’kuima, kukwera n’kuima. Motero nthawi zina mukamaona ngati kuti mwaima, mumangozindikira kuti mwafika pena.”

Kuphunzira chinenero china ndi ntchito ya moyo wonse. Motero muzisangalala pophunzira chinenerocho, ndipo musamalimbane n’kuchita zinthu molondola nthawi zonse. (Salmo 100:2) Simungalephere kulakwitsa. Kulakwitsa ndi mbali ya kuphunzira. Mkristu wina atayamba kulalikira mu Chitaliyana, anafunsa mwininyumba kuti, “Kodi tsache la moyo mumalidziwa?” Iyeyu amafuna kunena kuti “cholinga cha moyo.” Wamboni wina amene akuphunzira Chipolishi anapempha abale ndi alongo mumpingo kuti aimirire n’kuimba galu m’malo monena kuti nyimbo. Ndipo chifukwa cholakwitsa pang’ono katchulidwe ka mawu enaake, munthu wina amene ankaphunzira Chitchainizi anauza anthu kuti azikhulupirira shelufu ya mabuku ya Yesu m’malo monena kuti azikhulupirira dipo. Ubwino wa kulakwitsa n’ngwakuti kumakuthandizani kusaiwala njira yolondola yonenera mawuwo.

Kuthandiza Mumpingo

Sikuti ndi zinenero zokha zimene zimagawanitsa anthu. Nthawi zambiri kusiyana kwa chikhalidwe, mafuko, ndiponso mayiko ndiko kumagawanitsa anthu kwambiri. Komabe, zinthu zimenezi n’zotheka kuzithetsa. Munthu wina wophunzira yemwe anachita kafukufuku wokhudza magulu achipembedzo a chinenero cha Chitchainizi ku Ulaya ananena kuti Mboni za Yehova “siziona mtundu wa munthu.” Iye anati pakati pa Mboni za Yehova “nkhani ya mtundu wa munthu ilibe kanthu, ndipo chinenero amangochiona ngati njira yophunzirira mawu a Mulungu.” N’zoona kuti kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo n’kumene kumathandiza Akristu oona kuiwalako za kusiyana kwa mitundu yawo. Kwa amene ‘anavala umunthu watsopano palibe Mhelene ndi Myuda kapena wochoka kunja.’​—Akolose 3:10, 11.

Motero, anthu onse mumpingo ayenera kuyesetsa kulimbikitsa mgwirizano. Kuti atero ayenera kuzolowera mmene anthu a chinenero chatsopanocho amaganizira, mmene amamvera ndiponso mmene amachitira zinthu. Mungapewe kudzigawanitsa ndi anthu a mtundu winawo posaumirira kwambiri zokonda zanu. (1 Akorinto 1:10; 9:19-23) Phunzirani kukonda mbali zabwino za zikhalidwe zonse. Musaiwale kuti chikondi chenicheni ndicho chinthu chofunikira kwambiri kuti mukhale ndi mgwirizano weniweni.

Mipingo yambiri ya zinenero zina imayamba ngati timagulu ting’onoting’ono, ndipo nthawi zambiri anthu ochuluka mumpingomo amakhala amene akuphunzira chinenero china, pamodzi ndi ena amene angoyamba kumene kuphunzira mfundo za m’Baibulo. Motero, m’magulu ngati amenewa m’posavuta kusemphana mawu ndi munthu poyerekezera ndi mipingo yokhazikika bwinobwino. Choncho, zochita za Akristu omwe ali achikulire mwauzimu ziyenera kukhala zothandiza kuti mipingoyi ikhale yabata. Mawu ndiponso zochita zosonyeza chikondi ndiponso kukoma mtima zimathandiza kuti mumpingo mukhale mzimu wabwino kuti atsopano azitha kukula mwauzimu.

Anthu amene adzipereka kukathandiza kumpingo wa chinenero china ayeneranso kudziwa kuti pali zinthu zina zimene ena sangathe kuchita bwinobwino. Rick, yemwe ndi mkulu mu mpingo wina wotere, analongosola kuti: “Abale ena achatsopano mwina sangadziwe kuyendetsa zinthu bwinobwino mumpingo mofanana ndi abale a m’mipingo yokhazikika. Komabe ngakhale atapanda maluso ena iwowa amakhala achikondi ndiponso ansangala kwambiri. Ndipotu anthu ambiri achidwi akubwera m’choonadi.” Mukamayesetsa nthawi zonse kupezeka pa misonkhano ndi pa zochitika zina mumpingo ndi kudzipereka m’njira ina iliyonse imene mungathe, mungapindulitse kwambiri mpingo, ngakhale musanadziwe kwenikweni chinenerocho. Pochita zinthu mogwirizana, aliyense angathandize kuti mpingo upite patsogolo mwauzimu.

Kukhalabe Olimba Mwauzimu

Mbale wina watsopano mumpingo wa chinenero china anamva mlongo wina akuthandiza mwana wake kukonzekera ndemanga. Mwanayo anati: “Amayi, kodi sitingafupikitse yankholi?” Mlongoyo anayankha kuti: “Ayi, mayankho aafupi tisiyire amene akuphunzira chinenero.”

Kwa munthu wamkulu, zimakhala zofooketsa ndiponso zolefula mwauzimu ngati sukutha kulankhula bwinobwino kwa miyezi kapenanso zaka zingapo. Janet, amene tsopano amalankhula bwinobwino Chisipanishi akukumbukira kuti: “Sindinkachedwa kukhumudwa ndikamalankhula Chisipanishi chothyokathyoka.” Hiroko, amene anaphunzira Chingelezi, akukumbukira kuti panthawiyo ankaganiza kuti, ‘Ngakhale agalu ndi amphaka a m’gawoli akudziwa mawu ambiri a Chingelezi kuposa ine.’ Ndipo Kathie anati: “Ngakhale kuti ndinali ndi maphunziro a Baibulo ambiri ndipo kope langa linali lodzaza ndi maulendo obwereza, nditasamukira mumpingo wa Chisipanishi, ndinapezeka kuti ndilibe ngakhale phunziro limodzi. Ndinkangoona kuti palibe chimene ndikuchita.”

Pamenepa m’pamene pamafunika kuganiza zinthu zolimbikitsa. Hiroko atafooka anati: “Ngati ena akutha, ndiye kuti inenso ndingathe.” Kathie anati: “Ndinkadzilimbitsa mtima ndikaganizira za mwamuna wanga, yemwe akupita patsogolo kwambiri ndipo akuthandiza kwambiri mumpingo. Ndikudziwa kuti ntchito idakalipo, komabe pang’ono ndi pang’ono kulalikira ndi kuphunzitsa anthu Baibulo kwayamba kundiphwekera moti ndikusangalala.” Mwamuna wake Jeff, anavomereza kuti: “N’zokhumudwitsa ukamapanda kumva zinthu zonse zimene zikulengezedwa ku mpingo ndiponso zimene zikunenedwa pa misonkhano ya akulu. Ndimayenera kudzichepetsa n’kupempha ena kuti andilongosolere zonse zimene zanenedwa, ndipo abale amandithandizadi.”

Kuti musafooke mwauzimu, panthawi imene muli mumpingo wachinenero china, muyenera kuonetsetsa kuti simukunyalanyaza thanzi lanu lauzimu. (Mateyu 5:3) Kazuyuki, amene wakhala akutumikira m’gawo la Chipwitikizi kwa zaka zambiri anati: “Ndibwino kudya chakudya chauzimu chokwanira. N’chifukwa chake pa banja lathu, tonse timawerenga ndi kukonzekera misonkhano limodzi m’chinenero chathu ndiponso m’Chipwitikizi.” Ena amapita ku misonkhano ya m’chinenero chawo nthawi ndi nthawi. Komanso dziwani kuti kupuma mokwanira n’kofunika zedi.​—Marko 6:31.

Kuwerengera Mtengo

Ngati mukuganiza zosamukira ku mpingo wa chinenero china, muyenera kuwerengera kaye mtengo wochitira zimenezo. (Luka 14:28) Muyenera kuganizira kwambiri za moyo wanu wauzimu ndi ubwenzi wanu ndi Yehova. Pempherani kwa Yehova kuti akuthandizeni kuona bwinobwino mmene zinthu zilili m’moyo wanu. Ganiziraninso mkazi kapena mwamuna wanu komanso ana anu. Dzifunseni kuti, ‘Kodi zinthu zili bwino m’moyo wanga moti ndalimbadi mtima ndiponso ndakonzeka mwauzimu kuyambapo ntchito yotenga nthawi yaitali ngati imeneyi?’ N’chinthu chanzeru kuyesetsa mmene mungathere kuchita zinthu zokuthandizani ndiponso zothandiza banja lanu mwauzimu. Ngati muli wofalitsa waufumu, mumakhala ndi zochita zambiri ndiponso wosangalala kulikonse kumene mukutumikira.

Pali zabwino zambiri kwa anthu amene angathe kutumikira mumpingo wachinenero china. Barbara, yemwe anasamukira ku mpingo wa Chisipanishi pamodzi ndi mwamuna wake anati: “Ichi n’chimodzi mwa zinthu zimene ndasangalala nazo kwambiri m’moyo wanga. Zimakhala ngati wayambiranso kuphunzira choonadi. Ndimayamikira kwambiri mwayi umenewu, makamaka chifukwa choti ifeyo sitingathe kukakhala amishonale ku dziko lina.”

Padziko lonse, anthu ambirimbiri a zaka zosiyanasiyana akuphunzira chinenero china pofuna kupititsa patsogolo uthenga wabwino. Ngati muli m’gulu la anthu amenewa, khalani ndi zifukwa zabwino ndipo pewani maganizo osalimbikitsa. Ndipo chofunika kwambiri n’chakuti dalirani Yehova kuti adalitse khama lanu.​—2 Akorinto 4:7.

[Chithunzi patsamba 18]

Kuphunzitsidwa chinenero ndi mphunzitsi wodziwa bwino ntchito yake kumakuthandizani kuphunzira mwamsanga ndiponso mosavuta

[Chithunzi patsamba 20]

Mukamaphunzira chinenero china, osanyalanyaza moyo wanu wauzimu