Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’ngokalamba Koma Amanya-lanyazidwa ndi Kuzunzidwa

N’ngokalamba Koma Amanya-lanyazidwa ndi Kuzunzidwa

N’ngokalamba Koma Amanya-lanyazidwa ndi Kuzunzidwa

TSIKU linalake mlonda wa usiku akuzungulira pa ntchito yake, anaona zinthu zochititsa nthumanzi kwambiri. Panja pa nyumba ina m’dera la anthu olemera, anaona anthu awiri akufa. Linali banja lokalamba lomwe linadumpha kuchokera pa windo la chisanu ndi chitatu la nyumba ya nsanjika. Ngakhale kuti anadzipha m’njira yochititsa nthumanzi, chifukwa chimene anadziphera chinali choopsa kwambiri. Kakalata kamene anakapeza m’thumba la mwamunayo kanali kakuti: “Tikudzipha chifukwa mwana wathu ndi mkazi wake amatichitira nkhanza ndi kutizunza nthawi zonse.”

Nkhaniyi mwina n’njachilendo, koma vuto limeneli n’lofala kwambiri. N’zoonadi, anthu okalamba akuzunzidwa pafupifupi padziko lonse lapansi. Mwachitsanzo, taonani izi:

• Kafukufuku wina anati, anthu anayi mwa anthu 100 alionse okalamba ku Canada, ananena kuti achibale awo kawirikawiri amawachitira nkhanza kapena kuwadyera masuku pamutu. Komabe, anthu ambiri okalamba amachita manyazi kapena kuopa kwambiri kulankhula za mavuto awo. Akatswiri amati, chiwerengero chenicheni mwina chingakhale anthu teni mwa anthu 100 alionse.

• “Dziko la India, limene mabanja awo amaoneka ngati amagwirizana, likugwa chifukwa cha chiwerengero chachikulu cha anthu okalamba omwe safunidwa ndi ana awo,” inatero magazini ya India Today.

• Malinga ndi kafukufuku wodalirika kwambiri amene wachitidwa “anthu a ku United States a zaka 65 kapena kuposerapo okwana wani miliyoni mpaka 2 miliyoni avulazidwa, kudyeredwa masuku pamutu, kapena kuchitidwa nkhanza mwamtundu wina ndi munthu amene amamudalira kuti angawasamalire kapena kuwateteza,” linatero bungwe la National Center on Elder Abuse. Wachiwiri kwa loya wina wamkulu mu mzinda wa San Diego, m’chigawo cha California anati, kuzunza anthu okalamba ndi “imodzi mwa nkhani zovuta kwambiri zimene mabungwe osungitsa malamulo akulimbana nazo masiku ano.” Anawonjezera kuti: “Ndikuona kuti vutoli liwonjezeka pa zaka zowerengeka zikubwerazi.”

• Ku Canterbury, m’dziko la New Zealand, anthu ali ndi nkhawa yaikulu yoti anthu okalamba ndi amene akuzunzidwa ndi achibale awo, makamaka achibale amene amamwa mankhwala osokoneza bongo, mowa, kapena amene ali ndi mavuto otchova juga. Chiwerengero cha anthu okalamba omwe anakanena ku polisi atachitidwa nkhanza ku Canterbury chinakwera kwambiri kuchokera pa 65 m’chaka cha 2002 kufika pa 107 m’chaka cha 2003. Mkulu wa bungwe lomwe lakhazikitsidwa kuti lithane ndi nkhanza zimenezi anati, chiwerengero chimene chaperekedwa “changokhala mbali yaing’ono chabe ya anthu amene akuzunzidwa.”

• Bungwe lina lotchedwa Federation of Bar Associations la ku Japan linanena kuti “okalamba amene akuzunzidwa akufunika kusamalidwa kwambiri kuposa ana amene amagwiriridwa kapena ena amene amachitiridwa nkhanza zina panyumba,” inatero nyuzipepala ya The Japan Times. N’chifukwa chiyani nyuziyi inatero? Chifukwa choyamba n’chakuti, “poyerekezera ndi kuchitira nkhanza ana kapena mnzako amene uli naye pabanja, kuzunza anthu okalamba sikudziwika msanga, chifukwa chakuti nthawi zina, anthu okalamba amadziimba mlandu ana awo akamawachitira chiwawa, komanso chifukwa chakuti boma ndiponso akuluakulu oona zimenezi, padakali pano akulephera kupeza njira yothetsera vutoli.”

Zitsanzo zowerengeka za zomwe zikuchitika padzikozi, zimatipangitsa kufunsa kuti: N’chifukwa chiyani anthu ambiri okalamba amanyalanyazidwa ndi kuzunzidwa? Kodi pali chiyembekezo chilichonse choti zinthu zimenezi zidzasintha? Kodi n’chiyani chingalimbitse mtima anthu okalamba?