Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani Mukapange Ophunzira, ndi Kuwabatiza

Pitani Mukapange Ophunzira, ndi Kuwabatiza

Pitani Mukapange Ophunzira, ndi Kuwabatiza

“Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza,  . .  ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.”​—Mateyu 28:19, 20.

1. Kodi mtundu wa Israyeli unasankha kuchita chiyani pamene unali m’munsi mwa phiri la Sinai?

ZAKA pafupifupi 3,500 zapitazo, anthu onse a mtundu winawake analumbira kwa Mulungu. Atasonkhana m’munsi mwa phiri la Sinai, Aisrayeli ananena poyera kuti: “Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita.” Kuyambira nthawi imeneyo, Aisrayeli anakhala anthu odzipereka kwa Mulungu, ‘chuma chake chapadera.’ (Eksodo 19:5, 8; 24:3) Iwo analakalaka kutetezedwa ndi iye ndiponso kukhala m’dziko “moyenda mkaka ndi uchi” mpaka mibadwo yambiri yam’tsogolo.​—Levitiko 20:24.

2. Kodi masiku ano anthu angakhale paubwenzi wotani ndi Mulungu?

2 Koma wamasalmo Asafu anati, Aisrayeli ‘sanasunge chipangano cha Mulungu ndipo anakana kuyenda m’chilamulo chake.’ (Salmo 78:10) Analephera kusunga lumbiro limene makolo awo analumbira kwa Yehova. M’kupita kwa nthawi, mtunduwo sunalinso paubwenzi wapadera ndi Mulungu. (Mlaliki 5:4; Mateyu 23:37, 38) Chifukwa cha zimenezi, Mulungu “anayang’anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake.” (Machitidwe 15:14) Ndipo m’masiku otsiriza ano, Mulungu akusonkhanitsa pamodzi “khamu lalikulu, loti palibe munthu [akhoza] kuliwerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe,” omwe mosangalala akunena kuti: “Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.”​—Chivumbulutso 7:9, 10.

3. Kodi munthu amafunika kuchita chiyani kuti akhale paubwenzi ndi Mulungu?

3 Kuti tikhale pakati pa anthu amene ali ndi ubwenzi wapadera ndi Mulungu, tifunika kudzipereka kwa Iye ndi kuonetsa poyera kudzipereka kwathu mwa kubatizidwa m’madzi. Kuchita zimenezi ndiko kumvera lamulo la Yesu kwa ophunzira ake lakuti: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Aisrayeli ankamvetsera pamene “buku la Chipangano” linkawerengedwa. (Eksodo 24:3, 7, 8) Chifukwa cha zimenezi, anamvetsa zimene Yehova anafuna kuti iwo achite. N’chimodzimodzinso masiku ano. Munthu asanaganize zobatizidwa, amafunika kudziwa molondola chifuniro cha Mulungu chomwe chili m’Mawu ake, Baibulo.

4. Kodi munthu afunika kuchita chiyani kuti ayenerere ubatizo? (Phatikizanipo bokosi lili pamwambali.)

4 N’zoonekeratu kuti, Yesu anafuna kuti ophunzira ake asanabatizidwe akhale kaye ndi maziko olimba a chikhulupiriro chawo. Iye sanangouza otsatira ake kupita kukapanga ophunzira koma anawauzanso kuti akawaphunzitse ‘kusunga zinthu zonse zimene anawalamulira.’ (Mateyu 7:24, 25; Aefeso 3:17-19) Motero, anthu amene amayenerera ubatizo nthawi zambiri amakhala ataphunzira Baibulo kwa miyezi ingapo kapena kwa chaka chimodzi kapenanso ziwiri. Amatero kuti asafulumire kusankha zochita komanso azidziwa bwinobwino zimene akuchitazo. Panthawi ya ubatizo, ofuna kubatizidwa amafunsidwa mafunso awiri ofunika kwambiri ndipo amayankha kuti, inde. Kuonanso mosamala tanthauzo la mafunso awiri a paubatizo amenewa kutithandiza tonsefe chifukwa Yesu anagogomezera kuti, Inde wathu akhale inde, ndi Iyayi, iyayi.​—Mateyu 5:37.

Kulapa Ndiponso Kudzipereka

5. Kodi n’zinthu ziwiri ziti zofunika zimene funso loyamba la paubatizo limagogomezera?

5 Funso loyamba la paubatizo limafunsa wofuna kubatizidwa ngati walapa, kusiya moyo wake wakale n’kudzipereka kwa Yehova kuti achite chifuniro chake. Funso limeneli limagogomezera zinthu ziwiri zofunika zimene munthu ayenera kuchita asanabatizidwe. Zimenezi ndizo, kulapa ndi kudzipereka.

6, 7. (a) N’chifukwa chiyani onse ofuna kubatizidwa afunika kulapa? (b) Kodi munthu afunika kusintha chiyani akalapa?

6 N’chifukwa chiyani munthu afunika kulapa asanabatizidwe? Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Ife tonsenso tinagonera . . . kale, m’zilakolako za thupi lathu.” (Aefeso 2:3) Tisanadziwe molondola chifuniro cha Mulungu, moyo wathu unali wogwirizana ndi makhalidwe ndiponso mfundo zimene dziko limayendera. Mulungu wa nthawi ino, Satana, anali kulamulira moyo wathu. (2 Akorinto 4:4) Koma titadziwa chifuniro cha Mulungu, tinasankha kusakhala “moyo m’thupi kutsata zilakolako za anthu, koma chifuniro cha Mulungu.”​—1 Petro 4:2.

7 Moyo watsopano umenewu umapindulitsa kwambiri. Chofunika kwambiri n’chakuti, umathandiza munthu kukhala paubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova. Davide anayerekezera ubwenzi umenewu ndi kuitanidwa kukalowa “m’chihema” ndi ‘m’phiri lopatulika’ la Mulungu, womwe ndi mwayi waukulu kwambiri. (Salmo 15:1) N’zoonekeratu kuti, Yehova sangangoitana aliyense koma okhawo ‘oyenda mokwanira, nachita chilungamo, nanena zoonadi mumtima mwawo.’ (Salmo 15:2) Malinga ndi mmene moyo wathu unalili tisanaphunzire choonadi, tingafunike kusintha khalidwe ndi umunthu wathu kuti tichite zimenezi. (1 Akorinto 6:9-11; Akolose 3:5-10) Chomwe chingapangitse munthu kuti asinthe motero ndiko kulapa, kapena kuti kumva chisoni chifukwa cha moyo wathu wakale, ndiponso kufuna kwambiri kusangalatsa Yehova. Zimenezi zimathandiza munthu kusinthiratu, kusiya moyo wodzikonda wa dziko ndi kukhala moyo wosangalatsa Mulungu.​—Machitidwe 3:19.

8. Kodi timadzipereka bwanji, ndipo kodi ubatizo umagwirizana bwanji ndi kudzipereka?

8 Mbali yachiwiri ya funso loyamba la paubatizo imafunsa ofuna kubatizidwa ngati adzipereka kwa Yehova kuti achite chifuniro chake. Kudzipereka n’chinthu chofunika kwambiri chimene munthu ayenera kuchita asanabatizidwe. Timadzipereka mwa kupemphera, kumuuza Yehova kudzera mwa Kristu kuti tikufunitsitsa ndi mtima wonse kupereka moyo wathu kwa Iye. (Aroma 14:7, 8; 2 Akorinto 5:15) Ndiyeno Yehova amakhala Mbuye wathu ndipo timakhala anthu ake. Ndipo, mofanana ndi Yesu timasangalala kuchita chifuniro cha Mulungu. (Salmo 40:8; Aefeso 6:6) Lonjezo lofunika limeneli timalipanga kamodzi kokha. Popeza timadzipereka tili patokha, kulengeza poyera patsiku laubatizo kumadziwitsa aliyense kuti tadzipereka kwa Atate wathu wa kumwamba.​—Aroma 10:10.

9, 10. (a) Kodi tifunika kuchita chiyani kuti tichite chifuniro cha Mulungu? (b) Ngakhale akuluakulu a Anazi anazindikira motani kudzipereka kwathu?

9 Kodi timafunika kuchita chiyani kuti titsanzire Yesu pochita chifuniro cha Mulungu? Yesu anati kwa ophunzira ake: “Ngati munthu akufuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo ndipo anditsate ine mosalekeza.” (Mateyu 16:24, NW) Pa lembali Yesu ananena zinthu zitatu zimene tifunika kuchita. Choyamba, ‘tidzikane’ tokha. M’mawu ena, tikane maganizo odzikonda amene timakhala nawo ndipo tilolere kuti Mulungu atilangize ndi kutitsogolera. Chachiwiri, ‘tinyamule mtengo wathu wozunzikirapo.’ M’nthawi ya Yesu mtengo wozunzikirapo unali kuimira kuchititsidwa manyazi ndi kuvutika. Chifukwa choti ndife Akristu, timavomereza kuti nthawi zina tidzavutika chifukwa cha uthenga wabwino. (2 Timoteo 1:8) Ngakhale kuti anthu angatitsutse ndi kutinyoza, mofanana ndi Kristu ‘timanyoza manyazi’ ndipo timakhala achimwemwe podziwa kuti tikusangalatsa Mulungu. (Ahebri 12:2) Chomaliza, timatsata Yesu “mosalekeza.”​—Salmo 73:26; 119:44; 145:2.

10 N’zochititsa chidwi kuti, ngakhale anthu ena otsutsa amazindikira kuti kudzipereka kwa Mulungu kumene Mboni za Yehova zasonyeza kuti zim’tumikire ndi mtima wonse n’kofunika. Mwachitsanzo, m’ndende yozunzirako anthu ya Buchenwald mu ulamuliro wa Anazi ku Germany, Mboni zimene zinakana kusiya chikhulupiriro chawo ankaziuza kuti zisaine pepala lomwe linali ndi mawu akuti: “Ndidakali Wophunzira Baibulo wodzipereka ndipo sindidzaswa lonjezo langa kwa Yehova.” Zoonadi, mawuwa amafotokoza bwino kwambiri maganizo a atumiki onse okhulupirika a Mulungu.​—Machitidwe 5:32.

Kudziwika Kuti Ndinu wa Mboni za Yehova

11. Kodi munthu amene wabatizidwa amakhala ndi mwayi wotani?

11 Funso lachiwiri, choyamba limafunsa wofuna kubatizidwa ngati akuzindikira kuti ubatizo wake umamudziwikitsa kuti ndi wa Mboni za Yehova. Akabatizidwa amakhala mtumiki woikidwa wodziwika ndi dzina la Yehova. Umenewu ndi mwayi waukulu ndiponso udindo wofunika kwambiri. Ubatizo umachititsanso munthu wobatizidwayo kukhala ndi chiyembekezo chopulumuka kosatha, malinga ngati akhalabe wokhulupirika kwa Yehova.​—Mateyu 24:13.

12. Kodi mwayi wodziwika ndi dzina la Yehova umabweretsa udindo wotani?

12 Ndithudi, ndi mwayi wapadera kwambiri kudziwika ndi dzina la Mulungu wamphamvuyonse, Yehova. Mneneri Mika anati: “Mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m’dzina la mlungu wake, ndipo ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthawi yomka muyaya.” (Mika 4:5) Komabe, mwayi umenewu umabwera ndi udindo. Tiziyesetsa kuti moyo wathu uzilemekezetsa dzina la Yehova, limene timadziwika nalo. Monga mmene Paulo anakumbutsira Akristu ku Roma, ngati munthu achita zinthu mosemphana ndi zimene amakhulupirira, dzina la Mulungu ‘limachitidwa mwano,’ kapena kunyozedwa.​—Aroma 2:21-24.

13. N’chifukwa chiyani atumiki odzipereka a Yehova ali ndi udindo wochitira umboni za Mulungu wawo?

13 Munthu akakhala wa Mboni za Yehova, amalandiranso udindo wochitira umboni za Mulungu wake. Yehova anauza mtundu wodzipereka wa Israyeli kuti ukhale mboni zake n’cholinga choti achitire umboni zoti iye ndi Mulungu wosatha. (Yesaya 43:10-12, 21) Koma mtunduwo unalephera kukwaniritsa udindo umenewu, ndipo m’kupita kwa nthawi Yehova anawakana. Masiku ano, Akristu oona amanyadira kukhala ndi mwayi wochitira umboni dzina la Yehova. Timachita zimenezi chifukwa timamukonda ndipo timafuna kuti dzina lake liyeretsedwe. Kodi tingasiyirenji kuuza ena pamene tikudziwa choonadi chonena za Atate wathu wa kumwamba ndi chifuniro chake? Timamva mofanana ndi mtumwi Paulo amene anati: “Chondikakamiza ndigwidwa nacho; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino.”​—1 Akorinto 9:16.

14, 15. (a) Kodi gulu la Yehova limatithandiza bwanji kukula mwauzimu? (b) Kodi pali zinthu zotani zimene zimatithandiza mwauzimu?

14 Funso lachiwiri nalonso limakumbutsa wofuna kubatizidwa udindo wake wochita zinthu mogwirizana ndi gulu la Yehova lotsogozedwa ndi mzimu. Sitili tokha potumikira Mulungu, ndipo timafunikira kuthandizidwa ndi kulimbikitsidwa ndi gulu lonse la abale. (1 Petro 2:17; 1 Akorinto 12:12, 13) Gulu la Mulungu limatithandiza kwambiri kuti tikule mwauzimu. Limatipatsa mabuku ambiri ofotokoza za m’Baibulo amene amatithandiza kupitirizabe kudziwa zinthu molondola, kuchita zinthu mwanzeru tikakumana ndi mavuto, ndiponso kukhala ndi ubwenzi wolimba ndi Mulungu. Mofanana ndi mayi amene amaonetsetsa kuti mwana wake amadya ndi kusamalidwa bwino, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amatipatsa chakudya chauzimu chambiri panthawi yake chotithandiza kukula mwauzimu.​—Mateyu 24:45-47; 1 Atesalonika 2:7, 8.

15 Pa misonkhano ya mlungu ndi mlungu, anthu a Yehova amaphunzitsidwa ndi kulimbikitsidwa kuti akhale Mboni zokhulupirika za Yehova. (Ahebri 10:24, 25) Sukulu ya Utumiki wa Mulungu imatiphunzitsa kulankhula ndi anthu, ndipo Msonkhano wa Utumiki umatiphuzitsa kulengeza uthenga wathu mogwira mtima. Pa misonkhano yathu ndiponso pophunzira patokha mabuku ofotokoza za m’Baibulo, timaona mzimu wa Yehova ukugwira ntchito potsogolera gulu lake. Mwa kugwiritsa ntchito zinthu zomwe timalandira nthawi zonse, Mulungu amatichenjeza, amatiphunzitsa kukhala atumiki ogwira mtima, ndipo amatithandiza kukhala atcheru mwauzimu.​—Salmo 19:7, 8, 11; 1 Atesalonika 5:6, 11; 1 Timoteo 4:13.

Chomwe Chimalimbikitsa Munthu Kubatizidwa

16. Kodi n’chiyani chimatilimbikitsa kudzipereka kwa Yehova?

16 Chotero, mafunso awiri a paubatizo amakumbutsa ofuna kubatizidwa kufunika kwa ubatizo wa m’madzi ndi maudindo amene umabweretsa. Ndiyeno, n’chiyani chimene chiyenera kuwalimbikitsa kuti abatizidwe? Timakhala akristu obatizidwa osati chifukwa choti wina amatikakamiza kutero, koma chifukwa chakuti Yehova ‘amatikoka.’ (Yohane 6:44) Popeza “Mulungu ndiye chikondi,” iye amalamulira chilengedwe chonse mwachikondi, osati mokakamiza. (1 Yohane 4:8) Timakonda Yehova chifukwa cha makhalidwe ake abwino ndiponso mmene amachitira nafe zinthu. Yehova anatipatsa Mwana wake wobadwa yekha ndipo watilonjeza tsogolo labwino kwambiri. (Yohane 3:16) Ifenso timalimbikitsidwa kupereka moyo wathu kwa iye.​—Miyambo 3:9; 2 Akorinto 5:14, 15.

17. Kodi ife sitinadzipereke kuti tichite chiyani?

17 Sitimadzipereka kuti tikwaniritse mfundo zinazake kapena kuchita ntchito inayake koma timadzipereka kwa Yehova. Ntchito imene Mulungu wapatsa anthu ake ingasinthe, koma kudzipereka kwawo kwa iye sikusintha. Mwachitsanzo, zimene Yehova anauza Abrahamu kuti achite n’zosiyana ndi zimene anauza Yeremiya. (Genesis 13:17, 18; Yeremiya 1:6, 7) Koma onse awiri anachita ntchito imene Mulungu anawauza kuti achite chifukwa choti ankakonda Yehova ndipo ankafuna kuchita chifuniro chake mokhulupirika. M’nthawi ya mapeto ino, otsatira a Kristu onse obatizidwa amayesetsa kutsatira lamulo la Kristu la kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Kuchita ntchito imeneyi ndi mtima wonse ndi njira yabwino kwambiri yosonyeza kuti timakonda Atate wathu wa kumwamba ndipo tinadziperekadi kwa iye.​—1 Yohane 5:3.

18, 19. (a) Kodi timalengeza chiyani kwa anthu onse tikamabatizidwa? (b) Kodi tiphunzira chiyani m’nkhani yotsatira?

18 Mosakayikira, ubatizo umatithandiza kukhala ndi madalitso ambiri, koma sitiyenera kuuona mopepuka. (Luka 14:26-33) Ubatizo ndi chinthu chofunika kwambiri kuposa udindo uliwonse. (Luka 9:62) Tikabatizidwa, timakhala tikulengeza kwa anthu onse kuti: “Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu ku nthawi za nthawi: Adzatitsogolera kufikira imfa.”​—Salmo 48:14.

19 Nkhani yotsatira ifotokozanso mafunso ena amene angakhalepo okhudza ubatizo wa m’madzi. Kodi munthu angakhale ndi zifukwa zomveka zosafunira kubatizidwa? Kodi msinkhu wa munthu ungamulepheretse kubatizidwa? Kodi anthu onse angalemekeze bwanji mwambo wa ubatizo?

Kodi Mungafotokoze?

• N’chifukwa chiyani Mkristu aliyense amafunika kulapa asanabatizidwe?

• Kodi timafunika kuchita chiyani ngati tadzipereka kwa Mulungu?

• Kodi mwayi wodziwika ndi dzina la Yehova umabweretsa maudindo otani?

• Kodi n’chiyani chiyenera kutilimbikitsa kubatizidwa?

[Mafunso]

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 22]

Mafunso Awiri a Paubatizo

Pa maziko a nsembe ya Yesu Kristu, kodi mwalapa machimo anu ndi kudzipereka kwa Yehova kuti muchite chifuniro chake?

Kodi mukuzindikira kuti kudzipereka ndi kubatizidwa kwanu kukutanthauza kuti tsopano ndinu wa Mboni za Yehova wogwirizana ndi gulu la Mulungu lotsogoleredwa ndi mzimu?

[Chithunzi patsamba 23]

Kudzipereka ndi lonjezo lofunika kwambiri limene mumapanga mwa kupemphera kwa Yehova

[Chithunzi patsamba 25]

Ntchito yathu yolalikira imasonyeza kudzipereka kwathu kwa Mulungu