Umphawi Masiku Ano
Umphawi Masiku Ano
VICENTE * nthawi zambiri amakoka chikuku chodzaza ndi katundu m’misewu ya mumzinda wa São Paulo, ku Brazil. Amatolera makatoni, zitsulo zotha ntchito, ndi mapulasitiki. Kukada, amagona m’mphepete mwa msewu pansi pa chikuku chakecho, atayalapo katoni. Chiphokoso cha magalimoto ndi mabasi ambirimbiri omwe amadutsa mumsewuwo anangofika pochizolowera. Nthawi inayake, iyeyu anali ndi banja, nyumba, ndiponso anali pantchito, koma zonsezo zinapita. Tsopano amakhala moyo wovutika m’misewu.
N’zomvetsa chisoni kuti padziko lonse pali anthu ambiri onga Vicente, omwe ali paumphawi wadzaoneni. M’mayiko osauka, anthu ambiri amangokhala m’misewu kapena m’nyumba zazisakasa. N’zofala kuona anthu opemphetsa, monga olumala, akhungu, ndiponso azimayi oyamwitsa ana. Magalimoto akaima pa maloboti, ana amathamangira pakati pa msewu n’kumatsatsa zinthu monga masiwiti, pofuna kupezako kangachepe.
N’zovuta kulongosola chifukwa chimene palili umphawi woterewu. Magazini ya ku Britain yotchedwa The Economist inati: “Kuthetsa umphawi kuyenera kukhala kosavuta panopo chifukwa choti, mosiyana ndi kale lonse, anthu alemera kwambiri, adziwa kwambiri zachipatala, afika patali kwambiri pa luso la zaumisiri ndiponso pa nzeru zawo.” N’zoona kuti anthu ambiri apindula ndi nzeru zimenezi. M’misewu ya m’mizinda ikuluikulu ya m’mayiko ena osauka mumachita kuti thothotho ndi magalimoto atsopano aphuliphuli. Masitolo akuluakulu n’ngodzaza ndi zipangizo zamakono, ndipo anthu ofuna kugula zinthuzi sasowa ayi. Masitolo awiri ku Brazil anachita chionetsero chofuna kukopa makasitomala ambiri. Anakhala otsegula usiku wonse kuyambira pa 23 mpaka pa 24 December, 2004. Sitolo imodziyo inaitana ovina kuti adzasangalatse makasitomala. Chionetserochi chinakopa makasitomala pafupifupi 500,000!
* Komabe ngakhale kuti ntchito zoterezi n’zolimbitsa mtima ndithu, magazini yomweyi inanena kuti: “Palinso zifukwa zambiri zosonyeza kuti n’zokayikitsa kuti zolinga zimenezi zikukwaniritsidwa. Mayiko ambiri akunyinyirika kupereka ndalama ku thumba lothandiza pantchitoyi chifukwa choti nthawi zambiri ndalamazo siziwafika anthu oyenera kuthandizidwawo.” Tsoka ilo, chifukwa cha ziphuphu ndiponso malamulo ochedwetsa zinthu, ndalama zambiri zomwe zimaperekedwa ndi maboma osiyanasiyana, mabungwe a padziko lonse, ndiponso anthu sizifika n’komwe kwa anthu ofunika thandizowo.
Komabe, pali anthu ambiri amene chuma choterechi amangochionera patali basi. Kusiyana kwakukulu pakati pa olemera ndi osauka kwachititsa anthu ambiri kuona kuti m’pofunika kuchitapo kanthu mwamsanga pofuna kuchepetsa umphawi. Magazini ya ku Brazil yotchedwa Veja inati: “Chaka chino [cha 2005] nkhondo yolimbana ndi umphawi ndiyo iyenera kukhala nkhani yaikulu yoti atsogoleri a mayiko akambirane.” Magaziniyo inanenaponso za maganizo okhala ndi ntchito yotchedwa Marshall Plan yomwe cholinga chake n’kuthandiza mayiko osauka kwambiri, makamaka a ku Africa.Yesu ankadziwa kuti umphawi ndi vuto lomwe lidzapitirire. Iye anati: “Nthawi zonse muli nawo aumphawi pamodzi nanu.” (Mateyu 26:11) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti umphawi sudzatha padziko pano? Kodi anthu sangachitepo chilichonse kuti vutoli lithe? Kodi Akristu angachitepo chiyani kuti athandize osauka?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 2 Dzinali talisintha.
^ ndime 5 Marshall Plan inali ntchito yokonzedwa ndi dziko la United States yomwe cholinga chake chinali chothandiza mayiko a ku Ulaya kuti chuma chawo chiyambenso kuyenda bwino pambuyo pa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse.