Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuphunzitsa Mwana Momugwira Mtima

Kuphunzitsa Mwana Momugwira Mtima

Kuphunzitsa Mwana Momugwira Mtima

KODI munayamba mwamvapo chisoni mutaona mwana akuchita masewera ankhondo? Chifukwa choti zosangalatsa zambiri masiku ano zikumakhala zachiwawa, masewera otere afala kwabasi ngakhale pakati pa ana aang’ono zedi. Kodi mungathandize bwanji mwana kuti asiye kuchita masewera ankhondo n’kuyamba kuchita masewera amtendere? Waltraud, mayi wina amene wakhala mmishonale wa Mboni za Yehova kwa nthawi yaitali ku Africa, anapeza njira yothandizira kamnyamata kena kuchita zimenezi.

Chifukwa cha nkhondo, Waltraud anachoka m’dziko limene ankakhala n’kusamukira m’dziko lina ku Africa. Kumeneko anayamba kuphunzira Baibulo ndi mayi yemwe anali ndi mwana wamwamuna wa zaka zisanu. Nthawi zonse akapita kunyumba kwa mayiyo ankapeza mwana uja akusewera ndi kamfuti kapulasitiki. Iye analibe choseweretsa china chilichonse kupatulapo mfutiyi. Waltraud anali asanamuonepo mwanayu akulozetsa penapake mfutiyi, koma nthawi zonse mwanayo ankatsegula mfutiyo n’kumaitseka, ngati kuti akulowetsamo zipolopolo.

Waltraud anati kwa mwanayo: “Werner, kodi ukudziwa chifukwa chimene ndinabwerera kwanu kuno? N’chifukwa choti kwathu ndinathawa anthu oopsa amene ankawombera anthu anzawo ndi mfuti zokhala ngati mfuti yakoyi. Kodi ukuganiza kuti kuwombera anthu anzako ndi bwino?”

Werner anayankha kuti: “Ayi, sibwino.”

Waltraud anati: “Wayankha bwino.” Kenaka anafunsa kuti: “Kodi ukudziwa chimene ndimabwerera kunyumba kwanu kuno mlungu uliwonse? N’chifukwa choti Mboni za Yehova zimafuna kuthandiza ena kukhala mwamtendere ndi Mulungu komanso ndi anzawo.” Atapempha kaye mayi a Werner, Waltraud anauza mwanayu kuti: “Ukandipatsa mfuti yakoyo, ndikaitaya, n’kukakugulira galimoto yoseweretsa ya matayala anayi. Ndalonjeza.”

Werner anapereka mfuti yake yoseweretsa ija. Anadikirira milungu inayi, ndipo mapeto ake anasangalala kwambiri kulandira galimoto yake yoseweretsa ija, yomwe inali yamatabwa.

Kodi inuyo mumalankhula ndi ana anu, n’kumayesetsa kuwaphunzitsa mogwira mtima moti mpaka afike potaya zoseweretsa zilizonse zokhudzana ndi zida zankhondo? Ngati mumatero ndiye kuti mukuwaphunzitsa zinthu zowapindulitsa pamoyo wawo wonse.