Abusa Omwe Ndi ‘Zitsanzo kwa Gulu’ la Nkhosa
Abusa Omwe Ndi ‘Zitsanzo kwa Gulu’ la Nkhosa
‘Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu . . . mwaufulu . . . , mwachangu . . . , okhala zitsanzo kwa gululo.’—1 PETRO 5:2, 3.
1, 2. (a) Kodi Yesu anapatsa mtumwi Petro udindo wotani, ndipo n’chifukwa chiyani Yesu sanalakwitse kukhulupirira Petro? (b) Kodi Yehova amawaona bwanji abusa amene wasankha?
NTHAWI ya Pentekoste wa mu 33 C.E. itatsala pang’ono kukwana, Petro ndi ophunzira ena asanu ndi mmodzi anali kudya chakudya m’mawa, chimene Yesu anawakonzera m’mphepete mwa nyanja ya Galileya. Imeneyi sinali nthawi yoyamba kuti Petro aone Yesu woukitsidwayo, ndipo mosakayikira ankasangalala kwambiri kudziwa kuti Yesu ali moyo. Koma Petro ayeneranso kuti anali ndi mantha. Chifukwa choti, masiku ochepa zimenezi zisanachitike, anali atakana pamaso pa anthu kuti sankam’dziwa Yesu. (Luka 22:55-60; 24:34; Yohane 18:25-27; 21:1-14) Kodi Yesu anadzudzula Petro, yemwe anali atalapa, chifukwa choti analibe chikhulupiriro? Ayi. M’malo mwake anapatsa Petro udindo wodyetsa ndi kuweta “ana a nkhosa” a Yesu. (Yohane 21:15-17) Monga momwe nkhani ya m’Baibulo yofotokoza mbiri ya mpingo wachikristu wa m’nthawi ya atumwi ikusonyezera, Yesu sanalakwitse kukhulupirira Petro. Petro limodzi ndi atumwi ena ndiponso amuna akulu ku Yerusalemu, anaweta mpingo wachikristu panthawi imene unkayesedwa kwambiri ndiponso nthawi imene unkawonjezeka mofulumira.—Machitidwe 1:15-26; 2:14; 15:6-9.
2 Masiku ano, Yehova kudzera mwa Yesu Kristu, wasankha amuna oyenerera kuti atumikire monga abusa auzimu kutsogolera nkhosa Zake panthawi yovuta kwambiri m’mbiri ya anthu. (Aefeso 4:11, 12; 2 Timoteo 3:1) Kodi pali chifukwa chomveka choti Yehova akhulupirire amuna amenewa? Umboni woti chifukwa chilipo ndi ubale wamtendere wa Akristu padziko lonse. N’zoona kuti abusa amenewa amatha kulakwa monga momwe Petro analili. (Agalatiya 2:11-14; Yakobo 3:2) Ngakhale ndi choncho, Yehova sawakayikira kuti angathe kusamalira nkhosa zimene Iye ‘anagula ndi mwazi’ wa Mwana wake. (Machitidwe 20:28) Yehova amawakonda kwambiri amuna amenewa ndipo amawaona kuti ndi “oyenera ulemu wowirikiza.”—1 Timoteo 5:17.
3. Kodi abusa auzimu angakhale bwanji ndi mtima wochita zinthu mwachangu ndiponso mofunitsitsa?
3 Kodi abusa auzimu amakhala bwanji ndi mtima wochita zinthu mwachangu ndiponso mofunitsitsa, mwakutero n’kukhala zitsanzo kwa gulu la nkhosa? Mofanana ndi Petro ndiponso abusa ena a m’nthawi ya atumwi, abusawa amadalira mzimu woyera wa Mulungu, umene umawapatsa mphamvu zimene amafunikira kuti achite ntchito zawo. (2 Akorinto 4:7) Mzimu woyera umabalanso zipatso za mzimu mwa iwo, zimene ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, ndi chiletso. (Agalatiya 5:22, 23) Tiyeni tikambirane njira zina zimene abusa angakhalire chitsanzo chabwino posonyeza zipatso zimenezi pamene akuweta nkhosa za Mulungu zimene afunika kuzisamalira.
Kondani Gulu la Nkhosa Ndiponso Nkhosa Iliyonse Payokha
4, 5. (a) Kodi Yehova ndi Yesu amasonyeza motani kuti amakonda gulu la nkhosa? (b) Kodi zina mwa njira zimene abusa auzimu amasonyezera kuti amakonda nkhosa ndi zotani?
4 Khalidwe lalikulu kwambiri la mzimu wa Yesaya 65:13, 14; Mateyu 24:45-47) Koma salekera pamenepa. Iye amaganiziranso nkhosa iliyonse payokha. (1 Petro 5:6, 7) Yesu nayenso amakonda nkhosa. Iye anataya moyo wake chifukwa cha nkhosazi, ndipo nkhosa iliyonse amaidziwa ‘dzina.’—Yohane 10:3, 14-16.
Mulungu ndi chikondi. Yehova amasonyeza kuti amakonda gulu lonse la nkhosa polipatsa chakudya chauzimu chochuluka. (5 Abusa auzimu amatsanzira Yehova ndi Yesu. Iwo amasonyeza kuti amakonda gulu lonse la nkhosa za Mulungu mwa kukhala odzipereka pophunzitsa mpingo. Nkhani zawo zochokera m’Baibulo zimathandiza kudyetsa ndi kuteteza nkhosa, ndipo khama lawo pochita zimenezi limaonekera kwa onse. (1 Timoteo 4:13, 16) Zimene sizimaonekera kwenikweni ndi nthawi imene amagwiritsa ntchito polongosola zinthu m’mafaelo a mpingo, polemba makalata, popanga ndandanda, ndiponso posamalira zinthu zina zambiri. Amachita zimenezi kuti misonkhano ya mpingo ndi ntchito zina zichitike “koyenera ndi kolongosoka.” (1 Akorinto 14:40) Mbali yaikulu ya ntchito zimenezi ikamachitika sionekera kwa anthu ambiri mu mpingo. Ndipo ntchito imeneyi amaichita chifukwa cha chikondi.—Agalatiya 5:13.
6, 7. (a) Kodi ndi njira imodzi iti imene abusa amadziwira bwino nkhosa? (b) N’chifukwa chiyani nthawi zina n’zothandiza kuuzako mkulu mmene tikumvera?
6 Abusa achikristu achikondi amayesetsa kusonyeza chidwi nkhosa iliyonse mu mpingo. (Afilipi 2:4) Njira imodzi imene abusa amadziwira bwino nkhosa iliyonse payokha ndi mwa kulalikira limodzi ndi nkhosayo. Nthawi zambiri Yesu ankayenda ndi otsatira ake pochita ntchito yolalikira ndipo ankagwiritsa ntchito nthawi imeneyo kuwalimbikitsa. (Luka 8:1) Mbusa wina wachikristu wokhwima mwauzimu anati: “Imodzi mwa njira zabwino kwambiri zodziwira ndiponso zolimbikitsira mbale kapena mlongo ndiyo kugwira naye limodzi ntchito ya utumiki wa kumunda.” Ngati posachedwapa simunakhale ndi mwayi wogwira ntchito limodzi ndi mmodzi wa akulu mu utumiki wa kumunda, bwanji osakonza mwamsanga nthawi kuti muchite zimenezi?
7 Chifukwa cha chikondi, Yesu ankatha kusangalala ndiponso kumva chisoni limodzi ndi otsatira ake. Mwachitsanzo, pamene ophunzira ake 70 anabwera mokondwera kuchokera kolalikira, Yesu “anakondwera.” (Luka 10:17-21) Koma pamene anaona mmene imfa ya Lazaro inakhudzira Mariya ndi achibale ake ndiponso mabwenzi ake, “Yesu analira.” (Yohane 11:33-35) Mofananamo, abusa achikondi masiku ano amakhudzidwa mtima ndi zimene zikuchitikira nkhosa. Chikondi chimawalimbikitsa ‘kukondwera nawo akukondwera’ ndiponso ‘kulira nawo akulira.’ (Aroma 12:15) Khalani omasuka kufotokozera abusa achikristu mmene mukumvera mukasangalala kapena kukhumudwa. Kumva kuti mukusangalala kudzawalimbikitsa. (Aroma 1:11, 12) Kudziwa ziyeso zanu kungawathandize kuti akulimbikitseni ndi kukutonthozani.—1 Atesalonika 1:6; 3:1-3.
8, 9. (a) Kodi mkulu wina ankasonyeza bwanji kuti amakonda mkazi wake? (b) Kodi kukonda banja lake n’kofunika motani kwa mbusa?
8 Chikondi chimene mbusa ali nacho pa gulu la nkhosa chimaonekera m’njira imene amasamalira banja lake. (1 Timoteo 3:1, 4) Ngati ndi wokwatira, chikondi ndi ulemu umene amasonyeza mkazi wake umakhala chitsanzo choti amuna ena atengere. (Aefeso 5:25; 1 Petro 3:7) Taonani mawu a mkazi wina wachikristu, dzina lake Linda. Mwamuna wake asanamwalire anatumikira monga woyang’anira kwa zaka zoposa 20. Mkaziyu anati: “Mwamuna wanga nthawi zonse ankakhala wotanganidwa kwambiri kusamalira mpingo. Koma ankachita zinthu m’njira yoti inenso ndinkadzimva kuti ndinali kum’chirikiza. Nthawi zambiri ankayamikira thandizo langa, ndipo akamasuka tinkasangalalira limodzi. Chifukwa cha zimenezi, ndinkaona kuti ankandikonda kwambiri ndipo sindinkachita nsanje kuti amatha nthawi yambiri akutumikira mpingo.”
9 Ngati mbusa wachikristu ali ndi ana, angathe kupereka chitsanzo kwa makolo ena polangiza ana ake mwachikondi ndiponso kuwayamikira nthawi zonse. (Aefeso 6:4) Ndipotu, chikondi chimene amasonyeza banja lake chimakhala umboni nthawi zonse woti amachitadi zinthu mogwirizana ndi udindo wake umene anapatsidwa ndi mzimu woyera.—1 Timoteo 3:4, 5.
Limbikitsani Chimwemwe ndi Mtendere mwa Kulankhulana
10. (a) Kodi n’chiyani chimene chingasokoneze chimwemwe ndi mtendere mu mpingo? (b) Kodi ndi nkhani iti imene ikanasokoneza mtendere mu mpingo wa m’nthawi ya atumwi, ndipo nkhani imeneyi inathetsedwa bwanji?
10 Mzimu woyera ungathandize Mkristu aliyense payekha kukhala ndi chimwemwe ndiponso mtendere mu mtima. Ungateronso pa bungwe la akulu ndiponso pa mpingo wonse. Koma kulephera kulankhulana momasuka kungasokoneze chimwemwe ndi mtendere umenewu. Solomo anati: “Zolingalira zizimidwa popanda upo.” (Miyambo 15:22) Komabe, kulankhulana momasuka ndiponso mwaulemu kumalimbikitsa chimwemwe ndi mtendere. Mwachitsanzo, pamene nkhani ya mdulidwe inatsala pang’ono kusokoneza mtendere wa mpingo wa m’nthawi ya atumwi, bungwe lolamulira ku Yerusalemu linapempha mzimu woyera kuti ulitsogolere. Akulu amenewa anafotokozanso maganizo awo pa nkhaniyi, omwe anali osiyanasiyana. Atakambirana kwambiri, anagwirizana chochita. Atauza mipingo zimene onse anasankha, abale “anakondwera chifukwa cha chisangalatso chake.” (Machitidwe 15:6-23, 25, 31; 16:4, 5) Analimbikitsa chimwemwe ndi mtendere.
11. Kodi akulu angalimbikitse bwanji chimwemwe ndi mtendere mu mpingo?
11 N’chimodzimodzi masiku ano, abusa amalimbikitsa chimwemwe ndi mtendere mu mpingo mwa kulankhulana bwino. Mavuto akatsala pang’ono kusokoneza mtendere wa mpingo, abusa amakumana ndipo amakambirana momasuka maganizo awo. Amamvetsera mwaulemu zimene abusa anzawo akunena. (Miyambo 13:10; 18:13) Akapempherera mzimu woyera, amasankha zinthu mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo ndiponso mogwirizana ndi malangizo ofalitsidwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47; 1 Akorinto 4:6) Bungwe la akulu likagamula zinthu mogwiritsa ntchito Malemba, mkulu aliyense amagonjera zimene mzimu woyera watsogolera mwa kuchirikiza chigamulocho ngakhale ngati maganizo ake sanavomerezedwe ndi ambiri pa bungwelo. Kudzichepetsa koteroko kumalimbikitsa chimwemwe ndi mtendere ndipo kumakhala chitsanzo chabwino kwambiri kwa nkhosa cha mmene tingayendere ndi Mulungu. (Mika 6:8) Kodi mumavomereza modzichepetsa chigamulo chozikidwa pa Baibulo chimene abusa amapanga mu mpingo?
Khalani Woleza Mtima ndi Wachifundo
12. N’chifukwa chiyani Yesu anafunika kukhala woleza mtima ndiponso wachifundo pochita zinthu ndi atumwi?
12 Yesu anali woleza mtima ndiponso wachifundo pochita zinthu ndi atumwi, ngakhale kuti iwo ankalakwa mobwerezabwereza. Mwachitsanzo, Yesu anayesa mobwerezabwereza kuwagogomezera kufunika kokhala odzichepetsa. (Mateyu 18:1-4; 20:25-27) Koma patsiku lomaliza la moyo wa Yesu padziko lapansi, iye atangowapatsa phunziro la kudzichepetsa mwa kusambitsa mapazi awo, ‘panakhala kutsutsana mwa iwo, ndani wa iwo ayesedwe wamkulu.’ (Luka 22:24; Yohane 13:1-5) Kodi Yesu anadzudzula atumwi akewo? Ayi, anakambirana nawo mwachifundo, ndi kuwauza kuti: “Wamkulu ndani, iye wakuseama pachakudya kapena wakutumikirapo? Si ndiye wakuseama pachakudya kodi? Koma ine ndili pakati pa inu monga ngati wotumikira.” (Luka 22:27) M’kupita kwa nthawi, kuleza mtima ndiponso chifundo cha Yesu limodzi ndi chitsanzo chake chabwino, zinakhudza mitima ya atumwiwo.
13, 14. Kodi ndi nthawi iti kwenikweni pamene abusa amafunikira kukhala achifundo?
13 Mofananamo, mbusa wauzimu angafunike kupereka uphungu mobwerezabwereza kwa munthu amene ali ndi chofooka chinachake. Mbusayo angakwiyire munthuyo. Koma mbusa akamakumbukira kuti nayenso amalakwa zingam’thandize kukhala woleza mtima ndi wachifundo kwa mbale wake wochita zosalongosokayo. Mwa kuchita zimenezi amatsanzira Yesu ndi Yehova, amene amasonyeza makhalidwe amenewa kwa Akristu onse, kuphatikizapo abusa.—1 Atesalonika 5:14; Yakobo 2:13.
14 Nthawi zina abusa angafunikire kupereka uphungu wamphamvu kwa munthu amene wachita tchimo lalikulu. Ngati munthuyo ndi wosalapa, abusa amafunika kuchotsa wolakwayo mu mpingo. (1 Akorinto 5:11-13) Ngakhale n’choncho, zimene abusa amachita ndi munthuyo zimasonyeza kuti akudana ndi tchimolo osati iyeyo. (Yuda 23) Abusa amene amachita zinthu mwachifundo angathandize kuti m’kupita kwa nthawi nkhosa yotayikayo ibwerere mu mpingo mosavuta.—Luka 15:11-24.
Chikhulupiriro Chimalimbikitsa Ntchito Zabwino
15. Kodi imodzi mwa njira zimene abusa amatsanzira ubwino wa Yehova ndi iti, ndipo n’chiyani chimene chimawalimbikitsa kuchita zimenezi?
15 “Yehova achitira chokoma onse,” ngakhale anthu amene sayamikira zimene amawachitira. (Salmo 145:9; Mateyu 5:45) Ubwino wa Yehova umaoneka makamaka chifukwa choti amatumiza anthu ake kulalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’ (Mateyu 24:14) Abusa amasonyeza ubwino wa Mulungu mwa kutsogolera pa ntchito yolalikira imeneyi. Kodi n’chiyani chimawalimbikitsa kuyesetsa mosatopa? Chikhulupiriro cholimba mwa Yehova ndi malonjezo ake.—Aroma 10:10, 13, 14.
16. Kodi abusa angachite bwanji “chokoma” kwa nkhosa?
16 Kuphatikiza pa kuchitira “onse chokoma” mwa kulalikira, abusa ali ndi udindo wochita chokoma “makamaka [kwa] iwo a pa banja la chikhulupiriro.” (Agalatiya 6:10) Njira imodzi imene amachitira zimenezi ndi mwa kupanga maulendo aubusa olimbikitsa. Mkulu wina anati: “Ndimasangalala ndi maulendo aubusa. Maulendowa amandipatsa mwayi woti ndiyamikire abale ndi alongo chifukwa cha kuyesayesa kwawo ndiponso kuwathandiza kudziwa kuti timayamikira khama lawo.” Nthawi zina, abusa angauze munthu mmene angachitire bwino kwambiri utumiki wake kwa Yehova. Pochita zimenezi, abusa anzeru amatsanzira mtumwi Paulo. Taonani mmene anauzira abale ku Tesalonika. Iye anati: “Tikhulupirira mwa Ambuye za inu, kuti mumachita, ndiponso mudzachita zimene tikulamulirani.” (2 Atesalonika 3:4) Mawu osonyeza kukhulupirira nkhosa ngati amenewa amathandiza nkhosazo kukhala ndi maganizo abwino ndiponso kutha ‘kumvera atsogoleri’ mosavuta. (Ahebri 13:17) Abusa akakulimbikitsani pa ulendo waubusa, bwanji osawayamikira chifukwa chokuyenderani?
Kufatsa Kumafuna Kudziletsa
17. Kodi Petro anaphunzira chiyani kwa Yesu?
17 Yesu anali wofatsa ngakhale pamene ena am’kwiyitsa. (Mateyu 11:29) Pamene anaperekedwa ndi kumangidwa, Yesu anali wofatsa ndipo anadziletsa kwambiri. Monyanyuka mtima, Petro anasolola lupanga ndi kubwezera. Koma Yesu anam’kumbutsa kuti: “Uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi awiri?” (Mateyu 26:51-53; Yohane 18:10) Petro anamvetsa phunziro limeneli ndipo nthawi ina anakumbutsa Akristu kuti: “Kristu anamva zowawa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake . . . amene pochitidwa chipongwe sanabwezera chipongwe, pakumva zowawa, sanaopsa.”—1 Petro 2:21-23.
18, 19. (a) Kodi ndi liti kwenikweni pamene abusa amafunikira kukhala ofatsa ndi odziletsa? (b) Kodi tikambirana mafunso ati m’nkhani yotsatira?
18 Mofananamo, abusa abwino amakhala ofatsa ngakhale pamene ena akuwachitira zinthu mosalungama. Mwachitsanzo, anthu ena amene iwo angafune kuwathandiza mu mpingo sangayamikire thandizolo. Ngati munthu amene akufunikira thandizo ali wofooka kapena wodwala mwauzimu, angalankhule “mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga” pamene akupatsidwa uphungu. (Miyambo 12:18) Komabe, mofanana ndi Yesu, abusa sayankha mwaukali kapena kuchita zinthu mopanda chifundo. M’malo mwake, amadziletsa ndipo amasonyezabe chifundo. Zimenezi zingathandize munthu amene akufunikira thandizoyo. (1 Petro 3:8, 9) Polandira uphungu, kodi mumatengera chitsanzo cha akulu chokhala ofatsa ndiponso odziletsa?
19 Mosakayikira, Yehova ndi Yesu amayamikira khama la abusa ambiri amene amasamalira mwaufulu gulu la nkhosa lapadziko lonse. Yehova ndi Mwana wake amakondanso kwambiri atumiki othandiza ambiri amene amathandiza akulu ‘potumikira oyera mtima.’ (Ahebri 6:10) Ndiyeno, n’chifukwa chiyani abale ena obatizidwa angazengerezere kukalamira “ntchito yabwino” imeneyi? (1 Timoteo 3:1) Ndipo kodi Yehova amaphunzitsa bwanji anthu amene amawaika kukhala abusa? Tikambirana mafunso amenewa m’nkhani yotsatira.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi ndi njira ziti zimene akulu amasonyezera kuti amakonda gulu la nkhosa?
• Kodi anthu onse mu mpingo angalimbikitse bwanji chimwemwe ndi mtendere?
• N’chifukwa chiyani abusa amakhala oleza mtima ndiponso achifundo akamapereka uphungu?
• Kodi akulu amasonyeza bwanji ubwino ndi chikhulupiriro?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 18]
Chikondi chimalimbikitsa akulu kutumikira mpingo
[Zithunzi patsamba 18]
Iwo amapezanso nthawi yokhala ndi mabanja awo pa zosangalatsa . . .
. . . ndi mu utumiki
[Chithunzi patsamba 20]
Kulankhulana bwino pakati pa akulu kumalimbikitsa chimwemwe ndi mtendere mu mpingo