Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Moyo Wanga Unasintha Nditadziwa Chifukwa Chimene Mulungu Amalolera Anthu Kuvutika

Moyo Wanga Unasintha Nditadziwa Chifukwa Chimene Mulungu Amalolera Anthu Kuvutika

Mbiri ya Moyo Wanga

Moyo Wanga Unasintha Nditadziwa Chifukwa Chimene Mulungu Amalolera Anthu Kuvutika

YOSIMBIDWA NDI HARRY PELOYAN

N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthu azivutika? Funso limenelo linandivutitsa kuyambira ndili mwana. Makolo anga anali anthu akhama pantchito, oona mtima, ndiponso okonda banja lawo. Koma bambo anga sanali munthu wokonda zopembedza ndipo mayi anga ankangozikonda pang’ono basi. Motero onse sakanatha kundiyankha funsoli.

NDINKADZIFUNSA kwambiri za funsoli makamaka panthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse ndiponso pambuyo pa nkhondoyi, pamene ndinali m’gulu la asilikali a dziko la United States a nkhondo ya pamadzi kwa zaka zoposa zitatu. Nkhondoyo itatha, ndinatumizidwa m’sitima yopita ku China kukasiya katundu wothandizira anthu. Kumeneko ndinakhalako pafupifupi chaka chathunthu ndipo ndinaona anthu ambiri akuvutika kwambiri.

Anthu a ku China ndi anzeru ndiponso olimbikira ntchito. Koma ambiri anali pamavuto adzaoneni chifukwa cha umphawi ndiponso nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Zinandikhudza kwambiri kuona tiana tokongola ndithu, koma tambiri mwa ito tonyentchera chifukwa chosowa zakudya m’thupi ndiponso titavala masanza, tikupemphetsa kwa ifeyo tikamachoka panyanja kupita kumtunda.

Sindinkamvetsa Chifukwa Chake

Ndinabadwa mu 1925 ndipo ndinakulira ku California, ku United States. M’moyo wanga wonse ndinali ndisanaonepo zinthu ngati zomwe ndinaona ku China zija. Motero nthawi zambiri ndinkadzifunsa kuti, ‘Ngati kulidi Mlengi wamphamvuyonse, iye angalole bwanji kuti anthu ambirimbiri, makamaka ana osalakwa, azivutika chonchi?’

Ndinkadzifunsanso kuti, ngati Mulunguyo alikodi, n’chifukwa chiyani akulola zinthu kufika powonongeka motere? Bwanji akulola kuti anthu ambirimbiri apululidwe, afe m’njira zosiyanasiyana ndiponso kuti avutike zaka zambirimbiri? Anthutu anavutika kwambiri makamaka pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, pamene anthu oposa 50 miliyoni anafa. Komanso pa nkhondo yonseyo, n’chifukwa chiyani anthu a chipembedzo chimodzi ankaphana molimbikitsidwa ndi azibusa awo, chifukwa choti anthuwo anali ochokera m’mayiko osiyana basi?

Makina Oonera Zinthu Zakutali

Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itayamba mu 1939 n’kuyamba kupha anthu ambirimbiri, ndinkaona kuti n’zosatheka kuti kunja kuno kuli Mulungu. Kenaka, kusukulu tikuphunzira sayansi, ana asukulu tonse tinauzidwa kuti tipange chinthu chilichonse chokhudzana ndi zasayansi. Popeza ndinkachita chidwi ndi sayansi ya zakuthambo, ndinaganiza zopanga makina aakulu oonera zakutali okhala ndi galasi lalikulu masentimita 20.

Kuti ndipange makinawa, ndinagula galasi lokhuthala pafupifupi masentimita atatu ndipo linali lalikulu masentimita 20. Ndinapita nalo kwa wodula magalasi kuti alidule mwakuti likhale lozungulira. Kenaka ndinayamba chintchito cholipala pamanja kuti likhale lolowa pakati pake. Nthawi yanga yonse yopumula pa telemu imeneyo inathera pantchitoyi. Galasilo litatha ndinaliika pa paipi yaitali yachitsulo ndipo makinawa ndinawaikira magalasi okulitsa zinthu okhala ndi mphamvu zosiyanasiyana.

Tsiku lina, kunja kulibe mwezi ndinapita panja ndi makina anga aja kwa nthawi yoyamba n’kuwalozetsa kumwamba kuti ndione mayiko ena amene amazungulira dziko lapansili. Ndinachita kakasi poona kuchuluka kwa nyenyezi, miyezi ndiponso mayiko ena angati dziko lapansili ndiponso kuona dongosolo la zinthu zonsezi. Kenaka ndinachita kufika poima mutu n’tadziwa kuti nyenyezi zina zimene ndinkaona, kwenikweni sizinali nyenyezi koma inali milalang’amba yokhala ndi nyenyezi zochuluka mosawerengeka, ngati mlalang’amba wathu wa Milky Way.

Ndinkaganiza motere: ‘Ndithu zimenezi sizinakhalepo zokha ayi. Palibe chinthu chokhala ndi dongosolo chimene chimangokhalapo mwamwayi. Chilengedwechi chili ndi dongosolo lapamwamba zedi moti chimaoneka kuti chinakonzedwa ndi katswiri wanzeru zakuya kwambiri. Kodi n’kutheka kuti Mulungu alikodi?’ Zimene ndinaona ndi makina oonera zinthu zakutaliwo zinandipangitsa kuti ndisiye kukakamira kwambiri mfundo yakuti kulibe Mulungu.

Kenaka ndinadzifunsa kuti: ‘Ngati kulidi Mulungu wamphamvu ndiponso wanzeru zotha kupanga chilengedwe chonse chodabwitsachi, kodi sangathe kukonza zinthu padziko pano kuti zikhale bwino? Ndipo kodi analoleranji n’komwe kuti zinthu ziipe chonchi?’ Anthu odziwa zachipembedzo omwe ndinawafunsa mafunsowa, sankandiyankha zogwira mtima.

Nditamaliza sukulu ya sekondale ndiponso nditakhala zaka zingapo ku koleji ndinalowa m’gulu la asilikali a ku America a nkhondo yapamadzi. Komabe, abusa omwe ali asilikali sanathenso kundiyankha mafunso angawo. Nthawi zambiri anthu amene anali achipembedzo ankanena zinthu monga zakuti, “Ambuye n’ngovuta kumumvetsa.”

Ndinapitiriza Kufufuza

Nditachoka ku China, ndinapitirizabe kudzifunsa mafunso okhudza chifukwa chimene Mulungu amalolera kuti anthu azivutika. Mafunsowa anandibwereranso, makamaka pamene ndinaona manda a asilikali pa zilumba zosiyanasiyana zimene tinaimapo m’njira tikubwerera kwathu kudutsa nyanja ya Pacific. Pafupifupi manda onsewo anali manda a anyamata amene anafa adakali aang’ono.

Nditabwerera ku United States n’kupatsidwa ufulu wochoka m’gulu la asilikali, ndinali nditatsala chaka chimodzi kuti ndimalize maphunziro anga pa yunivesite ya Harvard ku Cambridge, Massachusetts. Ndinamaliza maphunziro angawo ndipo ndinalandira digiri yanga, koma sindinabwerere kumudzi ku California. Ndinaganiza zokhala kwakanthawi kudera la kum’mawali, kuti ndiyese kupeza mayankho a mafunso anga. Motero ndinaganiza zopita ku New York City, komwe kunali zipembedzo zambirimbiri ndipo ndinatero pofuna kuti ndizipita ku mapemphero a zipembedzozi kukamva zimene amaphunzitsa.

Ku New York, azakhali anga dzina lawo Isabel Kapigian, anandiitana kuti ndizikakhala kunyumba kwawo. Iwowo ndi ana awo awiri, Rose ndi Ruth, anali Mboni za Yehova. Poganiza kuti ziphunzitso zawo sindingachite nazo chidwi, ndinayamba kupita ku mapemphero zipembedzo zina, kucheza ndi anthu a zipembedzozo ndiponso kuwerenga mabuku awo. Ndinkawafunsa kuti andiuze chifukwa chimene Mulungu amalolera kuti anthu azivutika, koma nawonso analibe yankho ngati ine ndemwe. Ndinafika poganiza kuti mwina Mulunguyonso kulibeko.

Kupeza Mayankho

Kenaka ndinapempha azakhali angawo ndi ana awo kuti andipatseko mabuku awo ena kuti ndione zimene Mboni za Yehova zimanena. Nditawerenga mabuku awowo, ndinaona mwamsanga kuti Mboni n’zosiyana kwambiri ndi zipembedzo zina. Mayankho awo anali ochokera m’Baibulo ndipo anali ogwira mtima kwabasi. Posakhalitsa, ndinayankhidwa mafunso anga onena za chifukwa chimene Mulungu amalolera kuvutika.

Koma si pokhapo ayi, ndinaonanso kuti zochita za Mboni za Yehova zinkagwirizananso ndi zikhulupiriro zawo zozikidwa m’Baibulo. Mwachitsanzo, ndinafunsa azakhali angawo kuti andiuze zimene achinyamata a Mboni za Yehova anachita ku Germany panthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Kodi analowa nawo magulu a nkhondo a kumeneko n’kumanena kuti “Hitler ndiye Mpulumutsi Wathu!,” n’kumachitira sawatcha mbendera yokhala ndi chizindikiro cha chipani cha Nazi? Yankho la funsoli linali lakuti ayi, sanatero. Ndipo chifukwa chokana kulowerera m’nkhondoyo, anagwidwa n’kukawaponya ku ndende zozunzirako anthu ndipo kumeneko ambiri anaphedwa. Iwo analongosola kuti Mboni za Yehova kulikonseko zinakana kumenya nawo nkhondoyo. Ngakhale m’mayiko a ndale za demokalase, achinyamata a Mboni za Yehova anaponyedwa m’ndende chifukwa chosafuna kumenya nawo nkhondoyo.

Kenaka azakhaliwo anandiuza kuti ndiwerenge lemba la Yohane 13:35, lomwe limati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” Akristu oona ayenera kukhala ndi chizindikiro chimenechi m’dziko lililonse limene akukhalamo padziko lonse. Sangapezeke akuchita nawo nkhondo m’gulu linalake, n’kumaphana chifukwa chosiyana mitundu. Iwo anafunsa kuti: “Kodi ungaganizire Yesu ndi ophunzira ake akumenyana, ena gulu ili ena gulu linalo n’kumaphana pa nkhondo zimene Aroma ankachita?”

Anandipemphanso kuti ndiwerenge 1 Yohane 3:10-12. Lembali limati: “M’menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a Mdyerekezi: yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake. . . . Tikondane wina ndi mnzake: osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake.”

Baibulo silinena zinthu mopita m’mbali pankhaniyi. Limati Akristu oona amakondana, ngakhale atakhala a mayiko osiyana. Motero sangaphe abale awo auzimu kapenanso munthu wina aliyense. N’chifukwa chake ponena za ophunzira ake, Yesu anati: “Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi.”​—Yohane 17:16.

Chomwe Mulungu Amalolera Kuti Anthu Azivutika

Posakhalitsa ndinadziwa kuti Baibulo limatiuza chifukwa chimene Mulungu amalolera anthu kuvutika. Baibulo limalongosola kuti Mulungu atalenga makolo athu oyamba, anawalenga angwiro ndipo anawaika m’munda wa paradaiso. (Genesis 1:26; 2:15) Anawapatsanso mphatso yabwino kwambiri: ufulu wosankha. Koma anayenera kugwiritsa ntchito bwino ufuluwo. Akanamvera Mulungu ndi malamulo ake, akanapitiriza kukhala angwiro m’paradaiso. Akanafutukula paradaisoyo kuti mpaka afike padziko lonse. Ana awo nawonso akanakhala angwiro, moti pakutha kwa nthawi, dzikoli likanakhala paradaiso wokongola wokhala ndi anthu angwiro komanso osangalala.​—Genesis 1:28.

Komabe, ngati Adamu ndi Hava akanasankha kuchita zofuna zawo osati za Mulungu, ndiye kuti Mulunguyu sakanalola kuti akhalebe anthu angwiro. (Genesis 2:16, 17) N’zomvetsa chisoni kwa anthufe kuti makolo athu oyambirirawa sanagwiritse ntchito bwino ufulu wawo wosankhawu ndipo anasankha kusachita zofuna za Mulungu. Analimbikitsidwa kutero ndi mngelo wopanduka amene anadzatchedwa kuti Satana Mdyerekezi. Iyeyu ankalakalaka kumachita zofuna zake osati za Mulungu ayi ndiponso ankalakalaka kumalambiridwa ngati Mulungu.​—Genesis 3:1-19; Chivumbulutso 4:11.

Motero, Satana anakhala “mulungu wa nthawi ino ya pansi pano.” (2 Akorinto 4:4) Baibulo limati: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Yesu anati Satana ndiye “mkulu wa dziko lapansi.” (Yohane 14:30) Kusamvera kwa Satana ndi makolo athu oyamba n’komwe kunabweretsa kupanda ungwiro, chiwawa, imfa, chisoni, ndiponso kuvutika pakati pa anthu onse.​—Aroma 5:12.

“Sikuli kwa Munthu”

Pofuna kusonyeza mmene moyo wa anthu ungakhalire ngati atapanda kumvera malamulo a Mlengi, Mulungu walola kuti papite zaka zambirimbiri tikuona zotsatirapo za kusamveraku. Nthawi imeneyi yapatsa anthu onse mwayi wovomerezana ndi Baibulo kuti indedi, “njira ya munthu siili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake. Yehova, mundilangize.”​—Yeremiya 10:23, 24.

Tsopano patha zaka zambirimbiri, ndipo tikutha kuona kuti kudzilamulira popanda Mulungu kwatibweretsera mavuto osaneneka. Motero, Mulungu sasiya kuti anthu apitirizebe kuyesa izi ndi izi podzilamulira popanda kumumvera Iye ndiponso kumvera malamulo ake.

Tsogolo Losangalatsa

Ulosi wa m’Baibulo umasonyeza kuti posachedwa, Mulungu athetsa dziko loipa ndiponso lankhanzali. Ulosiwu umati: “Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”​—Salmo 37:10, 11.

Ulosi wa pa Danieli 2:44 umati: “Masiku a mafumu aja [maulamuliro onse omwe alipo panopa] Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.” Zikadzatero Yehova sadzalolanso kuti anthu adzilamulire okha. Dziko lonse lapansi lizidzalamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu. Mu ulamuliro umenewu, dziko lonse lidzakhala paradaiso ndipo anthu adzafika pokhala angwiro n’kukhala ndi moyo wosangalala kwamuyaya. Baibulo limalonjeza kuti: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.” (Chivumbulutso 21:4) Mulungutu watikonzera tsogolo labwino zedi!

Moyo Wanga Unasintha

Kupeza mayankho ogwira mtima a mafunso omwe ndinali nawo kunasintha moyo wanga. Kuyambira pamenepo, ndinafunitsitsa kutumikira Mulungu ndi kuthandiza ena kupeza mayankho amenewa. Ndinazindikira kuti m’pofunika kumvera mawu a pa 1 Yohane 2:17 akuti: “Dziko lapansi [dongosolo la zinthu lilipoli lomwe likulamulidwa ndi Satana] lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthawi zonse.” Moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu ndinkaufuna kwambiri. Ndinaganiza zokhala ku New York n’kuyamba kupita ku misonkhano ya mpingo wina wa Mboni za Yehova kumeneko, ndipo ndinathandiza anthu ambiri kuphunzira zimene ndinaphunzirazo.

Mu 1949, ndinakumana ndi Rose Marie Lewis. Iyeyu, ndiponso mayi ake omwe dzina lawo ndi Sadie, komanso ang’ono ake ndi akulu ake sikisi onse anali a Mboni za Yehova. Rose ankatumikira Mulungu kwa nthawi zonse mu ntchito yolalikira. Anali mtsikana wakhalidwe labwino kwambiri, ndipo ananditenga mtima nthawi yomweyo. Tinakwatirana mu June 1950 n’kukhazikika ku New York. Tinkasangalala ndi ntchito yomwe tinkachita ndipo tinali ndi chimwemwe chifukwa cha chiyembekezo chodzakhala kosatha m’dziko latsopano la Mulungu.

Mu 1957, ine ndi mkazi wanga tinaitanidwa kukatumikira mwa nthawi zonse ku likulu la dziko lonse la Mboni za Yehova, lomwe lili ku Brooklyn, ku New York. Pofika mwezi wa June mu 2004 tinali titakwatirana, n’kumakhala mosangalala kwa zaka 54, ndipo tinali titatumikira ku likululi kwa zaka 47. Pa zaka zimenezi tinadalitsidwa kwambiri potumikira Yehova limodzi ndi Akristu anzathu ambirimbiri.

Vuto Lalikulu Kwambiri Pamoyo Wanga

N’zomvetsa chisoni kuti kumayambiriro kwa mwezi wa December mu 2004, mkazi wanga Rose Marie anamupeza ndi matenda a khansa omwe anachititsa chotupa mbali imodzi ya mapapo ake. Madokotala ananena kuti chotupacho chikumka chikula mofulumira ndipo m’pofunika kuti achichotse. Anamuchita opaleshoni mu December yemweyo, ndipo patatha pafupifupi mlungu umodzi, dokotala anachita opaleshoniyo analowa m’chipinda chimene Rose anagonekedwa, ineyo ndili momwemo, n’kunena kuti: “Inu a Rose Marie, mwachira. Mungathe kupita kunyumba tsopano.”

Koma patangotha masiku angapo chabe titabwerera kunyumba, mkazi wangayo anayamba kumva ululu wadzaoneni m’mimbamu ndiponso mbali zina za thupi lake. Ululuwo unapitirira motero tinapita naye kuchipatala kuti akamuyezenso. Anapeza kuti magazi a m’ziwalo zingapo za m’mimba mwake ankangoundana motero mpweya wofunikira umene umakhala m’magazi unkalephera kufika bwinobwino ku ziwalozo. Madokotalawo anayesa zonse zimene akanatha kuchita monga anthu koma analephera. Moti patangotha milungu yochepa chabe, pa January 30, 2005, ndinakumana ndi vuto lalikulu kwambiri pamoyo wanga wonse. Mkazi wanga wokondedwa, Rose Marie anamwalira.

Panthawiyi, ndinali ndi zaka pafupifupi 80 ndipo pamoyo wanga ndinali nditaona anthu ambiri akuvutika, koma zinali zosiyana kwambiri ndi kufa kwa mkazi wanga. Monga Baibulo limanenera, ineyo ndi Rose Marie tinali “thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Ndinali nditaona mmene anthu ena anali kuvutikira anzawo ndiponso achibale awo akamwalira. Ndipo ine ndemwe zimenezi zinali zitandichitikirapo. Koma ululu wa kufa kwa mkazi wanga unandipyoza mozama kwambiri komanso unakhala kwa nthawi yaitali. Tsopano ndikutha kumvetsa kukula kwa chisoni chimene anthu akhala akumva kwa zaka zambirimbirizi chifukwa cha kufa kwa okondedwa awo.

Komabe, chandithandiza kwambiri ndicho kumvetsa chiyambi cha mavutowa ndi mmene adzathere. Lemba la Salmo 34:18 limati: “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.” Chofunika kuti tithe kupirira mavuto oterewa ndicho kudziwa kuti Baibulo limaphunzitsa kuti akufa adzauka, kuti anthu adzauka kumanda n’kukhala ndi mwayi wokhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu. Lemba la Machitidwe 24:15 limati: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” Rose Marie ankakonda kwambiri Mulungu. Sindikukayika kuti Mulungu nayenso ankam’konda ndiponso kuti adzam’kumbukira n’kumuukitsa nthawi yake ikadzakwana, ndipo tikuyembekeza kuti zimenezi zichitika posachedwa.​—Luka 20:38; Yohane 11:25.

N’zoona kuti munthu wokondedwa akamwalira timakhala ndi chisoni chachikulu, komatu chimwemwe chodzamulandira wokondedwayo akadzaukitsidwa chidzaposa chisonichi. (Marko 5:42) Mawu a Mulungu amalonjeza kuti: “Akufa anu adzakhala ndi moyo . . . Dziko lapansi lidzatulutsa mizimu [“akufa,” NW].” (Yesaya 26:19) N’zotheka kuti ambiri mwa anthu “olungama” otchulidwa pa Machitidwe 24:15 ndi amene adzayambirire kuukitsidwa. Zimenezitu zidzakhala zosangalatsa kwambiri! Ndipo Rose Marie adzakhala m’gulu la anthu amene adzaukitsidwewo. Iyeyu adzalandiridwa ndi manja onse a anthu omukonda. Zidzakhalatu zosangalatsa kwambiri panthawiyo kukhala m’dziko lopanda mavuto aliwonse!

[Zithunzi patsamba 9]

Ndili ku China ndinaona anthu akuvutika

[Zithunzi patsamba 10]

Kuyambira mu 1957, ndakhala ndikutumikira ku likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova ku Brooklyn

[Chithunzi patsamba 12]

Ndinakwatira Rose Marie mu 1950

[Chithunzi patsamba 13]

Mu 2000, pa chikondwerero choti takwanitsa zaka 50 tili m’banja