Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

N’chifukwa chiyani m’Chilamulo cha Mose zinthu zina zachibadwa zokhudza kugonana ndi kubereka zinkatengedwa kuti ndi zinthu “zodetsa” munthu?

Mulungu analenga anthu kuti azigonana chifukwa ankafuna kuti aziberekana komanso kuti okwatirana azisangalala. (Genesis 1:28; Miyambo 5:15-18) Koma mu chaputala 12 ndi 15 cha buku la Levitiko timapezamo malamulo atsatanetsatane onena za zinthu zodetsa munthu zokhudza mwamuna akagona kuipa, mkazi akakhala kumwezi, ndiponso akabereka. (Levitiko 12:1-6; 15:16-24) Aisrayeli anapatsidwa malamulo amenewa kuti azikhala ndi moyo wathanzi ndi makhalidwe abwino kwambiri. Malamulowa ankagogomezeranso kupatulika kwa magazi ndi kufunika koteteza mtunduwo kumachimo.

Mwa zinthu zina, malamulo okhudza kugonana ndi kuberekawa anathandiza kuti mtundu wa Aisrayeli uzikhala wathanzi. Buku lakuti The Bible and Modern Medicine limati: “Lamulo lolemekeza nthawi imene mkazi ali kumwezi n’kuletsa kugonana panthawiyo linali njira yothandiza kwambiri yopewera matenda enaake ofalitsidwa m’njira ya kugonana . . . komanso linali njira yoteteza khansa ya m’chiberekero.” Malamulo amenewa anateteza anthu a Mulungu ku matenda amene iwo sanali kuwadziwa kapena amene sakanatha kuwazindikira. Kukhala aukhondo pa zinthu zokhudza kugonana kunathandiza mtunduwo kuchulukana ndipo Mulungu anali ataudalitsa poulonjeza kuti udzachuluka ndi kukhala mtundu waukulu. (Genesis 15:5; 22:17) Malamulo amenewa anatetezanso maganizo a anthu a Mulungu. Pomvera malamulowa, amuna ndi akazi ankaphunzira kukhala anthu odziletsa.

Komabe, nkhani yaikulu pa kudetsedwa kosiyanasiyana kokhudza nkhani za kugonana, inali kutuluka kapena kutayika kwa magazi. Lamulo la Mulungu pankhani ya magazi linatsindika m’maganizo mwa Aisrayeli za kupatulika kwa magazi komanso ntchito yapadera ya magazi pa zinthu zokhudza kulambira Yehova, kapena kuti popereka nsembe ndi kuteteza anthu ku machimo.​—Levitiko 17:11; Deuteronomo 12:23, 24, 27.

Motero, malamulo atsatanetsatanewo anali okhudzana kwambiri ndi kupanda ungwiro kwa anthu. Aisrayeli ankadziwa kuti Adamu ndi Hava atachimwa, sakanabereka ana angwiro. Motero chifukwa cha uchimo umenewu, ana awo anayenera kukhala opanda ungwiro n’kumafa. (Aroma 5:12) Chifukwa cha zimenezi, moyo umene makolo ankapatsa ana amene abereka unkakhala wopanda ungwiro ndiponso wauchimo, ngakhale kuti poyamba Mulungu anakonza kuti anthu akakwatirana azigwiritsa ntchito ziwalo zoberekera popatsa ana awo moyo wangwiro.

Motero malamulo okhudza kuyeretsa ankakumbutsa Aisrayeli za uchimo umene anabadwa nawo komanso zoti m’pofunika nsembe ya dipo yoti iphimbe machimo a anthu komanso kuti anthuwo akhalenso angwiro. Inde, nsembe zanyama zimene Aisrayeliwa ankapereka sizinakwaniritse zimenezi. (Ahebri 10:3, 4) Cholinga cha Chilamulo cha Mose chinali chokonzekeretsa Aisrayeli kudzalandira Kristu ndi kuwathandiza kumvetsa kuti ndi nsembe yangwiro ya Yesu yokha imene ingachititse kuti Mulungu akhululukiredi anthu machimo awo, n’kutsegula njira ya ku moyo wosatha kwa anthu okhulupirika.​—Agalatiya 3:24; Ahebri 9:13, 14.