Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mwakonzekera Kupulumuka?

Kodi Mwakonzekera Kupulumuka?

Kodi Mwakonzekera Kupulumuka?

“Talowani, iwe ndi a ku nyumba ako onse m’chingalawamo; chifukwa ndakuona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m’mbadwo uno.”​—GENESIS 7:1.

1. Kodi Yehova anakonza njira yotani yopulumutsira anthu m’masiku a Nowa?

M’MASIKU a Nowa, Yehova ‘anatengera dziko la osapembedza chigumula,’ koma anakonzanso njira yoti anthu ena apulumukire. (2 Petro 2:5) Mulungu woona anapatsa Nowa, yemwe anali wolungama, malangizo atsatanetsatane omangira chingalawa choti anthu ndi nyama apulumukiremo Chigumula chomwe chinachitika padziko lonse lapansi. (Genesis 6:14-16) Mofanana ndi mtumiki wokhulupirika aliyense wa Yehova, “anachita Nowa, monga mwa zonse anam’lamulira iye Mulungu.” Inde, “momwemo anachita.” Mwa zina, ifeyo tili ndi moyo lerolino chifukwa cha kumvera kwa Nowa.​—Genesis 6:22.

2, 3. (a) Kodi anthu a m’masiku a Nowa anatani ndi ntchito yomwe Nowa anali kuchita? (b) Kodi Nowa analowa m’chingalawa ali ndi chikhulupiriro chotani?

2 Kumanga chingalawa sinali ntchito yamasewera. N’zachidziwikire kuti anthu ambiri ankadabwa ndi ntchito yomwe Nowa ndi banja lake anali kuchita. Komabe, izi zinali zosakwanira kuwatsimikizira anthuwo kuti anafunika kulowa m’chingalawamo kuti apulumuke. Pomalizira pake, Mulungu anasiya kuleza mtima ndi dziko loipa la nthawi imeneyo.​—Genesis 6:3; 1 Petro 3:20.

3 Nowa ndi banja lake atagwira ntchito yovuta kwambiri kwa zaka makumi angapo, Yehova anauza Nowa kuti: “Talowani, iwe ndi a ku nyumba ako onse m’chingalawamo; chifukwa ndakuona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m’mbadwo uno.” Pokhala ndi chikhulupiriro kuti mawu a Yehova achitika, “analowa Nowa ndi ana ake ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake m’chingalawamo.” Yehova anatseka chitseko pofuna kuteteza olambira ake. Chigumula chitabwera padziko lapansi, chingalawa chomwe Mulungu anauza anthu kuti amange, chinali njira yodalirika yopulumutsira anthu ndi nyama.​—Genesis 7:1, 7, 10, 16.

Kufanana kwa Masiku a Nowa ndi Masiku Athu Ano

4, 5. (a) Kodi Yesu anayerekeza nthawi ya kukhalapo kwake ndi chiyani? (b) Kodi pali kufanana kotani pakati pa masiku a Nowa ndi masiku athu ano?

4 “Monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika [“kukhalapo,” NW] kwake kwa Mwana wa munthu.” (Mateyu 24:37) Ndi mawu amenewa, Yesu anasonyeza kuti nthawi ya kukhalapo kwake kosaoneka idzafanana ndi masiku a Nowa, ndipo ndi mmene zachitikiradi. Makamaka kuyambira mu 1919, uthenga wochenjeza anthu wofanana ndi womwe Nowa anapereka wakhala ukulengezedwa kwa athu a mitundu yonse. Zimene anthu ambiri achita atamva uthengawu sizikusiyana ndi zimene anthu a m’masiku a Nowa anachita.

5 Ndi Chigumula, Yehova anawononga dziko lomwe ‘linadzala ndi chiwawa.’ (Genesis 6:13) Kwa onse omwe ankawaona, zinali zosachita kufunsa kuti Nowa ndi banja lake sankachita nawo ziwawa zimenezi, koma ankagwira mwamtendere ntchito yomanga chingalawa. Apa tikuonanso kufanana kwina ndi masiku athu ano. Tsopano anthu a maganizo abwino akutha “kuzindikira [kusiyana] pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosam’tumikira.” (Malaki 3:18) Anthu opanda tsankho amayamikira kuona mtima, kukoma mtima, kukonda mtendere, ndiponso khama la Mboni za Yehova ndipo makhalidwe amenewa amasiyanitsa anthu a Mulungu ndi dzikoli. Mboni zimakana ziwawa za mtundu uliwonse ndipo zimatsogoleredwa ndi mzimu wa Yehova. N’chifukwa chake zili pamtendere ndiponso zimakonda chilungamo.​—Yesaya 60:17.

6, 7. (a) Kodi anthu a m’masiku a Nowa analephera kuzindikira chiyani, ndipo zikufanana motani ndi masiku ano? (b) Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zikusonyeza kuti anthu ambiri amaona kuti Mboni za Yehova ndi zosiyana ndi anthu ena?

6 Anthu a m’masiku a Nowa sanazindikire kuti Nowa anali kuthandizidwa ndi Mulungu ndiponso kuti anali kuchita zimene Mulunguyo anamuuza. Motero sanaone kufunika kwa ntchito yake yolalikira ndiponso kumvera uthenga wake wowachenjeza. Nanga bwanji masiku ano? Ngakhale kuti anthu ambiri amachita chidwi ndi zochita ndiponso khalidwe la Mboni za Yehova, ambiri salabadira uthenga wabwino ndiponso machenjezo a m’Baibulo. Anthu oyandikana nawo nyumba, mabwana, kapena achibale awo angathe kuyamikira kwambiri makhalidwe abwino a Akristu oona, koma angamanene kuti, “Koma kungoti ndi Mboni za Yehova.” Chimene anthuwa amanyalanyaza n’chakuti Mboni ndi anthu achikondi, amtendere, achifundo, okoma mtima, ofatsa, ndiponso odziletsa chifukwa chakuti zimatsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. (Agalatiya 5:22-25) Makhalidwe amenewa ayenera kuthandiza anthu kukhulupirira mosavuta uthenga wawo.

7 Mwachitsanzo, m’dziko la Russia Mboni za Yehova zinali kumanga Nyumba ya Ufumu. Bambo wina amene anaima n’cholinga cholankhula ndi mmodzi wa anthu ogwira ntchito pamalowo, anati: “Sindinaonepo zinthu ngati zimene zikuchitika panozi! Palibe kusuta fodya, kulankhula mawu achipongwe, ndipo palibe woledzera ngakhale mmodzi! Kodi mungakhale Mboni za Yehova anthu inu?” Mmodzi wa ogwira ntchitowo anafunsa bamboyo kuti, “Kodi mukhulupirira ndikanena kuti siine wa Mboni?” Mwamsangamsanga bamboyo anayankha kuti, “Sindingakhulupirire kuti siinu Amboni.” Mumzinda wina wa ku Russia komweko, meya wa mzindawo anachita chidwi kwambiri ataona Mboni zikumanga Nyumba ya Ufumu yawo yatsopano. Iye ananena kuti ngakhale kuti poyamba ankaona kuti zipembedzo zonse ndi zofanana, maganizo amenewo anatha ataona kusadzikonda kwa Mboni za Yehova. Izi ndi zitsanzo ziwiri zokha za mmene anthu a Yehova alili osiyana ndi anthu amene satsatira mfundo za Baibulo.

8. Kodi kuti tipulumuke mapeto a dziko loipali zikudalira chiyani?

8 M’nthawi ya mapeto a “dziko lapansi lakale” lomwe linawonongedwa pa Chigumula, Nowa anali “mlaliki [wokhulupirika] wa chilungamo.” (2 Petro 2:5) M’masiku omaliza ano a dongosolo ili za zinthu, anthu a Yehova akulengeza miyezo yolungama ya Mulungu ndiponso akulengeza uthenga wabwino wonena za mwayi womwe ulipo wopulumuka n’kulowa m’dziko latsopano. (2 Petro 3:9-13) Nowa ndi banja lake loopa Mulungu anapulumukira m’chingalawa, nakonso kupulumuka kwa anthu a masiku ano kukudalira chikhulupiriro ndiponso kugwirizana kwambiri ndi mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova la m’chilengedwe chonse.

Chikhulupiriro N’chofunika Kuti Munthu Apulumuke

9, 10. N’chifukwa chiyani chikhulupiriro chili chofunika kuti tipulumuke mapeto a dongosolo la zinthu la Satanali?

9 Kodi munthu ayenera kuchita chiyani kuti apulumuke chiwonongeko chomwe chayandikira cha dziko lino lomwe lagona mwa Satana? (1 Yohane 5:19) Choyamba akufunika kudziwa kuti tikufunikira kutetezedwa. Kenako ayenera kutsatira njira zotitetezerazo. Anthu a m’masiku a Nowa anapitiriza kugwira ntchito zawo monga mwa nthawi zonse ndipo sanaone kufunika kotetezedwa pa vuto lomwe linali litayandikira. Analibe chikhulupiriro mwa Mulungu.

10 Koma Nowa ndi banja lake anaona kufunika kotetezedwa ndi kupulumutsidwa. Komanso anali ndi chikhulupiriro mwa Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, Yehova Mulungu. “Wopanda chikhulupiriro sikutheka kum’kondweretsa [Yehova],” analemba motero mtumwi Paulo, “pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.” Paulo anapitiriza motere: “Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m’nyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chili monga mwa chikhulupiriro.”​—Ahebri 11:6, 7.

11. Kodi tingaphunzire chiyani tikaona mmene Yehova anatetezera anthu m’nthawi zakale?

11 Kuti tipulumuke mapeto a dongosolo lino la zinthu, tikufunika kuchita zambiri osati kungokhulupirira chabe kuti dongosololi liwonongedwa ayi. Tikufunika kukhulupirira njira imene Mulungu wakonza pofuna kutipulumutsa ndipo tisonyeze chikhulupiriro chathucho mwa kuitsatira mosamala. N’zoona kuti tiyenera kukhulupirira nsembe ya dipo ya Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu. (Yohane 3:16, 36) Komabe, ndi bwino kumakumbukira kuti anthu okhawo omwe anali m’chingalawa cha Nowa ndiwo anapulumuka Chigumula. N’chimodzimodzinso ndi midzi yopulumukira ya ku Israyeli wakale. Munthu wopha mnzake mwangozi ankapulumuka akathawira m’midzi imeneyi ndi kukhalamo mpaka imfa ya mkulu wa ansembe. (Numeri 35:11-32) Pa mliri wakhumi ku Igupto m’masiku a Mose, ana oyamba kubadwa a Aigupto anaphedwa, koma ana a Aisrayeli anapulumuka. Chifukwa chiyani? Yehova analangiza Mose kuti: “[Aisrayeli] azitengako mwazi [wa mwana wankhosa wa Paskha], naupake pa mphuthu za mbali ndi ya pamwamba m’nyumba zimene adyeramo. . . . Koma inu, asatuluke munthu pakhomo pa nyumba yake kufikira m’mawa.” (Eksodo 12:7, 22) Kodi ndi mwana woyamba uti wa Aisrayeli amene akanayesa dala kunyalanyaza malangizo omwe Mulungu anawapatsa, n’kutuluka m’nyumba yomwe inali ndi chizindikiro cha mwazi wopakidwa pa mphuthu ziwiri za nyumba ndi pamwamba pa khomo?

12. Kodi aliyense wa ife ayenera kudzifunsa funso lotani, ndipo n’chifukwa chiyani?

12 Motero m’pomveka kuganizira mofatsa mmene zinthu zilili kwa ifeyo patokha. Kodi tili m’kati mwa makonzedwe a Yehova otipulumutsira mwauzimu? Chisautso chachikulu chikadzayamba, anthu amene akutsatira makonzedwe amenewa opulumutsira anthu adzasangalala kwambiri. Koma ena, adzalira chifukwa cha chisoni ndiponso chifukwa chonong’oneza bondo.

Kusintha Zinthu Mwapang’onopang’ono Kumatikonzekeretsa Kupulumuka

13. (a) Kodi kusintha zinthu m’gulu la Yehova kwathandiza motani? (b) Fotokozani zina mwa zinthu zomwe zasintha mwapang’onopang’ono.

13 Yehova wakhala akusintha zinthu mwapang’onopang’ono m’mbali ya padziko lapansi ya gulu lake. Izi zathandiza kukongoletsa, ndiponso kulimbikitsa makonzedwe ake otipulumutsira mwauzimu komanso zathandiza kuti makonzedwewa akhale okhazikika. Kuchokera m’zaka za m’ma 1870 mpaka mu 1932, akulu ndi madikoni ankasankhidwa ndi mpingo mwa kuchita voti. Mu 1932 akulu osankhidwa mwa voti aja analowedwa m’malo ndi komiti ya utumiki yomwe mpingo unkasankha mwa kuchita voti ndipo cholinga chake chinali choti ithandize wotsogolera utumiki amene ankachita kuikidwa mu mpingo. Mu 1938 anakonza zoti atumiki onse mu mpingo azichita kuikidwa mogwirizana ndi mfundo za m’Malemba. Motsogoleredwa ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, kuyambira mu 1972, anthu akhala akuikidwa mogwirizana ndi ziyeneretso za m’Malemba ndipo mipingo imalandira kalata zoika oyang’anira ndi atumiki othandiza. Pazaka zonse zapitazi, ntchito za Bungwe Lolamulira zawonjezeka ndipo zina ndi zina zasinthidwa n’cholinga choti ntchito za bungweli ziziyenda bwino.

14. Kodi ndi sukulu yotani yomwe inayamba mu 1959?

14 Mu 1950, kuganizira mofatsa lemba la Salmo 45:16 kunasonyeza kuti m’pofunika kukhala ndi dongosolo lophunzitsira anthu mosalekeza. Lembali limati: “M’malo mwa makolo ako mudzakhala ana ako, udzawaika akhale mafumu m’dziko lonse lapansi.” Akulu omwe panopa akutsogolera m’mipingo akulandira maphunziro owathandiza pantchito zauzimu panopa komanso pambuyo pa Armagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Sukulu ya Utumiki wa Ufumu inayamba mu 1959. Nthawi imeneyo, maphunziro ake, omwe ankakhala a mwezi umodzi, anali kwenikweni a atumiki a mipingo, dzina la oyang’anira otsogolera panthawiyo. Panopo sukuluyi inasintha n’cholinga choti izithandiza oyang’anira onse ndiponso atumiki othandiza. Pambuyo pake, abale amenewa amakaphunzitsa Mboni za Yehova m’mipingo mwawo. Motero, anthu onse amalandira chithandizo mwauzimu ndiponso amathandizidwa kuti akhale ogwira mtima kwambiri mu utumiki monga olengeza uthenga wabwino wa Ufumu.​—Marko 13:10.

15. Kodi ndi njira ziwiri ziti zimene zimathandiza kuti mpingo wachikristu ukhale woyera?

15 Anthu ofuna kukhala mumpingo wachikristu amakhala ndi zinthu zofunika kuzikwaniritsa. M’pomveka kuti anthu onyoza masiku ano saloledwa kulowa mpingo wachikristu, ngati mmene zinalili kale pamene anthu otere sanaloledwe kulowa m’chingalawa cha Nowa. (2 Petro 3:3-7) Makamaka kuchokera mu 1952, Mboni za Yehova zalimbikitsa makonzedwe othandiza kuteteza mpingo, omwe ndi ochotsa ochimwa osalapa. Ndi zoona kuti anthu ochimwa amene alapa moona mtima amathandizidwa mwachikondi ‘kulambula misewu yolunjika yoyendamo mapazi awo.’​—Ahebri 12:12, 13; Miyambo 28:13; Agalatiya 6:1.

16. Kodi zinthu zili bwanji ndi anthu a Yehova pankhani yauzimu?

16 Sizodabwitsa kuti zinthu zikuwayendera bwino mwauzimu anthu a Yehova komanso sikuti ndi zongochitika mwangozi ayi. Kudzera mwa mneneri Yesaya, Yehova anati: “Taonani atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala; taonani, atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu; taonani, atumiki anga adzasangalala, koma inu mudzakhala ndi manyazi, taonani, atumiki anga adzaimba ndi mtima wosangalala, koma inu mudzalira ndi mtima wachisoni; ndipo mudzafuula chifukwa cha kusweka mzimu.” (Yesaya 65:13, 14) Yehova akupitiriza kutipatsa chakudya chauzimu chochuluka, chomwe ndi chapanthawi yake ndiponso chopatsa thanzi, ndipo chimatithandiza kukhala olimba mwauzimu.​—Mateyu 24:45.

Konzekerani Kupulumuka

17. Kodi n’chiyani chingatithandize kukonzekera kupulumuka?

17 Tsopano, mosiyana ndi m’mbuyo monsemu, ndi nthawi ‘yoganizirana wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, koma kudandaulirana.’ (Ahebri 10:23-25) Kuyanjana kwambiri ndi umodzi mwa mipingo yoposa 98,000 ya Mboni za Yehova komanso kukhala achangu mu mpingowo kungatithandize kukonzekera kupulumuka. Pamene tikuyesetsa kusonyeza “munthu watsopano” ndiponso kukhala akhama kwambiri kuthandiza ena kuti adziwe zimene Yehova wakonza pofuna kutipulumutsa, okhulupirira anzathu adzatithandiza.​—Aefeso 4:22-24; Akolose 3:9, 10; 1 Timoteo 4:16.

18. N’chifukwa chiyani mukufunitsitsa kuyanjana kwambiri ndi mpingo wachikristu?

18 Satana ndi dziko lake loipali akufunitsitsa kutikopa kuti tichoke mu mpingo wachikristu. Koma n’zotheka kuti tipitirize kukhala mu mpingowu ndi kupulumuka mapeto a dongosolo loipali la zinthu. Kukonda Yehova ndiponso kuyamikira zimene wakonza kuti zitithandize kupulumuka zitilimbikitse kukhala ndi mtima wofunitsitsa kulepheretsa zochita za Satana. Kuganizira madalitso omwe tili nawo panopa kungatithandize kuchita zimenezi. M’nkhani yotsatirayi tikambirana ena mwa madalitsowo.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi masiku athu ano akufanana motani ndi masiku a Nowa?

• Kuti munthu apulumuke akufunika kukhala ndi khalidwe liti?

• Kodi ndi kusintha mwapang’onopang’ono kotani komwe kwalimbitsa makonzedwe a Yehova otitetezera?

• Kodi tingakonzekere motani kupulumuka?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 22]

Anthu a m’masiku a Nowa sanalabadire zonena zake

[Chithunzi patsamba 23]

Kulabadira uthenga wochenjeza wa Mulungu n’kopindulitsa

[Chithunzi patsamba 24]

Kodi cholinga cha Sukulu ya Utumiki wa Ufumu n’chiyani?

[Chithunzi patsamba 25]

Ino ndi nthawi yoyanjana kwambiri ndi mpingo wachikristu