Yehova Amaphunzitsa Abusa a Nkhosa Zake
Yehova Amaphunzitsa Abusa a Nkhosa Zake
“Yehova apatsa nzeru; kudziwa ndi kuzindikira kutuluka m’kamwa mwake.”—MIYAMBO 2:6.
1, 2. N’chifukwa chiyani amuna obatizidwa amakalamira udindo wowonjezeka mu mpingo?
“NDINASANGALALA kwambiri pamene ndinaikidwa kukhala mkulu. Ndinaona ntchito imeneyi kukhala mwayi wapadera wowonjezerera utumiki wanga kwa Yehova. Ndinkaona kuti ndiyenera kumuyamikira chifukwa cha zinthu zonse zimene wandichitira. Ndinkafunanso kuyesetsa mmene ndikanathera kuthandiza anthu a mu mpingo monga momwe akulu ena anandithandizira,” anatero Nick, yemwe watumikira monga mkulu kwa zaka seveni. Koma ngakhale kuti anali wosangalala analinso ndi nkhawa. Nick anapitiriza kuti: “Popeza ndinali ndisanakwanitse zaka 30 pamene ndinaikidwa kukhala mkulu, ndinkada nkhawa kuti ndilibe mtima wozindikira ndiponso nzeru, zomwe ndi zofunika kuti ndithe kuweta bwino mpingo.”
2 Anthu amene Yehova amawaika kuti asamalire nkhosa zake ali ndi zifukwa zambiri zokhalira achimwemwe. Mtumwi Paulo anakumbutsa akulu a ku Efeso chifukwa chimodzi pogwira mawu a Yesu, akuti: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Kukhala mtumiki wothandiza kapena mkulu kumapatsa amuna obatizidwa njira zina zoti atumikirire Yehova ndiponso mpingo. Mwachitsanzo, atumiki othandiza amagwira ntchito limodzi ndi akulu. Atumiki othandizawa nawonso amachita ntchito zina zambiri zotenga nthawi yambiri koma zimene ndi zofunika. Abale amenewa amachita utumiki wofunika umenewu chifukwa cha kukonda Mulungu ndiponso anansi awo.—Marko 12:30, 31.
3. N’chifukwa chiyani ena angazengereze kukalamira maudindo mu mpingo?
3 Nanga bwanji Mkristu amene akuzengereza kukalamira udindo chifukwa choti akuona kuti ndi wosakwanira kukhala mtumiki wothandiza ndipo m’kupita kwa nthawi n’kudzakhala mkulu? Mofanana ndi Nick, angakhale ndi nkhawa yoti alibe luso lofunika kuti akhale mbusa wabwino. Monga mbale wobatizidwa, kodi ndinu mmodzi wa anthu amene amamva chonchi? Nkhawa yotero ndi yomveka chifukwa choti Yehova amaona mmene abusa akusamalira nkhosa. Yesu anati: “Munthu aliyense adamupatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere zoposa.”—Luka 12:48.
4. Kodi Yehova amathandiza bwanji anthu amene amawaika kuti asamalire nkhosa zake?
4 Kodi Yehova amayembekezera anthu amene amawaika kukhala atumiki othandiza ndiponso akulu kusamalira maudindo awo popanda thandizo? Ayi. M’malo mwake, amapereka thandizo labwino kuti athe kukwanitsa ntchito yawo ndiponso kuichita bwino. Monga mmene tafotokozera m’nkhani yapitayi, Yehova amawapatsa mzimu wake woyera, umene chipatso chake chimawathandiza kusamalira nkhosa mwachikondi. (Machitidwe 20:28; Agalatiya 5:22, 23) Ndiponso, Yehova amawapatsa nzeru, kudziwa, ndi kuzindikira. (Miyambo 2:6) Kodi amachita bwanji zimenezi? Tiyeni tikambirane njira zitatu zimene Yehova amagwiritsa ntchito pophunzitsa anthu amene amawaika kuti asamalire nkhosa zake.
Kuphunzitsidwa ndi Abusa Odziwa Ntchito Yawo
5. N’chifukwa chiyani Petro ndi Yohane anali abusa abwino?
5 Mtumwi Petro ndi mtumwi Yohane atakaonekera pamaso pa Sanihedrini, oweruza a nzeru zadzikoli a khoti limeneli, anaona atumwiwa kukhala “osaphunzira ndi opulukira.” Koma iwo ankatha kuwerenga ndi kulemba, ngakhale Machitidwe 4:1-4, 13) N’zoona, iwo anali atalandira mzimu woyera. (Machitidwe 1:8) Koma zinalinso zosakayikitsa ngakhale kwa oweruza akhungu mwauzimu aja kuti Yesu anali atawaphunzitsa amunawa. Pamene anali nawo padziko lapansi, Yesu anaphunzitsa atumwi mmene angasonkhanitsire anthu onga nkhosa ndiponso mmene angawetere anthu amenewa akakhala mbali ya mpingo.—Mateyu 11:29; 20:24-28; 1 Petro 5:4.
kuti sanaphunzire Malemba m’sukulu za Arabi. Ngakhale zinali choncho, Petro ndi Yohane limodzi ndi ophunzira ena anakhala aphunzitsi ogwira mtima, ndipo anathandiza ambiri mwa anthu amene anawamvetsera kukhala okhulupirira. Kodi anthu wamba amenewa anakhala bwanji aphunzitsi odabwitsa? Akhotili atamvetsera Petro ndi Yohane, “anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu.” (6. Kodi Yesu ndi Paulo anasonyeza chitsanzo chotani pankhani yophunzitsa ena?
6 Yesu ataukitsidwa anapitiriza kuphunzitsa anthu amene anaikidwa kukhala abusa. (Chivumbulutso 1:1; 2:1–3:22) Mwachitsanzo, Yesu anasankha Paulo ndipo anaonetsetsa kuti waphunzitsidwa. (Machitidwe 22:6-10) Paulo anayamikira kwambiri maphunziro amene analandira ndipo anaphunzitsanso akulu ena zimene anaphunzira. (Machitidwe 20:17-35) Mwachitsanzo, anagwiritsa ntchito nthawi yambiri ndiponso mphamvu zake pophunzitsa Timoteo kukhala “wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi” potumikira Mulungu. (2 Timoteo 2:15) Amuna amenewa anakhala mabwenzi okondana kwambiri. M’mbuyomo, ponena za Timoteo, Paulo analemba kuti: “Monga mwana achitira atate wake, anatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino.” (Afilipi 2:22) Paulo sanafune kuti Timoteo kapena munthu wina akhale wophunzira wake. M’malo mwake, analimbikitsa okhulupirira anzake ‘kum’tsanzira monga mmene iye anatsanzirira Kristu.’—1 Akorinto 11:1.
7, 8. (a) Kodi ndi nkhani yotani yomwe ikusonyeza phindu limene limakhalapo akulu akatsanzira Yesu ndiponso Paulo? (b) Kodi ndi liti pamene akulu ayenera kuyamba kuphunzitsa abale oti angadzakhale atumiki othandiza ndi akulu?
7 Potsanzira Yesu ndi Paulo, abusa odziwa ntchito amayamba ndi iwo kuphunzitsa abale obatizidwa ndipo iwonso amakhala ndi zotsatirapo zabwino. Taonani za Chad. Iye analeredwa m’banja limene mayi ndi bambo anali osiyana zipembedzo ndipo waikidwa kukhala mkulu posachedwapa. Iye akuti: “Kwa zaka zambiri, akulu osiyanasiyana okhwima mwauzimu anandithandiza kuti ndichite bwino mwauzimu. Chifukwa choti bambo anga anali wosakhulupirira, akuluwa anali nane ndi chidwi kwambiri ndipo anakhala monga abambo anga auzimu. Iwo ankakonza nthawi yoti andiphunzitse mu utumiki, ndipo nthawi ina, mkulu winawake anandiphunzitsa kuchita ntchito za pampingo zimene ndinapatsidwa.”
8 Monga momwe nkhani ya Chad ikusonyezera, abusa ozindikira bwino amayambiratu kuphunzitsa abale oti angadzakhale atumiki othandiza ndi akulu, anthuwo asanakwanitse n’komwe zinthu zonse zowayenereza kusamalira maudindo amenewa. N’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika? Chifukwa choti Baibulo limalamula kuti atumiki othandiza ndi akulu omwe afunika kukhala ndi khalidwe ndiponso moyo wauzimu wabwino kwambiri asanaikidwe kuti atumikire. Iwo amafunika “ayambe ayesedwe.”—1 Timoteo 3:1-10.
9. Kodi abusa okhwima mwauzimu ali ndi udindo wotani, ndipo n’chifukwa chiyani?
9 Poti abale obatizidwa amafunika kuyesedwa, n’koyenera kuti ayambe aphunzitsidwa kaye. Mwachitsanzo: Ngati mwana wa sukulu wauzidwa kulemba mayeso ovuta a zinthu zimene aphunzitsi ake sanam’phunzitsepo, kodi angakhoze mayesowo? N’zoonekeratu kuti sangakhoze. Chotero, maphunziro ndi ofunika. Koma aphunzitsi akhama saphunzitsa ana asukulu kuti adzangokhoza mayeso koma kuti adzathenso kugwiritsa ntchito zimene akuphunzirazo. Mofananamo, akulu akhama amathandiza abale obatizidwa kukhala ndi makhalidwe amene amafunika kwa mwamuna woikidwa mwa kuwaphunzitsa zinthu zinazake. Iwo amachita zimenezi osati chabe kuti athandize abalewa kuikidwa pautumiki komanso kuti awathandize kuti adzathe kusamalira bwino nkhosa. 2 Timoteo 2:2) N’zoona kuti abale obatizidwa amafunika kuchita mbali yawo ndiponso kuyesetsa mwakhama kukwaniritsa zowayenereza kukhala atumiki othandiza kapena akulu. (Tito 1:5-9) Koma, pokhala ofunitsitsa kuphunzitsa abale amene akukalamira udindo mu mpingo, abusa odziwa ntchito angathandize abalewa kuti athe kukwaniritsa mwamsanga zofunika.
(10, 11. Kodi abusa angaphunzitse bwanji ena kuti akhale ndi maudindo enanso?
10 Kodi abusa odziwa ntchito angaphunzitse motani kwenikweni anthu ena kusamalira ntchito za mpingo? Choyamba, abusa ayenera kuchita chidwi ndi abale mu mpingo, kugwira nawo ntchito ya utumiki wa kumunda nthawi zonse ndiponso kuwathandiza kukhala aluso kwambiri ‘polunjika nawo bwino mawu a choonadi.’ (2 Timoteo 2:15) Abusa okhwima mwauzimu amakambirana ndi abale amenewa madalitso amene angapeze chifukwa chotumikira ena ndiponso chimwemwe chimene iwo amakhala nacho chifukwa chokhala ndi zolinga zauzimu komanso kuzikwaniritsa. Iwo amaperekanso mokoma mtima malingaliro ofotokoza mmene mbale angachitire bwino kuti akhale ‘chitsanzo kwa gulu’ la nkhosa.—1 Petro 5:3, 5.
11 Mbale akaikidwa kukhala mtumiki wothandiza, abusa anzeru amapitiriza kumuphunzitsa. Bruce yemwe watumikira monga mkulu kwa zaka pafupifupi 50, anati: “Ndimakonda kucheza ndi yemwe waikidwa kumene kukhala mtumiki wothandiza ndipo ndimakambirana naye malangizo ofalitsidwa ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Timawerenganso malangizo aliwonse okhudza ntchito imene wapatsidwa, ndiyeno ndimakonda kugwira naye ntchitoyo kufikira ataidziwa bwino.” Mtumiki wothandiza akayamba kudziwa zinthu zambiri, angaphunzitsidwenso ntchito yoweta. Bruce akupitiriza kufotokoza kuti: “Ndikamapita ndi mtumiki wothandiza paulendo waubusa, ndimamuthandiza kusankha malemba amene angalimbikitse munthu kapena banja limene tikacheze nalo. Kudziwa kugwiritsa ntchito Malemba mogwira mtima chonchi n’kofunika kuti mtumiki wothandiza adzakhale mbusa wabwino.”—Ahebri 4:12; 5:14.
12. Kodi abusa odziwa ntchito angaphunzitse bwanji akulu omwe aikidwa kumene?
12 Abusa oikidwa kumene nawonso angapindule kwambiri pophunzitsidwa zina ndi zina. Nick, yemwe tam’tchula kale uja, anati: “Zimene oyang’anira awiri achikulire anandiphunzitsa zinandithandiza kwambiri. Nthawi zambiri abale amenewa ankadziwa mmene tiyenera kusamalira nkhani zina. Iwo nthawi zonse ankamvetsera malingaliro anga moleza mtima ndipo ankawaona kukhala ofunika ngakhale pamene sanali kugwirizana nawo. Ndinaphunzira zambiri mwa kuona mmene ankachitira zinthu modzichepetsa ndiponso mwaulemu kwa abale ndi alongo mu mpingo. Akulu amenewa anandithandiza kwambiri kuona kufunika kogwiritsa ntchito Baibulo mwaluso pothetsa mavuto kapena polimbikitsa ena.”
Kuphunzitsidwa ndi Mawu a Mulungu
13. (a) Kodi mbale amafunika chiyani kuti akhale mbusa wabwino? (b) N’chifukwa chiyani Yesu anati: “Chiphunzitso changa sichili changa”?
13 Ndithudi, Mawu a Mulungu, Baibulo, ali ndi malamulo, mfundo za chikhalidwe, ndi zitsanzo zimene mbusa amafunikira kuti akhale “woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.” (2 Timoteo 3:16, 17) Ngakhale mbale atakhala wophunzira bwino, koma chimene chingamuthandize kukhala mbusa wabwino ndicho kudziwa ndiponso kugwiritsa ntchito bwino Malemba. Taganizirani chitsanzo cha Yesu. Iye anali munthu wodziwa zinthu koposa, wozindikira koposa ndiponso mbusa wauzimu wanzeru kuposa aliyense amene anakhalako padziko lapansi. Koma ngakhale ndi choncho, sanadalire nzeru zake zokha pophunzitsa nkhosa za Yehova. Iye anati: “Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine.” Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anatamanda Atate wake wa kumwamba? Iye anafotokoza kuti: “Iye wolankhula zochokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha.”—Yohane 7:16, 18.
14. Kodi abusa amapewa bwanji kufuna ulemu wa iwo eni?
14 Abusa okhulupirika amapewa kufuna ulemu wa iwo eni. Uphungu ndi chilimbikitso chimene amapatsa ena zimachokera m’Mawu a Mulungu, osati mu nzeru zawo. Iwo amadziwa kuti ntchito ya mbusa ndiyo kuthandiza nkhosa kukhala ndi “mtima wa Kristu” osati maganizo a akulu. (1 Akorinto 2:14-16) Mwachitsanzo, bwanji ngati mkulu yemwe akuthandiza banja lina kuthana ndi mavuto aukwati akupereka uphungu malinga ndi zimene wakumana nazo pamoyo wake m’malo mogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo ndiponso malangizo a m’mabuku a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”? (Mateyu 24:45) N’kutheka kuti wapereka uphungu wakewo chifukwa chotengera miyambo ya m’dera limene akukhala ndiponso zimene iyeyo akudziwa. N’zoona kuti miyambo ina si yoipa, ndipo n’kutheka kuti mkuluyo angadziwe zinthu zina pamoyo. Koma nkhosa zimapindula kwambiri ngati abusa azilimbikitsa kumvetsera mawu a Yesu ndiponso zonena za Yehova m’malo momvetsera maganizo a anthu kapena mfundo za miyambo ya m’deralo.—Salmo 12:6; Miyambo 3:5, 6.
Kuphunzitsidwa ndi “Kapolo Wokhulupirika ndi Wanzeru”
15. Kodi ndi ntchito yotani imene Yesu anapatsa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” ndipo chifukwa chimodzi chimene chathandiza kuti gulu la kapolo lichite bwino pantchitoyi n’chotani?
15 Abusa monga mtumwi Petro, Yohane, ndi Paulo onse anali a gulu lomwe Yesu anatcha kuti “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Gulu la kapolo limeneli lapangidwa ndi abale a Yesu odzozedwa ndi mzimu omwe ali padziko lapansi pano, ndipo akuyembekezera kudzalamulira limodzi ndi Kristu m’mwamba. (Chivumbulutso 5:9, 10) M’masiku ano otsiriza a dongosolo lino, chiwerengero cha abale a Kristu omwe atsala padziko lapansi chatsika, monga momwe ziyenera kukhalira. Koma ntchito imene Yesu anawauza kuti achite, yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu mapeto asanafike, tsopano yafika m’madera ambiri kuposa kale lonse. Ngakhale zili choncho, gulu la kapolo lakhala likuchita bwino kwambiri pantchitoyi. Chifukwa chiyani? Chifukwa chimodzi n’choti laphunzitsa a “nkhosa zina” kuti alithandize pantchito yolalikira ndi kuphunzitsa. (Yohane 10:16; Mateyu 24:14; 25:40) Masiku ano, ntchito yaikulu ikuchitidwa ndi gulu lokhulupirika la nkhosa zina limeneli.
16. Kodi gulu la kapolo limaphunzitsa bwanji amuna oikidwa?
1 Akorinto 4:17) N’chimodzimodzinso masiku ano. Bungwe Lolamulira, gulu laling’ono la akulu odzozedwa amene amaimira gulu la kapolo, limapatsa mphamvu anthu amene akuliimira kuti aziphunzitsa ndi kuika atumiki othandiza ndi akulu m’mipingo miyandamiyanda padziko lonse lapansi. Kuwonjezera apo, Bungwe Lolamulira limakonza masukulu ophunzitsa abale a m’Komiti ya Nthambi, oyang’anira oyendayenda, akulu, ndi atumiki othandiza za mmene angasamalire bwino nkhosa. Malangizo ena amaperekedwa kudzera m’makalata, m’nkhani zofalitsidwa mu Nsanja ya Olonda, ndiponso m’mabuku ena, monga buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova. *
16 Kodi gulu la kapolo limaphunzitsa bwanji? M’nthawi ya atumwi, oimira gulu la kapolo anapatsidwa mphamvu yoti aziphunzitsa ndi kuika oyang’anira m’mipingo. Ndipo oyang’anira nawonso ankaphunzitsa anthu mu mpingo. (17. (a) Kodi Yesu wasonyeza bwanji kuti amakhulupirira gulu la kapolo? (b) Kodi abusa auzimu angasonyeze bwanji kuti amakhulupirira gulu la kapolo?
17 Yesu anakhulupirira kwambiri gulu la kapololi moti analiika kuyang’anira “zinthu zake zonse,” kutanthauza zinthu zake zonse zauzimu padziko lapansi. (Mateyu 24:47) Abusa oikidwa nawonso amasonyeza kuti amakhulupirira gulu la kapolo mwa kugwiritsa ntchito malangizo omwe amalandira kuchokera ku Bungwe Lolamulira loimira kapoloyu. N’zoonadi, abusa akamaphunzitsa ena, akakhala ndi mtima wofuna kuphunzitsidwa ndi Mawu a Mulungu, ndiponso akamagwiritsa ntchito zimene aphunzitsidwa ndi gulu la kapolo, amalimbikitsa kugwirizana pakati pa nkhosa. Ndife oyamikira kwambiri kuti Yehova waphunzitsa amuna amene amasamalira kwambiri munthu aliyense mu mpingo wachikristu.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 16 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi abusa okhwima mwauzimu amaphunzitsa bwanji ena?
• Kodi n’chifukwa chiyani abusa sagwiritsa ntchito maganizo awo akamaphunzitsa?
• Kodi abusa amasonyeza bwanji kuti amakhulupirira gulu la kapolo, ndipo n’chifukwa chiyani amatero?
[Mafunso]
[Zithunzi pamasamba 24, 25]
Akulu achikristu amaphunzitsa achinyamata mu mpingo
[Zithunzi patsamba 26]
“Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amaphunzitsa akulu zinthu zambiri