Mtengo wa “Chotengera Chochepa Mphamvu”
Mtengo wa “Chotengera Chochepa Mphamvu”
“AMUNA inu, khalani [ndi akazi anu] monga mwa chidziwitso,” analemba choncho mtumwi Petro, “ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu.” (1 Petro 3:7) Kodi pamenepa Malemba akunyoza mkazi pomutchula kuti “chotengera chochepa mphamvu”? Tiyeni tione zimene mlembi wouziridwa ameneyu ankatanthauza poyambirira.
Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “ulemu” amatanthauza “mtengo, phindu . . . kulemekeza.” Motero mwamuna wachikristu amafunika kukonda mkazi wake, ndi kum’ganizira monga chinthu chamtengo wapatali chomwe chingasweke mosavuta. Kumeneku sikuti ndi kunyoza ngakhale pang’ono. Mwachitsanzo, taganizirani za nyali zamaluwa za Tiffany. Kunena zoona, nyali zokongola kwambiri zimenezi zimathadi kusweka mosavuta. Kodi nyali zimenezi n’zotsika mtengo chifukwa chakuti zimasweka mosavuta? Ayi. Mu 1997 nyali yoyambirira ya Tiffany anaigulitsa madola 2.8 miliyoni. Kapangidwe kake, koti ingathe kusweka mosavuta, m’malo moti kakadaitsitsa mtengo n’kamenenso kanathandizira kuti nyaliyi ikhale yokwera mtengo kwambiri.
Umu ndi mmenenso zilili ndi mkazi. Kum’patsa ulemu monga chotengera chochepa mphamvu sikum’chotsa ulemu kapena kum’nyoza ayi. Kukhala ndi mkazi “monga mwa chidziwitso” kukutanthauza kuti mwamuna amaganizira zimene mkaziyo angathe ndi zimene sangathe kuchita, zimene amakonda ndi zimene sakonda, ndiponso maganizo a mkaziyo. Mwamuna wachikondi amazindikira mfundo yakuti iye ndi mkazi wake ndi osiyana umunthu wawo. Amaganizira mkazi wakeyo “kuti mapemphero [ake, mwamunayo] angaletsedwe.” (1 Petro 3:7) Mwamuna amene salemekeza mkazi wake monga munthu wamayi angathe kuwonongetsa ubwenzi wake ndi Mulungu. N’zoonekeratu kuti Mawu a Mulungu sanyoza akazi, koma amawalemekeza.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
© Christie’s Images Limited 1997