Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthana ndi Zopinga ku Panama

Kuthana ndi Zopinga ku Panama

Kuthana ndi Zopinga ku Panama

“PANAMA ali ngati mlatho wa dziko lonse.” Zaka 50 zapitazo, mawu amenewa anamveka m’pulogalamu ina yotchuka ya pawailesi m’dziko la ku Central America la Panama. Masiku ano, mawuwa amasonyeza maganizo amene anthu ambiri ali nawo okhudza dziko limeneli.

Dziko la Panama lili ngati mlatho wolumikiza North ndi South America. Komanso, pa ngalande yotchuka ya Panama Canal pali mlatho wa Bridge of the Americas. Ngalande imeneyi, yomwe panagona luso la uinjiniya, inadula dziko la Panama pawiri, n’kulumikiza nyanja zamchere, zomwe ndi Atlantic ndi Pacific. Izi zimathandiza kuti sitima za panyanja zikuluzikulu za padziko lonse zizidutsapo maola owerengeka chabe m’malo mozungulira nyanja yaikulu, n’kutha masiku kapena milungu kumene. Zoonadi, dziko la Panama lili ngati mlatho wofunika kwambiri kwa mayiko ambiri a dziko lapansi.

Dzikoli Lili ndi Anthu Osiyanasiyana

Dziko la Panama lilinso ndi anthu ochokera ku mayiko ndi mitundu yosiyanasiyana. Anthu amenewa, limodzi ndi mitundu yambirimbiri ya eni nthaka, achititsa kuti ku Panama kukhale anthu a magulu osiyanasiyana omwe angomwazikana m’dziko lonse lokongolali. Komano, kodi n’zotheka kugwirizanitsa zikhalidwe, zipembedzo, ndiponso zinenero zosiyanasiyana, kuti anthuwo akhale ndi maganizo ndi cholinga chimodzi mogwirizana ndi choonadi chamtengo wapatali chopezeka m’Mawu a Mulungu?

Inde, n’zotheka. Mawu a mtumwi Paulo omwe ali pa Aefeso 2:17, 18 akusonyeza kuti Akristu oyambirira, Ayuda ndi Akunja, anachitadi zimenezi chifukwa cha mphamvu yogwirizanitsa anthu ya nsembe ya Kristu. Paulo analemba kuti: “Mmene [Yesu] anadza, analalikira Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu akutali, ndi mtendere kwa iwo apafupi; kuti mwa Iye ife tonse awiri tili nawo malowedwe athu kwa Atate, mwa Mzimu mmodzi.”

Masiku ano, mofanana ndi zimenezi, Mboni za Yehova zikulengeza “Uthenga Wabwino wa mtendere” ku Panama, kwa anthu ndi magulu ochokera m’zipembedzo zosiyanasiyana, ndiponso nthawi zina ochokera kumadera akutali. Anthu omwe ‘alowera’ kwa Yehova amakhala ogwirizana, zomwe ndi zosangalatsa kwambiri. Izi zachititsa kuti ku Panama kupangidwe mipingo ya zinenero zisanu ndi chimodzi, zomwe ndi Chisipanya, Chikantonizi, Chinenero Chamanja cha ku Panama, Chingelezi, ndi zinenero zina ziwiri za eni nthaka, zomwe ndi Chikuna ndiponso Chingobe (Chigwami). N’zolimbikitsa kuona mmene anthu a zinenero zimenezi akhalira ogwirizana popembedza Yehova.

Kuthana ndi Zopinga ku Comarca

Mtundu wa a Ngobe ndiwo mtundu waukulu mwa mitundu isanu ndi itatu ya eni nthaka ku Panama. Mtunduwu uli ndi anthu pafupifupi 170,000, ndipo ambiri mwa iwo amakhala m’dera lina lalikulu lomwe posachedwapa anakonza zoti likhale comarca, kapena kuti malo otetezedwa. Mbali yaikulu ya derali ndi yamapirimapiri amene ali ndi nkhalango zowirira ndipo kawirikawiri anthu amafikako mwa kuyenda pansi, komanso kuli madera ena a m’mphepete mwa nyanja omwe munthu angafikeko podzera kunyanja yaikulu. Anthu amakonda kumanga midzi yawo kufupi ndi mitsinje, yomwe imawathandiza pankhani ya kayendedwe, komanso midzi ina ili m’mphepete mwa nyanja. Anthu ambiri ku comarca si olemera chifukwa amangodalira ulimi wa khofi kumapiri, kusodza, kapena ulimi wa mbewu zina. Anthu kumeneku ali m’Matchalitchi Achikristu. Komabe, pali ena a chipembedzo china cha m’derali chotchedwa Mama Tata. Ena amakaonana ndi a sukia (asing’anga) akadwala kapena akamavutitsidwa ndi mizimu yoipa. Ngakhale kuti anthu ambiri amalankhula Chisipanya, koma Chingobe ndi chimene amachimva bwino.

Kupalasa Mabwato Kuti Akafike Kumene Kuli Anthu

Mboni za Yehova zimadziwa kuti m’pofunika kuwathandiza anthu kuphunzira choonadi, osati mongowafika m’maganizo mokha, komanso pamtima. Izi zingalimbikitse anthuwo kusintha moyo wawo n’cholinga chokhala mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Motero, apainiya apadera omwe anatumizidwa ku magawo asanu ndi atatu a derali aphunzira Chingobe mothandizidwa ndi Mboni za chinenerochi, zopezeka m’derali.

Mipingo 14 yomwe yapangidwa m’derali ikuoneka kuti ingathe kukula kwambiri. Mwachitsanzo, zaka zingapo zapitazo, Dimas ndi mkazi wake Gisela, omwe ndi apainiya apadera, anatumizidwa ku mpingo wina waung’ono wa ofalitsa pafupifupi 40, m’dera la m’mphepete mwa nyanja la Tobobe. Sikuti zinali zophweka kuti azolowere maulendo apafupipafupi a pabwato okalalikira kwa anthu odzichepetsa okhala m’gombe la nyanja ya Atlantic. Dimas ndi Gisela anaona kuti madzi abata a m’nyanja yamchere amatha kusintha mwadzidzidzi n’kuyamba kuwinduka kwambiri. Nthawi zambiri ankamva kuphwanya manja ndi msana chifukwa chopalasa bwato kuchoka pamudzi wina kupita pa wina. Vuto lina linali kuphunzira chinenero cha anthu a m’deralo. Komabe, chifukwa cha kudzipereka ndiponso khama lawo, mu 2001 anthu 552 anasonkhana pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu.

M’gombe la kufupi ndi Tobobe kuli mudzi wa Punta Escondida. Kwa kanthawi ndithu, kunja kukacha bwino, kagulu ka ofalitsa kanali kuyenda pabwato kuchoka ku mudzi umenewu kubwera ku Tobobe, pofuna kudzachita misonkhano, ndipo zinkaoneka kuti n’zotheka kukhazikitsa mpingo watsopano m’dera limenelo. Poganizira zimenezi, Dimas ndi Gisela anapemphedwa kuti asamukire ku Punta Escondida. Pasanathe n’komwe zaka ziwiri, kagulu ka ku Punta Escondida kanakhala mpingo wa ofalitsa 28, ndipo avereji ya osonkhana pa nkhani ya onse mlungu ndi mlungu inali 114. Mu 2004, mpingo watsopanowo unasangalala pamene anthu okwana 458 anafika pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu.

Kuthana ndi Vuto la Kusatha Kulemba ndi Kuwerenga

Kwa anthu ambiri a mitima yabwino, kudziwa kulemba ndi kuwerenga kwawathandiza kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova. Umu ndi mmene zinalili ndi Fermina, mayi wachitsikana wochokera ku dera la mapiri ku comarca. Amishonale Amboni omwe anali kugwira ntchito m’dera lakutali lomwe iye ankakhala, anaona kuti Fermina anali kumvetsera bwino kwambiri uthenga wa Ufumu. Atapemphedwa kuti aziphunzira naye Baibulo, iye anayankha kuti akufuna kuphunzira zambiri. Komabe, panali vuto. Ankalankhula Chisipanya ndi Chingobe, koma sankatha kuwerenga kapena kulemba zinenero zonse ziwirizi. Mmodzi wa amishonalewo anadzipereka kuti am’phunzitse, pogwiritsa ntchito kabuku ka Dziperekeni pa Kuwerenga ndi Kulemba. *

Fermina anali wophunzira wabwino kwambiri, ankakonzera bwino zoti aphunzire, ankachita ntchito yonse yomwe anapatsidwa kukachitira kunyumba, ndiponso ankayeserera masipelo bwinobwino. M’chaka chimodzi chokha, anadziwa zambiri moti anayamba kuphunzira naye kabuku ka Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu! * Atakonza za misonkhano, Fermina anayamba kupezekapo. Koma, chifukwa cha umphawi m’banja mwake, zinkamuvuta kwambiri kupeza ndalama zoyendera kuti apite ku misonkhano ndi ana ake. Mpainiya wina, yemwe anadziwa za vuto la Fermina, anamuuza kuti aganize zoti azisoka ndi kumagulitsa zovala zamakolo za amayi a Chingobe. Fermina anatero, ndipo ngakhale kuti anali ndi zosowa zina pamoyo wake, iye ankaonetsetsa kuti akugwiritsa ntchito ndalama zomwe wapeza kuyendera kupita ku misonkhano yachikristu. Iye ndi banja lake anasamukira kudera lina tsopano, ndipo akupitiriza kupita patsogolo mwauzimu. Iwo akusangalala chifukwa choti anaphunzira kulemba ndi kuwerenga komanso chifukwa choti adziwa Yehova, zomwe ndi zofunika kwambiri.

Kuthana ndi Vuto Lolepheretsa Kulalikira Ogontha

Ku Panama, mabanja ambiri omwe ali ndi wachibale wawo wogontha amachita naye manyazi. Nthawi zina, anthu ogonthawo amamanidwa mwayi wophunzira. Anthu ambiri ogontha amaona kuti anthu akuwasala, chifukwa choti n’zovuta kulankhula nawo.

Motero, zinali zoonekeratu kuti panafunika kuchitapo kanthu kuti anthu a vutoli amve uthenga wabwino. Chifukwa cholimbikitsidwa ndi woyang’anira woyendayenda, kagulu ka apainiya ndiponso anthu ena akhama anaganiza zoyamba kuphunzira Chinenero Chamanja cha ku Panama. Khama lawoli linapindula.

Pofika chakumapeto kwa chaka cha 2001, mu mzinda wa Panama City munakhazikitsidwa gulu la chinenero chamanja. Anthu ofika pamisonkhano ankakwana pafupifupi 20. Abale ndi alongowo atazolowera chinenerochi, iwo ankatha kulalikira kwa anthu ambiri omwe kanali koyamba “kumva” choonadi cha m’Baibulo m’chinenero chawo. Nazonso Mboni zambiri zomwe zili ndi ana amene ali ndi vuto la kumva zinayamba kufika pa misonkhano ndipo zinaona kuti ana awo anali kumva mosavuta ziphunzitso za m’Baibulo ndiponso anayamba kukonda kwambiri choonadi. Nthawi zambiri makolo anali kuphunzira kulankhula ndi ana awo ogontha, motero anali kulankhula bwino ndi ana awowo. Makolo anatha kuthandiza ana awo mwauzimu ndipo mabanja anali kukhala olimba. Izi zikuoneka bwino pa zimene zinachitikira Elsa ndi mwana wake wamkazi, dzina lake Iraida.

Mboni ina ya m’gulu la chinenero chamanja inamva za Iraida, n’kupita kukamuona, ndi kum’gawira kabuku kakuti Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! * Iraida anasangalala kwambiri ndi zimene ankaphunzira m’zithunzi zokhudza dziko latsopano. Anayamba kuphunzira naye Baibulo pogwiritsa ntchito kabukuka. Atamaliza kuphunzira naye kabukuka, anayamba kuphunzira kabuku ka Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? * Apa, Iraida anayamba kupempha amayi ake kuti am’thandize kukonzekera ndi kum’fotokozera zomwe zili m’kabukuko.

Elsa anali ndi mavuto awiri: Popeza sanali Mboni, sankadziwa choonadi cha m’Baibulo, ndiponso sankadziwa chinenero chamanja. Iye anali atauzidwa kuti sayenera kulankhula ndi manja ndi mwana wakeyo koma kuti mwanayo ndiye anafunika kuphunzira kulankhula motulutsa mawu. Motero, sankalankhulana kwambiri monga mayi ndi mwana wake. Chifukwa cha pempho la Iraida loti am’thandize, Elsa anapempha kuti Mboni ya mu mpingo iziphunzira naye. Iye anati: “Ndinapempha izi chabe chifukwa cha mwana wanga, chifukwa chakuti ndinali ndisanaonepo Iraida ali ndi chidwi kwambiri ndi zinthu.” Elsa anayamba kuphunzira ngati mmene mwana wake anali kuchitira ndiponso anaphunzira chinenero chamanja. Pamene Elsa anayamba kucheza kwambiri ndi mwana wakeyo, mavuto olankhulana kunyumba kwawo anachepa. Iraida anayamba kusankha anzake osewera nawo, ndipo anali kugwirizana ndi mpingo. Panopa, mayi ndi mwana wakeyu amafika pa misonkhano yachikristu nthawi zonse. Elsa wabatizidwa posachedwapa, ndipo nayenso Iraida watsala pang’ono kubatizidwa. Elsa anati, kwanthawi yoyamba, akudziwa mwana wake ndiponso kuti tsopano angathe kukambirana za zinthu zofunika kwambiri, zomwe onse awiri amazikonda kwambiri.

Gulu la chinenero chamanja, lomwe linakhala mpingo mu April 2003, lakula tsopano kufika pa ofalitsa Ufumu okwana pafupifupi 50, ndipo anthu oposa chiwerengero chimenechi amafika pamisonkhano. Pamisonkhanopo pamakhala anthu ambiri ogontha. Magulu ena a chinenero chamanja akukhazikitsidwa m’mizinda itatu ya kunja kwa mzinda wa Panama City. Ngakhale kuti padakali zambiri zoti zichitike m’munda umenewu, n’zosakayikira kuti pachitika zambiri pofuna kugwirizanitsa ogontha omwe ali ndi mtima wabwino ndi Mlengi wawo wachikondi, Yehova Mulungu.

Izi ndi chitsanzo chabe cha zimene zikuchitika m’dziko lonse la Panama. Ngakhale kuti akuchokera m’zikhalidwe, zinenero ndi m’madera osiyanasiyana, anthu ambiri agwirizana pa kupembedza Mulungu mmodzi yekha woona. Choonadi cha m’Mawu a Yehova chafika bwinobwino kwa anthu ngakhale kuti m’dzikoli, lomwe anthu ambiri amati “lili ngati mlatho wa dziko lonse,” muli zopinga zosiyanasiyana.​—Aefeso 4:4.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 16 Kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 21 Kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 21 Kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mapu patsamba 8]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

NYANJA YA CARIBBEAN

PANAMA

Tobobe

NYANJA YA PACIFIC

Panama Canal

[Chithunzi patsamba 8]

Azimayi achikuna atagwira nsalu zopeta

[Chithunzi patsamba 9]

Mmishonale akulalikira mayi wachingobe

[Chithunzi patsamba 10]

Mboni zachingobe zikukwera bwato kukakhala nawo pa tsiku la msonkhano wapadera

[Zithunzi patsamba 11]

Anthu ku Panama amva choonadi cha m’Baibulo ngakhale kuti ndi osiyana zikhalidwe ndi zinenero

[Chithunzi patsamba 12]

Phunziro la “Nsanja ya Olonda” m’chinenero chamanja

[Chithunzi patsamba 12]

Elsa ndi mwana wake, Iraida, akusangalala kulankhulana zinthu zopindulitsa

[Mawu a Chithunzi patsamba 8]

Ship and Kuna women: © William Floyd Holdman/​Index Stock Imagery; village: © Timothy O’Keefe/​Index Stock Imagery