Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Ali ndi Mphamvube?

Kodi Mulungu Ali ndi Mphamvube?

Dzamvereni Nkhani Yakuti . . .

Kodi Mulungu Ali ndi Mphamvube?

TSIKU sililowa popanda kumva nkhani za zinthu monga masoka achilengedwe, matenda oopsa, akuluakulu ochita zakatangale, uchigawenga, nkhondo, kapena umbanda. Kaya nkhanizi zimakukhudzani inuyo kapena ayi, n’zosakayikitsa kuti mumadzifunsa kuti dzikoli likulowera kuti ndiponso kuti kodi zinthu zisintha?

Pofuna kuyankha mafunso amenewa, Mboni za Yehova m’mayiko opitirira 200 padziko lonse zidzakhala ndi nkhani ya anthu onse ya mutu wakuti “Kodi Mulungu Ali ndi Mphamvube pa Zochitika za Padziko Lapansi Pano?” Nkhaniyi idzalongosola zimene Mulungu amanena ndi kulonjeza m’Mawu ake osanama, Baibulo, pa mafunso ofunika otsatirawa:

Kodi Mulungu amaganizira zochitika za padziko lapansi pano?

Kodi anthu amawaona bwanji?

Kodi inuyo amakuganizirani pa moyo wanu?

M’madera ambiri nkhaniyi idzakambidwa Lamlungu, pa April 30, 2006, ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. Mboni za kwanuko zingasangalale kukuuzani nthawi ndi malo amene akakambire nkhaniyi.

Mukuitanidwa ndi manja awiri kukamvetsera nkhani yolimbikitsa ya m’Baibuloyi yomwe n’njaulere ndipo idzayankha mokhutiritsa funso lakuti: Kodi Mulungu Ali ndi Mphamvube pa Zochitika za Padziko Lapansi Pano?