Ufulu Wokhala ndi Dzina
Ufulu Wokhala ndi Dzina
MUNTHU aliyense ali ndi ufulu wokhala ndi dzina. Ku Tahiti, ngakhale khanda longobadwa kumene lomwe lathawidwa, loti bambo ndi mayi ake sakudziwika, amalipatsa dzina. Ofesi yosunga kaundula imapereka dzina la mwanayo ndi la bambo ake.
Komabe, pali munthu wina amene tinganene kuti akumanidwa ufulu umenewu, womwe pafupifupi munthu wina aliyense ali nawo. N’zodabwitsa kuti munthu ameneyu ndi “Atate, amene kuchokera kwa Iye fuko lonse la m’mwamba ndi la padziko alitcha dzina.” (Aefeso 3:14, 15) Anthu ambiri amakana kugwiritsa ntchito dzina la Mlengi monga momwe lilili m’Baibulo. M’malo mwake, amakonda kugwiritsa ntchito mayina aulemu monga “Mulungu,” “Ambuye,” “Atate Wosatha.” Ndiyeno, kodi dzina lake ndi ndani? Wamasalmo akuyankha funso limeneli. Akuti: “Inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.”—Salmo 83:18.
Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1800 pamene amishonale a London Missionary Society anafika ku Tahiti, anthu a m’zilumba za Polynesia ankapembedza milungu yosiyanasiyana. Mulungu aliyense anali ndi dzina lake, ndipo milungu ikuluikulu inali Oro ndi Taaroa. Pofuna kusiyanitsa Mulungu wotchulidwa m’Baibulo ndi milungu ina, amishonalewo sanazengereze, anayamba kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu, lolembedwa kuti Iehova, m’Chitahiti.
Dzina limeneli linafala kwambiri ndipo anthu ankalitchula kwambiri akamacheza ndiponso m’makalata omwe ankalemberana. Mfumu Pomare Yachiwiri ya ku Tahiti, yomwe inalamulira chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1800, inkagwiritsa ntchito kwambiri dzinali m’makalata ake. Umboni wa zimenezi ndi kalata yomwe taisindikiza panoyi, yomwe inalembedwa m’Chingelezi ndipo ili m’nyumba yosungiramo zinthu zochititsa chidwi ya Museum of Tahiti and Its Islands. Kalatayi ikutsimikizira kuti panthawi imeneyo anthu sankadana ndi kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu. Komanso, dzina la Mulungu likutchulidwa maulendo ambirimbiri m’Baibulo loyambirira la Chitahiti, lomwe linamalizidwa kulembedwa mu 1835.
[Chithunzi patsamba 32]
Mfumu Pomare Yachiwiri
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
King and letter: Collection du Musée de Tahiti et de ses Îles, Punaauia, Tahiti