Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ine Ndili Nanu”

“Ine Ndili Nanu”

“Ine Ndili Nanu”

‘Mthenga wa Yehova . . . ananena . . . kuti, Ine ndili nanu, ati Yehova.’​—HAGAI 1:13.

1. Kodi ndi zochitika zaulosi ziti zofanana ndi zochitika m’masiku athu ano zimene Yesu anatchula?

TIKUKHALA m’nthawi ya zochitika zazikulu m’mbiri ya anthu. Mogwirizana ndi kukwaniritsidwa kwa ulosi wa m’Baibulo, takhala tili mu “tsiku la Ambuye” kuyambira mu 1914. (Chivumbulutso 1:10) N’kutheka kuti mukuidziwa nkhani yokhudza maulosi amenewa, moti mukudziwa kuti Yesu anayerekeza “masiku a Mwana wa munthu” m’mphamvu ya Ufumu wake ndi “masiku a Nowa” komanso “masiku a Loti.” (Luka 17:26, 28) Motero Baibulo limasonyeza kuti zochitika m’masiku a Nowa ndi m’masiku a Loti zinalosera zochitika m’masiku athu ano. Koma pali zochitika zinanso zofanana ndi zochitika m’masiku athu ano, zofunika kuti tiziganizire kwambiri.

2. Kodi Yehova anatuma Hagai ndi Zekariya kuchita chiyani?

2 Tiyeni tione mmene zinalili m’mbuyomo m’masiku a aneneri achihebri, omwe ndi Hagai ndi Zekariya. Kodi aneneri okhulupirika awiriwa anapereka uthenga wanji umene ukukhudza mwachindunji anthu a Yehova m’nthawi yathu ino? Hagai ndi Zekariya anali ‘amithenga a Yehova’ omwe anatumidwa kwa Ayuda atabwerako ku ukapolo wa ku Babulo. Anatumidwa kukatsimikizira Aisrayeli kuti Mulungu adzawathandiza pantchito yomanganso kachisi. (Hagai 1:13; Zekariya 4:8, 9) Ngakhale kuti mabuku omwe Hagai ndi Zekariya analemba ndi ang’onoang’ono, mabukuwa ali mbali ya ‘malemba onse amene adawauzira Mulungu, amene ndi opindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.’​—2 Timoteo 3:16.

Ulosi wa M’mabukuwa Ukutikhudza

3, 4. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi chidwi ndi uthenga wa Hagai ndi Zekariya?

3 Mosakayikira, uthenga wa Hagai ndi Zekariya unali wopindulitsa kwa Ayuda a m’nthawi yawo, ndipo zimene iwo analosera zinakwaniritsidwa panthawiyo. Komano tingadziwe bwanji kuti zimene zili m’mabuku awiriwa zikutikhudza? Yankho tikulipeza pa Ahebri 12:26-29. Palembali, mtumwi Paulo anagwira mawu lemba la Hagai 2:6, limene limanena kuti Mulungu ‘adzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi.’ Kugwedeza kumeneku ‘kudzagubuduza mipando yachifumu ya maufumu, ndi kuwonongeratu mphamvu ya maufumu a amitundu.’​—Hagai 2:22.

4 Pogwira mawu Hagai, Paulo anatchula zimene zidzachitikire “maufumu a amitundu,” ndipo anafotokoza kuti Ufumu wosagwedera umene Akristu odzozedwa adzalandire ndi wapamwamba koposa. (Ahebri 12:28) Mungathe kuona pamenepa kuti ulosi wa Hagai ndi Zekariya unali kunena za nthawi imene inali isanakwane pamene buku la Ahebri linkalembedwa, m’nthawi ya atumwi. Tikunena pano, padziko lapansi pano padakali ena mwa Akristu odzozedwa, omwe adzalowe limodzi ndi Yesu mu Ufumu wa Mesiya. Motero, maulosi a Hagai ndi Zekariya ndi ofunika m’masiku athu ano.

5, 6. Kodi zinthu zinali bwanji Hagai ndi Zekariya asanayambe ntchito yawo?

5 Buku la Ezara limafotokoza mmene zinthu zinalili Hagai ndi Zekariya asanayambe kulemba maulosi awo. Ayuda atabwerako ku ukapolo wa ku Babulo mu 537 B.C.E., Bwanamkubwa Zerubabele ndi Mkulu wa Ansembe Yoswa (kapena kuti Yesuwa), anayang’anira ntchito yomanga maziko a kachisi watsopano mu 536 B.C.E. (Ezara 3:8-13; 5:1) Ngakhale kuti izi zinali zosangalatsa kwambiri, sipanapite nthawi yaitali, Ayudawo anayamba kugwidwa mantha. Adani awo, “anthu a m’dziko anafooketsa manja a anthu Ayuda, nawavuta pomanga,” limatero lemba la Ezara 4:4. Adani amenewa, makamaka Asamariya, anali kunenera Ayuda zonama. Otsutsawa anachititsa kuti mfumu ya Perisiya iletse ntchito yomanga kachisiyo.​—Ezara 4:10-21.

6 Changu chimene anthuwo anali nacho poyamba kumanga kachisi chinatheratu. Ayuda anayamba kudzikundikira zinthu zaumwini. Koma m’chaka cha 520 B.C.E., patapita zaka 16 chimangireni maziko a kachisi, Yehova anadzutsa Hagai ndi Zekariya kuti alimbikitse anthu kuyambanso ntchito yomanga kachisi. (Hagai 1:1; Zekariya 1:1) Polimbikitsidwa ndi amithenga a Mulungu, ndiponso pokhala ndi umboni wonse wakuti Yehova awathandiza, Ayuda anayambanso kumanga kachisi mpaka kum’maliza m’chaka cha 515 B.C.E.​—Ezara 6:14, 15.

7. Kodi mmene zinthu zinalili m’masiku a aneneriwa, zikufanana motani ndi masiku ano?

7 Kodi mukudziwa tanthauzo la zonsezi kwa ife? Tili ndi ntchito yoti tichite yokhudzana ndi kulalikira “uthenga . . . wabwino wa Ufumu.” (Mateyu 24:14) Nkhondo yoyamba ya padziko lonse itangotha, anthu analimbikitsidwa kwambiri kuchita ntchito imeneyi. Mofanana ndi kuti Ayuda akale anamasulidwa ku ukapolo ku Babulo, nawonso atumiki a Yehova amakono anamasulidwa ku ukapolo wa Babulo Wamkulu, yemwe ndi ufumu wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga. Anthu odzozedwa a Mulungu anadzipereka pantchito yolalikira, kuphunzitsa, ndi kutsogolera anthu kuti ayambe kulambira koona. Ntchitoyi ikupitirira lerolino komanso ikuchitika m’madera ambiri, ndipo n’kutheka kuti inuyo mukuchita nawo ntchito imeneyi. Ino ndiyo nthawi yoti ntchitoyi ichitike, chifukwa mapeto a dziko loipali ali pafupi kwambiri. Ntchito yomwe Mulungu watipatsayi iyenera kupitirira mpaka pamene Yehova adzalowerere pa zochita za anthu pa ‘chisautso chachikulu.’ (Mateyu 24:21) Izi zidzathetsa kuipa ndi kutsegula njira yoti kulambira koona kufike padziko lonse.

8. N’chifukwa chiyani tingakhale ndi chikhulupiriro chakuti Mulungu ali nafe pantchito yathu?

8 Monga momwe maulosi a Hagai ndi Zekariya akusonyezera, tingakhale ndi chikhulupiriro choti Yehova ali nafe ndipo atidalitsa ngati tikuchita nawo ntchitoyi ndi mtima wonse. Ngakhale kuti anthu ena akuyesetsa kupondereza atumiki a Mulungu kapena kuletsa ntchito yomwe iwo anapatsidwa, palibe boma lililonse lomwe laimitsa ntchito yolalikira. Ganizirani mmene Yehova wadalitsira ntchito ya Ufumu kuti ikule kuyambira pamene nkhondo yoyamba ya padziko lonse inatha kudzafika m’nthawi yathu ino. Komabe, padakali ntchito yaikulu yoti tichite.

9. Kodi ndi zochitika zakale ziti zomwe tiyenera kuziganizira ndipo n’chifukwa chiyani?

9 Kodi zimene tingaphunzire kwa Hagai ndi Zekariya zingatilimbikitse motani kumvera lamulo la Mulungu lolalikira ndi kuphunzitsa? Tiyeni tione zina mwa zinthu zimene tingaphunzire m’mabuku awiri a m’Baibulo amenewa. Mwachitsanzo, taonani mfundo zingapo zokhudza ntchito yomanga kachisi yomwe Ayuda obwerera kwawo anafunika kuchita. Monga tafotokozera kale, Ayuda amene anabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Babulo sanapitirize ntchito yawo yomanga kachisi. Atamanga maziko, anafooka pantchitoyo. Kodi ndi malingaliro olakwika otani amene iwo anakhala nawo? Ndipo kodi tingaphunzirepo chiyani?

Tisakhale ndi Malingaliro Olakwika

10. Kodi Ayuda anali ndi malingaliro olakwika ati, ndipo chotsatirapo chake chinali chiyani?

10 Ayuda amene anabwerera kwawo anali kunena kuti: “Nthawi siinafike.” (Hagai 1:2) Poyamba kumanga kachisi, pamene anamanga maziko ake mu 536 B.C.E., iwo sankanena kuti “nthawi siinafike.” Koma posapita nthawi, anagonjera chitsutso cha anthu oyandikana nawo ndiponso kulowererapo kwa boma. Ayudawo anayamba kuika mtima wawo pa nyumba zawo ndi katundu wawo. Poona kusiyana komwe kunalipo pakati pa nyumba zawo zomwe zinali zotchingidwa ndi matabwa abwino kwambiri ndi kachisi amene anali wosamaliza, Yehova anawafunsa kuti: “Kodi imeneyi ndiyo nthawi yakuti inu nokha mukhala m’nyumba zanu zotchingidwa m’katimo, ndi nyumba iyi ikhale yopasuka?”​—Hagai 1:4.

11. N’chifukwa chiyani Yehova anafunika kulangiza Ayuda a m’nthawi ya Hagai?

11 Inde, Ayuda anali atasintha zinthu zimene anali kuziika patsogolo m’moyo wawo. M’malo motsogoza cholinga cha Yehova chomanga kachisi, anthu a Mulungu anayamba kungoganiza za iwo eni ndi nyumba zawo. Iwo ananyalanyaza ntchito yomanga nyumba yolambiriramo ya Mulungu. Mawu a Yehova omwe ali pa Hagai 1:5 analimbikitsa Ayuda kuti ‘mtima wawo usamalire njira zawo.’ Yehova anali kuwauza kuti asinkhesinkhe zimene anali kuchita ndi kuona mmene zinali kuwakhudzira polephera kutsogoza ntchito yomanga kachisi pamoyo wawo.

12, 13. Kodi lemba la Hagai 1:6 likufotokoza motani moyo wa Ayuda, ndipo kodi vesili likutanthauza chiyani?

12 Mukhoza kuona nokha kuti, kulakwitsa komwe Ayuda anachita poika zinthu zina patsogolo, kunawalowetsa m’mavuto. Taonani maganizo a Mulungu omwe ali pa Hagai 1:6: “Mwadzala zambiri, koma mututa pang’ono; mukudya, koma osakhuta; mukumwa, koma osakoledwa; mudziveka, koma palibe wofundidwa; ndi iye wolembedwa ntchito yakulipidwa alandirira kulipirako m’thumba lobooka.”

13 Ayuda anali m’dziko limene Mulungu anawapatsa, koma dzikolo silinali kutulutsa zakudya zochuluka monga mmene iwo anali kuyembekezerera. Yehova sanali kuikapo madalitso ake, monga momwe anali atawachenjezera kale. (Deuteronomo 28:38-48) Popanda iye kuwathandiza, Ayudawo anali kubzala, koma anali kukolola zochepa kwambiri, zosawakwanira. Popanda madalitso a Yehova, iwo sankatha kupeza zovala zofunda bwino. Zinali kuonekanso ngati kuti ndalama zimene alandira monga malipiro pa ntchito imene agwira anali kuziika m’thumba lobookabooka, moti mwini ndalamazo sankapindula nazo. Kodi mawu akuti “mukumwa, koma osakoledwa” akutanthauza chiyani kwenikweni? Mawu amenewa sakutanthauza kuti kukoledwa, kapena kuti kuledzera, kukanakhala chizindikiro chakuti Mulungu akuwadalitsa ayi. Mulungu amadana ndi kuledzera. (1 Samueli 25:36; Miyambo 23:29-35) M’malo mwake, mawu amenewa akusonyezanso kuti Ayuda analibe madalitso a Mulungu. Vinyo aliyense yemwe ankapanga anali wochepa, osati wochuluka woti akamwa n’kukoledwa naye. Pa Hagai 1:6, Baibulo la Malembo Oyera limati: “Mumamwa, koma osapha ludzu.”

14, 15. Kodi ndi phunziro lotani lomwe tikulipeza pa Hagai 1:6?

14 Phunziro kwa ife pa zonsezi si la mamangidwe ndi kakongoletsedwe ka nyumba ayi. Kale kwambiri anthuwa asanapite ku ukapolo, mneneri Amosi anadzudzula anthu olemera mu Israyeli chifukwa cha “nyumba zaminyanga” ndiponso chifukwa ‘chogona pa makama aminyanga.’ (Amosi 3:15; 6:4) Nyumba zawo zochititsa kasozo ndiponso katundu wawo wokongolayo sizinakhalitse. Adani awo anawalanda zinthu zimenezi. Komabe, patatha zaka zambiri, pambuyo pa ukapolo wa zaka 70, ambiri mwa anthu a Mulungu sanatolepo phunziro lililonse pamenepa. Nanga bwanji ifeyo? Ndi bwino kuti aliyense wa ife adzifunse kuti: ‘Kunena zoona, kodi ndimaikirapo mtima motani pa nyumba yanga ndiponso kuikongoletsa? Nanga bwanji zokonza za maphunziro owonjezera pofuna kukulitsa luso pantchito yanga, ngakhale kuti kuchita zimenezi kungafune nthawi yambiri ndithu kwa zaka zingapo, n’kusokoneza zinthu zofunika kwambiri pa moyo wanga wauzimu?’​—Luka 12:20, 21; 1 Timoteo 6:17-19.

15 Zimene timawerenga pa Hagai 1:6 ziyenera kutithandiza kuganizira mfundo yakuti timafunikira madalitso a Mulungu pa moyo wathu. Ayuda akale aja analibe madalitso a Mulungu, ndipo zotsatirapo zake zinali zoopsa kwambiri. Kaya ndife olemera kapena ayi, ngati sitilandira madalitso a Yehova, n’zodziwikiratu kuti moyo wathu wauzimu udzasokonekera kwambiri. (Mateyu 25:34-40; 2 Akorinto 9:8-12) Komano, kodi tingatani kuti tilandire madalitso amenewo?

Yehova Amathandiza ndi Mzimu Wake

16-18. Kalekalelo, kodi lemba la Zekariya 4:6 linatanthauzanji?

16 Mneneri mnzake wa Hagai, Zekariya, anauziridwa kuti asonyeze njira yomwe Yehova analimbikitsira ndi kudalitsira anthu odzipereka panthawiyo. Ndipo izi zikusonyeza mmenenso angakudalitsireni. Timawerenga kuti: “Ndi khamu la nkhondo ayi, ndi mphamvu ayi, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu.” (Zekariya 4:6) N’kutheka kuti vesili talimva akuligwira mawu nthawi zambiri, koma kodi linatanthauzanji kwa Ayuda m’masiku a Hagai ndi Zekariya, ndipo kodi likutanthauzanji kwa inu?

17 Kumbukirani kuti mawu ouziridwa a Hagai ndi Zekariya anathandiza kwambiri panthawiyo. Zimene aneneri awiriwa ananena zinalimbikitsa Ayuda okhulupirika. Hagai anayamba kulosera m’mwezi wachisanu ndi chimodzi m’chaka cha 520 B.C.E. Zekariya anayamba kulosera m’mwezi wachisanu ndi chitatu chaka chomwecho. (Zekariya 1:1) Monga momwe mukuonera pa Hagai 2:18, ntchito yomanga maziko inayambikanso mwakhama m’mwezi wachisanu ndi chinayi. Choncho Ayuda analimbikitsidwa kuchitapo kanthu, ndipo anamvera Yehova, ali ndi chikhulupiriro kuti iye awathandiza. Mawu a pa Zekariya 4:6 akunena za thandizo la Mulungu.

18 Ayuda atabwerera kwawo mu 537 B.C.E., analibe gulu lankhondo. Koma Yehova anawateteza ndi kuwatsogolera paulendo wawo wochokera ku Babulo. Ndipo mzimu wake unawatsogolera pamene anayamba ntchito yomanga kachisi, patangotha nthawi yochepa atafika kwawoko. Ayudawo atayambanso ndi mtima wonse ntchito yomanga kachisiyo, iye anawathandiza ndi mzimu wake woyera.

19. Kodi mzimu wa Mulungu unagonjetsa mphamvu zazikulu ziti?

19 Mwa masomphenya asanu ndi atatu, Zekariya anatsimikiziridwa kuti Yehova adzakhala ndi anthu ake, amene adzapitiriza ntchito yomanga kachisi mokhulupirika mpaka kuimaliza. Masomphenya achinayi, olembedwa m’chaputala 3, akusonyeza kuti Satana anali pa kalikiliki kulimbana ndi Ayuda kuti asamalize ntchito yawo yomanga kachisi. (Zekariya 3:1) Mosakayikira, Satana sakanakondwa kuona Yoswa, Mkulu wa Ansembe akuchita utumiki wothandiza anthu pakachisi watsopano. Ngakhale kuti Mdyerekezi anali pa kalikiliki kujejemetsa Ayuda kuti asamange kachisiyo, mzimu wa Yehova unathandiza kwambiri pochotsa zopinga ndi kupatsa Ayuda mphamvu zopitirizira ntchitoyo mpaka kumaliza kumanga kachisi.

20. Kodi mzimu woyera unawathandiza motani Ayuda kuchita chifuniro cha Mulungu

20 Panaoneka ngati kuti panali chopinga chosatheka kuchisuntha, chitsutso cha akuluakulu a boma omwe anachititsa kuti ntchitoyo iletsedwe. Koma Yehova analonjeza kuti chooneka ngati “phiri” chimenechi chidzachotsedwa ndipo pamalopo padzakhala “chidikha.” (Zekariya 4:7) Ndipo n’zimene zinachitikadi! Mfumu Dariyo Woyamba anaifufuza nkhaniyo, ndipo anapeza chikalata cha Koresi chololeza Ayuda kumanganso kachisi. Motero Dariyo anachotsa chiletsocho ndipo analamula kuti Ayuda apatsidwe ndalama za m’thumba la mfumu kuti zikathandize pantchitoyo. Ukutu kunali kusintha kodabwitsa kwambiri kwa zinthu! Kodi mzimu wa Mulungu unathandiza kuti zimenezi zichitike choncho? N’zosakayikitsa kuti unatero. Kachisiyo anamalizidwa m’chaka cha 515 B.C.E., m’chaka chachisanu ndi chimodzi cha ulamuliro wa Dariyo Woyamba.​—Ezara 6:1, 15.

21. (a) M’nthawi zakale, kodi Mulungu ‘anagwedeza amitundu onse’ motani, ndipo kodi “zofunika za amitundu onse” zinafika motani? (b) Kodi zimenezi zakwaniritsidwa motani masiku ano?

21 Pa Hagai 2:5, mneneriyo anakumbutsa Ayuda za chipangano chimene Mulungu anachita nawo pa phiri la Sinai, pamene “phiri lonse linagwedezeka kwambiri.” (Eksodo 19:18) M’masiku a Hagai ndi Zekariya, Yehova anali kudzagwedezanso zinthu, monga mmene mawu ophiphiritsa a m’mavesi 6 ndi 7 akusonyezera. Zinthu mu Ufumu wa Perisiya zinali kudzasokonezeka, koma ntchito ya pakachisi inali yoti idzapitirira mpaka kumapeto. Anthu osakhala Ayuda, amene akutchedwa “zofunika za amitundu onse,” adzayamba kulemekeza Mulungu limodzi ndi Ayuda pamalo olambirira amenewo. Pa kukwaniritsidwa kwakukulu m’masiku athu ano, Mulungu ‘wagwedeza amitundu’ mwa ntchito yathu yachikristu yolalikira, ndipo “zofunika za amitundu onse” zabwera kudzapembedza Mulungu limodzi ndi otsalira a odzozedwa. Kunena zoona, odzozedwa ndi ankhosa zina tsopano akudzaza nyumba ya Yehova ndi ulemerero. Olambira oona amenewa akudikirira ndi chikhulupiriro nthawi yomwe Yehova ‘adzagwedeze miyamba ndiponso dziko lapansi’ m’lingaliro linanso. Adzachita zimenezi n’cholinga chogubuduza ndi kuwononga mphamvu za maufumu ndi amitundu.​—Hagai 2:22.

22. Kodi amitundu ‘akugwedezedwa’ motani, ndipo zotsatirapo zake ndi zotani, koma kodi n’chiyani chomwe chichitike posachedwapa?

22 Takumbutsidwa za mmene zinthu zagwedezekera m’mbali zosiyanasiyana zoimiridwa ndi “miyamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi mtunda.” Mwachitsanzo, Satana Mdyerekezi ndi ziwanda zake anawaponyera kudziko lapansi. (Chivumbulutso 12:7-12) Komanso, ntchito yolalikira yomwe akuitsogolera odzozedwa a Mulungu yagwedezadi zinthu za padziko lapansi m’dongosolo lino la zinthu. (Chivumbulutso 11:18) Ngakhale zili choncho, “khamu lalikulu” la zinthu zofunika za amitundu onse lagwirizana ndi Israyeli wauzimu potumikira Yehova. (Chivumbulutso 7:9, 10) A khamu lalikulu akugwira ntchito limodzi ndi Akristu odzozedwa polalikira uthenga wabwino wakuti posachedwapa Mulungu adzagwedeza amitundu pa Armagedo. Zimenezi zidzatsegula njira yoti kulambira koona kubwerere paungwiro padziko lonse.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi ndi liti ndipo zinthu zinali motani pamene Hagai ndi Zekariya anali kutumikira?

• Kodi inu mungagwiritse ntchito motani uthenga womwe Hagai ndi Zekariya anapereka?

• Kodi n’chifukwa chiyani mukuona kuti mawu a pa Zekariya 4:6 ndi olimbikitsa?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 20]

Zimene Hagai ndi Zekariya analemba zimatitsimikizira kuti Mulungu ali nafe

[Chithunzi patsamba 23]

“Kodi imeneyi ndiyo nthawi yakuti inu nokha mukhale m’nyumba zanu zotchingidwa m’katimo, ndi nyumba iyi ikhale yopasuka?”

[Chithunzi patsamba 24]

Anthu a Yehova akuthandiza pantchito yopeza anthu ‘ofunika a amitundu’