Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pewani Kulambira Konyenga!

Pewani Kulambira Konyenga!

Pewani Kulambira Konyenga!

“Tulukani pakati pawo, ndipo patukani, ati Ambuye, ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka.”​—2 AKORINTO 6:17.

1. Kodi anthu ambiri oona mtima moyo wawo wauzimu n’ngotani?

ANTHU ambiri oona mtima sadziwa zoona zake za Mulungu ndiponso za tsogolo la anthu. Motero amasokonezeka kwambiri chifukwa chosadziwa zoona pa nkhani zimenezi, zomwe n’zofunika kwambiri pa moyo wawo wauzimu. Anthu ambirimbiri amavutika chifukwa cha zikhulupiriro, miyambo, ndi zikondwerero zosakondweretsa Mlengi. N’zotheka kuti anansi kapena abale anu enaake amakhulupirira zoti anthu oipa akapsa kumoto, zoti mwa Mulungu muli anthu atatu, zoti pali chinachake mwa munthu sichifa munthuyo akafa, kapena ziphunzitso zina zabodza.

2. Kodi atsogoleri azipembedzo achita zotani, ndipo zimenezi zapangitsa chiyani?

2 Kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri ali mumdima wauzimuwu? N’zodabwitsa kuti n’chifukwa cha chipembedzo, makamaka magulu komanso atsogoleri a zipembedzo amene akhala akulimbikitsa maganizo otsutsana ndi maganizo a Mulungu. (Marko 7:7, 8) Chifukwa cha zimenezi anthu ambiri anyengedwa n’kukhulupirira kuti akulambira Mulungu woona, pamene kwenikweni akuchita zinthu zomuipira. Zonsezi n’chifukwa cha zipembedzo zonyenga.

3. Kodi ndani ali patsogolo polimbikitsa kulambira konyenga, ndipo Baibulo limalongosola chiyani za iye?

3 Pali munthu wina wosaoneka amene akulimbikitsa zipembedzo zonyenga. Mtumwi Paulo ananena za munthu ameneyu motere: ‘Mulungu wa nthawi ino ya pansi pano anachititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.’ (2 Akorinto 4:4) ‘Mulungu wa nthawi ino ya pansi pano’ si wina ayi koma Satana Mdyerekezi. Iyeyu ndiye ali patsogolo polimbikitsa kulambira konyenga. Paulo analemba kuti: “Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika. Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumiki ake adzionetsa monga atumiki a chilungamo.” (2 Akorinto 11:14, 15) Satana amachititsa kuti zinthu zoipa zizioneka ngati zabwino ndipo amanyenga anthu kukhulupirira mabodza.

4. Kodi Chilamulo cha Mulungu kwa Aisrayeli chinati chiyani pankhani ya aneneri onyenga?

4 N’chifukwa chake Baibulo limaletseratu kulambira konyenga. Mwachitsanzo, pankhani ya aneneri onyenga, anthu osankhidwa a Mulungu anachenjezedwa mosapita m’mbali ndi Chilamulo cha Mose. Aliyense wolimbikitsa ziphunzitso zabodza ndiponso kulambira konyenga anayenera kuphedwa chifukwa choti “ananena chosiyanitsa ndi Yehova.” Aisrayeli anawalamula kuti ‘azichotsa choipacho pakati pawo.’ (Deuteronomo 13:1-5) Inde, Yehova amaona kuti kulambira konyenga n’chinthu choipa kwambiri.​—Ezekieli 13:3.

5. Kodi ndi machenjezo otani amene tiyenera kuwamvera masiku ano?

5 Mofanana ndi Yehova, Yesu Kristu ndi atumwi ake ankadananso kwambiri ndi kulambira konyenga. Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Yang’anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m’kati mwawo ali afisi olusa.” (Mateyu 7:15; Marko 13:22, 23) Paulo analemba kuti “mkwiyo wa Mulungu, wochokera kumwamba, uonekera pa chisapembedzo chonse ndi chosalungama cha anthu, amene akanikiza pansi choonadi.” (Aroma 1:18) Akristu oona akufunika kumvera machenjezo amenewa n’kupewa aliyense amene akukanikizira pansi choonadi cha Mawu a Mulungu kapena amene akufalitsa ziphunzitso zabodza.​—1 Yohane 4:1.

Chokani mu ‘Babulo Wamkulu’

6. Kodi ‘Babulo Wamkulu’ anamufanizira ndi chiyani m’Baibulo?

6 Taganizirani zimene buku la Chivumbulutso limanena pankhani ya zipembedzo zonyenga. Limazifanizira ndi hule loledzera lomwe lili ndi mphamvu pa mafumu ndi mitundu yambirimbiri ya anthu. Mkazi wophiphiritsirayu akuchita chigololo ndi mafumu ambiri ndipo waledzera ndi magazi a olambira oona a Mulungu. (Chivumbulutso 17:1, 2, 6, 18) Iyeyu ali ndi dzina lolembedwa pamphumi pake logwirizana ndi khalidwe lake lonyansalo. Dzina lake ndi ‘Babulo Wamkulu, amayi wa achigololo ndi wa zonyansitsa za dziko.’​—Chivumbulutso 17:5.

7, 8. Kodi zipembedzo zonyenga zachita chigololo m’njira yotani, ndipo zotsatirapo zake n’zotani?

7 Zimene Malemba amafotokoza zokhudza Babulo Wamkulu zimagwirizanadi ndi zipembedzo zonse zonyenga padziko lapansi. Ngakhale kuti zipembedzo zambirimbiri zimene zilipozi sizogwirizana monga gulu limodzi, koma cholinga chawo n’chimodzi. Ngati hule la m’buku la Chivumbulutso, zipembedzo zonyenga zili ndi mphamvu zambiri pa maboma. Monga mkazi wosakhulupirika ku lumbiro lake la ukwati, zipembedzo zonyenga nazo zakhala zikugwirizana ndi maboma osiyanasiyana a ndale. Wophunzira Yakobo anati: “Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.”​—Yakobo 4:4.

8 Kulowerera kwa zipembedzo zonyenga m’ndale za mayiko kwaika anthu m’mavuto adzaoneni. Katswiri wina wa ndale ku Africa kuno Dr. Xolela Mangcu anati “mbiri ya anthu n’njodzaza ndi zitsanzo za anthu ambirimbiri amene apululuka chifukwa chakuti zipembedzo zimalowerera m’ndale.” Posachedwapa nyuzipepala ina inati: “Nkhondo zoopsa ndiponso zimene zapulula anthu ambiri masiku ano . . . zimayambira pa zipembedzo.” Anthu ambirimbiri ataya moyo wawo m’nkhondo zolimbikitsidwa ndi zipembedzo. Babulo Wamkulu wazunzanso ndi kupha atumiki oona a Mulungu, ndipo, m’njira yophiphiritsira, iye waledzera ndi magazi awo.​—Chivumbulutso 18:24.

9. Kodi buku la Chivumbulutso limasonyeza motani chidani chimene Yehova ali nacho pa kulambira konyenga?

9 Umboni wakuti Yehova amadana ndi kulambira konyenga n’ngwakuti Baibulo limanena kuti Babulo Wamkulu adzaona zakuda. Lemba la Chivumbulutso 17:16 limati: “Nyanga khumi udaziona, ndi chilombo, izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo, nizidzam’khalitsa wabwinja wausiwa, nizidzadya nyama yake, nizidzam’psereza ndi moto.” Choyamba, chilombo chachikulu chidzam’khadzula n’kumupha kenaka n’kudya m’nofu wake. Ndiyeno thupi lonse lotsala pamenepo lidzaotchedwa. Izi n’zofanana ndi zimene posachedwapa maboma a padziko lonse adzachite ku zipembedzo zonyenga. Mulungu ndiye adzachititse zimenezi. (Chivumbulutso 17:17) Babulo Wamkulu, kapena kuti ufumu wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga, udzawonongedwa. “Sudzapezedwanso konse.”​—Chivumbulutso 18:21.

10. Kodi zipembedzo zonyenga tiyenera kuziona motani?

10 Kodi Akristu oona ayenera kumuona motani Babulo Wamkulu? Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti: “Tulukani mmenemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake.” (Chivumbulutso 18:4.) Amene akufuna kudzapulumuka ayenera kuchoka m’zipembedzo zonyenga nthawi isanathe. Yesu Kristu ali padziko lapansi analosera kuti m’masiku otsiriza, padzakhala anthu ambiri onena mwachinyengo kuti akum’tsatira iyeyo. (Mateyu 24:3-5) Anthu oterewa iye adzawakana kuti: “Sindinakudziwani inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusayeruzika.” (Mateyu 7:23) Yesu Kristu, yemwe tsopano anaikidwa kukhala Mfumu, sazifuna ngakhale pang’ono zipembedzo zonyenga.

Mungapewe Bwanji?

11. Kodi tiyenera kutani kuti tipewe kulambira konyenga?

11 Akristu oona amapewa kulambira konyenga, ndipo amakana ziphunzitso za zipembedzo zonyenga. Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kupewa mapulogalamu a chipembedzo a pa wailesi ndi pa TV ndiponso mabuku achipembedzo onenera mabodza Mulungu ndiponso Mawu ake. (Salmo 119:37) Komanso tiyenera kupewa misonkhano kapena maphwando alionse okonzedwa ndi bungwe lililonse lokhudzana ndi kulambira konyenga. Ndiponso tionetsetse kuti sitikuchirikiza kulambira konyenga m’njira ina iliyonse. (1 Akorinto 10:21) Kuchita zinthu zimenezi kumatiteteza kuti tisasocheretsedwe “ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu.”​—Akolose 2:8.

12. Kodi munthu angathetse bwanji ubale wake wonse ndi magulu a zipembedzo zonyenga?

12 Nanga bwanji ngati munthu amene akufuna kukhala wa Mboni za Yehova panopo ali membala wa chipembedzo chonyenga? Nthawi zambiri, kulemba kalata yochoka m’chipembedzocho kumapereka umboni wakuti munthuyo sakufunanso kuonedwa monga membala wa chipembedzo chonyengacho. M’pofunika kuti munthuyo azipeweratu chilichonse chokhudza kulambira konyenga. Maganizo a munthu amene akufuna kukhala wa Mboniyo ayenera kuonetseratu kwa gulu lachipembedzolo ndiponso anthu onse omuona kuti iyeyo wathetsadi ubale uliwonse ndi gululo pankhani za kulambira.

13. Kodi Baibulo limapereka malangizo otani pa nkhani ya kufunika kopewa kulambira konyenga?

13 Mtumwi Paulo anati: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima? Ndipo Kristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupira? Ndipo chiphatikizo chake n’chanji ndi kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? . . . Chifukwa chake tulukani pakati pawo, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka.” (2 Akorinto 6:14-17) Tiyenera kumvera mawu amenewa popewa kulambira konyenga. Kodi malangizo a Paulowa akutanthauza kuti tiyeneranso kupewa mayanjano alionse ndi anthu a m’zipembedzo zonyenga?

‘Yendani Mwanzeru’

14. Kodi tiyenera kupeweratu anthu onse amene ali mu zipembedzo zonyenga? Longosolani.

14 Kodi olambira oona ayenera kupeweratu kucheza ndi aliyense wolambira monyenga? Kodi tiyenera kukaniratu kucheza ndi anthu amene si Akristu anzathu? Yankho ndi loti ayi. Lamulo lachiwiri pa malamulo awiri aakulu kwambiri limati: “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.” (Mateyu 22:39) Anansi athu tikamawauza uthenga wabwino wa Ufumu timakhala tikuwasonyeza chikondi. Timawasonyezanso chikondi chathu tikamaphunzira nawo Baibulo ndi kuwathandiza kuzindikira kuti ayenera kusiya kulambira konyenga.

15. Kodi tanthauzo la ‘kusakhala mbali ya dziko’ n’chiyani?

15 Ngakhale kuti timalalikira uthenga wabwino kwa anansi athu, sitiyenera kukhala “a dziko lapansi” chifukwa ndife otsatira a Yesu. (Yohane 15:19) Mawu akuti “dziko” pa lembali amatanthauza anthu amene atalikirana ndi Mulungu. (Aefeso 4:17-19; 1 Yohane 5:19) Sitili mbali ya dziko m’njira yakuti timapewa maganizo, mawu, ndi makhalidwe amene Yehova amaipidwa nawo. (1 Yohane 2:15-17) Kuphatikiza apo, mogwirizana ndi mfundo yakuti “mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma,” timapewa kugwirizana kwambiri ndi anthu amene satsatira mfundo zachikristu. (1 Akorinto 15:33) Kusakhala mbali ya dziko kumatanthauza kukhala “wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.” (Yakobo 1:27) Motero, kusakhala mbali ya dziko sikutanthauza kuti tisamachite chilichonse ndi anthu ena.​—Yohane 17:15, 16; 1 Akorinto 5:9, 10.

16, 17. Kodi Akristu ayenera kukhala nawo motani anthu amene sakudziwa choonadi cha m’Baibulo?

16 Nanga kodi tiyenera kukhala motani ndi anthu amene sadziwa choonadi cha m’Baibulo? Paulo analemba mawu awa ku mpingo wa ku Kolose: “Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kuchita machawi nthawi ingatayike. Mawu anu akhale m’chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.” (Akolose 4:5, 6) Mtumwi Petro analemba kuti: “Mum’patulikitse Ambuye Kristu m’mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha.” (1 Petro 3:15) Paulo analangiza Akristu kuti “asachitire mwano munthu aliyense, asakhale andewu, akhale aulere, naonetsere chifatso chonse pa anthu onse.”​—Tito 3:2.

17 Poti ndife Mboni za Yehova, tiyenera kupewa kuchitira ena mwano kapena kuwanyoza. Tisamatchule anthu a zipembedzo zina ndi mayina achipongwe. M’malo mwake tikhale okoma mtima ngakhale tikamanyozedwa kapena kulankhulidwa mwachipongwe ndi mwininyumba, mnansi, kapena mnzathu wa kuntchito.​—Akolose 4:6; 2 Timoteo 2:24.

“Gwira Chitsanzo cha Mawu a Moyo”

18. Kodi anthu amene amayambiranso kulambira konyenga moyo wawo wauzimu umafika potani?

18 Zingakhale zomvetsa chisoni ngati titayambiranso kulambira konyenga koma titaphunzira kale choonadi cha m’Baibulo. Baibulo limalongosola zinthu zomvetsa chisoni zimene njira yotereyi imabweretsa ponena kuti: “Pakuti ngati, adatha kuthawa zodetsa za dziko lapansi mwa chizindikiritso cha Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Kristu, akodwanso nazo, nagonjetsedwa, zotsiriza zawo zidzaipa koposa zoyambazo. . . . Chidawayenera iwo cha nthanthi yoona, galu wabwerera ku masanzi ake, ndi nkhumba idasambayi yabwerera kukunkhulira m’thope.”​—2 Petro 2:20-22.

19. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala atcheru kudziteteza ku chinthu chilichonse chimene chingawononge moyo wathu wauzimu?

19 Tiyenera kukhala atcheru kudziteteza ku zinthu zilizonse zimene zingawononge moyo wathu wauzimu. Zinthu zoterezi zilipodi. Mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Mzimu anena monenetsa, kuti m’masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziwanda.” (1 Timoteo 4:1) Tikukhala “m’masiku otsiriza” otchulidwa pa lembali. Anthu amene sapewa kulambira konyenga angathe ‘kutengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusokeretsa.’​—Aefeso 4:13, 14.

20. Kodi tingadziteteze bwanji kuti tisasokonezeke ndi kulambira konyenga?

20 Kodi tingadziteteze bwanji kuti tisasokonezeke ndi chipembedzo chonyenga? Taganizirani zimene Yehova watipatsa. Watipatsa Mawu a Mulungu, Baibulo. (2 Timoteo 3:16, 17) Yehova watipatsanso chakudya chauzimu kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45) Tikamakula m’choonadi, kodi sitiyenera kumafuna kudya ‘chakudya chotafuna cha anthu akulu misinkhu’ n’kumakonda kusonkhana ndi anzathu n’kumaphunzira choonadi? (Ahebri 5:13, 14; Salmo 26:8) Tiyeni tiyesetse kugwiritsa ntchito zinthu zimene Yehova watipatsa kuti tipitirize ‘kugwira chitsanzo cha mawu a moyo’ amene tinamva. (2 Timoteo 1:13) Tikatero tingathe kupewa kulambira konyenga.

Mwaphunzirapo Chiyani?

• Kodi ‘Babulo Wamkulu’ n’chiyani?

• Kodi tiyenera kutani kuti tipewe kulambira konyenga?

• Kodi tiyenera kupewa zinthu zotani zomwe zingathe kuwononga moyo wathu wauzimu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 28]

Kodi mukudziwa chifukwa chimene Baibulo limafanizira ‘Babulo Wamkulu’ ndi mkazi wachigololo?

[Chithunzi patsamba 29]

‘Babulo Wamkulu’ watsala pang’ono kuwonongedwa

[Chithunzi patsamba 31]

Timawasonyeza “chifatso ndi mantha” anthu amene si Akristu anzathu