Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsanzirani Kristu Mukamalamulira Ena

Tsanzirani Kristu Mukamalamulira Ena

Tsanzirani Kristu Mukamalamulira Ena

ZAKA zingapo zapitazo, ofufuza za khalidwe la anthu anapeza zinthu zochititsa chidwi kwambiri. Anthu amene ankachita nawo kafukufuku ameneyu anagawidwa m’magulu awiri. Anthu a m’gulu limodzi anaikidwa kukhala alonda ndipo anauzidwa kuti aziyang’anira anthu a m’gulu linalo, amene anaikidwa kukhala akaidi. Kodi chinachitika n’chiyani?

“Patapita masiku ochepa,” ochita kafukufukuwo ananena kuti, “[alonda] ambiri ankagwiritsa ntchito mawu otukwana ndipo anali ankhanza. Nthawi zambiri ankapereka zibalo. Koma amene anakhala akaidiwo anali amantha kwambiri ndipo ankagonjera pa chilichonse.” Pamapeto pake ochita kafukufukuwo anati: Munthu aliyense angagwere mu msampha wa kugwiritsa ntchito ulamuliro mosayenera.

Kulamulira Ena Moyenera ndi Mosayenera

N’zoona kuti kugwiritsa ntchito ulamuliro moyenera kumathandiza. Anthu amatsogoleredwa bwino ndipo amakhala athanzi, auzimu ndipo savutika maganizo. (Miyambo 1:5; Yesaya 48:17, 18) Koma monga mmene kafukufuku amene watchulidwa pamwambapa wasonyezera, nthawi zonse pamakhala msampha woti wina angagwiritse ntchito ulamuliro mosayenera. Baibulo limanena za msampha umenewu ndipo limati: “Polamulira woipa anthu ausa moyo.”​—Miyambo 29:2; Mlaliki 8:9.

Pamakhala mavuto aakulu ngati wina agwiritsa ntchito mosayenera ulamuliro wake, ngakhale ngati akuchita zimenezo ndi zolinga zabwino. Mwachitsanzo, posachedwapa gulu lina la aphunzitsi achipembedzo ku Ireland linapepesa poyera chifukwa cha mmene aphunzitsi ena anagwiritsira ntchito ulamuliro wawo poyang’anira ana amene ankawasamalira. Mosakayikira, zolinga za ambiri mwa aphunzitsi amenewa zinali zabwino, koma njira zimene ena anagwiritsa ntchito zinali zoipa kwambiri. Nyuzipepala ina (The Irish Times) inanena kuti “ana ambiri anavulazidwa maganizo chifukwa cha chiwawa ndi nkhanza yaikulu imene aphunzitsi ambiri achipembedzowoanali kuchita.” Choncho, kodi mungalamulire bwanji ena kuti muwathandize kuchita bwino m’malo moti akhale adani anu chifukwa cha zimene mumalankhula ndi kuchita?​—Miyambo 12:18.

“Mphamvu Zonse” Zinapatsidwa kwa Yesu Kristu

Taganizirani chitsanzo cha Yesu Kristu. Iye atatsala pang’ono kupita kumwamba, anauza ophunzira ake kuti: ‘Mphamvu zonse zapatsidwa kwa ine Kumwamba ndi padziko lapansi.’ (Mateyu 28:18) Kodi mawu amenewa anachititsa ophunzira ake kukhala ndi mantha? Kodi anaona kuti Yesu tsopano adzasonyeza mzimu wofanana ndi Akaisara a ku Roma, amene ankadziwika ndi khalidwe lopondereza aliyense amene ankafuna kuukira boma?

Baibulo limasonyeza momveka bwino kuti sanatero. Yesu Kristu anagwiritsa ntchito ulamuliro mofanana ndi mmene Atate wake anachitira. Ngakhale kuti Yehova ndiye Wolamulira wa Chilengedwe Chonse woyenerera, iye amafuna kuti anthu ake azimutumikira mwaufulu osati mwamantha, kapena mosaganiza, ndipo safuna kuti azingomumvera osayamba aganizira kaye. (Mateyu 22:37) Yehova sagwiritsa ntchito ulamuliro wake mosayenera. Masomphenya ochititsa chidwi amene Ezekieli anaona amasonyeza zimenezi.

M’masomphenya amenewa, Ezekieli anaona angelo anayi amene anachirikiza ulamuliro wa Mulungu. Mngelo aliyense anali ndi nkhope zinayi. Ezekieli analemba kuti: “Mafaniziro a nkhope zawo zinali nayo nkhope ya munthu; ndi izi zinayi zinali nayo nkhope ya mkango pa mbali ya ku dzanja lamanja; ndi izi zinayi zinali nayo nkhope ya ng’ombe pa mbali ya ku dzanja lamanzere; izi zinayi zinali nayonso nkhope ya chiombankhanga.” (Ezekieli 1:10) Nkhope zinayi zimenezi zimaimira makhalidwe anayi aakulu a Mulungu omwe iye amawasonyeza mwangwiro. Makhalidwe amenewa m’Mawu a Mulungu ndi: chikondi, chomwe chikuimiridwa ndi nkhope ya munthu; chilungamo, chomwe chikuimiridwa ndi nkhope ya mkango; ndi nzeru, zomwe zikuimiridwa ndi nkhope ya chiombankhanga. Makhalidwe atatu amenewa amayendera limodzi ndi khalidwe lachinayi lomwe ndi mphamvu, lomwe likuimiridwa ndi nkhope ya ng’ombe. Kodi zonsezi zikutanthauza chiyani? Masomphenyawa akusonyeza kuti Yehova sagwiritsa ntchito mphamvu zake ndiponso ulamuliro wake wopanda malire m’njira imene sili yogwirizana ndi makhalidwe ake ena aakulu.

Potsanzira Atate wake, Yesu Kristu nthawi zonse anagwiritsa ntchito ulamuliro wake mwachikondi, mwanzeru ndiponso mwachilungamo. Ophunzira a Yesu anatsitsimulidwa potumikira pansi pa ulamuliro wake. (Mateyu 11:28-30) Khalidwe limene Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu amalionetsera kwambiri ndi chikondi, osati mphamvu kapena ulamuliro.​—1 Akorinto 13:13; 1 Yohane 4:8.

Kodi Mumalamulira Ena Motani?

Kodi inuyo mukuchita bwanji pankhani imeneyi? Mwachitsanzo, m’banja, kodi mumagwiritsa ntchito mphamvu zanu kulamulira banja lanu kuti lichite zinthu mogwirizana ndi mmene inuyo mukufunira? Kodi ena amavomereza maganizo anu chifukwa chokuopani kapena chifukwa chokukondani? Kodi a m’banja lanu amakugonjerani chifukwa cha mphamvu zimene muli nazo? Kuti mitu ya mabanja ithe kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna m’banja, iyenera kuganizira mafunso amenewa.​—1 Akorinto 11:3.

Bwanji ngati muli ndi ulamuliro winawake mu mpingo wachikristu? Kuti muone ngati mukuugwiritsa ntchito bwino yerekezerani zochita zanu ndi mfundo zouziridwa ndi Yehova Mulungu ndiponso chitsanzo chimene Yesu Kristu anasonyeza.

“Kapolo wa Ambuye . . . akhale . . . waulere [“wodekha,” NW] pa onse, . . . woleza, wolangiza iwo akutsutsana mofatsa.”​—2 Timoteo 2:24, 25.

Anthu ena mu mpingo woyambirira wachikristu anali ndi ulamuliro waukulu. Mwachitsanzo, Timoteo ankatha ngakhale ‘kulamulira ena kuti asaphunzitse kanthu kena.’ (1 Timoteo 1:3) Ngakhale ndi choncho, ndife otsimikiza kuti Timoteo anasonyeza makhalidwe a Mulungu pa zonse zimene anachita. Tingakhale otsimikiza choncho chifukwa anachitadi mogwirizana ndi malangizo a Paulo akuti ayenera kulangiza “mofatsa,” ndiponso kukhala ‘wodekha kwa onse’ poyang’anira mpingo wachikristu. Chifukwa chakuti iye anali wachinyamata, anafunika kuchita zinthu monga mwana waulemu kwa anthu achikulire ndipo kwa achinyamata anafunika kukhala ngati mbale woganizira ena. (1 Timoteo 5:1, 2) Ngati mpingo wachikristu umasamalidwa mwachikondi choncho, umasonyeza mzimu wosangalala ndi wachikondi, osati mzimu wosaganizira ena ndiponso wankhanza umene umakhala pa kampani ya malonda.​—1 Akorinto 4:14; 1 Atesalonika 2:7, 8.

“Mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye awo, ndipo akulu awo amachita ufumu pa iwo. Sikudzakhala chomwecho kwa inu ayi; koma amene aliyense akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu.”​—Mateyu 20:25, 26.

Olamulira adziko ankhanza “amadziyesa okha ambuye” mwa kuuza anthu kuchita zofuna zawo ndi kuwakakamiza kuchita zinthu mwa njira inayake. Ndipo amawawopseza kuti adzawalanga ngati sachita zimene auzidwa. Koma Yesu Kristu anagogomezera kutumikira ena osati kuwakakamiza kuchita zinthu. (Mateyu 20:27, 28) Iye nthawi zonse ankakonda ophunzira ake ndi kuwasamalira bwino. Mukatsatira chitsanzo cha Yesu, anthu ena savutika kugwirizana nanu. (Ahebri 13:7, 17) Iwo savutikanso kugonjera ulamuliro wanu ndipo amatha kuchita zinthu zoposa zimene mwawapempha. Amachita zimenezi mwaufulu osati mokakamizidwa.​—Mateyu 5:41.

“Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, . . . osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.”​—1 Petro 5:2, 3.

Masiku ano oyang’anira amazindikira kuti Mulungu wawapatsa udindo wosamalira moyo wauzimu wa onse mu mpingo. Amaona kuti udindo umenewu ndi wofunika kwambiri. Posamalira gulu la nkhosa la Mulungu, amayesetsa kuchita zimenezi mwaufulu, mwakhama ndiponso mwachikondi. Mofanana ndi mtumwi Paulo, amachita khama polimbitsa chikhulupiriro cha anthu amene akuwayang’anira, osati mochita ufumu pa chikhulupiriro chawo.​—2 Akorinto 1:24.

Pakafunika kupereka uphungu woyenera, akulu amachita zimenezi mu mzimu wa chifatso n’cholinga chothandiza wolakwa kapena kuthandiza Mkristu mnzawo kuti achite bwino mwauzimu. Iwo amakumbukira mawu a mtumwi Paulo akuti: “Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.”​—Agalatiya 6:1; Ahebri 6:1, 9-12.

“Kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, . . . Khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.”​—Akolose 3:13, 14.

Kodi mungachite bwanji ndi munthu amene walephera kutsatira bwinobwino miyezo yachikristu? Kodi mumaganizira za kupanda ungwiro kwake, monga mmene Yehova ndi Yesu Kristu amachitira? (Yesaya 42:2-4) Kapena kodi mumaumirirabe kuti mulimonse mmene zinthu zilili m’pofunika kuti zioneke kuti lamulo la Mulungu lagwira ntchito basi? (Salmo 130:3) Kumbukirani kuti, ngati pangapezeke chifukwa choyenera, ndi bwino kum’komera mtima munthu koma musamalekerere pamene pakuoneka kuti m’posayenera kulekerera. Kuchita zinthu mwachikondi kudzathandiza kuti anthu amene mukuwalamulira azikudalirani ndi kukukhulupirirani kwambiri ndipo inunso mudzachita chimodzimodzi.

Ngati mwapatsidwa ulamuliro uliwonse, muziyesetsa kutsanzira Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu pogwiritsa ntchito ulamuliro umenewo. Kumbukirani mmene wamasalmo anafotokozera bwino kwambiri mmene Yehova amalamulira anthu ake. Davide anaimba kuti: “Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa. Andigonetsa ku busa lamsipu: anditsogolera ku madzi odikha. Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m’mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.” Mofananamo, ponena za Yesu timawerenga kuti: “Ine ndine Mbusa Wabwino; ndipo ndizindikira zanga, ndi zanga zindizindikira ine, monga Atate andidziwa ine, ndi ine ndim’dziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosa.” Kodi tingakhale ndi zitsanzo zina zabwino pankhani yolamulira ena mwachikondi kuposa Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu?​—Salmo 23:1-3; Yohane 10:14, 15.

[Mawu Otsindika patsamba 18]

Nthawi zonse, Yehova amasonyeza chilungamo, nzeru, ndi chikondi, pogwiritsa ntchito ulamuliro

[Chithunzi patsamba 18]

Nthawi zina, akulu amafunika kupatsa anthu olakwa uphungu wachikondi

[Chithunzi patsamba 19]

Paulo analangiza Timoteo kukhala mwana waulemu ndiponso mbale woganizira ena

[Chithunzi patsamba 20]

Yesu Kristu amagwiritsa ntchito ulamuliro wake mwanzeru, mwachilungamo ndiponso mwachikondi