Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chiyani Chingakuthandizeni Kumvetsa Baibulo?

N’chiyani Chingakuthandizeni Kumvetsa Baibulo?

N’chiyani Chingakuthandizeni Kumvetsa Baibulo?

“IZI munazibisira anzeru ndi ozindikira, ndipo munaziululira ana amakanda.” (Luka 10:21) Mawu amenewa, amene Yesu ananena polankhula ndi Atate ake akumwamba, amasonyeza kuti tiyenera kukhala ndi mtima wabwino kuti timvetse Baibulo. Nzeru za Yehova zimaonekera mwa njira yakuti ndi anthu odzichepetsa ndi ophunzitsika okha amene angathe kulimvetsa bwinobwino buku limeneli.

Ambirife kudzichepetsa kumativuta. Tonsefe tinabadwa ndi mtima wodzikuza. Komanso, tikukhala mu “masiku otsiriza,” pakati pa anthu “odzikonda okha, . . . odzitamandira, odzikuza.” (2 Timoteo 3:1-4) Timalephera kumvetsa Mawu a Mulungu chifukwa cha zinthu ngati zimenezi. N’zomvetsa chisoni kuti tonsefe mwanjira inayake timakhudzidwa kapena kutengera khalidwe lodzikonda la anthu amene tayandikana nawo. Nangano, kodi mungatani kuti mukhale ndi mtima wofuna kumvetsa Baibulo?

Kukonzekeretsa Mtima ndi Maganizo

Ezara, mtsogoleri wakale wa anthu a Mulungu, “adaikiratu, [“anakonzekeretsa,” NW] mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova.” (Ezara 7:10) Kodi pali njira iliyonse yoti n’kutithandiza kukonzekeretsa mtima wathu? Inde. Choyambirira, tiyenera kukhala ndi mtima wolemekeza Malemba. Polembera kalata Akristu anzake, mtumwi Paulo anati: “Pakulandira mawu a Uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mawu a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mawu a Mulungu.” (1 Atesalonika 2:13) Ngakhale kuti anthu ndi amene anagwiritsidwa ntchito kulemba Malemba amenewa, zimene analemba zinali zochokera kwa Yehova. Kuzindikira mfundo yofunika kwambiri imeneyi kungatithandize kukhala ndi mtima wofuna kumvetsa zimene tikuwerenga.​—2 Timoteo 3:16.

Njira ina yokonzekeretsa mtima wathu ndiyo pemphero. Popeza Baibulo linauziridwa ndi mzimu woyera, tingamvetse bwino uthenga wake ngati titathandizidwa ndi mzimu woyera womwewo. Tifunikira kupempha thandizo limeneli. Taonani kuti imeneyi ndiyo inali nkhawa ya wamasalmo amene analemba kuti: “Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu; ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.” (Salmo 119:34) Popemphera tiyenera kupempha, osati nzeru zotithandiza kumvetsa Malemba zokha, komanso tiyenera kupempha kuti tikhale ndi mtima wabwino umene ungatithandize kuti tivomereze zimene Baibulo limanena. Kuti timvetse Baibulo, tifunikira kulemekeza chilichonse chimene chili choonadi.

Mukamasinkhasinkha n’cholinga choti mukhale ndi mtima wabwino, muziganizira za ubwino wophunzira Baibulo. Pali zifukwa zambiri zowerengera Mawu a Mulungu, koma chifukwa chachikulu koposa ndicho chakuti limatithandiza kuyandikana ndi Mulungu. (Yakobo 4:8) Tikamawerenga mmene Yehova amamvera zinthu zosiyanasiyana zikamachitika, mmene amakondera anthu amene amamukonda, ndi mmene amachitira ndi anthu amene asiya kum’tumikira, m’pamene timam’dziwa bwino kwambiri. Cholinga chathu chachikulu tikamawerenga Baibulo nthawi zonse chikhale chofuna kum’dziwa bwino Mulungu ndipo tikatero tidzalimbitsa ubwenzi wathu ndi iye.

Zimene Zingatilepheretse Kumvetsa Baibulo

Kodi n’chiyani chimene chingatilepheretse kumvetsa Mawu a Mulungu? Chinthu chimodzi ndicho kugonjera kwambiri anthu amene timawaona kuti ndi olemekezeka. Mwachitsanzo, mungamatsatire zikhulupiriro ndi maganizo a anthu amene mumawapatsa ulemu kwambiri. Nangano bwanji ngati anthu amenewa sakutsatira kapena kulemekeza kwenikweni choonadi cha m’Mawu a Mulungu? Zikatero, kumakhala kovuta kumvetsa zimene Baibulo kwenikweni limaphunzitsa. N’chifukwa chake Baibulo limatilimbikitsa kufufuza mosamala zinthu zimene tikuphunzitsidwa.​—1 Atesalonika 5:21.

Mayi a Yesu, Mariya, anakumanapo ndi vuto limeneli. Iwo anakula motsatira miyambo yachiyuda. Ankayesetsa kusunga Chilamulo cha Mose ndipo n’zosakayikitsa kuti ankapita ku kachisi. Kenako anadzazindikira kuti kulambira kumene makolo awo anawaphunzitsa sikunali kovomerezeka kwa Mulungu. N’chifukwa chake Mariya anavomereza chiphunzitso cha Yesu ndipo anali mmodzi mwa anthu oyamba kulowa mu mpingo wachikristu. (Machitidwe 1:13, 14) Pochita zimenezi, sikuti Mariya anali kunyoza makolo ake kapena chikhalidwe chawo ayi, iye anali kungosonyeza chabe kuti amakonda Mulungu kwambiri. Ngati tikufuna kuti tipindule ndi Baibulo, monga mmene anachitira Mariya, nafenso tiyenera kugonjera kwambiri Mulungu koposa wina aliyense.

N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri salemekeza choonadi cha m’Baibulo. Ena amakhutira ndi kutsatira miyambo yabodza ya chipembedzo. Ena amaoneka kuti salemekeza choonadi chifukwa cha zolankhula ndi khalidwe lawo. N’chifukwa chake kutsatira choonadi cha m’Baibulo si nkhani yophweka ayi. Kungakulekanitseni ndi anzanu, anansi anu, ogwira nawo ntchito, ngakhalenso anthu a pabanja panu. (Yohane 17:14) Komabe, munthu wanzeru Solomo analemba kuti: “Gula ntheradi, osaigulitsa; nzeru, ndi mwambo, ndi luntha.” (Miyambo 23:23) Ngati mumalemekezadi choonadi, Yehova adzakuthandizani kumvetsa Baibulo.

Koma vuto linanso limene lingakulepheretseni kumvetsa uthenga wa m’Baibulo ndilo kusafuna kugwiritsa ntchito zimene limanena. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwa kwa iwo. Chifukwa unalemera mtima wa anthu awa, ndipo m’makutu awo anamva mogontha.” (Mateyu 13:11, 15) Ambiri a anthu amene Yesu analankhula nawo anali osamvera, osafuna kusintha. Zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi wamalonda wina wotchulidwa m’fanizo la Yesu. Atapeza ngale ya mtengo wapatali, anagulitsa zonse zomwe anali nazo kuti agule ngaleyo. Nkhani yomvetsa choonadi cha m’Baibulo iyenera kukhala ya mtengo wapatali chimodzimodzi kwa Ife.​—Mateyu 13:45, 46.

Vuto la Kusaphunzitsika

Vuto lalikulu limene limachititsa kuti anthu asamvetse Baibulo ndilo kusaphunzitsika. Munthu angavutike kuvomereza mfundo zatsopano kuchokera kwa munthu wina amene akuoneka kuti ndi wotsika. Koma dziwani kuti ngakhale atumwi a Yesu Kristu anali “anthu osaphunzira ndi opulukira.” (Machitidwe 4:13) Paulo anafotokoza bwino zimenezi pamene anati: “Penyani maitanidwe anu, abale, kuti saitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi; ambiri amphamvu, mfulu zambiri, iyayi; koma Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akachititse manyazi anzeru; ndipo zofooka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akachititse manyazi zamphamvu.” (1 Akorinto 1:26, 27) Ngati mukuona kuti n’zokuvutani kuphunzitsidwa ndi munthu wotsika, kumbukirani kuti munthuyo akungogwiritsidwa ntchito chabe ndi Mulungu kukuphunzitsani. Kodi pangakhalenso mwayi wina woposa kuphunzitsidwa ndi Yehova, mphunzitsi wathu wamkulu?​—Yesaya 30:20; 54:13.

Mkulu wa gulu la nkhondo la Asuri wotchedwa Namani, anali munthu amene anavutika kulandira uphungu kuchokera kwa munthu wotsika. Pofuna kuti achiritsidwe khate lake, anapita kukaonana ndi mneneri wa Yehova, Elisa. Komano, malangizo a Mulungu onena za mmene Namani achiritsidwire anaperekedwa kwa mtumiki wa Elisa. Malangizowo komanso mmene anaperekedwera zinayesa kudzichepetsa kwa Namani, kotero kuti poyamba anakana kumvera mawu a mneneri wa Mulunguyo. Komano patapita nthawi Namani anasintha maganizo ake ndipo anachiritsidwa. (2 Mafumu 5:9-14) Timakumana ndi vuto lofanana ndi limeneli pamene tikufuna kuphunzira Baibulo. Tingaphunzire kuti ngati tikufuna kuchira mwauzimu ndi kusintha khalidwe lathu, tifunikira kutsatira njira yatsopano ya moyo. Kodi tidzadzichepetsa ndi kulola kuti munthu wina atiphunzitse zimene tifunikira kuchita? Anthu amene ali ndi mtima wophunzitsika ndiwo okhawo amene angasangalale kumvetsa Baibulo.

Mwamuna wina waudindo wake mu ufumu wa Kandake, mfumukazi ya ku Aitiopiya, anasonyeza mtima wabwino kwambiri. Anali akubwerera ku Africa pamene anapezana ndi wophunzira Filipo. Filipo atam’funsa mwamunayo ngati anali kumvetsa chimene ankawerenga, mdindoyo anadzichepetsa kwambiri ndipo anayankha kuti: “Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine?” Kenako, atamvetsa Mawu a Mulungu, anabatizidwa. Pambuyo pake, “anapita njira yake wokondwera.”​—Machitidwe 8:27-39.

Mboni za Yehova zambiri ndi anthu wamba. Koma mlungu uliwonse zimachititsa maphunziro a Baibulo m’nyumba za anthu oposa sikisi miliyoni. Popeza Baibulo limaphunzitsa njira yabwino ya moyo, limafotokoza chiyembekezo chodalirika cha m’tsogolo, ndipo limasonyeza mmene anthu angapangire ubwenzi wabwino ndi Mulungu, anthu ambiri aona kuti kuphunzira Baibulo ndi kulimvetsa n’kosangalatsa koposa. Inunso mungasangalale ndi mwayi umenewu.

[Chithunzi patsamba 7]

Namani anavutika kumvera malangizo a mtumiki

[Chithunzi patsamba 7]

Kumvetsa Baibulo kumatsitsimula mtima