Mfundo Zazikulu za Chigawo Choyamba cha Masalmo
Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za Chigawo Choyamba cha Masalmo
KODI ndi mutu uti umene ungayenerere buku la m’Baibulo lodzaza ndi mawu otamanda Mlengi wathu, Yehova Mulungu? Palibenso mutu wina womwe ungaliyenerere kwambiri kuposa wakuti Masalmo, kapena kuti Zitamando. Buku lalitali limeneli la m’Baibulo lili ndi nyimbo zolembedwa bwino zofotokoza za makhalidwe abwino a Mulungu ndi ntchito zake zamphamvu ndiponso maulosi ambirimbiri. Zambiri mwa nyimbo zake zili ndi maganizo amene olemba nyimbozo anali nawo ali m’mavuto. Mawu opezeka m’bukuli analembedwa m’nyengo ya zaka pafupifupi 1,000, kuchokera m’masiku a mneneri Mose mpaka pambuyo pa ukapolo. Olemba bukuli anali Mose, Mfumu Davide, ndi anthu ena. Akuti Ezara ndiye amene anagawa bukuli kuti likhale mmene lilili panopa.
Kuyambira kale kwambiri, buku la Masalmo linagawidwa m’zigawo zisanu za nyimbo: (1) Masalmo 1 mpaka 41, (2) Masalmo 42 mpaka 72, (3) Masalmo 73 mpaka 89, (4) Masalmo 90 mpaka 106, ndi (5) Masalmo 107 mpaka 150. Nkhani ino ili ndi mfundo za m’chigawo choyamba. M’chigawo chimenechi, masalmo ena onse kusiyapo atatu okha analembedwa ndi Mfumu Davide, ya Israyeli wakale. Amene analemba Salmo 1, 10, ndi 33 sakudziwika.
“MULUNGU WANGA, NGAKA YANGA”
Salmo loyamba litafotokoza kuti wodala ndi munthu amene amakondwera ndi chilamulo cha Yehova, salmo lachiwiri likufotokoza nkhani yokudza Ufumu. * Mawu ambiri m’chigawo cha masalmo chimenechi ndi mapempho opita kwa Mulungu. Mwachitsanzo, m’Masalmo 3 mpaka 5, 7, 12, 13, ndi 17 akupempha kupulumutsidwa kwa adani. Salmo 8 limafotokoza za ukulu wa Yehova pomusiyanitsa ndi munthu.
Pofotokoza za Yehova kuti ndi Mtetezi wa anthu ake, Davide anaimba kuti: “Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye.” (Salmo 18:2) M’Salmo 19 Yehova akutamandidwa kuti ndiye Mlengi ndi Wopereka Malamulo, m’Salmo 20 akutchedwa Mpulumutsi, ndipo m’Salmo 21 akutchedwa Mpulumutsi wa Mfumu yake yodzozedwa. Salmo 23 likufotokoza kuti Yehova ndi Mbusa Wamkulu, pamene Salmo 24 likusonyeza kuti iye ndi Mfumu yaulemerero.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
2:1, 2—Kodi ndi “zopanda pake” zotani zimene amitundu akulingalira? “Zopanda pake” zimenezi ndi nkhawa zomwe maboma a anthu amakhala nazo nthawi zonse zofuna kuti ulamuliro wawo upitirire. Izi ndi zopanda pake chifukwa chakuti cholinga chawo chidzalephereka. Kodi magulu a amitundu angayembekezeredi kuti adzapambana ‘potsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake’?
2:7—Kodi “chitsimikizo [cha] Yehova” n’chiyani? Chitsimikizo chimenechi ndi pangano la Ufumu, limene Yehova anapangana ndi Mwana wake wokondedwa, Yesu Kristu.—Luka 22:28, 29.
2:12—Kodi olamulira a amitundu ‘angapsompsone Mwanayo’ motani? M’nthawi za m’Baibulo kupsompsona kunkasonyeza ubwenzi ndiponso kukhulupirika. Inali njira yolandirira alendo. Mafumu a dziko lapansi akulamulidwa kuti apsompsone Mwanayo, kutanthauza kuti am’landire ndi kuvomereza kuti iye ndi Mfumu ya Umesiya.
3:timawu tapamwamba—Kodi timawu tapamwamba tomwe analemba m’masalmo ena cholinga chake n’chiyani? Timawu timeneti nthawi zina timatchula dzina la mlembi ndi kufotokoza zimene zinali kuchitika panthawi yomwe ankalemba salmo limenelo, monga momwe zilili ndi Salmo 3, kapena kusonyeza chimodzi mwa ziwirizi. Timawuti timathanso kufotokoza cholinga kapena ntchito ya nyimbo inayake (Salmo 4 ndi 5) komanso malangizo a kaimbidwe ka nyimboyo (Salmo 6).
11:3—Kodi ndi maziko otani amene akupasuka? Amenewa ndi maziko amene amanga anthu pamodzi—malamulo, bata, ndi chilungamo. Zimenezi zikasokonekera, pamakhala chisokonezo pakati pa anthu ndipo sipakhala chilungamo. Zikatero, munthu aliyense “wolungama” ayenera kudalira Mulungu ndi mtima wonse.—Salmo 11:4-7.
21:3—Kodi “korona wa golidi woyengetsa” akuimira chiyani? Baibulo silitchula kuti koronayu anali weniweni kapena wophiphiritsa kukongola kwambiri chifukwa chakuti Davide anapambana nkhondo zambiri. Komabe, vesi limeneli likulosera korona waufumu amene Yesu analandira kuchokera kwa Yehova mu 1914. Ponena kuti koronayu ndi wagolide, zikusonyeza kuti ulamuliro wake ndi wapamwamba kwambiri.
22:1, 2—Kodi n’chifukwa chiyani Davide anamva ngati Yehova wamusiya? Davide anali atapanikizika kwambiri ndi adani ake moti ‘mtima wake unanga sera; wosungunuka m’kati mwa matumbo ake.’ (Salmo 22:14) N’kutheka kuti iye ankaona ngati Yehova wamusiya. Yesu atapachikidwa, anamvanso chimodzimodzi. (Mateyu 27:46) Mawu a Davide akusonyeza mmene ankamvera ndi mavuto ake monga munthu. Koma, malinga ndi pemphero lake lomwe lili pa Salmo 22:16-21, n’zoonekeratu kuti Davide sanasiye kukhulupirira Mulungu.
Zimene Tikuphunzirapo:
1:1. Tiyenera kupewa kuyanjana ndi anthu amene sakonda Yehova.—1 Akorinto 15:33.
1:2. Tisalole tsiku kudutsa popanda kuganizira zinthu zauzimu.—Mateyu 4:4.
4:4. Tikakalipa, ndi bwino kusalankhula chilichonse kuti tisanene zinthu zimene tinganong’oneze nazo bondo pambuyo pake.—Aefeso 4:26.
4:5. Nsembe zathu zauzimu zimakhala “nsembe za chilungamo” pokhapokha ngati tili ndi zolinga zabwino ndiponso khalidwe lathu likugwirizana ndi zofuna za Yehova.
6:5. Kodi pangakhalenso chifukwa china chabwino chofuna kukhalira ndi moyo?—Salmo 115:17.
9:12. Yehova amafuna chamwazi, kutanthauza kuti amaona ngati pakhala kukhetsedwa mwazi kuti alange munthu wokhetsa mwaziyo, koma amakumbukira “kulira kwa ozunzika.”
15:2, 3; 24:3-5. Olambira oona ayenera kulankhula choonadi ndi kupewa malumbiro onama ndiponso miseche.
15:4. Pokhapokha ngati tazindikira kuti tapanga lonjezo lotsutsana ndi Malemba, tiyenera kuyesetsa kuchita zimene talonjeza, ngakhale zitakhala zovuta.
15:5. Popeza ndife olambira Yehova, tiyenera kusamala kuti tisagwiritse ntchito ndalama molakwika.
17:14, 15. “Anthu a dziko lapansi pano” amadzipereka kuti akhale pabwino, akhale ndi banja, ndiponso kuti adzasiyire ena cholowa. Nkhawa yaikulu m’moyo wa Davide inali kupanga mbiri yabwino kwa Mulungu n’cholinga ‘chopenyerera nkhope yake,’ kapena kuti kuyanjidwa ndi Yehova. ‘Atauka’ ndi kuona malonjezo a Yehova, Davide ‘anakhuta ndi maonekedwe Ake,’ kapena kuti kusangalala pokhala ndi Yehovayo. Mofanana ndi Davide kodi nafenso sitingaike mtima wathu pa chuma chauzimu?
19:1-6. Ngati chilengedwe, chomwe sichilankhula kapena kuganiza, chimalemekeza Yehova, kuli bwanji ifeyo amene timatha kuganiza, kulankhula, ndi kulambira?—Chivumbulutso 4:11.
19:7-11. Timapindula kwambiri ndi zimene Yehova amafuna.
19:12, 13. Zolakwa ndi kudzitama ndi machimo omwe tiyenera kupewa.
19:14. Tiyenera kusamala ndi zimene timachita komanso zimene timanena ndi kuganiza.
‘MUNDIGWIRIZIZA MU UNGWIRO WANGA’
M’masalmo awiri oyambirira m’gulu limeneli, Davide akufotokoza cholinga cha pansi pa mtima wake chofuna kuyenda mwangwiro. Anaimba kuti: “Koma ine, ndidzayenda m’ungwiro wanga.” (Salmo 26:11) M’pemphero lopempha kukhululukidwa machimo, iye anati: “Pamene ndinakhala chete mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse.” (Salmo 32:3) Davide akutsimikizira anthu okhulupirira Yehova kuti: “Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwawo.”—Salmo 34:15.
Malangizo omwe ali m’Salmo 37 anali ofunika kwambiri kwa Aisrayeli ndipo n’ngofunikanso kwa ifeyo, amene tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ a dongosolo lino za zinthu! (2 Timoteo 3:1-5) Polankhula mwaulosi za Yesu Kristu, Salmo 40:7, 8 limati: “Taonani, ndadza; m’buku mwalembedwa za Ine: Kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali m’kati mwa mtima mwanga.” Salmo lomalizira m’chigawo chimenechi likufotokoza za pempho la Davide loti Yehova am’thandize m’zaka za masautso pambuyo pa tchimo limene anachita ndi Batiseba. Anaimba kuti: ‘Ndipo ine, mundigwiriziza mu ungwiro wanga.’—Salmo 41:12.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
26:6—Mofanana ndi Davide, kodi tingazungulire motani guwa la nsembe la Yehova? Guwa la nsembe likuimira chifuniro cha Yehova cholandira nsembe ya dipo ya Yesu Kristu yowombolera anthu. (Ahebri 8:5; 10:5-10) Timazungulira guwa la nsembe la Yehova mwa kukhulupirira nsembe imeneyi.
29:3-9—Kodi kuyerekeza mawu a Yehova ndi kugunda kwa bingu komwe kumachititsa mantha, kukusonyeza chiyani? Zikungotanthauza izi: Mphamvu zochititsa mantha za Yehova!
31:23—Kodi munthu wodzitama amabwezeredwa motani zochuluka? Zimene akutchula pano kuti adzabwezeredwa ndi chilango. Munthu wolungama amabwezeredwa m’njira ya chilango chochokera kwa Yehova chifukwa cha zimene waphonyetsa mwangozi. Popeza munthu wodzitama sasiya kuchita zoipa, amabwezeredwa zochuluka ndi chilango chokhwima.—Miyambo 11:31; 1 Petro 4:18.
33:6—Kodi “mpweya” wa m’kamwa mwa Yehova n’chiyani? Mpweya umenewu ndi mphamvu yomwe Mulungu amagwiritsa ntchito, kapena kuti mzimu woyera, imene anagwiritsa ntchito polenga miyamba yomwe timaonayi. (Genesis 1:1, 2) Umatchedwa mpweya wa m’kamwa mwake chifukwa chakuti, mofanana ndi kupuma mwamphamvu, mzimuwu ungathe kutumizidwa kukagwira ntchito kutali kwambiri.
35:19—Kodi pempho la Davide loti asalole adani ake kum’tsinzinira likutanthauza chiyani? Kutsinzina kukanasonyeza kuti adani a Davide akusangalala chifukwa cha kuyenda bwino kwa zolinga zawo zomuchitira zoipa. Davide anapempha kuti zimenezi zisachitike.
Zimene Tikuphunzirapo:
26:4. N’chinthu chanzeru kupewa kuyanjana ndi anthu otyasika pa Intaneti, kusukulu kapena kuntchito kwathu, amene amakhala ngati anzathu koma akuganizira zachinyengo, anthu ampatuko amene amadzionetsa ngati anthu achilungamo, ndiponso anthu achiphamaso.
26:7, 12; 35:18; 40:9. Tiyenera kutamanda Yehova poyera pa misonkhano yachikristu.
26:8; 27:4. Kodi timakonda kupita ku misonkhano yachikristu?
26:11. Pamene Davide anali kufotokoza cholinga chake chofuna kupitiriza kuyenda mwangwiro, iye anapemphanso kuti awomboledwe. Inde, n’zotheka kukhala okhulupirika ngakhale kuti ndife opanda ungwiro.
29:10. Mwa kukhala pa “Chigumula,” Yehova akusonyeza kuti amalamulira bwinobwino mphamvu zake.
30:5. Khalidwe lalikulu la Yehova ndi chikondi, osati mkwiyo.
32:9. Yehova safuna kuti tikhale ngati kavalo ndi bulu amene amamvera chifukwa cha zingwe zimene amam’mangirira kapena chifukwa cha mkwapulo. M’malo mwake, amafuna kuti tisankhe kumumvera chifukwa chakuti tamvetsa chifuniro chake.
33:17-19. Palibe dongosolo lililonse lopangidwa ndi anthu, ngakhale litakhala lamphamvu chotani, lomwe lingabweretse chipulumutso. Tiyenera kukhulupirira Yehova ndi Ufumu wake.
34:10. Izitu ndi zolimbikitsa kwambiri kwa anthu amene amaika patsogolo zinthu za Ufumu m’moyo wawo!
39:1, 2. Oipa akamafufuza nkhani n’cholinga chofuna kuvulaza okhulupirira anzathu, ndi bwino ‘kusunga pakamwa pathu ndi cham’kamwa,’ n’kukhala chete.
40:1, 2. Kuyembekezera Yehova kungatithandize kupirira vuto la kupsinjika maganizo ndi ‘kutuluka m’dzenje la chitayiko.’
40:5, 12. Zoipa kapena zofooka zathu, zingachuluke motani, sizidzatilefula ngati sitiiwala mfundo yakuti madalitso athu ndi ‘ochuluka mosawerengeka.’
‘Adalitsike Yehova’
Kunena zoona masalmo 41 a m’chigawo choyambachi n’ngokhazika mtima pansi ndiponso olimbikitsa kwambiri. Kaya tikukumana ndi mayesero kapena kuvutitsidwa ndi chikumbumtima, timapeza mphamvu komanso chilimbikitso m’chigawo chimenechi cha Mawu amphamvu a Mulungu. (Ahebri 4:12) Masalmo amenewa ali ndi malangizo odalirika kwambiri. Amatitsimikizira mobwerezabwereza kuti kaya tikumane ndi mavuto otani, Yehova sangatisiye.
Chigawo choyambachi chikumaliza ndi mawu akuti: ‘Adalitsike Yehova, Mulungu wa Israyeli, kuchokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha. Amen, ndi Amen.’ (Salmo 41:13) Pambuyo poona masalmo amenewa, kodi sitinalimbikitsidwe kudalitsa kapena kuti kutamanda Yehova?
[Mawu a M’munsi]
[Mawu Otsindika patsamba 19]
Ngati chilengedwe chomwe sichilankhula kapena kuganiza chimalemekeza Yehova, ndiye kuli bwanji ifeyo!
[Chithunzi patsamba 17]
Davide ndiye analemba ambiri mwa masalmo 41 oyambirira
[Chithunzi patsamba 18]
Kodi mukudziwa salmo limene limafotokoza kuti Yehova ndi Mbusa Wamkulu?
[Chithunzi patsamba 20]
Musalole tsiku kudutsa popanda kuganizira zinthu zauzimu
[Mawu a Chithunzi patsamba 17]
Stars: Courtesy United States Naval Observatory
[Mawu a Chithunzi patsamba 19]
Stars, pages 18 and 19: Courtesy United States Naval Observatory
[Mawu a Chithunzi patsamba 20]
Stars: Courtesy United States Naval Observatory