Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”

“Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”

“Tiyenera Kumvera Mulungu Koposa Anthu”

“Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”

MAGULU ankhondo awiri aimitsana, gulu lina lili tsidya limodzi la chigwa ndipo gulu lina lili tsidya linalo. Asilikali a Israyeli akhala akuchita mantha kwa masiku 40 ndipo akhala akunyozedwa mobwerezabwereza ndi Goliati, ngwazi ya Afilisti.​—1 Samueli 17:1-4, 16.

Goliati akunyoza Aisrayeli mofuula, amvekere: “Mudzisankhire munthu, atsikire kwa ine. Akakhoza iyeyo kuponyana ndi ine ndi kundipha, tidzakhala ife akapolo anu; koma ine ndikam’laka, ndi kumupha, tsono mudzakhala inu akapolo athu, ndi kutitumikira ife. . . . Ine ndinyoza makamu a nkhondo a Israyeli lero; mundipatse munthu, kuti tilimbane ife awiri.”​—1 Samueli 17:8-10.

Kalekale, sizinali zachilendo kuti ngwazi za asilikali ziimire magulu awo a nkhondo ndi kuti awiriwo amenyane. Gulu la wopambana pa kumenyana kumeneku ndilo linkapambana nkhondoyo. Koma msilikali amene akunyoza Israyeliyu si msilikali wamba. Ndi wojintcha ndiponso wamtali, mochititsa mantha. Koma, ponyoza asilikali a anthu a Yehova, Goliati akungodziitanira mavuto.

Imeneyi sikuti ndi nkhondo wamba ayi. Ndi nkhondo ya pakati pa Yehova ndi milungu ya Afilisti. M’malo molimba mtima n’kutsogolera asilikali ake polimbana ndi adani a Mulungu, Mfumu Sauli ya Israyeli yagwidwa mantha aakulu kwambiri.​—1 Samueli 17:11.

Mnyamata Adalira Yehova

Asilikali ali chilili chomwechi, mnyamata wina, amene anadzozedwa kale kuti adzakhale mfumu ya Israyeli akubwera kudzaona abale ake omwe ali m’gulu la asilikali a Sauli. Dzina lake ndi Davide. Atamva zimene Goliati akunena, iye akufunsa kuti: “Mfilisti uyu wosadulidwa ndiye yani, kuti azinyoza makamu a Mulungu wamoyo?” (1 Samueli 17:26) Kwa Davide, Goliati akuimira Afilisti ndi milungu yawo. Davide sakusangalala ndi zimenezi ndipo pofuna kuteteza dzina la Yehova ndi Israyeli, iye akufuna kumenyana ndi munthu wachikunja ameneyu. Koma Mfumu Sauli ikunena kuti: “Sukhoza iwe kukomana ndi Mfilisti uyu kukaponyana naye; pakuti iwe ndiwe mnyamata.”​—1 Samueli 17:33.

Maganizo a Sauli ndi a Davide akusiyana kwambiri. Sauli akaona Davide, akungoganizira za mbusa wachinyamata amene akufuna kumenyana ndi munthu wojintcha ndi wokakala mtima. Koma kwa Davide, Goliati ndi munthu wamba amene akunyoza Ambuye Mfumu Yehova. Davide akulimba mtima chifukwa akudziwa bwino kuti Mulungu sangalolere kuti dzina Lake ndiponso anthu Ake anyozedwe popanda kulanga munthu wochita zimenezo. Ngakhale kuti Goliati akudzitamandira chifukwa cha mphamvu zake, Davide akudalira Yehova, ndipo akuona zinthu mogwirizana ndi mmene Mulungu akuonera.

“Ine Ndafika kwa Iwe M’dzina la Yehova”

Pali zifukwa zomveka zimene zikupangitsa Davide kukhala ndi chikhulupiriro chotere. Iye akukumbukira kuti Mulungu anam’thandiza kupulumutsa nkhosa zake kwa chimbalangondo ndiponso kwa mkango. Mbusa wachinyamatayu sakukayikira kuti ulendo uno, Yehova am’thandiza kuthana ndi mdani wachifilisti wochititsa mantha ameneyu. (1 Samueli 17:34-37) Atatenga chida choponyera miyala ndi miyala isanu yosalala, Davide akunyamuka kukamenyana ndi Goliati.

Davide wasankha kuti achite ntchito yooneka ngati yosatheka imeneyi chifukwa chodalira mphamvu zimene Yehova amapereka. Iye akuuza Mfilistiyu molimba mtima kuti: “Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m’dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israyeli amene iwe unawanyoza. Lerolino Yehova adzakupereka iwe m’dzanja langa . . . Kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israyeli kuli Mulungu. Ndi msonkhano wonse uno udzazindikira kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga, kapena ndi mkondo; pakuti Yehova ndiye mwini nkhondo.”​—1 Samueli 17:45-47.

Kodi chikuchitika n’chiyani? Nkhani youziridwayi imatiuza kuti: “Davide anapambana Mfilistiyo ndi mwala wa choponyera chake, nakantha Mfilistiyo, namupha. Koma m’dzanja la Davide munalibe lupanga.” (1 Samueli 17:50) Analibe lupanga m’manja, koma Yehova Mulungu anam’thandiza kwambiri. *

Pa kumenyana kwawoku, zinaoneka kuti Davide sanalakwitse kukhulupirira Yehova. Ngati tikufunika kusankha pakati pa kuopa anthu ndi kudalira mphamvu zopulumutsa za Yehova, n’zosachita kufunsa kuti tingasankhe chiyani: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” (Machitidwe 5:29) Komanso, tikamaona mavuto mofanana ndi mmene Yehova Mulungu akuwaonera, sitingatekeseke nawo ngakhale atakhala aakulu kwambiri.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Onani Kalendala ya 2006 ya Mboni za Yehova, mwezi wa May ndi June.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 9]

KODI GOLIATI ANALI WAMKULU BWANJI?

Pa 1 Samueli 17:4-7 timamva kuti Goliati anali wamtali kuposa mikono isanu ndi umodzi​—pafupifupi mamita atatu. Malaya ake ausilikali omwe anali amkuwa akusonyeza kuti Mfilistiyu anali wamkuludi ndiponso wamphamvu kwambiri. Malayawo ankalemera makilogalamu 57! Mtengo wa mkondo wake unali ngati mtanda woombera nsalu, ndipo mutu wachitsulo wa mkondowo unkalemera makilogalamu 7. N’kutheka kuti zida zankhondo za Goliati zinali zolemera kwambiri kuposa Davide mwiniyo!