Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Ali Nalo Cholinga Chotani Dziko Lapansili?

Kodi Mulungu Ali Nalo Cholinga Chotani Dziko Lapansili?

Kodi Mulungu Ali Nalo Cholinga Chotani Dziko Lapansili?

N’CHIFUKWA chiyani mumasangalala kuyenda mu paki kapena kudutsa m’munda wa maluwa onunkhira bwino, pamene mukuwongola miyendo? Kodi n’chifukwa chiyani mumamva bwino mumtima mukaona nyanja yokongola kapena mapiri akuluakulu, nsonga zawo zitabisika m’mitambo? N’chifukwa chiyani nthawi zina mumaima kuti mumvetsere mbalame zikuimba mosangalala m’mitengo? Ndipo n’chifukwa chiyani mumasangalala kwambiri kuona insa ikuthamangathamanga kapena nkhosa zikudya m’madambo?

Pali yankho limodzi la mafunso onsewa. Tinalengedwa kuti tikhale m’Paradaiso! Poyamba, makolo athu oyambirira, omwe ndi Adamu ndi Hava, ankakhala m’malo oterowo. Makolo athuwa ndi amene anatipatsira chikhumbo chokhala m’Paradaiso, ndipo Mlengi wawo, Yehova Mulungu, ndiye anawapatsa chikhumbo chimenechi. Iye anadziwa kuti anthufe tingasangalale kukhala m’Paradaiso chifukwa anatilenga ndi makhalidwe ofunika kuti tisangalale ndi malo oterowo padziko lapansi lokongola.

Kodi Yehova analengeranji dziko lapansili? “Analiumba [kuti] akhalemo anthu.” (Yesaya 45:18) ‘Mlengi wa dziko lapansi’ anapatsa Adamu ndi Hava paradaiso wokongola woti akhalemo, munda wa Edene. (Yeremiya 10:12; Genesis 2:7-9, 15, 21, 22) Ayenera kuti anasangalala kwambiri ndi mitsinje, maluwa ndi mitengo ya m’munda umenewu. Kumwamba ankatha kuona mbalame zokongola, nyama zamitundumitundu zinali lakalaka padziko, ndipo panalibe iliyonse yowopseza anthu. M’madzi oyera bwino a dziko lapansili munali nsomba ndiponso zamoyo zina. Ndipo chosangalatsa kwambiri chinali chakuti Adamu ndi Hava anali kukhalira limodzi. Akanatha kubereka ana ndi kukulitsa Paradaiso yemwe anali kukhalamo, ndipo akanachita ntchito yosangalatsayi limodzi ndi banja lawo lomwe likanakula.

Ngakhale kuti dzikoli si paradaiso panopa, tingathe kuliyerekezera ndi nyumba yabwino ya banja losangalala. Dziko lapansili, lomwe Mulungu anatipatsa kuti tikhalemo, lili ndi zinthu zofunika pamoyo wathu​—kuwala, kutentha, madzi, ndi chakudya. Timasangalala kwambiri ndi kuwala ndiponso kutentha kwa dzuwa komanso kuwala kwa mwezi. (Genesis 1:14-18) M’kati mwa dzikoli muli zinthu monga malasha ndi mafuta, zomwe tingathe kugwiritsa ntchito kutenthetsera zinthu. Tili ndi madzi chifukwa cha kusintha kwa madzi kuchoka padziko pano n’kukapanga mitambo ndi kudzagwa monga mvula, ndiponso chifukwa cha mitsinje, nyanja zikuluzikulu ndi zing’onozing’ono, zomwe zili padzikoli. Ndiponso dziko lapansili lili ndi udzu wobiriwira wambiri.

Mofanana ndi mmene anthu amasungira chakudya m’nyumba, dziko lili ndi chakudya chochuluka kwambiri. Yehova ‘amatipatsa nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yathu ndi chikondwero’ chifukwa cha mbewu za kuminda ndiponso mitengo ya zipatso. (Machitidwe 14:16, 17) Popeza kuti dzikoli ndi malo abwino kukhalamo, ndiye taganizirani mmene zinthu zidzakhalire “Mulungu wolemekezeka [kapena kuti, wachisangalalo],” Yehova, akadzalipanga kukhala paradaiso!​—1 Timoteo 1:11.

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

COVER: Earth: NASA photo; Stars: NASA, ESA and AURA/​Caltech