Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kutumikira Kristu Mfumu Mokhulupirika

Kutumikira Kristu Mfumu Mokhulupirika

Kutumikira Kristu Mfumu Mokhulupirika

“Anam’patsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, am’tumikire.”​—DANIELI 7:14.

1, 2. Kodi tikudziwa bwanji kuti Kristu sanakhale ndi mphamvu zonse za Ufumu mu 33 C.E.?

KODI ndi wolamulira uti amene angafere anthu ake kenako n’kudzakhalanso ndi moyo n’kulamulira monga mfumu? Kodi ndi mfumu iti imene ingakhale padziko lapansi, kulimbikitsa anthu ake kuti aidalire ndi kuikhulupirira ndiyeno n’kukalamulira ili kumwamba? Munthu yekhayo amene anachita zimenezi ndiponso zinthu zina zambiri ndi Yesu Kristu. (Luka 1:32, 33) Pa Pentekoste 33 C.E., Kristu atamwalira, kuukitsidwa ndi kupita kumwamba, Mulungu ‘anapatsa iye akhale mutu pamtu pa zonse.’ (Aefeso 1:20-22; Machitidwe 2:32-36) Mwa njira imeneyi Kristu anayamba kulamulira koma sanayambe kulamulira aliyense. Anthu oyamba kuwalamulira anali Akristu odzozedwa ndi mzimu, amene amapanga Israyeli wauzimu, “Israyeli wa Mulungu.”​—Agalatiya 6:16; Akolose 1:13.

2 Patapita zaka pafupifupi 30 kuchokera pa Pentekoste mu 33 C.E., mtumwi Paulo anatsimikizira kuti Kristu anali asanakhale ndi mphamvu zonse za Ufumu, koma anali “pa dzanja lamanja la Mulungu chikhalire; kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ake aikidwa akhale mpando ku mapazi ake.” (Ahebri 10:12, 13) Ndiyeno, cha m’ma 96 C.E., mtumwi wokalamba Yohane anaoneratu m’masomphenya Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, Yehova, akuika Kristu Yesu kukhala Mfumu ya Ufumu wa kumwamba womwe unali utangokhazikitsidwa kumene. (Chivumbulutso 11:15; 12:1-5) Panopo tingathe kuona umboni wochuluka wotsimikizira kuti Kristu anayamba kulamulira monga Mfumu Yaumesiya mu 1914. *

3. (a) Kodi uthenga wabwino wa Ufumu wakhala ndi mbali yatsopano yotani kuyambira 1914? (b) Kodi ndi mafunso otani amene tingadzifunse?

3 Kuyambira 1914 uthenga wabwino wa Ufumu wakhala ndi mbali yatsopano yosangalatsa. Kristu wakhala akulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa kumwamba wa Mulungu ngakhale kuti akuchita zimenezi “pakati pa adani” ake. (Salmo 110:1, 2; Mateyu 24:14; Chivumbulutso 12:7-12) Ndiponso, padziko lonse lapansi, anthu ake okhulupirika akumvera ndi mtima wonse ulamuliro wake mwa kuchita nawo ntchito yapadziko lonse yophunzitsa Baibulo imene sinachitikepo m’mbiri yonse ya anthu. (Danieli 7:13, 14; Mateyu 28:18) Akristu odzozedwa ndi mzimu, ‘ana a Ufumu’ amatumikira monga “akazembe oimira Kristu.” Odzozedwa amenewa amathandizidwa mokhulupirika ndi khamu limene likumka liwonjezeka la “nkhosa zina” za Kristu, limene limatumikira monga nthumwi za Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 13:38; 2 Akorinto 5:20, Chipangano Chatsopano Mu Chichewa Cha Lero; Yohane 10:16) Ngakhale zili choncho, tifunika kudzipenda aliyense payekha kuti tione ngati timamveradi ulamuliro wa Kristu. Kodi ndife okhulupirika nthawi zonse kwa iye? Kodi tingakhale bwanji okhulupirika kwa Mfumu imene ikulamulira kumwamba? Koma choyamba, tiyeni tikambirane zifukwa zimene tiyenera kukhalira okhulupirika kwa Kristu.

Mfumu Yosavuta Kuitumikira Mokhulupirika

4. Kodi Yesu anachita chiyani monga Mfumu yosankhidwiratu panthawi ya utumiki wake padziko lapansi?

4 Maziko akuti tikhale okhulupirika kwa Kristu ndiwo kuyamikira zimene anachita ndiponso makhalidwe ake abwino kwambiri. (1 Petro 1:8) Nthawi imene Yesu anali padziko lapansi monga Mfumu yosankhidwiratu, anachita zochepa chabe kusonyeza zimene adzachite akadzayamba kulamulira padziko lonse nthawi ya Mulungu ikadzakwana. Iye anadyetsa anthu anjala. Anachiritsa odwala, akhungu, olumala, ogontha, ndi osalankhula. Ngakhale anthu ena akufa anawaukitsa. (Mateyu 15:30, 31; Luka 7:11-16; Yohane 6:5-13) Kuwonjezera pamenepa, kudziwa za moyo wa Yesu wa padziko lapansi kumatithandiza kuzindikira makhalidwe ake monga Wolamulira wam’tsogolo wa dziko lapansi. Makamaka khalidwe lake lachikondi chololera kuvutikira ena. (Marko 1:40-45) Mogwirizana ndi mfundo imeneyi, akuti Napoléon Bonaparte anati: “Ineyo, Alexander, Caesar, ndi Charlemagne tinakhazikitsa maufumu amphamvu, koma kodi tinakwanitsa bwanji zimenezi? Mwa kugwiritsa ntchito mphamvu. Ndi Yesu Kristu yekha amene anakhazikitsa ufumu wake mwa kugwiritsa ntchito chikondi, ndipo panopo anthu ambirimbiri akhoza kum’fera.”

5. N’chifukwa chiyani anthu ankakopeka ndi khalidwe la Yesu?

5 Chifukwa chakuti Yesu anali wofatsa ndiponso wodzichepetsa, anthu amene anali othodwa ndi mavuto ndiponso nkhawa ankatsitsimulidwa ndi ziphunzitso zake zolimbikitsa ndiponso umunthu wake wabwino. (Mateyu 11:28-30) Ana ankamasuka naye. Anthu odzichepetsa ndiponso ozindikira, mofunitsitsa anakhala ophunzira ake. (Mateyu 4:18-22; Marko 10:13-16) Chifukwa choganizira ndiponso kulemekeza ena, akazi ambiri oopa Mulungu anali okhulupirika kwa iye. Ena mwa akazi amenewa anagwiritsa ntchito nthawi, mphamvu ndiponso katundu wawo kum’samalira pamene ankachita utumiki wake.​—Luka 8:1-3.

6. Kodi Yesu anasonyeza motani kukhudzika mtima nthawi imene Lazaro anamwalira?

6 Kristu anakhudzika mtima kwambiri pamene bwenzi lake la pamtima Lazaro anamwalira. Chisoni cha Mariya ndi Marita chinamukhudza kwambiri moti analephera kudziletsa kuti asadzume ndipo “analira.” Ngakhale kuti Yesu ankadziwa kuti aukitsa Lazaro posachedwa, ‘anavutika mwini’ m’mtima chifukwa cha chisoni chachikulu. Ndiyeno, chifukwa cha chikondi ndi chifundo, Yesu anagwiritsa ntchito mphamvu zake zomwe Mulungu anam’patsa ndi kuukitsa Lazaro kwa akufa.​—Yohane 11:11-15, 33-35, 38-44.

7. Kodi n’chifukwa chiyani tifunika kukhala okhulupirika kwa Yesu? (Onaninso bokosi patsamba 31.)

7 Timachita chidwi kwambiri ndi khalidwe la Yesu lokonda kwambiri zinthu zabwino ndiponso lodana ndi chinyengo komanso kuipa. Kawiri konse anathamangitsa molimba mtima amalonda adyera mu kachisi. (Mateyu 21:12, 13; Yohane 2:14-17) Ndiponso, ali padziko lapansi, anakumana ndi mavuto osiyanasiyana, ndipo mwa kutero anaona mavuto amene timakumana nawo. (Ahebri 5:7-9) Yesu ankadziwanso mmene zimakhalira ngati anthu akukuda ndiponso ngati akukuchitira zinthu mopanda chilungamo. (Yohane 5:15-18; 11:53, 54; 18:38–19:16) Pomaliza, Yesu molimba mtima analolera kuphedwa mwankhanza kuti akwaniritse chifuniro cha Atate wake ndiponso kuti apereke moyo wosatha kwa anthu ake. (Yohane 3:16) Kodi makhalidwe otero a Kristu sakulimbikitsani kupitirizabe kum’tumikira mokhulupirika? (Ahebri 13:8; Chivumbulutso 5:6-10) Kodi chofunika n’chiyani kuti tilamulidwe ndi Kristu Mfumu?

Kukhala Woyenera Kulamulidwa ndi Kristu

8. Kodi anthu olamulidwa ndi Kristu ayenera kukhala otani?

8 Taganizirani izi: Kuti munthu akhale nzika ya dziko lina nthawi zambiri amayenera kukwaniritsa mfundo zina zofunika. Anthu omwe akufuna kukhala m’dziko lina amafunika kukhala akhalidwe labwino ndiponso omvera malamulo ena aukhondo. Mofananamo, anthu olamulidwa ndi Kristu ayenera kukhala akhalidwe labwino kwambiri ndiponso amoyo wabwino mwauzimu.​—1 Akorinto 6:9-11; Agalatiya 5:19-23.

9. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife okhulupirika kwa Kristu?

9 Yesu Kristu akufunanso kuti anthu omwe akuwalamulira akhale okhulupirika kwa iye ndi Ufumu wake. Anthuwo amasonyeza kuti ndi okhulupirika mwa kutsatira zimene Yesu anaphunzitsa nthawi imene anali padziko lapansi monga Mfumu yosankhidwiratu. Mwachitsanzo, m’malo mofuna zinthu zakuthupi, amaika patsogolo zofunika za Ufumu ndiponso kuchita chifuniro cha Mulungu. (Mateyu 6:31-34) Iwo amayesetsanso ndi mtima wonse kusonyeza umunthu wonga wa Kristu, ngakhale panthawi zovuta kwambiri. (1 Petro 2:21-23) Ndiponso, anthu olamulidwa ndi Kristu amatsatira chitsanzo chake mwa kuyamba iwo kuchitira ena zabwino.​—Mateyu 7:12; Yohane 13:3-17.

10. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife okhulupirika kwa Kristu (a) m’banja ndi (b) mu mpingo?

10 Otsatira a Yesu amasonyezanso kuti ndi okhulupirika kwa iye mwa kukhala ndi makhalidwe ake m’mabanja mwawo. Mwachitsanzo, amuna amakhala okhulupirika kwa Mfumu yawo ya kumwambayi mwa kutsanzira makhalidwe a Kristu pa zimene amachitira akazi ndi ana awo. (Aefeso 5:25, 28-30; 6:4; 1 Petro 3:7) Akazi amasonyeza kuti ndi okhulupirika kwa Kristu mwa kukhala ndi makhalidwe abwino ndiponso “mzimu wofatsa ndi wachete.” (1 Petro 3:1-4; Aefeso 5:22-24) Ana amakhala okhulupirika kwa Kristu ngati atsatira chitsanzo chake chokhala omvera. Pamene anali wachinyamata, Yesu ankamvera makolo ake, ngakhale kuti iwo anali opanda ungwiro. (Luka 2:51, 52; Aefeso 6:1) Anthu olamulidwa ndi Kristu amayesetsa mokhulupirika kumutsanzira mwa kumverana chisoni, kukonda abale ndiponso kukhala achifundo kwambiri. Amayesetsa kukhala monga Kristu, “odzichepetsa; osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe.”​—1 Petro 3:8, 9; 1 Akorinto 11:1.

Anthu Omvera Malamulo Ake

11. Kodi anthu olamulidwa ndi Kristu amamvera malamulo ati?

11 Monga momwe anthu amene akufuna kukhala nzika za dziko lina amakhalira omvera malamulo a dziko lawo latsopanolo, anthu olamulidwa ndi Kristu amamvera “chilamulo cha Kristu” mwa kuchita zinthu mogwirizana ndi zonse zimene Yesu anaphunzitsa ndi kulamula. (Agalatiya 6:2) Iwo, makamaka amakhala okhulupirika pomvera ‘lamulo lachifumu’ la chikondi. (Yakobo 2:8) Kodi malamulo amenewa amafuna kuti achite chiyani?

12, 13. Kodi timamvera bwanji “chilamulo cha Kristu” mokhulupirika?

12 Anthu olamulidwa ndi Kristu ndi opanda ungwiro ndipo amalakwa. (Aroma 3:23) Motero, afunika kupitiriza ‘kukonda abale ndi chikondi chosanyenga’ kotero kuti ‘akondane kwenikweni kuchokera m’mtima.’ (1 Petro 1:22) “Ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake,” Akristu mokhulupirika amagwiritsa ntchito lamulo la Kristu mwa “kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha.” Kumvera lamulo limeneli kumawathandiza kuti azinyalanyaza kupanda ungwiro kwa ena ndiponso kuti azipeza zifukwa zoti azikondana wina ndi mnzake. Kodi simuyamikira kukhala ndi anthu amene avala chikondi, chomwe ndi “chomangira cha mtima wamphumphu,” chifukwa chomvera mokhulupirika Mfumu yathu yachikondi?​—Akolose 3:13, 14.

13 Ndiponso, Yesu anafotokoza kuti chikondi chimene anasonyeza n’choposa chimene anthu amasonyezana nthawi zambiri. (Yohane 13:34, 35) Ngati timangokonda anthu amene amatikonda, palibe chinthu ‘choposa ena’ chimene tikuchita. Ngati zili choncho ndiye kuti chikondi chathu n’chosakwanira. Yesu anatilimbikitsa kutsanzira chikondi cha Atate wake mwa kukhala ndi chikondi cha chilungamo ngakhale kwa adani amene amatida ndiponso kutizunza. (Mateyu 5:46-48) Chikondi chimenechi chimalimbikitsanso nzika za Ufumu kuti zipirire mokhulupirika pantchito yawo yofunika. Kodi ntchito imeneyi ndi iti?

Kukhulupirika Kwawo Kumayesedwa

14. Kodi n’chifukwa chiyani ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri?

14 Nzika za Ufumu wa Mulungu tsopano zili ndi ntchito yofunika ‘yochitira umboni Ufumu wa Mulungu.’ (Machitidwe 28:23) Kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri chifukwa choti Ufumu Waumesiya udzatsimikizira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira chilengedwe chonse. (1 Akorinto 15:24-28) Tikamalalikira uthenga wabwino, anthu amene amamvetsera amakhala ndi mwayi wokhala nzika za Ufumu wa Mulungu. Kuwonjezera apo, Kristu Mfumu adzaweruza anthu mogwirizana ndi mmene anthuwo amalabadirira uthenga umenewu. (Mateyu 24:14; 2 Atesalonika 1:6-10) Motero, njira yaikulu imene timasonyezera kukhulupirika kwathu kwa Kristu ndiyo mwa kumvera lamulo lake louza ena za Ufumu.​—Mateyu 28:18-20.

15. N’chifukwa chiyani kukhulupirika kwa Akristu kumayesedwa?

15 N’zoona kuti Satana amatsutsa ntchito yolalikira m’njira iliyonse imene angathe. Ndipo anthu olamulira savomereza mphamvu za Kristu zomwe Mulungu anam’patsa. (Salmo 2:1-3, 6-8) N’chifukwa chake Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake. Ngati anandilondalonda ine, adzakulondalondani inunso.” (Yohane 15:20) Motero, otsatira a Kristu ali pankhondo yauzimu imene imayesa kukhulupirika kwawo.​—2 Akorinto 10:3-5; Aefeso 6:10-12.

16. Kodi nzika za Ufumu zimapereka bwanji “zake za Mulungu kwa Mulungu”?

16 Komabe nzika za Ufumu wa Mulungu zimakhalabe zokhulupirika kwa Mfumu yawo yosaoneka ndipo zimalemekeza anthu olamulira. (Tito 3:1, 2) Yesu anati: “Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu.” (Marko 12:13-17) N’chifukwa chake anthu a Kristu amamvera malamulo a boma amene sakusemphana ndi malamulo a Mulungu. (Aroma 13:1-7) Koma pamene bwalo lalikulu lamilandu la a Yuda linanyalanyaza malamulo a Mulungu mwa kulamula ophunzira a Yesu kuti asiye kulalikira, ophunzirawo mwaulemu koma molimba mtima ananena kuti ayenera “kumvera Mulungu koposa anthu.”​—Machitidwe 1:8; 5:27-32.

17. N’chifukwa chiyani tingakhale olimba mtima pamene kukhulupirika kwathu kukuyesedwa?

17 N’zoonekeratu kuti anthu a Kristu amafunika kulimba mtima kwambiri kuti akhale okhulupirika kwa Mfumu yawo akamazunzidwa. Komabe Yesu anati: “Odala muli inu mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha ine. Sekerani, sangalalani: chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu m’Mwamba.” (Mateyu 5:11, 12) Mawu amenewa anagwiradi ntchito kwa otsatira oyambirira a Kristu. Ngakhale pamene anakwapulidwa chifukwa chopitiriza kulalikira za Ufumu, anasangalala chifukwa choti “anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo. Ndipo masiku onse, m’Kachisi ndi m’nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.” (Machitidwe 5:41, 42) N’zoyamikika pamene nanunso mukusonyeza mzimu wokhala okhulupirika popirira mavuto, matenda, kufedwa, kapena chitsutso.​—Aroma 5:3-5; Ahebri 13:6.

18. Kodi mawu a Yesu kwa Pontiyo Pilato akusonyeza chiyani?

18 Yesu adakali Mfumu yosankhidwiratu, anafotokozera Pontiyo Pilato yemwe anali Kazembe wa Roma kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.” (Yohane 18:36) N’chifukwa chake, nzika za Ufumu wa kumwamba sizichita nkhondo ndi wina aliyense kapena kuthandizira mkangano uliwonse. Chifukwa chokhala okhulupirika kwa “Kalonga wa mtendere,” izo sizitenga nawo mbali m’mikangano yogawanitsa anthu ya dzikoli.​—Yesaya 2:2-4; 9:6, 7.

Anthu Okhulupirika Adzadalitsidwa Kosatha

19. N’chifukwa chiyani anthu a Kristu sayenera kukayikira kuti tsogolo lawo n’labwino?

19 Anthu okhulupirika a Kristu, “Mfumu ya mafumu,” sakukayikira kuti tsogolo lawo n’labwino. Iwo akuyembekeza mwachidwi kuti posachedwapa Yesu adzasonyeza mphamvu zake zaufumu. (Chivumbulutso 19:11–20:3; Mateyu 24:30) Otsalira a odzozedwa okhulupirika, ‘ana a Ufumu’ akuyembekeza mwachidwi cholowa chawo cha mtengo wapatali chokhala mafumu limodzi ndi Kristu kumwamba. (Mateyu 13:38; Luka 12:32) “Nkhosa zina” zokhulupirika za Kristu zikuyembekeza mwachidwi nthawi imene Mfumu yawo idzanena kuti: “Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu [Paradaiso wa padziko lapansi wa] Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi.” (Yohane 10:16; Mateyu 25:34) Motero, nzika zonse za Ufumu zipitirize ndi mtima wonse kutumikira Kristu Mfumu mokhulupirika.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Onani buku la Kukambitsirana za m’Malemba, pa kamutu kakuti, “Kodi n’chifukwa ninji Mboni za Yehova zimanena kuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa mu 1914?” masamba 231 mpaka 233, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mungafotokoze?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala okhulupirika kwa Kristu?

• Kodi anthu a Kristu amasonyeza motani kukhulupirika kwawo kwa iye?

• N’chifukwa chiyani tikufuna kukhala okhulupirika kwa Kristu Mfumu?

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 31]

MAKHALIDWE ENANSO ABWINO KWAMBIRL A KRISTU

Kusakondera​Yohane 4:7-30.

Chifundo​Mateyu 9:35-38; 12:18-21; Marko 6:30-34.

Chikondi chololera kuvutikira ena​—Yohane 13:1; 15:12-15.

Kukhulupirika​Mateyu 4:1-11; 28:20; Marko 11:15-18.

Kuganizira ena​Marko 7:32-35; Luka 7:11-15; Ahebri 4:15, 16.

Kulolera​Mateyu 15:21-28.

[Chithunzi patsamba 29]

Mwa kusonyezana chikondi, timamvera mokhulupirika “chilamulo cha Kristu”

[Zithunzi patsamba 31]

Kodi makhalidwe a Kristu amakulimbikitsani kumutumikira mokhulupirika?