Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi tingaphunzirepo chiyani pa lamulo lopezeka pa Eksodo 23:19, lakuti: “Usaphike mwana wa mbuzi mu mkaka wa make”?

Lamulo la m’Chilamulo cha Moseli, lomwe limapezeka katatu m’Baibulo, lingatithandize kuona kuti ndi zinthu zotani zimene Yehova amaziona kuti n’zoyenera, kuti Yehova n’ngwachifundo, ndiponso kuti n’ngokoma mtima. Komanso limasonyeza kuti Yehova amadana kwambiri ndi kulambira konyenga.​—Eksodo 34:26; Deuteronomo 14:21.

Kuphika mwana wa mbuzi kapena nyama ina iliyonse mu mkaka wa mayi ake n’kosemphana ndi chilengedwe cha Yehova. Mulungu anapereka mkaka n’cholinga choti mbuzi iziyamwitsira mwana wake kuti azikula. Motero monga mmene ananenera munthu wina wophunzira kwambiri, kuphika mwanayo mu mkaka wa make, kumasonyeza “kunyoza mgwirizano wa pakati pa mayi ndi mwana wake, umene Mulungu anakhazikitsa ndi kuuyeretsa.”

Kuphatikizanso apo, anthu ena amanena kuti n’zotheka kuti kuphika mwana mu mkaka wa make unali mwambo wachikunja woitanitsira mvula. Ngati izi zili zoona, ndiye kuti lamulo loletsa zimenezi linateteza Aisrayeli ku miyambo yotereyi ya anthu a mitundu yowazungulira, yomwe inali yopusa ndiponso yankhanza. Chilamulo cha Mose chinaletsa mwachindunji kutsatira malamulo a mitundu imeneyo.​—Levitiko 20:23.

Potsiriza, lamulo limeneli likusonyeza chikondi cha Yehova. Kwenikweni, Chilamulo chinali ndi malamulo angapo oterewa oletsa kuchitira nkhanza zinyama ndiponso kuchita zinthu zosemphana ndi chilengedwe cha Yehova. Mwachitsanzo, malamulo ena a Chilamulo ankaletsa zopereka nsembe chiweto chimene sichinakwanitse masiku seveni chili ndi mayi wake. Ankaletsanso zopha chiweto ndi mwana wake pa tsiku lomwelo, ndiponso zopita pa chisa n’kutenga mbalame pamodzi ndi mazira ake kapena anapiye ake.​—Levitiko 22:27, 28; Deuteronomo 22:6, 7.

N’zoonekeratu, kuti malamulo ambirimbiri a m’Chilamulo aja sanali malamulo ongofuna kuletsa zinthu zosiyanasiyana ayi. Chilamulo n’chopindulitsa m’njira zosiyanasiyana. Mfundo zake zimatithandiza kukhala ndi makhalidwe apamwamba kwambiri amene amasonyezadi makhalidwe abwino kwambiri a Yehova.​—Salmo 19:7-11.

[Mawu a Chithunzi patsamba 31]

© Timothy O’Keefe/​Index Stock Imagery