Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi n’chiyani chikuchititsa kuti “zofunika za amitundu onse” zifike ‘m’nyumba’ ya kulambira koona?​—Hagai 2:7.

Kudzera mwa mneneri Hagai, Yehova analosera kuti: “Ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero.” (Hagai 2:7) Kodi kugwedeza “amitundu onse” ndiko kukuchititsa kuti “zofunika” za amitundu, kutanthauza anthu oona mtima, ziyambe kulambira koona? Yankho n’lakuti ayi.

Taonani chimene chikugwedeza amitundu, kapena kuwanjenjemeretsa ndiponso zomwe zikuchitika chifukwa cha kunjenjemeraku. Baibulo limanena kuti ‘amitundu akuphokosera, ndipo anthu akulingalira zopanda pake.’ (Salmo 2:1) “Zopanda pake” zimene ‘akulingalirazi’ n’zofuna kupitiriza ulamuliro wawo. Palibenso chinthu china chimene amanjenjemera nacho kwambiri kuposa chilichonse chimene chingaopseze ulamuliro wawo.

Ntchito imene Mboni za Yehova zikuchita padziko lonse, yolalikira za Ufumu wa Mulungu womwe unakhazikitsidwa ndiyo ikuopseza amitundu. Ndipotu, Ufumu wa Mulungu womwe Yesu Kristu ndiye wolamulira wake “udzaphwanya ndi kutha maufumu . . . onse [opangidwa ndi anthu].” (Danieli 2:44) Amitundu akunjenjemera ndi uthenga wachiweruzo womwe ndi mbali ya ntchito yathu yolalikira. (Yesaya 61:2) Kunjenjemeraku kukuwonjezeka pamene ntchito yolalikirayi ikumka nifalikira m’madera ambiri ndiponso ikugwiridwa mwamphamvu kwambiri. Kodi kugwedeza koloseredwa pa Hagai 2:7 ndi chizindikiro cha chiyani?

Pa Hagai 2:6, timawerenga kuti: “Atero Yehova wa makamu: Kamodzinso, katsala kanthawi, ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi mtunda womwe.” Pogwira mawu vesi limeneli, mtumwi Paulo analemba kuti: “Adalonjeza, ndi kuti, Kamodzinso ndidzagwedeza, si dziko lokha, komanso m’mwamba. Ndipo ichi, chakuti kamodzinso, chilozera kusuntha kwake kwa zinthu zogwedezeka, monga kwa zinthu zolengedwa, kuti zinthu zosagwedezeka [Ufumu] zikhale.” (Ahebri 12:26, 27) Zoonadi, dongosolo lonse la zinthu limene lilipoli lidzawonongedwa kuti papezeke malo a dziko latsopano lopangidwa ndi Mulungu.

Anthu oona mtima akukopeka ndi kulambira koona koma osati chifukwa chakuti amitundu akugwedezedwa, kapena kunjenjemeretsedwa ayi. Chimene chikuwakokera kwa Yehova ndiponso kuti ayambe kumulambira ndi chimenenso chikuchititsa kuti amitundu agwedezeke, chomwe ndi kulalikira padziko lonse za Ufumu wa Mulungu womwe unakhazikitsidwa. Kulengezedwa kwa “Uthenga Wabwino wosatha” kukukoka anthu a mtima wofuna choonadi kuti ayambe kulambira Mulungu woona.​—Chivumbulutso 14:6, 7.

Uthenga wa Ufumu ndi uthenga wachiweruzo ndiponso chipulumutso. (Yesaya 61:1, 2) Kulalikira uthengawu padziko lonse kukugwedeza amitundu ndiponso kukubweretsa zofunika za amitundu zimene zikubweretsa ulemerero kwa Yehova.