Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumvetsa Baibulo N’chinthu Chosangalatsa

Kumvetsa Baibulo N’chinthu Chosangalatsa

Kumvetsa Baibulo N’chinthu Chosangalatsa

BAIBULO lili ndi choonadi cha mtengo wapatali chochokera kwa Mulungu. Limatiuza za cholinga cha moyo, zimene zimachititsa kuti anthu azivutika, ndiponso limafotokoza za tsogolo la anthu. Limatiphunzitsa mmene tingapezere chimwemwe, anzathu, ndi mmene tingathetsere mavuto. Koposa zonse, timaphunziramo zochuluka zokhudza Mlengi wathu ndi Atate wathu wakumwamba Yehova. N’zosangalatsa kudziwa zinthu ngati zimenezi, ndipo moyo wathu umakhala ndi cholinga chabwino.

Baibulo limayerekezera kuphunzira za Mulungu ndi kudya. Yesu anati: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4; Ahebri 5:12-14) Monga mmene zilili kuti timadya tsiku ndi tsiku kuti tikhale ndi moyo, n’chimodzimodzinso ndi kuwerenga Mawu a Mulungu. Timafunika kuwerenga Baibulo nthawi zonse kuti tilandire madalitso a moyo wosatha amene Mulungu walonjeza.

Kudya n’kosangalatsa chifukwa chakuti mmenemo ndi mmene Mulungu anatilengera ndipo n’kofunika kwambiri kuti tikhale ndi moyo. Komabe, pali chinthu chinanso chofunika kwambiri chimene sitiyenera kuchinyalanyaza ngati tikufuna kukhala achimwemwe. Yesu anati: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusowa kwawo kwauzimu.” (Mateyu 5:3, NW) Tingathetse kusowa kwathu kwauzimu mwa kumvetsa Mawu a Mulungu. Choncho n’zotheka ndithu kukhala anthu achimwemwe.

N’zoona kuti ena zimawavuta kulimvetsa bwino Baibulo. Mwachitsanzo nthawi zina mungafunikire kuthandizidwa kuti mumvetse mwambo winawake wachilendo kapena mawu ena okuluwika otchulidwa m’Baibulo. Ndiyenso pali maulosi olembedwa mophiphiritsira amene mungawamvetse bwino pokhapokha mutawerenga malemba ena a m’Baibulo ofotokoza nkhani yomweyo. (Danieli 7:1-7; Chivumbulutso 13:1, 2) Ngakhale izi zili choncho, mukhozabe kulimvetsa Baibulo. Kodi mungakhulupirire bwanji kuti n’zotheka ndithu kulimvetsa Baibulo?

Aliyense Atha Kulimvetsa

Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Ndi buku limene Mulungu amaligwiritsa ntchito kutifotokozera zolinga zake. Kodi mukuganiza kuti Mulungu akadatipatsa buku losamveka kapena loti azilimva anthu ophunzira okha? Ayi, Yehova sangakhale woipa mtima choncho. Kristu Yesu ananena kuti: “Ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzam’pempha mkate, adzam’patsa mwala? Kapena nsomba, nadzam’ninkha njoka m’malo mwa nsomba? Kapena akadzam’pempha dzira kodi adzam’patsa chinkhanira? Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akum’pempha Iye?” (Luka 11:11-13) Zimenezi zikutitsimikizira kuti n’zotheka kumvetsa Baibulo, ndikuti ngati titam’pempha Mulungu moona mtima, iye adzatithandiza kumvetsa Mawu ake. Ndipotu ngakhale ana akhoza kumvetsa ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo.​—2 Timoteo 3:15.

N’zoona kuti kumvetsa Baibulo kumafuna khama. Komano, kuchita zimenezo kukhoza kutithandiza kwambiri ndipo n’kolimbikitsa. Ataukitsidwa, Yesu anaonekera kwa ophunzira ake awiri ndipo analankhula nawo za maulosi a m’Baibulo. Nkhani imene inalembedwa ndi Luka imati: “Anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse, nawatanthauzira iwo m’malembo onse zinthu za Iye yekha.” Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Tsiku lomwelo madzulo, pamene ophunzirawa amayesa kukumbutsana zimene anamva, anauzana wina ndi mnzake kuti: “Mtima wathu sunali wotentha m’kati mwathu nanga mmene analankhula nafe m’njira, mmene anatitsegulira malembo?” (Luka 24:13-32) Kuphunzira Mawu a Mulungu kunali kosangalatsa kwa ophunzirawa chifukwa chakuti kunalimbikitsa chikhulupiriro chawo chokhudza malonjezo a Mulungu ndipo kunawatsimikizira kuti m’tsogolo zinthu zidzakhala bwino kwambiri.

Kumvetsa Mawu a Mulungu sikuli ngati ntchito yakalavula gaga ayi. Iko n’kosangalatsa ndi kopindulitsa monga mmene zilili ndi kudya chakudya cha pamtima panu. Kodi tingachite chiyani kuti tithe kumvetsa bwino Mawu a Mulungu? Nkhani yotsatira ifotokoza zimene mungachite kuti musangalale “ndi kum’dziwadi Mulungu.”​—Miyambo 2:1-5.

[Chithunzi patsamba 4]

Monga tate wachikondi, Yehova watipatsa mzimu wake kuti utithandize kumvetsa Baibulo