Tsanzirani Yesu Poganizira Osauka
Tsanzirani Yesu Poganizira Osauka
KUSAUKA ndiponso kuponderezedwa kunayamba kale kwambiri patangopita nthawi pang’ono anthu atalengedwa. Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisrayeli cholinga chake chinali choteteza anthu osauka ndi kuwachepetsera mavuto, koma nthawi zambiri Aisrayeliwo ankanyalanyaza Chilamulocho. (Amosi 2:6) Mneneri Ezekieli anawadzudzula chifukwa cha zinthu zomwe ankachitira anthu osauka. Iye anati: “Anthu a m’dziko anazunzazunza, nalandalanda mwachiwawa, napsinja ozunzika ndi aumphawi, nazunza mlendo wopanda chifukwa.”—Ezekieli 22:29.
Zinthu zinalinso chimodzimodzi Yesu ali padziko lapansi pano. Atsogoleri achipembedzo sankaganizirako ngakhale pang’ono za anthu osauka. Akuti atsogoleriwo anali “okonda ndalama” ndipo ‘ankawononga nyumba za akazi amasiye’ komanso ankaganizira kwambiri zosunga miyambo yawo kuposa kuthandiza okalamba ndi osauka. (Luka 16:14; 20:47; Mateyu 15:5, 6) N’zochititsa chidwi kuti m’fanizo la Yesu la Msamariya wachifundo, wansembe ndi Mlevi ataona munthu wovulala, anamulambalala n’kuyenda tsidya lina la msewu m’malo mopatuka kuti akam’thandize.—Luka 10:30-37.
Yesu Ankaganizira Anthu Osauka
Nkhani za m’Mauthenga Abwino zonena za moyo wa Yesu zimasonyeza kuti iye ankamvetsa mavuto a anthu osauka ndipo ankaganizira 2 Akorinto 8:9) Ataona khamu la anthu, Yesu “anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36) Nkhani ya mkazi wosauka wamasiye imasonyeza kuti Yesu anachita chidwi kwambiri ndi ndalama yochepa imene mkaziyo anapereka osati ndi mphatso zikuluzikulu zimene olemera anapereka “mwa unyinji wawo.” Yesu anakhudzidwa mtima chifukwa mkaziyu “mwa kusowa kwake anaikamo za moyo wake, zonse anali nazo.”—Luka 21:4.
kwambiri zosowa zawo. Ngakhale kuti Yesu anakhalapo kumwamba, anadzikhuthula, n’kukhala munthu, ndipo ‘chifukwa cha ife anakhala wosauka.’ (Sikuti Yesu ankangowamvera chisoni anthu osauka koma ankaganiziranso zosowa zawo. Iye ndi ophunzira ake anali ndi thumba lapadera lothandizira Aisrayeli osauka. (Mateyu 26:6-9; Yohane 12:5-8; 13:29) Yesu ankalimbikitsa anthu ofuna kukhala om’tsatira kuti azidziwa udindo wawo wothandiza ovutika. Iye anauza wolamulira wachinyamata wachuma kuti: “Gulitsa zilizonse uli nazo, nugawire osauka; ndipo udzakhala nacho chuma chenicheni m’Mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.” Munthuyu anakana kusiyana nacho chuma chakecho, kusonyeza kuti ankakonda kwambiri chumacho kuposa mmene ankakondera Mulungu ndiponso anthu anzake. Motero, analibe makhalidwe ofunikira kuti akhale wophunzira wa Yesu.—Luka 18:22, 23.
Otsatira Kristu Amaganizira Osauka
Yesu atamwalira, atumwi ndi anthu ena om’tsatira anapitiriza kuchita zinthu moganizira osauka. Cha m’ma 49 C.E., mtumwi Paulo anakumana ndi Yakobo, Petro, ndi Yohane n’kukambirana za ntchito yolalikira uthenga wabwino imene Ambuye Yesu Kristu anam’patsa Pauloyo. Iwo anagwirizana zoti Paulo ndi Barnaba apite kwa “amitundu,” kuti azikalalikira makamaka Akunja. Komabe, Yakobo ndi anzakewo analimbikitsa Paulo ndi Barnaba kuti ‘akumbukire aumphawi.’ Ndipo Paulo ‘anafulumira kuchita zimenezo.’—Agalatiya 2:7-10.
Panthawi ya ulamuliro wa Mfumu Klaudiyo, mbali zosiyanasiyana za Ufumu wa Roma kunali njala. Pothandizapo, Akristu a ku Antiokeya “yense monga anakhoza, anatsimikiza mtima kutumiza zothandiza abale akukhala m’Yudeya; ichonso anachita, natumiza kwa akulu mwa dzanja la Barnaba ndi Saulo.”—Machitidwe 11:28-30.
Nawonso Akristu oona masiku ano amadziwa kuti otsatira Yesu ayenera kuganizira osauka, makamaka Akristu oona anzawo. (Agalatiya 6:10) Motero, amayesetsa kuganizira anzawo amene akusowa zinthu zofunikira pamoyo. Mwachitsanzo, mu 1998 mbali yaikulu ya kumpoto cha kum’mawa kwa dziko la Brazil kunali chilala. Chilalachi chinawonongetsa mbewu za mpunga, nyemba, ndi chimanga, n’kuchititsa kuti m’dziko lonselo mukhale njala yomwe inali isanawonekepo kwa zaka 15. M’madera ena, anthu ankasowa ngakhale madzi akumwa. Nthawi yomweyo a Mboni za Yehova m’zigawo zina za dzikolo anakonza makomiti opereka chithandizo ndipo posakhalitsa, anasonkhanitsa chakudya chambiri ndipo analipira magalimoto kuti anyamule katunduyo.
Mboni za Yehova zomwe zinali kupereka chithandizochi zinalemba kalata yonena kuti: “Tikusangalala kwambiri kuti tathandiza abale athu, makamaka chifukwa choti tikudziwa kuti potero tasangalatsa mtima wa Yehova. Sitiiwala Yakobo 2:15, 16.” Mavesi amenewa amati: “Mbale kapena mlongo akakhala wausiwa, nichikam’sowa chakudya cha tsiku lake, ndipo wina wa inu akanena nawo, Mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosowa za pathupi; kupindula kwake n’chiyani?”
mawu a paMumpingo wina wa Mboni za Yehova mumzinda wa São Paulo, mayi wina wosauka, wa Mboni, yemwe ndi wodzichepetsa ndiponso wakhama amavutika nthawi zambiri kuti apeze zinthu zofunika pamoyo wake. Mayiyu anati: “Ngakhale ndili wosauka, uthenga wa m’Baibulo wandithandiza kwambiri pamoyo wanga. Chipanda a Mboni anzanga kundithandiza sindikudziwa kuti chikanandichitikira n’chiyani.” Panthawi ina, Mkristu ameneyu anafunika kukachitidwa opaleshoni kuchipatala koma analephera kukwanitsa kulipira ndalama za kuchipatalako. Zitatero, abale ndi alongo achikristu mumpingo anamuthandiza kulipira ndalamazo kuti akachitidwe opaleshoniyo. Akristu oona padziko lonse amathandiza Akristu anzawo akavutika.
Komabe, ngakhale kuti zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri, n’zachidziwikire kuti sizingathetseretu umphawi ayi. Maboma amphamvu ndiponso mabungwe akuluakulu achithandizo padziko lonse ayesetsa kuthandizako apo ndi apo koma alephera kuthetseratu vuto la umphawi lomwe n’lakale kwambiri. Motero, funso n’lakuti, Kodi ndi njira yabwino iti imene idzathetseretu umphawi ndiponso mavuto ena amene akuvutitsa anthu?
Zimene Baibulo Limaphunzitsa Zimathandiza Kosatha
Nkhani za m’Mauthenga Abwino zimasonyeza kuti nthawi ndi nthawi Yesu Kristu ankachitira zinthu zabwino anthu osauka ndi anthu ovutika m’njira zosiyanasiyana. (Mateyu 14:14-21) Komabe kodi ndi ntchito iti imene iye anaikirapo maganizo kwambiri? Panthawi ina, atatha nthawi ndithu akuthandiza anthu ovutika, Yesu anauza ophunzira ake kuti: ‘Tiyeni kwina, ku midzi ili pafupi apa, kuti ndilalikire komwekonso.’ N’chifukwa chiyani Yesu analekeza ntchito yake yothandiza odwala ndi osauka n’kumakapitiriza kulalikira? Analongosola chifukwa chake ponena kuti, “pakuti ndadzera ntchito [yolalikira].” (Marko 1:38, 39; Luka 4:43) Inde, Yesu ankaona kuti m’pofunika kuthandiza anthu osauka, koma ntchito yake yaikulu inali yolalikira za Ufumu wa Mulungu.—Marko 1:14.
Popeza kuti Baibulo limalimbikitsa Akristu kuti ‘alondole mapazi ake,’ Akristu masiku ano akamathandiza ena amatsanzira chitsanzo cha Yesu poika patsogolo ntchito yofunika kwambiri. (1 Petro 2:21) Iwo amathandiza osauka monga ankachitira Yesu. Koma monga Yesu, nawonso ntchito yawo yaikulu kwambiri ndiyo kuphunzitsa ena za uthenga wabwino wa m’Baibulo wonena za Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 5:14-16; 24:14; 28:19, 20) Komano, kodi n’chifukwa chiyani kulalikira uthenga wa m’Mawu a Mulungu kuli kofunikira kuposa njira zina zothandizira ena?
Nkhani za anthu a m’mayiko osiyanasiyana padziko lonse zimasonyeza kuti anthu akamvetsa ndi kutsatira malangizo othandiza a Baibulo, amakhala okonzeka kuthana ndi mavuto a tsiku ndi tsiku a m’moyo, kuphatikizapo umphawi. Komanso, uthenga wa m’Baibulo wonena za Ufumu wa Mulungu womwe Mboni za Yehova zimalalikira masiku ano umapatsa anthu chiyembekezo 1 Timoteo 4:8) Kodi n’chiyembekezo chotani chimenechi?
chomwe chimawalimbitsa mtima ngakhale atakumana ndi mavuto aakulu motani. (Pa za tsogolo lathu, Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti: “Monga mwa lonjezano [la Mulungu] tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) Baibulo likanena kuti “dziko,” nthawi zina limakhala likutanthauza anthu amene akukhala padziko. (Genesis 11:1) Motero “dziko latsopano” lolungama limene linalonjezedwalo kwenikweni ndi anthu amene Mulungu akusangalala nawo. Mawu a Mulungu amalonjezanso kuti mu ulamuliro wa Kristu, anthu amenewa adzalandira moyo wosatha ndipo adzakhala moyo wosangalatsa m’Paradaiso padziko lapansi. (Marko 10:30) Munthu aliyense, ndi osauka omwe, angakhale ndi tsogolo losangalatsali. Mu “dziko latsopano” limenelo, vuto la umphawi lidzathetsedwa kwamuyaya.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 7]
KODI YESU “ADZAPULUMUTSA WAUMPHAWI” MOTANI?—Salmo 72:12
CHILUNGAMO: ‘Adzaweruza ozunzika a mwa anthu, adzapulumutsa ana aumphawi, nadzaphwanya wosautsa.’ (Salmo 72:4) Mu ulamuliro wa Kristu wa padziko lonse, chilungamo chidzakhalapo kwa aliyense. Sikudzakhalanso ziphuphu, zomwe zasaukitsa mayiko ambiri amene akanakhala olemera.
MTENDERE: ‘Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi.’ (Salmo 72:7) Umphawi wambiri padziko pano umayamba chifukwa cha mikangano ya anthu ndiponso nkhondo. Kristu adzabweretsa mtendere pena paliponse padziko lapansi, ndipo potero adzathetsa limodzi mwa mavuto akuluakulu amene amayambitsa umphawi.
CHIFUNDO: ‘Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nadzapulumutsa moyo wa aumphawi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wa mtengo pamaso pake.’ (Salmo 72:12-14) Osauka ndi ozunzidwa adzakhala mbali ya banja losangalala la anthu ogwirizana mu ulamuliro ndi Mfumu Yesu Kristu.
KUPEZA BWINO: ‘M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka.’ (Salmo 72:16) Mu ulamuliro wa Kristu, anthu adzakhala olemera ndi osasowa kanthu. Anthu sadzavutikanso ndi kusowa chakudya kapena zilala zimene nthawi zambiri zimasaukitsa anthu masiku ano.
[Chithunzi pamasamba 4, 5]
Yesu ankaganizira kwambiri zosowa za anthu osauka
[Chithunzi patsamba 6]
Uthenga wa Baibulo umapereka chiyembekezo chenicheni