Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumalankhulana Bwino?

Kodi Mumalankhulana Bwino?

Kodi Mumalankhulana Bwino?

“KALATA Yachikondi ya Munthu wa Zaka 60.” Umenewo unali mutu wa mpikisano umene a banki ina ya ku Japan anachita zaka zingapo zapitazo. Mpikisanowu unalimbikitsa anthu achijapani a zaka za m’ma 50 ndi m’ma 60 kunena mmene “amamveradi mumtima mwawo” ponena za akazi kapena amuna awo. Munthu wina yemwe analowa nawo mpikisanowu analembera mkazi wake kuti: “Ungaseke, koma sindingamve bwino ndikapanda kunena, ndiye ndikuuze zakukhosi kwanga: Sindikudziwa kuti ndikanatani popanda iwe.”

M’madera ambiri, kuphatikizapo mayiko a kum’mawa, chikhalidwe sichilimbikitsa anthu kulankhula zakukhosi momasuka. Ngakhale zili, anthu oposa 15,000 anapanga nawo mpikisano umenewu wa kalata yachikondi. Mpikisanowu unatchuka kwambiri moti anadzachitanso wina pambuyo pa umenewu ndipo panasindikizidwa mabuku a nkhani za m’makalata amenewo. Zimenezi zikusonyeza kuti anthu ambiri, amafuna atauza wokondedwa wawo mmene amam’kondera. Komabe, ena amakana kuchita zimenezo. Chifukwa chiyani? Zingakhale choncho chifukwa chakuti pamafunika khama ndi luso kuti auze munthu wina, kaya mkazi kapena mwamuna wawo, zakukhosi kwawo.

Hitoshi Kato, amene analemba buku lonena za kupuma pantchito anati, pakati pa mabanja achikulire ku Japan, nthawi zambiri akazi ndi amene amakadula chisamani chothetsa banja chifukwa chakuti amakhala atada kukhosi ndi amuna awo kwa zaka zambiri. Iye anati: “Koma zimenezi zimachitikanso chifukwa choti mwamuna ndi mkaziyo sanali kukambirana akakumana ndi zovuta.”

Mwamuna angadabwe mkazi wake akumupatsa kalata ya chisudzulo pamene wapuma pantchito. Kwa zaka zambiri iwo angakhale kuti sankauzana zakukhosi kwawo pofuna kuti mnzawo adziwe mmene akum’kondera. N’kutheka kuti angakhale atayesapo kuuzana zakukhosi koma ankalephera kukambirana bwinobwino. M’malo molimbitsa ubwenzi wawo, anapezeka kuti akukangana mobwerezabwereza.

Kodi mwamuna ndi mkazi wake angachite chiyani kuti athetse kusiyana maganizo kwawo mwamtendere ndi kulankhulana bwinobwino zakukhosi kwawo? Mungachite chidwi kudziwa kuti mfundo zothandiza kwambiri sizipezeka m’buku la posachedwapa lolembedwa ndi mlangizi wa za banja ayi, koma m’buku lina lakale lomwe ambiri alikonda kwa zaka zambiri. Buku lakelo ndi Baibulo.