Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani ‘Yophiphiritsira’ Yofunika kwa Ife

Nkhani ‘Yophiphiritsira’ Yofunika kwa Ife

Nkhani ‘Yophiphiritsira’ Yofunika kwa Ife

ZIKANAKHALA zovuta kwambiri kumvetsetsa mbali zina za m’Baibulo zikanapanda kufotokozedwanso m’Baibulo momwemo. Nkhani za m’Baibulo zonena za zinthu zomwe zinachitika kale nthawi zina zimangokhala zokhudza nkhani zimenezozo basi. Koma zina mwa nkhani zimenezi zimakhala ndi mfundo zakuya za choonadi zimene munthu sangathe kuzizindikira mosavuta. Chitsanzo chimodzi cha nkhani zoterezi ndi nkhani ya akazi awiri a m’banja la kholo lathu lakale, Abrahamu. Mtumwi Paulo anati nkhani imeneyo ndi ‘yophiphiritsira.’​—Agalatiya 4:23.

Nkhani imeneyi ndi yofunika kuti tiiganizire bwino chifukwa zomwe imaphiphiritsira n’zofunika kwambiri kwa anthu onse amene amafuna kudalitsidwa ndi Yehova Mulungu. Tisanaone chifukwa chake zili choncho, tiyeni tifotokoze bwino zinthu zimene zinachititsa Paulo kuulula tanthauzo la nkhani imeneyi.

Pakati pa Akristu oyambirira a ku Galatiya panali mavuto. Ena a iwo anali kusunga “masiku, ndi miyezi, ndi nyengo, ndi zaka,” zinthu zomwe zinali m’Chilamulo cha Mose. Anthu amenewa ankanena kuti, kuti anthu okhulupirira ayanjidwe ndi Mulungu, anafunika kumvera Chilamulo. (Agalatiya 4:10; 5:2, 3) Koma Paulo ankadziwa kuti Akristu sankafunika kutero. Kuti asonyeze zimenezi, anafotokoza nkhani imene Myuda aliyense ankaidziwa bwino.

Paulo anakumbutsa Agalatiyawo kuti Abrahamu, tate wa fuko la Ayuda, anabereka Ismayeli ndi Isake. Ismayeli anabadwa kwa Hagara, yemwe anali mdzakazi, ndipo Isake anabadwa kwa Sara, yemwe anali mfulu. Anthu okhala ku Galatiya amene ankalimbikitsa zomvera Chilamulo cha Mose mosakayikira ankadziwa nkhani yonena za momwe Sara analili wosabereka poyamba ndi momwe anapatsira Abrahamu mdzakazi wake Hagara kuti amuberekere mwana m’malo mwake. Ankadziwanso kuti Hagara atabereka Ismayeli, anayamba kunyoza akuka ake, Sara. Koma mogwirizana ndi lonjezo la Mulungu, Sara pamapeto pake anabereka Isake mu ukalamba wake. Kenaka Abrahamu anathamangitsa Hagara ndi Ismayeli chifukwa Ismayeli ankazunza Isake.​—Genesis 16:1-4; 17:15-17; 21:1-14; Agalatiya 4:22, 23.

Akazi Awiri, Mapangano Awiri

Paulo anafotokoza tanthauzo la zinthu zotchulidwa mu nkhani ‘yophiphiritsirayi.’ Iye analemba kuti: “Akaziwa ali mapangano awiri, mmodzi wa ku phiri la Sinai, akubalira ukapolo, ndiye Hagara. . . . Nafanana ndi Yerusalemu watsopano; pakuti ali muukapolo pamodzi ndi ana ake.” (Agalatiya 4:24, 25) Hagara ankaimira Israyeli weniweni, yemwe likulu lake linali Yerusalemu. Mtundu wa Ayuda unali pa pangano ndi Yehova chifukwa cha pangano la Chilamulo lomwe linakhazikitsidwa pa phiri la Sinai. Kudzera m’pangano limeneli, Aisrayeli nthawi zonse ankakumbutsidwa kuti anali akapolo a uchimo ndipo ankafunika kumasulidwa.​—Yeremiya 31:31, 32; Aroma 7:14-24.

Choncho, kodi Sara, yemwe anali mkazi ‘waufulu,’ ndi mwana wake Isake ankaimira chiyani? Paulo anafotokoza kuti Sara, yemwe anali “chumba,” kapena kuti wosabereka, ankaimira mkazi wa Mulungu, kapena kuti gulu la Mulungu lakumwamba. Mkazi wakumwamba ameneyu anali chumba m’lingaliro lakuti Yesu asanabwere, mkaziyo analibe “ana” odzozedwa ndi mzimu padziko lapansi. (Agalatiya 4:27; Yesaya 54:1-6) Koma pa Pentekoste wa mu 33 C.E., mzimu woyera unatsanuliridwa pa gulu la amuna ndi akazi amene panthawi imeneyo anabadwanso ngati ana a mkazi wakumwamba ameneyu. Ana amene anabadwa kwa gulu limeneli anayamba kuonedwa ngati ana a Mulungu ndipo anakhala olowa nyumba anzake a Yesu Kristu mu pangano latsopano. (Aroma 8:15-17) Mmodzi mwa ana amenewa, mtumwi Paulo, analemba kuti: ‘Yerusalemu wakumwamba ali waufulu, ndiwo amayi wathu.’​—Agalatiya 4:26.

Ana a Akazi Awiriwo

Malinga ndi nkhani ya m’Baibulo, Ismayeli ankazunza Isake. Mofanana ndi zimenezi, Chikristu chitangoyamba kumene, ana a Yerusalemu, yemwe anali paukapolo, ankanyoza ndi kuzunza ana a Yerusalemu wakumwamba. Paulo anafotokoza kuti: “Monga pompaja iye wobadwa monga mwa thupi [Ismayeli] anazunza wobadwa monga mwa Mzimu [Isake], momwemonso tsopano.” (Agalatiya 4:29) Yesu Kristu ataonekera pa dziko lapansi n’kuyamba kulengeza za Ufumu, atsogoleri achipembedzo achiyuda anachita zinthu zofanana ndi zimene Ismayeli, mwana wa Hagara, anachitira wolowa nyumba weniweni wa Abrahamu, Isake. Ananyoza ndi kuzunza Yesu Kristu, ndipo zikuoneka kuti ankadziona kuti iwowo ndiwo ana enieni a Abrahamu oyenera kulowa ufumu, pamene Yesu ankamuona ngati wongobwera.

Atsogoleri a Aisrayeli atatsala pang’ono kumupha, Yesu anati: “Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m’mapiko ake, koma inu simunafuna ayi! Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.”​—Mateyu 23:37, 38.

Nkhani youziridwa yonena zomwe zinachitika kalelo imasonyeza kuti mtundu wa Israyeli womwe unkaimiridwa ndi Hagara sunatulutse ana amene akanadzakhala olowa nyumba limodzi ndi Yesu. Ayuda amene modzitukumula ankakhulupirira kuti anali oyenerera kulandira cholowa chimenecho chifukwa cha mtundu wawo anakanidwa ndi Yehova ndipo anatayidwa kunja. N’zoona kuti Aisrayeli ena anadzakhala olowa nyumba limodzi ndi Kristu. Komabe, anapatsidwa mwayi umenewu chifukwa cha chikhulupiriro chawo mwa Yesu, osati chifukwa cha mtundu wawo.

Ena mwa anthu olowa nawo nyumba limodzi ndi Kristu amenewa anadzadziwika pa Pentekoste wa mu 33 C.E. Pamene nthawi inali kupita, Yehova anadzoza anthu ena kuti nawonso akhale ana a Yerusalemu wakumwamba.

Cholinga cha Paulo pofotokoza nkhani ‘yophiphiritsira’ imeneyi chinali kufuna kusonyeza kupambana kwa pangano latsopano poliyerekezera ndi pangano la Chilamulo lomwe mkhalapakati wake anali Mose. Palibe amene akanatha kuyanjidwa ndi Mulungu chifukwa chotsatira bwino Chilamulo cha Mose, chifukwa anthu onse ndi opanda ungwiro ndipo Chilamulo chinangoonetsa poyera ukapolo wawo ku uchimo. Komabe, monga momwe Paulo anafotokozera, Yesu anabwera “kuti akawombole iwo akumvera lamulo.” (Agalatiya 4:4, 5) Choncho kukhulupirira nsembe ya Kristu kunabweretsa ufulu womasula munthu ku ukapolo wa Chilamulo.​—Agalatiya 5:1-6.

Kufunika kwa Nkhaniyi kwa Ife

Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi chidwi ndi zomwe Paulo anafotokoza zokhudza nkhaniyi? Chifukwa chimodzi n’choti zimatithandiza kumvetsa bwino zinthu za m’Malemba zomwe sitikanazidziwa. Zimene anafotokozazi zimalimbitsa chikhulupiriro chathu choti Baibulo lonse n’logwirizana.​—1 Atesalonika 2:13.

Komanso, zinthu zimene zinkaimiridwa ndi nkhani imeneyi n’zofunika kuti ifeyo tidzakhale ndi chimwemwe m’tsogolo. Ana a Yerusalemu wakumwamba akanati asanaonekere, chiyembekezo chathu chikanangokhala ukapolo ku uchimo ndi imfa basi. Koma poyang’aniridwa mwachikondi ndi Kristu limodzi ndi olamula anzake a lonjezo la Mulungu kwa Abrahamu, “mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa.” (Genesis 22:18) Zimenezi zidzachitika anthu akadzamasukiratu ku zotsatirapo za uchimo, kupanda ungwiro, chisoni, ndi imfa. (Yesaya 25:8, 9) Imeneyo idzakhaladi nthawi yosangalatsa kwambiri.

[Chithunzi patsamba 11]

Pangano la Chilamulo linakhazikitsidwa pa phiri la Sinai

[Mawu a Chithunzi]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

[Chithunzi patsamba 12]

Kodi nkhani ‘yophiphiritsira’ imene Paulo anafotokoza imatanthauza chiyani?