Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ubwino Woyenda Mwangwiro

Ubwino Woyenda Mwangwiro

Ubwino Woyenda Mwangwiro

“Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.”​—MIYAMBO 10:22.

1, 2. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kuganizira kwambiri za tsogolo?

“ANTHUFE timalephera kusangalala ndi zimene tili nazo panopa . . . chifukwa choganizira kwambiri za tsogolo,” anatero bambo wina wa ku America wofufuza nzeru zapamwamba. Izi ndi zimene zimachitikira ana amene amaganizira kwambiri zomwe azidzachita akadzakula moti ana otere sadyerera ubwana wawo.

2 Nawonso anthu olambira Yehova angathe kukhala ndi maganizo ngati amenewa. Taonani zimene zingachitike. Tikulakalaka kuona malonjezo a Mulungu obweretsa paradaiso padziko lapansili akukwaniritsidwa. Tikufunitsitsa kudzakhala ndi moyo wopanda matenda, ukalamba, zopweteka, ndiponso mavuto. Ngakhale kuti sikulakwa kuyembekezera zinthu zimenezi, kodi chingachitike n’chiyani ngati tiganizira kwambiri madalitso akuthupi omwe talonjezedwa mpaka kufika polephera kuona madalitso auzimu omwe tili nawo panopa? Zingathe kukhala zinthu zomvetsa chisoni kwambiri. Tingathe kugwa ulesi mosavuta n’kuyamba ‘kudwala mu mtima chifukwa chakuti zomwe tikuyembekezera zikuzengereza’ kusiyana ndi mmene tinali kuganizira. (Miyambo 13:12) Tingathe kutaya mtima kapena kuyamba kudzimvera chisoni chifukwa cha mavuto. M’malo mopirira, zinthu zikakhala kuti sizikuyenda bwino, tingathe kuyamba kamtima kong’ung’udza. Tingapewe zonsezi ngati tiganizira ndi kuyamikira madalitso omwe tili nawo panopa.

3. M’nkhani ino, kodi tikambirana kwambiri za chiyani?

3 Lemba la Miyambo 10:22 limati: “Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.” Kodi kuyenda bwino kwa zinthu zauzimu pakati pa atumiki a Yehova amakono si madalitso ofunika kusangalalira? Tiyeni tikambirane mbali zina za zinthu zomwe zikutiyendera bwino mwauzimu ndi kuona tanthauzo la zimenezi kwa ifeyo. Kuganizira madalitso amene Yehova wapatsa anthu ‘olungama oyenda mwangwiro’ kutithandiza kwambiri kukhala ndi mtima wofuna kupitiriza kutumikira mosangalala Atate wathu wa kumwamba.​—Miyambo 20:7.

‘Madalitso Otilemeretsa’ Panopa

4, 5. Kodi ndi mfundo iti yomwe Baibulo limaphunzitsa imene imakusangalatsani kwambiri, ndipo n’chifukwa chiyani?

4 Timadziwa molondola ziphunzitso za Baibulo. Ambiri mwa Matchalitchi Achikristu amati amakhulupirira Baibulo. Koma sagwirizana chimodzi pa zimene limaphunzitsa. Ngakhale anthu a chipembedzo chimodzi nthawi zambiri amasiyana maganizo pa zimene Malemba amaphunzitsa kwenikweni. Komatu umu si mmene zilili ndi atumiki a Yehova ayi! Ngakhale kuti ndife osiyana mayiko ochokera, chikhalidwe, kapena mtundu, tikulambira Mulungu amene tikum’dziwa dzina lake. Sikuti ameneyu ndi Mulungu wosadziwika bwino, wokhala ndi mbali zitatu ayi. (Deuteronomo 6:4; Salmo 83:18; Marko 12:29) Tikudziwanso kuti nkhani yaikulu kwambiri yakuti Mulungu ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse ithetsedwa posachedwapa ndiponso kuti chifukwa cha kukhulupirika kwathu kwa iye, aliyense wa ife akukhudzidwa ndi nkhaniyi. Tikudziwa choonadi pankhani ya akufa ndipo sitiopa Mulungu winawake amene anthu ambiri amakhulupirira kuti amazunza anthu m’moto wa helo kapena kuwatumiza ku purigatoliyo.​—Mlaliki 9:5, 10.

5 Komanso timasangalala kwambiri kudziwa kuti sitinakhalepo mwangozi chifukwa cha kusanduka kwa zamoyo ayi. Koma tinalengedwa ndi Mulungu, m’chifanizo chake. (Genesis 1:26; Malaki 2:10) Wamasalmo anaimbira Mulungu wake kuti: “Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu n’zodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.”​—Salmo 139:14.

6, 7. Kodi ndi kusintha kotani kwa moyo wanu kapena wa anthu ena amene mukuwadziwa komwe kwabweretsa madalitso?

6 Tinamasuka ku zizolowezi ndi makhalidwe oipa. Nyuzipepala ndiponso mawailesi amachenjeza anthu nthawi ndi nthawi za kuopsa kosuta fodya, kumwa mowa kwambiri, ndiponso khalidwe la chiwerewere. Anthu ambiri salabadira machenjezo amenewa. Komano, kodi chimachitika n’chiyani munthu woona mtima akaphunzira kuti Mulungu woona amadana ndi zinthu zimenezi ndipo sasangalala ndi anthu amene amachita zimenezi? Munthu wotero amasiya makhalidwe amenewa! (Yesaya 63:10; 1 Akorinto 6:9, 10; 2 Akorinto 7:1; Aefeso 4:30) Ngakhale kuti pochita zimenezi cholinga chake kwenikweni chimakhala kufuna kusangalatsa Yehova Mulungu, iye amapindula m’njira inanso. Amakhala wathanzi ndiponso wamtendere m’maganizo.

7 Ambiri amavutika kusiya zizolowezi zoipa. Komabe, chaka ndi chaka anthu masauzande ambirimbiri amatha kuchita zimenezi. Amadzipereka kwa Yehova ndi kubatizidwa m’madzi, ndipo pochita zimenezi amasonyeza poyera kuti asiya makhalidwe amene Mulungu sasangalala nawo. Izitu ndi zolimbikitsa kwambiri kwa tonsefe. Timalimbikitsidwa kwambiri kupitiriza kukhala omasuka ku ukapolo wa uchimo ndi makhalidwe owononga moyo.

8. Kodi ndi malangizo otani a m’Baibulo amene amathandiza kuti banja lizikhala losangalala?

8 Timakhala ndi mabanja osangalala. M’mayiko ambiri mabanja akugwedezeka. Anthu m’mabanja ambiri amasudzulana, ndipo nthawi zambiri amasiya ana atasokonezeka maganizo kwambiri. M’mayiko ena a ku Ulaya, pa mabanja 100 alionse pali mabanja pafupifupi 20 oyendetsedwa ndi kholo limodzi. Kodi Yehova watithandiza motani kuyenda mwangwiro pankhaniyi? Chonde, tawerengani Aefeso 5:22–6:4, ndipo onani malangizo abwino kwambiri omwe Mawu a Mulungu amapereka kwa amuna, akazi, ndiponso ana. Mosakayikira, kutsatira zimene zili m’mavesiwa ndiponso m’Malemba ena kumalimbitsa mabanja, kumathandiza makolo kulera bwino ana, komanso kumathandiza kuti banja lizikhala losangalala. Kodi amenewa si madalitso omwe tiyenera kusangalalira?

9, 10. Kodi tsogolo lathu ndi losiyana motani ndi la anthu a dzikoli?

9 Tikudziwa kuti mavuto a dzikoli atha posachedwapa. Ngakhale kuti ntchito za sayansi ndi umisiri zapita patsogolo kwambiri ndiponso atsogoleri ena ali ndi khama lofuna kuthetsa mavuto a anthu, mavuto akuluakulu a moyo wa masiku ano sanathetsedwe. Chaposachedwapa, Klaus Schwab, amene anayambitsa bungwe lina lomwe cholinga chake ndi kuthana ndi mavuto omwe anthu timakumana nawo la World Economic Forum, ananena kuti “mndandanda wa mavuto omwe dzikoli likukumana nawo ukuwonjezeka pamene nthawi yowathetsera ikucheperachepera.” Iye anatchula za “mavuto amene sasankha mayiko, monga uchigawenga, kuwonongeka kwa chilengedwe ndiponso kusakhazikika kwa zachuma.” Schwab anamaliza motere: “Tsopano kusiyana ndi m’mbuyo monsemu, dziko likukumana ndi mikwingwirima yofunika kuti tonse tigwirizane ndiponso tipeze mwamsanga njira zolimbanirana nayo.” Pamene tikulowa m’katikati mwa zaka zino za m’ma 2000, tsogolo la anthu silikuoneka lolimbikitsa kwenikweni.

10 N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova wakonza dongosolo lomwe lidzathetse mavuto onse a anthu, limene ndi Ufumu wa Mulungu wa Mesiya. Ndi Ufumu umenewu, Mulungu woona ‘adzaletsa nkhondo’ ndi kubweretsa ‘mtendere wochuluka.’ (Salmo 46:9; 72:7) Mfumu yodzozedwa, yomwe ndi Yesu Kristu, ‘idzapulumutsa waumphawi, wozunzika ndi wosauka ku chinyengo ndi chiwawa.’ (Salmo 72:12-14) Ufumu umenewu ukadzayamba kulamulira dziko, sikudzakhala vuto la kuperewera kwa chakudya. (Salmo 72:16) Yehova ‘adzapukuta misozi yonse, kuichotsa pamaso pathu; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.’ (Chivumbulutso 21:4) Ufumuwu unakhazikitsidwa kale kumwamba ndipo posachedwapa udzathetsa mavuto alionse padziko lapansi pano.​—Danieli 2:44; Chivumbulutso 11:15.

11, 12. (a) Kodi kufunafuna zinthu zosangalatsa kumabweretsa chimwemwe chokhalitsa? Fotokozani. (b) Kodi n’chiyani chimene chimabweretsa chimwemwe chenicheni?

11 Timadziwa chimene chimachititsa anthu kukhala ndi chimwemwe chenicheni. Kodi n’chiyani chimene chimachititsa munthu kukhala ndi chimwemwe chenicheni? Katswiri wina wa zamaganizo ananena kuti pali zinthu zitatu zimene zimabweretsa chimwemwe​—zinthu zosangalatsa, kukhala ndi zochita (monga ntchito ndi kuchita zinthu ndi banja), ndiponso kukhala ndi cholinga (kuchita zinthu ndi cholinga kapena kuchita zinthu zothandiza anthu ena). Pa zinthu zitatuzi, iye anaika zinthu zosangalatsa pamapeto ndipo anati: “Izi ndi zochititsa chidwi chifukwa chakuti kwa anthu ambiri chinthu chofunika pa moyo wawo ndi zinthu zosangalatsa.” Kodi Baibulo limati chiyani za nkhaniyi?

12 Kalekale, Mfumu Solomo ya ku Israyeli inati: “Ndinati mumtima mwanga, Tiyetu, ndikuyese ndi chimwemwe; tapenya tsono zabwino; ndipo taona, ichinso ndi chabe. Ndinati, Kuseka ndi misala; ndi chimwemwe kodi chichita chiyani?” (Mlaliki 2:1, 2) Mogwirizana ndi zimene Malemba amanena, chimwemwe chilichonse chomwe anthu amapeza chifukwa cha zinthu zosangalatsa sichikhalitsa. Nanga bwanji za kukhala ndi zochita? Tili ndi ntchito yatanthauzo kwambiri yoti tigwire, ntchito yolengeza za Ufumu ndi kuphunzitsa anthu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Tikamauza ena uthenga wachipulumutso womwe uli m’Baibulo, timakhala tikugwira ntchito yomwe ingathe kudzapulumutsa ife eni ndiponso anthu amene atimvera. (1 Timoteo 4:16) Popeza ndife “antchito anzake a Mulungu,” timadzionera tokha kuti “kupatsa kutidalitsa [kapena kuti, kumatipatsa chimwemwe chambiri] koposa kulandira.” (1 Akorinto 3:9; Machitidwe 20:35) Chifukwa cha ntchito imeneyi tikukhala moyo watanthauzo ndiponso timapatsa Mlengi yankho loti apereke kwa Satana Mdyerekezi amene akumutonza. (Miyambo 27:11) Zoonadi, Yehova watisonyeza kuti kukhala odzipereka kwa iye kumabweretsa chimwemwe chenicheni komanso chokhalitsa.​—1 Timoteo 4:8.

13. (a) Kodi n’chifukwa chiyani Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndi madalitso osangalalira nawo? (b) Kodi inu mwapindula motani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu?

13 Timalandira maphunziro ofunika kwambiri ndiponso othandiza. Gerhard ndi mkulu mu mpingo wina wa Mboni za Yehova. Pofotokoza za ubwana wake, iye anati: “Ndili mwana ndinkavutika kwambiri kulankhula. Ndikapanikizidwa, sindinkatha kulankhula bwinobwino ndipo ndinkachita chibwibwi. Ndinkadziona kuti ndine wopanda ntchito ndipo zinandifoola kwambiri. Makolo anga anakonza zoti ndikaphunzire za kalankhulidwe koma sizinathandize. Vuto langa silinali katulutsidwe ka mawu m’kamwa, koma linali lokhudza ubongo. Koma panali makonzedwe abwino kwambiri a Yehova, omwe ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Kulembetsa m’sukulu imeneyi kunandilimbikitsa kwambiri. Ndinkayesetsa kuyeseza zimene ndaphunzira. Ndipo zinandithandiza kwambiri. Ndinayamba kulankhula bwinobwino, kupanikizika maganizo kunatha, ndipo ndinayamba kulimba mtima kwambiri mu utumiki. Panopa ndimatha kukamba nkhani za onse bwinobwino. Ndimayamikira kwambiri Yehova, amene anandithandiza kuti zinthu zikhale bwino pa moyo wanga kudzera m’sukuluyi.” Kodi mmene Yehova amatiphunzitsira kuti tithe kuchita ntchito yake, si chifukwa chosangalalira?

14, 15. Tikakhala m’mavuto, kodi pali chithandizo chotani chomwe tingalandire panthawi iliyonse? Perekani chitsanzo.

14 Ndife mabwenzi a Yehova ndiponso timathandizidwa ndi ubale wogwirizana wa padziko lonse. Katrin amene akukhala ku Germany, anada nkhawa kwambiri atamva za chivomezi ndi tsunami amene chivomezicho chinachititsa m’mayiko a kum’mwera chakum’mawa kwa Asia. Panthawi ya tsokali n’kuti mwana wake wamkazi ali m’dziko la Thailand. Mayiyu anakhala maola 32 osadziwa ngati mwana wakeyo ali moyo kapena ngati anali nawo pa chiwerengero cha anthu omwe anavulala kapena anafa, chomwe chinali kukwera nthawi ndi nthawi. Katrin atalandira telefoni yomutsimikizira kuti mwana wakeyo ali bwinobwino, mtima wake unakhala m’malo.

15 Kodi n’chiyani chinathandiza Katrin panthawi yomwe anathedwa nzeruyo? Iye analemba kuti: “Nthawi yaikulu inatha ndikupemphera kwa Yehova. Nthawi ndi nthawi ndinkaona kuti pemphero linali kundilimbikitsa kwambiri komanso kundipatsa mtendere wa m’maganizo. Komanso abale auzimu achikondi anabwera kudzandiona ndi kundilimbikitsa.” (Afilipi 4:6, 7) Panthawi yopweteka ngati imeneyi, zinthu zikanaipa kwambiri Katrin akanapanda kuthandizidwa ndi pemphero la kwa Yehova ndiponso kulimbikitsidwa ndi abale auzimu achikondi! Ubwenzi wathu wolimba ndi Yehova ndi Mwana wake komanso kuyanjana kwambiri ndi abale athu achikristu ndi madalitso apadera, ndipo n’ngamtengo wapatali moti sitingawanyalanyaze.

16. Fotokozani nkhani yosonyeza ubwino wa chiyembekezo choti akufa adzauka.

16 Tikuyembekezera kuti tidzaonanso okondedwa athu amene anamwalira. (Yohane 5:28, 29) Mnyamata wina, dzina lake Matthias, analeredwa monga wa Mboni za Yehova. Koma chifukwa chosazindikira madalitso omwe anali nawo, iye anachoka mumpingo wachikristu atasinkhukirapo. Panopa analemba kuti: “Kunena zoona sitinakambiranepo nkhani zikuluzikulu ndi abambo anga. Tinkakangana nthawi zambiri. Komabe abambo ankandifunira zabwino nthawi zonse. Ankandikonda kwambiri, koma ine sindinazindikire. Tsiku lina mu 1996, ndinakhala pafupi ndi pamene anagona akudwala. Ndinawagwira dzanja, uku ndikulira kwambiri, n’kuwapepesa pa zonse zimene ndinawalakwira ndiponso ndinawauza kuti ndinali kuwakonda kwambiri. Koma sanathe kundimva. Atadwala kwa nthawi yochepa, anamwalira. Ngati ndidzakhale ndi moyo n’kudzaona abambo ataukitsidwa, ndidzakonza zomwe ndinalakwa. Ndipo sindikukayikira kuti adzasangalala kwambiri kumva kuti tsopano ndine mkulu ndiponso kuti ine ndi mkazi wanga ndife apainiya.” Zoonadi, chiyembekezo choti akufa adzauka ndi madalitso aakulu kwambiri!

“Sawonjezerapo Chisoni”

17. Kodi kuganizira za madalitso a Yehova kuyenera kutithandiza motani?

17 Pofotokoza za Atate wake wa kumwamba, Yesu Kristu anati: “Iye amakwezera dzuwa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.” (Mateyu 5:45) Ngati Yehova Mulungu amadalitsa ngakhale anthu osalungama ndiponso oipa, ndiye kuli bwanji anthu amene amayenda mwangwiro! “Yehova . . . sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro,” limatero lemba la Salmo 84:11. Tikamaganizira mmene iye amasamalira mwapadera anthu omwe amam’konda, timayamikira ndiponso timakhala osangalala kwambiri!

18. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova sawonjezera chisoni pa madalitso ake? (b) N’chifukwa chiyani ambiri mwa atumiki okhulupirika a Mulungu amavutika?

18 “Madalitso a Yehova” ndiwo akuthandiza anthu ake kuti zinthu ziziwayendera bwino mwauzimu. Ndipo akutitsimikizira kuti “sawonjezerapo chisoni.” (Miyambo 10:22) Ndiyeno n’chifukwa chiyani ambiri mwa anthu okhulupirika a Mulungu amakumana ndi mavuto ndiponso mayesero, omwe amachititsa kuti azivutika kwambiri? Timavutika chifukwa cha zinthu zitatu makamaka. (1) Zochita zathu zauchimo. (Genesis 6:5; 8:21; Yakobo 1:14, 15) (2) Satana ndi ziwanda zake. (Aefeso 6:11, 12) (3) Dziko loipa. (Yohane 15:19) Ngakhale kuti Yehova amalola kuti zinthu zoipa zizitichitikira, sikuti iye ndiye amachititsa zinthuzo. Ndipotu, “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko.” (Yakobo 1:17) Madalitso a Yehova sabweretsa mavuto.

19. Kodi anthu oyenda mwangwiro akuyembekezera chiyani?

19 Kuti zinthu zizitiyendera bwino mwauzimu timafunika kukhala paubwenzi wolimba ndi Mulungu nthawi zonse. Tikakhala naye paubwenzi wolimba, ‘timadzikundikira tokha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti tigwire moyo weniweniwo,’ womwe ndi moyo wosatha. (1 Timoteo 6:12, 17-19) M’dziko latsopano la Mulungu lomwe likubwera, tidzapeza madalitso auzimu ndiponso akuthupi. Ndiyeno, anthu onse omwe ‘akumvera mawu a Yehova’ adzapeza moyo weniweniwo. (Deuteronomo 28:2) Ndiyetu tiyeni tiyesetse kwambiri kupitiriza kusangalala poyenda mwangwiro.

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• N’chifukwa chiyani si chinthu chanzeru kuganizira kwambiri za tsogolo?

• Kodi panopa tili ndi madalitso otani?

• Kodi n’chifukwa chiyani atumiki okhulupirika a Mulungu amavutika?

[Mafunso]