Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mulungu Amasamalira Okalamba

Mulungu Amasamalira Okalamba

Mulungu Amasamalira Okalamba

MASIKU ano si zodabwitsa kuona anthu okalamba akuzunzidwa. Kalekale, Baibulo linaneneratu kuti “masiku otsiriza” a dongosolo losaopa Mulunguli, anthu adzakhala “odzikonda okha, . . . opanda chikondi chachibadwidwe.” (2 Timoteo 3:1-3) Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “chikondi chachibadwidwe” angaphatikizepo chikondi chimene anthu apachibale amakhala nacho mwachibadwa. Mogwirizana ndi ulosi wa m’Baibulo umenewo, chikondi choterocho chikusowadi masiku ano.

Mosiyana kwambiri ndi anthu amene amazunza okalamba, Yehova Mulungu amayamikira kwambiri ndi kusamalira anthu okalamba. Taganizirani za mmene Baibulo limasonyezera zimenezi.

“Woweruza wa Akazi Amasiye”

Nkhawa ya Yehova Mulungu pa anthu okalamba imasonyezedwa m’Malemba Achihebri. Mwachitsanzo pa Salmo 68:5, Davide anatchula Mulungu kuti ndi “woweruza wa akazi amasiye,” amene kawirikawiri amakhala okalamba. * M’Mabaibulo ena, liwu lakuti “woweruza” analimasulira kuti, “woikira kumbuyo” “mtetezi,” ndi “wowamenyera ufulu.” N’zoonekeratu kuti Yehova amasamalira akazi amasiye. Ndipo Baibulo limati, ngati akazi amasiye akuzunzidwa, mkwiyo wa Yehova umayaka. (Eksodo 22:22-24) Mulungu ndiponso atumiki ake amalemekeza kwambiri akazi amasiye ndiponso anthu onse okalamba amene ali okhulupirika. Lemba la Miyambo 16:31 limasonyeza mmene Yehova Mulungu ndi anthu ake amaonera anthu amenewa. Limati: ‘Imvi ndiyo korona wa ulemu, ikapezedwa m’njira ya chilungamo.’

N’zosadabwitsa kuti kulemekeza okalamba ndi imodzi mwa mbali zofunika za Chilamulo chimene Yehova anapereka kwa Israyeli. Aisrayeli analamulidwa kuti: “Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba; nuope Mulungu wako; ine ndine Yehova.” (Levitiko 19:32) Choncho, mu Israyeli kulemekeza okalamba kunkagwirizana kwambiri ndi ubwenzi wa munthu aliyense ndi Yehova Mulungu. Munthu sakananena kuti amakonda Mulungu ngati akuzunza okalamba.

Akristu sali pansi pa Chilamulo cha Mose. Komabe, iwo ali pansi pa “lamulo la Kristu,” limene limakhudza kwambiri khalidwe ndi maganizo awo, kuphatikizapo kusonyeza chikondi ndi kudera nkhawa makolo ndiponso okalamba. (Agalatiya 6:2; Aefeso 6:1-3; 1 Timoteo 5:1-3) Ndipo Akristu amasonyeza chikondi osati chabe chifukwa choti anawalamula kutero komanso chifukwa chakuti mtima wawo umafuna kuchita zimenezo. Mtumwi Petro analimbikitsa Akristu kuti: “Mukondane kwenikweni kuchokera kumtima.”​—1 Petro 1:22.

Wophunzira wa Yesu, Yakobo anatipatsa chifukwa china chosamalira okalamba. Iye analemba kuti: “Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.” (Yakobo 1:27) Pa lembali ,Yakobo anatchula mfundo yochititsa chidwi kwambiri. Mfundoyi ikusonyeza mmene Yehova amawakondera kwambiri anthu amenewa.

Choncho, chofunika sikungopewa kuzunza anthu okalamba. M’malo mwake tiyenera kusonyeza kuti timawaderadi nkhawa mwa kuwathandiza. (Onani bokosi lakuti “Mmene Tingasonyezere Chikondi,” patsamba 6 ndi 7.) Yakobo analemba kuti: “Chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa.”​—Yakobo 2:26.

Kulimbikitsidwa “M’chisautso Chawo”

Palinso mfundo ina imene tingaphunzire kuchokera m’mawu a Yakobo. Dziwani kuti Yakobo anauza Akristu kuti azicheza ndi akazi amasiye ‘m’chisautso chawo.’ Liwu la Chigiriki limene analimasulira kuti “chisautso” makamaka limatanthauza mavuto, chizunzo, kapena kuvutika chifukwa cha mmene tikukhalira. N’zosachita kufunsa kuti ambiri mwa okalamba amakumana ndi mavuto oterewa. Ena ndi osungulumwa. Ena akuvutika maganizo chifukwa sangathe kuchita zinthu zambiri chifukwa cha ukalamba. Ngakhale ena amene akutumikira Mulungu mokwanira, angathe kufooka. Taganizirani za John, * amene wakhala akulengeza Ufumu wa Mulungu mokhulupirika kwa zaka zoposa 40, ndipo zaka 30 zomalizira wakhala mtumiki wapadera wa nthawi zonse. Tsopano John ali ndi zaka za m’ma 80, ndipo akuti nthawi zina amafooka. Ananena kuti: “Ndimayang’ana m’mbuyo n’kukumbukira zolakwa zanga, ndipo zolakwazo n’zambirimbiri. Ndimapitiriza kuganiza kuti ndikanatha kuchita bwino kuposa mmene ndinachitira.”

Anthu oterewa angalimbikitsidwe kudziwa kuti ngakhale Yehova ali wangwiro, sayembekezera kuti ife tikhalenso angwiro. Ngakhale kuti amadziwa zolakwa zathu, Baibulo limanena za iye kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye?” (Salmo 130:3) Inde, Yehova samangoyang’ana zolakwa zathu, koma amaona zimene zili mumtima mwa munthu. Kodi timadziwa bwanji zimenezi?

Mfumu Davide amene anachimwa ndiponso sanali wangwiro, anauziridwa ndi Mulungu polemba mawu otsatirawa, amene analembedwa pa Salmo 139:1-3, akuti: “Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa. Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali. Muyesa popita ine ndi pogona ine, ndi njira zanga zonse muzolowerana nazo.” Pano, mawu akuti ‘kuyesa’ amatanthauza “kupeta,” chimodzimodzi ndi mmene mlimi amapetera madeya kuti atsale ndi mpunga kapena tirigu. Mouziridwa ndi Mulungu, Davide akutitsimikizira kuti Yehova amadziwa mmene angapetere zolakwa zathu ndi kukumbukira ntchito zathu zabwino.

Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wachifundo, amakumbukira ndipo amaona ntchito zathu zabwino kukhala za mtengo wapatali ngati tipitirizabe kukhala okhulupirika kwa iye. Ndipotu, Baibulo limati iye angaone kuti n’kupanda chilungamo ngati ataiwala ntchito yathu ndi chikondi chimene tinachionetsera pa dzina lake.​—Ahebri 6:10.

“Zoyambazo Zapita”

Baibulo limasonyeza kuti Mulungu sanafune kuti anthu azivutika ndi ukalamba. Koma makolo athu oyambirira, mwamuna ndi mkazi woyamba, atapandukira Mlengi wawo, zotsatira zake n’zakuti anthu anayamba kukumana ndi mavuto aukalamba. (Genesis 3:17-19; Aroma 5:12) Koma zimenezi sizidzapitirira mpaka muyaya.

Monga mmene talongosolera kale, zambiri mwa zoipa zimene tikukumana nazo masiku ano, kuphatikizapo kuzunzika kwa anthu okalamba, zikupereka umboni wakuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ a dongosolo la zinthu lilipoli. (2 Timoteo 3:1) Chifuniro cha Mulungu n’chochotsa mavuto amene amabwera chifukwa cha uchimo, kuphatikizapo mavuto oipa amene amabwera chifukwa cha ukalamba ndiponso imfa. Baibulo limati: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”​—Chivumbulutso 21:4.

M’dziko latsopano la Mulungu, mavuto aukalamba adzakhala mbiri yakale. N’chimodzimodzinso ndi kuzunzika kwa okalamba. (Mika 4:4) Ngakhale anthu amene anamwalira ndipo Mulungu amawakumbukira adzaukitsidwa, kuti nawonso adzakhale ndi mwayi wokhala ndi moyo kosatha m’dziko lapansi la paradaiso. (Yohane 5:28, 29) Panthawi imeneyo, kuposa kale lonse, zidzaonekeratu kuti Yehova Mulungu amasamalira anthu onse amene amam’mvera, osati okalamba okha.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Komabe, akazi ena amasiye si okalamba. Umboni woti Mulungu amasamaliranso akazi amasiye amene si okalamba umapezeka mwachitsanzo pa lemba la Levitiko 22:13.

^ ndime 11 Si dzina lake lenileni.

[Bokosi/​Zithunzi pamasamba 6, 7]

Mmene Tingasonyezere Chikondi

Pakati pa Mboni za Yehova, akulu mu mpingo ndi amene amayambirira kusamalira okalamba. Iwo sanyalanyaza langizo la mtumwi Petro lakuti: “Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu.” (1 Petro 5:2) Kusamalira okalamba mwakuwathandiza, ndi mbali yosamalira gulu la Mulungu. Kodi zimenezi zingaphatikizepo chiyani?

Pamafunika kuleza mtima ndiponso mwina maulendo angapo okacheza ndi anthu okalamba mwachidwi, kuti mudziwe zosowa zawo zonse. Mwina pamafunika kuwathandiza kugula zinthu ndi kusamalira panyumba, thiransipoti yopitira kumisonkhano yachikristu, kuwerenga Baibulo ndi mabuku ena achikristu, ndiponso zinthu zina zambiri. Ngati n’kotheka, payenera kukonzedwa njira yothandiza ndiponso yodalirika yowathandizira. *

Bwanji ngati mbale kapena mlongo wokalamba mumpingo akufuna thandizo lamsangamsanga, mwina kapena akufuna thandizo la ndalama? Choyamba, zingakhale bwino kufufuza ngati mbale kapena mlongoyo ali ndi ana kapena achibale amene angathe kum’thandiza. Zimenezi zingagwirizane ndi zimene zinanenedwa pa 1 Timoteo 5:4 kuti: “Ngati wamasiye wina ali nawo ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m’banja lawo, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi n’cholandirika pamaso pa Mulungu.”

N’kutheka kuti mbale kapena mlongo wokalambayo akufuna kumuthandiza kudziwa ngati akuyenerera kulandira thandizo limene boma limapereka kwa anthu okalamba. Mwina abale ena mumpingomo angathe kuthandiza. Ngati sitingathe kumuthandiza m’njira zomwe tatchulazi, akulu angaone ngati n’koyenera kuti mpingo uthandize mbale kapena mlongoyo. Zimenezi nthawi zina zinkaloledwa mu mpingo wachikristu woyambirira, ndipo mtumwi Paulo analembera wantchito mnzake Timoteo kuti: “Asawerengedwe wamasiye ngati sanafikire zaka makumi asanu ndi limodzi, atakhala mkazi wa mwamuna mmodzi, wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.”​—1 Timoteo 5:9, 10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 25 Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani yakuti “Kukwaniritsa Zosowa za Okalamba Athu​—Chitokoso cha Mkristu,” mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 1988.

[Chithunzi patsamba 5]

Dorika anasamalira akazi amasiye omwe anafunikira thandizo.​—Machitidwe 9:36-39