Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukwaniritsa Zimene Zimafunika Paubatizo Wachikristu

Kukwaniritsa Zimene Zimafunika Paubatizo Wachikristu

Kukwaniritsa Zimene Zimafunika Paubatizo Wachikristu

“Chindiletsa ine n’chiyani ndisabatizidwe?”​—MACHITIDWE 8:36.

1, 2. Kodi Filipo anayamba bwanji kukambirana ndi mdindo wa ku Aitiopiya, ndipo n’chiyani chinasonyeza kuti munthuyu anali ndi chidwi ndi kulambira koona?

CHAKA chimodzi kapena ziwiri imfa ya Yesu itachitika, mwamuna wina wogwira ntchito m’boma anali paulendo wopita ku Gaza kuchokera ku Yerusalemu. Anafunika kuyenda pagaleta ulendo wotopetsa wa makilomita 1,500. Mwamuna wodzipereka ameneyu anali atayenda kuchokera ku Aitiopiya kupita ku Yerusalemu kukalambira Yehova. Pa ulendo wake wautali wobwerera kwawo, anagwiritsa ntchito nthawi yake mwa nzeru mwa kuwerenga Mawu a Mulungu. Zimenezi zinali umboni wa chikhulupiriro cha mwamunayu. Yehova anaona mwamuna wokhulupirikayu, ndipo mwa kugwiritsa ntchito mngelo, analangiza wophunzira Filipo kuti akam’lalikire.​—Machitidwe 8:26-28.

2 Filipo sanavutike kuyamba kukambirana naye, chifukwa choti mdindo wa ku Aitiopiya ankawerenga mokweza, monga mmene anthu ankachitira masiku amenewo. Chotero, Filipo anatha kumva kuti anali kuwerenga mpukutu wa Yesaya. Funso limodzi losavuta limene Filipo anafunsa mwamunayu linadzutsa chidwi chake. Iye anati: “Kodi muzindikira chimene muwerenga?” Zimenezi zinachititsa kuti ayambe kukambirana lemba la Yesaya 53:7, 8. Atakambirana lembali, Filipo analalikira kwa iye uthenga wabwino wonena za Yesu.​—Machitidwe 8:29-35.

3, 4. (a) N’chifukwa chiyani Filipo sanazengereze kubatiza Mwaitiopiya uja? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

3 Posapita nthawi, Mwaitiopiyayo anamvetsa udindo wa Yesu pa chifuniro cha Mulungu, ndiponso kufunika kokhala wophunzira wa Kristu wobatizidwa. Ataona madzi chapafupi, mwamunayu anafunsa Filipo kuti: “Chindiletsa ine n’chiyani ndisabatizidwe?” Zoonadi, zimenezi zinali zinthu zosachitikachitika. Mwaitiopiyayo anali mwamuna wachikhulupiriro amene anali atayamba kale kupembedza Mulungu monga munthu wotembenukira ku Chiyuda. Mwina sakanadzakhalanso ndi mwayi wina woti n’kubatizidwa kwa nthawi yaitali. Ndipo chofunika kwambiri n’choti, mwamunayu ankadziwa zimene Mulungu ankafuna kuti iye achite, ndipo ankafuna kuchita zimenezi ndi mtima wonse. Filipo anavomereza pempho lake mosangalala, ndipo Mwaitiopiyayo atabatizidwa “anapita njira yake wokondwera.” Zikuoneka kuti, atafika kwawo anakhala wolalikira wachangu wa uthenga wabwino.​—Machitidwe 8:36-39.

4 Ngakhale kuti munthu safunika kudzipereka ndi kubatizidwa mwaphuma kapena popanda kuganizirapo mwakuya, chitsanzo cha mdindo wa ku Aitiopiyayu chimasonyeza kuti nthawi zina anthu abatizidwapo asanathe nthawi yaitali kuchokera pamene anamvera choonadi cha Mawu a Mulungu. * Motero, n’kofunika kuganizira mafunso otsatirawa: Kodi munthu afunika kukonzekera bwanji asanabatizidwe? Kodi nkhani ya msinkhu wa munthu ndi yofunika kuiona motani? Kodi munthu ayenera kukhala atadziwa zinthu zauzimu zochuluka bwanji asanabatizidwe? Ndipo chofunika kwambiri n’chakuti, n’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti atumiki ake abatizidwe?

Pangano Losafunika Kuliswa

5, 6. (a) Kodi anthu a Mulungu m’nthawi yakale anasonyeza bwanji kuti anali kuyamikira chikondi Chake? (b) Kodi ndi ubwenzi wolimba wotani umene tingakhale nawo ndi Mulungu tikabatizidwa?

5 Yehova atapulumutsa Aisrayeli ku Igupto, anawalandira kukhala ‘chuma chake chapadera.’ Anawauza kuti adzawakonda ndi kuwateteza ndipo anawaika kukhala “mtundu wopatulika.” Koma kuti alandire madalitso amenewa, anthuwa anafunikira kusonyeza kuti akuyamikiradi chikondi cha Mulungu. Iwo anasonyeza zimenezi mwa kuvomereza kuchita “zonse adazilankhula Yehova” ndiponso kuchita naye pangano. (Eksodo 19:4-9) M’nthawi ya atumwi, Yesu analamula otsatira ake kupanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse, ndipo amene anamvera chiphunzitso chake anabatizidwa. Kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu anafunika kukhala ndi chikhulupiriro mwa Yesu Kristu kenako n’kubatizidwa.​—Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 2:38, 41.

6 Nkhani za m’Malemba zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amadalitsa anthu omwe amapanga ndi kusunga pangano lofunika kwambiri limeneli la kum’tumikira. Kudzipereka ndiponso kubatizidwa n’zinthu zofunika kwa Akristu zimene zingawathandize kulandira madalitso a Yehova. Kumasonyeza kuti ndife otsimikiza mtima kutsatira miyezo yake ndipo tikufuna kuti atitsogolere. (Salmo 48:14) Tikachita zimenezi, Yehova mophiphiritsa amatigwira mkono ndi kutitsogolera m’njira yoti tiyendemo.​—Salmo 73:23; Yesaya 30:21; 41:10, 13.

7. N’chifukwa chiyani timayenera kusankha tokha kudzipereka ndiponso kubatizidwa?

7 Zimene zingatilimbikitse kuti tidzipereke ndiponso tibatizidwe ndi kukonda Yehova ndi kufuna kum’tumikira. Munthu asabatizidwe chabe chifukwa choti winawake wamuuza kuti wakhala akuphunzira kwa nthawi yaitali kapena chifukwa choti anzake akubatizidwa. Makolo ndi Akristu ena okhwima maganizo angathe kulimbikitsa munthu kuganizira zodzipereka ndiponso kubatizidwa. Mtumwi Petro analimbikitsa anthu amene anamvetsera nkhani yake pa Pentekoste kuti ‘abatizidwe.’ (Machitidwe 2:38) Koma munthu aliyense afunika kusankha yekha kudzipereka, ndipo palibe munthu amene angatiuze kuti tidzipereke. Tifunikira kusankha tokha kutumikira Mulungu.​—Salmo 40:8.

Kukonzekera Ubatizo Mokwanira

8, 9. (a) N’chifukwa chiyani ubatizo wa makanda uli wosemphana ndi Malemba? (b) Kodi ana ayenera kukhala atadziwa zinthu zauzimu zochuluka bwanji asanabatizidwe?

8 Kodi ana angathe kudzipereka modziwa bwinobwino chomwe akuchita? Malemba satchula kuti munthu azibatizidwa pa msinkhu wakutiwakuti. Ngakhale ndi choncho, makanda sangakhale ndi chikhulupiriro, sangasankhe zinthu mwa chikhulupiriro, ndiponso sangathe kudzipereka kwa Mulungu. (Machitidwe 8:12) Ponena za Akristu a m’nthawi ya atumwi, wolemba mbiri Augustus Neander m’buku lake lakuti General History of the Christian Religion and Church anati: “Poyamba anthu aakulu okha ndi amene ankabatizidwa chifukwa choti anthu ankaona kuti munthu ankafunika kukhala ndi chikhulupiriro kuti abatizidwe.”

9 Ana ena amatha kumvetsa ndi kuyamba kutsatira mfundo zikuluzikulu za m’Baibulo ali aang’ono kwambiri. Koma ena zimawatengera nthawi. Wachinyamata asanabatizidwe ayenera kukhala ndi ubwenzi wolimba ndi Yehova, ayenera kumvetsa bwino ziphunzitso za m’Malemba zofunika ndiponso adziwe bwino tanthauzo la kudzipereka monga mmene zimakhalira ndi anthu aakulu.

10. Kodi munthu amafunika kuchita chiyani asanadzipereke ndiponso asanabatizidwe?

10 Yesu analangiza ophunzira ake kuphunzitsa atsopano zinthu zonse zimene anawalamulira. (Mateyu 28:20) Motero, atsopano amafunika kudziwa kaye choonadi, chimene chingawathandize kukhala ndi chikhulupiriro mwa Yehova ndi Mawu ake. (Aroma 10:17; 1 Timoteo 2:4; Ahebri 11:6) Ndiyeno, choonadi cha m’Malemba chikam’fika munthu pamtima, chimamulimbikitsa kulapa ndi kusiya moyo wake wakale. (Machitidwe 3:19) Pomaliza, munthuyo amafika poti akufuna kudzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa, monga momwe Yesu analamulira.

11. N’chifukwa chiyani n’kofunika kuchita nawo ntchito yolalikira nthawi zonse tisanabatizidwe?

11 Chinthu china chofunika kuti munthu afike pobatizidwa ndicho kuchita nawo ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Imeneyi ndiyo ntchito yofunika kwambiri imene Yehova wapatsa anthu ake m’masiku otsiriza ano. (Mateyu 24:14) Motero, ofalitsa osabatizidwa angakhale ndi mwayi wolankhula za choonadi kwa ena. Kuchita nawo ntchito imeneyi kumawakonzekeretsa kuti akadzabatizidwa adzathe kuchita nawo utumiki wa kumunda nthawi zonse ndiponso mwachangu.​—Aroma 10:9, 10, 14, 15.

Kodi Chinachake Chikukulepheretsani Kubatizidwa?

12. Kodi n’chiyani chimene chingalepheretse ena kubatizidwa?

12 Anthu ena safuna kubatizidwa chifukwa choopa udindo umene ubatizo umabweretsa. Iwo amazindikira kuti ayenera kusintha kwambiri kuti moyo wawo ugwirizane ndi miyezo ya Yehova. Kapena angachite mantha kuti zidzawavuta kuchita zimene Mulungu amafuna akadzabatizidwa. Ena angafike ngakhale poganiza kuti, “Mwina tsiku lina ndidzachita choipa ndipo ndidzachotsedwa mu mpingo.”

13. M’nthawi ya Yesu, kodi n’chiyani chinalepheretsa anthu ena kukhala otsatira ake?

13 M’nthawi ya Yesu, ena analola zofuna zawo ndi chikondi chimene anali nacho pa anthu a m’banja mwawo kuwalepheretsa kukhala ophunzira ake. Mlembi wina anati adzatsatira Yesu kulikonse kumene angapiteko. Koma Yesu ananena kuti masiku ambiri, analibe ngakhale malo ogona. Ndipo nthawi inanso Yesu atauza munthu wina womvetsera kuti akhale wotsatira wake, munthuyu anayankha kuti ayambe kaye “kuika maliro” a atate wake. Zikuoneka kuti, ankafuna kukhala kunyumba ndi kudikirira mpaka atate wake atamwalira m’malo motsatira Yesu ndipo kenako n’kudzachita zimenezi atate wake akamwalira. Pomaliza, munthu wina wachitatu anati, asanatsatire Yesu, anayenera “kulawirana” nawo a kunyumba kwake. Yesu anafotokoza kuti kuzengereza kotereku ndiko ‘kuyang’ana za kumbuyo.’ Motero, zikuoneka kuti anthu omwe amafuna kuzengereza, nthawi zonse amakhala ndi zifukwa zopewera udindo wawo wachikristu.​—Luka 9:57-62.

14. (a) Kodi Petro, Andreya, Yakobo, ndi Yohane anachita chiyani Yesu atawauza kuti akhale asodzi a anthu? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuzengereza kusenza goli la Yesu?

14 Chitsanzo cha Petro, Andreya, Yakobo ndi Yohane ndi chosiyana kwambiri ndi zimenezi. Yesu atawauza kuti amutsatire ndipo akhale asodzi a anthu, Baibulo limati: “Iwo anasiya pomwepo makokawo, nam’tsata iye.” (Mateyu 4:19-22) Chifukwa choti sanazengereze kutsatira Yesu, zimene anadzawauza nthawi ina zinawachitikira. Iye anati: “Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.” (Mateyu 11:29, 30) Ngakhale kuti ubatizo umabweretsa udindo umene uli ngati goli, Yesu akutilimbikitsa kuti goli limeneli n’lofewa ndiponso lopepuka ndipo lidzatitsitsimula kwambiri.

15. Kodi zitsanzo za Mose ndi Yeremiya zimasonyeza motani kuti tingadalire Mulungu kuti atithandize?

15 Inde, kudzimva wosakwanira n’kwachibadwa. Poyamba, Mose ndi Yeremiya anadziona kuti sangathe kuchita ntchito imene Yehova anawapatsa. (Eksodo 3:11; Yeremiya 1:6) Kodi Mulungu anawalimbikitsa bwanji? Iye anauza Mose kuti: “Ine ndidzakhala ndi iwe.” Ndipo analonjeza Yeremiya kuti: “Ine ndili ndi iwe kuti ndikulanditse iwe.” (Eksodo 3:12; Yeremiya 1:8) Ifenso tingadalire Mulungu kuti atithandize. Kukonda Mulungu ndi kum’khulupirira kungatithandize kuthetsa maganizo odzikayikira kuti mwina sitingathe kuchita zinthu mogwirizana ndi kudzipereka kwathu. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulibe mantha m’chikondi; koma chikondi changwiro chitaya kunja mantha.” (1 Yohane 4:18) Mwana wamng’ono angakhale ndi mantha kuyenda yekha, koma amalimba mtima akamayenda atagwira mkono wa bambo wake. Ifenso tikakhulupirira Yehova ndi mtima wathu wonse, iye akulonjeza kuti ‘adzawongola mayendedwe athu’ pamene tikuyenda limodzi naye.​—Miyambo 3:5, 6.

Mwambo Wolemekezeka

16. N’chifukwa chiyani munthu pobatizidwa amamizidwa thupi lonse m’madzi?

16 Ubatizo usanachitike pamakhala nkhani ya m’Malemba yofotokoza kufunika kwa ubatizo wachikristu. Nkhaniyi ikatha, ofuna kubatizidwa amapemphedwa kulengeza poyera chikhulupiriro chawo mwa kuyankha mafunso awiri a paubatizo. (Aroma 10:10; onani bokosi patsamba 22.) Ndiyeno, ofuna kubatizidwa amamizidwa m’madzi, kutsatira chitsanzo cha Yesu. Baibulo limasonyeza kuti Yesu atabatizidwa, “anatuluka m’madzi,” kapena kuti kuvuuka m’madzi. (Mateyu 3:16; Marko 1:10) N’zoonekeratu kuti, Yohane Mbatizi anali atamiza thupi lonse la Yesu m’madzi. * Kumiza thupi lonse ndi chizindikiro choyenera cha kusintha kwakukulu kumene tachita pamoyo wathu. Mophiphiritsa, timafa ku njira zakale za moyo ndi kuyambanso moyo watsopano wotumikira Mulungu.

17. Kodi anthu ofuna kubatizidwa ndiponso ena opezekapo angalemekeze bwanji mwambo wa ubatizo?

17 Mwambo wa ubatizo ndi wofunika kuulemekeza ndiponso kusangalala nawo. Baibulo limasonyeza kuti Yesu anali kupemphera pamene Yohane anamumiza mu mtsinje wa Yordano. (Luka 3:21, 22) Mogwirizana ndi chitsanzo cha Yesu, ofuna kubatizidwa masiku ano ayenera kusonyeza khalidwe labwino. Ndipo popeza Baibulo limatiuza kuti tizivala modzilemekeza pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku, tifunikadi kuvala modzilemekeza panthawi ya ubatizo wathu. (1 Timoteo 2:9) Anthu ena opezekapo nawonso angasonyeze ulemu mwa kumvetsera mwachidwi nkhani ya ubatizo ndiponso kuonerera mwadongosolo pamene ubatizo ukuchitika.​—1 Akorinto 14:40.

Ubwino wa Kukhala Mkristu Wobatizidwa

18, 19. Kodi ubatizo umabweretsa mwayi ndi madalitso otani?

18 Tikadzipereka kwa Mulungu ndiponso tikabatizidwa, timakhala m’banja lapadera. Choyamba, Yehova amakhala Atate ndiponso Bwenzi lathu. Tisanabatizidwe tinali osayanjidwa ndi Mulungu, koma tsopano timayanjana naye. (2 Akorinto 5:19; Akolose 1:20) Kudzera mu nsembe ya Kristu, tayandikira kwa Mulungu ndipo iye amayandikira kwa ife. (Yakobo 4:8) Mneneri Malaki anafotokoza mmene Yehova amasamalirira ndi kumvetsera anthu amene amagwiritsa ntchito ndiponso kudziwika ndi dzina lake. Ndipo amalemba mayina awo m’buku la chikumbukiro. Mulungu anati: “Adzakhala angaanga . . . ndipo ndidzawamvera chisoni monga momwe munthu amamvera chisoni mwana wake wom’tumikira.”​—Malaki 3:16-18, NW.

19 Ubatizo umatithandizanso kukhala m’gulu la abale a padziko lonse. Pamene mtumwi Petro anafunsa za madalitso amene ophunzira a Kristu adzalandire chifukwa cha kudzimana kwawo, Yesu analonjeza kuti: “Onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amayi, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzalowa moyo wosatha.” (Mateyu 19:29) Patapita zaka zambiri, Petro analemba za gulu lonse la abale la padziko lapansi. Iye anathandizidwa ndiponso analandira madalitso kuchokera kwa abale achikondi, ndipo ifenso tingatero.​—1 Petro 2:17; 5:9.

20. Kodi ubatizo umatipatsa chiyembekezo chosangalatsa chotani?

20 Kuwonjezera pamenepa, Yesu ananena kuti omutsatira iye adzalandira “moyo wosatha.” Ndithudi, kudzipereka ndiponso kubatizidwa kumatipatsa chiyembekezo choti ‘tikagwire moyo weniweniwo,’ moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu. (1 Timoteo 6:19) Palibenso njira ina yabwino kuposa imeneyi yokonzera tsogolo lathu ndi la banja lathu. Chiyembekezo chosangalatsa chimenechi chidzatithandiza ‘kuyenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthawi yomka muyaya.’​—Mika 4:5.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Ayuda limodzi ndi anthu otembenukira ku Chiyuda okwana 3,000 amene anamvetsera ulaliki wa Petro pa Pentekoste nawonso anabatizidwa mosazengereza. Ndipo, mofanana ndi mdindo wa ku Aitiopiya, anali atadziwa kale ziphunzitso ndiponso mfundo zofunika za Mawu a Mulungu.​—Machitidwe 2:37-41.

^ ndime 16 Buku la Vine’s Expository Dictionary of New Testament Words limati liwu la Chigiriki lakuti baʹpti·sma (ubatizo) limatanthauza “kuviika, kumiza ndi kuvuula.”

Kodi Mungafotokoze?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira chikondi cha Yehova ndipo tingachite bwanji zimenezi?

• Kodi munthu ayenera kudziwa zinthu zauzimu zochuluka bwanji asanabatizidwe?

• Kodi n’chifukwa chiyani sitiyenera kulephera kubatizidwa chifukwa choopa kuti tidzalephera kuchita zinthu zinazake kapena chifukwa choopa udindo umene ubatizo umabweretsa?

• Kodi Akristu obatizidwa a Yesu Kristu angakhale ndi madalitso apadera otani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 26]

“Chindiletsa ine n’ chiyani ndisabatizidwe?”

[Zithunzi patsamba 29]

Mwambo wa ubatizo ndi wofunika kuulemekeza ndiponso kusangalala nawo