“Ha! Ndikondadi Chilamulo Chanu”
“Ha! Ndikondadi Chilamulo Chanu”
“Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiriramo ine tsiku lonse.”—SALMO 119:97.
1, 2. (a) Kodi munthu amene anauziridwa kulemba Salmo 119 anakumana ndi mavuto otani? (b) Kodi iye anatani atakumana ndi zimenezi, ndipo anatero chifukwa chiyani?
MUNTHU amene analemba Salmo 119 anakumana ndi chiyeso chachikulu. Adani odzitukumula amene sankamvera chilamulo cha Mulungu ankamunyoza ndi kumunamizira nkhani zabodza. Nduna zinamupangira upo ndipo zinamuzunza. Anthu oipa anamuzinga, ndipo moyo wake unali pangozi. Zonsezi zinachititsa moyo wake ‘kusungunuka, [“kusowa tulo,” NW] ndi chisoni.’ (Salmo 119:9, 23, 28, 51, 61, 69, 85, 87, 161) Pokumana ndi chiyeso chimenechi, wamasalmoyo anaimba kuti: “Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiriramo ine tsiku lonse.”—Salmo 119:97.
2 Mwina mungafunse kuti, “Kodi chilamulo cha Mulungu chinalimbikitsa ndi kutonthoza bwanji wamasalmoyo?” Chomwe chinamulimbikitsa ndi chikhulupiriro chake choti Yehova ankamufunira zabwino. Kudziwa bwino ubwino wotsatira chilamulo chimenecho kunachititsa wamasalmoyo kukhala wosangalala, ngakhale anali ndi mavuto amene adani ake anam’bweretsera. Iye anadziwa kuti Yehova wamuchitira zabwino. Ndiponso, kugwiritsa ntchito malangizo a m’chilamulo cha Mulungu kunachititsa wamasalmoyo kukhala wanzeru kuposa adani ake ndipo kunateteza moyo wake. Kumvera chilamulo kunam’patsa mtendere wa mumtima ndi chikumbumtima chabwino.—Salmo 119:1, 9, 65, 93, 98, 165.
3. Kodi n’chifukwa chiyani zili zovuta kwa Akristu kuti azikhala moyo wotsatira miyezo ya Mulungu masiku ano?
3 Ena mwa atumiki a Mulungu masiku ano akukumananso ndi ziyeso zazikulu kwambiri za chikhulupiriro chawo. Mwina sitingakumane ndi chiyeso choika moyo wathu pangozi ngati mmene anachitira wamasalmoyo, koma tikukhala mu “nthawi zowawitsa.” Anthu ambiri amene timakhala nawo masiku ano sakonda zinthu zauzimu. Zolinga zawo pamoyo zimasonyeza kudzikonda ndi kukonda chuma, ndipo mtima wawo ndi wodzikuza ndi wopanda ulemu. (2 Timoteo 3:1-5) Akristu achinyamata nthawi zambiri amalimbana ndi zinthu zimene zimayesa khalidwe lawo labwino. Pa zochitika zoterozo, zikhoza kukhala zovuta kupitirizabe kukonda Yehova ndi zinthu zabwino. Kodi tingadziteteze bwanji?
4. Kodi wamasalmo anasonyeza bwanji kuti ankayamikira chilamulo cha Mulungu, ndipo kodi Akristu ayeneranso kuchita chimodzimodzi?
4 Chimene chinathandiza wamasalmoyo kuti athe kupirira mavuto amene ankakumana nawo, chinali kuthera nthawi kuphunzira chilamulo cha Mulungu ndi kusinkhasinkha za chilamulocho. Chifukwa chochita zimenezi, anayamba kuchikonda. Ndipotu, pafupifupi vesi lililonse la Salmo 119 limatchula mbali inayake ya chilamulo cha Yehova. * Masiku ano, Akristu sali pansi pa Chilamulo cha Mose, chomwe Mulungu anapatsa mtundu wakale wa Israyeli. (Akolose 2:14) Komabe, mfundo zomwe zili m’Chilamulocho zinakali zothandiza mpaka pano. Mfundo zimenezi zinalimbikitsa wamasalmo, monganso momwe zingalimbikitsire atumiki a Mulungu amene akuvutika ndi zovuta za moyo wamasiku ano.
5. Kodi ndi mbali ziti za Chilamulo cha Mose zomwe tikambirane?
5 Tiyeni tione momwe mbali zitatu zokha izi za Chilamulo cha Mose zingatilimbikitsire: lamulo lokhudza Sabata, lokhudza kukunkha, ndi loletsa kusirira. M’mbali iliyonse, tiona kuti kumvetsa mfundo zomwe zili maziko a malamulo amenewa n’kofunika kwambiri ngati tikufuna kuthana ndi mavuto amene timakumana nawo masiku ano.
Kukwaniritsa Zosowa Zathu Zauzimu
6. Kodi ndi zinthu zotani zimene anthu onse amafunikira?
6 Anthu analengedwa m’njira yoti amafunikira zinthu zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, kuti munthu akhalebe wathanzi labwino, amafunika chakudya, madzi, ndi pogona. Komabe, munthu amafunikanso kusamalira ‘zosowa zake zauzimu.’ Sangakhale ndi chimwemwe chenicheni ngati sachita zimenezo. (Mateyu 5:3, NW) Yehova ankaona kuti kukwaniritsa chosowa chimenechi kunali kofunika kwambiri moti analamula anthu ake kuti aziimitsa ntchito zawo kwa tsiku limodzi lathunthu mlungu uliwonse kuti asamalire zinthu zauzimu.
7, 8. (a) Kodi Mulungu anasiyanitsa bwanji tsiku la Sabata ndi masiku ena onse? (b) Kodi tsiku la Sabata linaikidwa n’cholinga chotani?
7 Lamulo lokhudza Sabata linagogomezera kufunika kochita zinthu zauzimu. Nthawi yoyamba imene Baibulo limatchula mawu oti “sabata” m’pamene limafotokoza za mana amene Mulungu anapereka m’chipululu. Aisrayeli anauzidwa kuti azitola mkate wozizwitsawu masiku sikisi. Patsiku la sikisi, anayenera kutola “mkate wofikira masiku awiri” chifukwa pa tsiku la seveni, sipanali kukhala mana aliwonse. Tsiku la seveni linali “Sabata lopatulika la Yehova,” lomwe aliyense anafunika kukhala kunyumba kwake. (Eksodo 16:13-30) Limodzi la Malamulo Khumi linati pa Sabata anthu asamagwire ntchito iliyonse. Tsiku limeneli linali lopatulika. Munthu amene sanasunge Sabata chilango chake chinali imfa.—Eksodo 20:8-11; Numeri 15:32-36.
8 Lamulo lokhudza Sabata linasonyeza nkhawa imene Yehova anali nayo pa moyo wakuthupi ndi wauzimu wa anthu ake. Yesu anati: “Sabata linaikidwa chifukwa cha munthu.” (Marko 2:27) Linapatsa Aisrayeli mpata wopuma komanso linawathandiza kuyandikira kwa Mlengi wawo ndi kumusonyeza chikondi. (Deuteronomo 5:12) Linali tsiku lomwe analipatula kuti pazichitika zinthu zauzimu basi. Zinthu zake zinaphatikizapo kulambirira pamodzi monga banja, kupemphera, ndi kusinkhasinkha za Chilamulo cha Mulungu. Lamulo lokhudza Sabata linateteza Aisrayeli kuti asamathe nthawi yawo yonse ndiponso mphamvu zawo zonse pofunafuna zinthu zakuthupi basi. Sabata linawakumbutsa kuti ubwenzi wawo ndi Yehova ndiwo unali chinthu chofunika kwambiri pamoyo wawo. Yesu anafotokozanso mfundo yosasintha imeneyo pamene ananena kuti: “Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.”—Mateyu 4:4.
9. Kodi lamulo lokhudza Sabata limapereka phunziro lotani kwa Akristu?
9 Anthu a Mulungu sakufunikanso kusunga sabata lenileni la maola 24 kuti azipuma, komabe lamulo lokhudza Sabata sikuti panopa ndi mbiri yakale chabe yochititsa chidwi. (Akolose 2:16) Kodi si chikumbutso choti nafenso tiyenera kuika zinthu zauzimu patsogolo? Zinthu zauzimu siziyenera kuiwalidwa chifukwa chofunafuna chuma kapena zosangalatsa. (Ahebri 4:9, 10) Choncho tingachite bwino kudzifunsa kuti: “Kodi n’chiyani chimatenga malo oyamba pamoyo wanga? Kodi ndikutsogoza kuphunzira Mawu a Mulungu, kupemphera, kupita ku misonkhano yachikristu, ndi kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu? Kapena kodi zinthu zina zikutenga malo a zinthu zimenezi?” Tikaika zinthu zauzimu patsogolo m’moyo wathu, Yehova akutitsimikizira kuti sitidzasowa zinthu zofunikira pamoyo.—Mateyu 6:24-33.
10. Kodi tingapindule bwanji chifukwa chopatula nthawi yoti tizichita zinthu zauzimu?
10 Nthawi imene timathera pophunzira Baibulo ndi mabuku ena ofotokoza za m’Baibulo, komanso kuganizira mwakuya uthenga wake, ikhoza kutithandiza kuyandikira kwa Yehova. (Yakobo 4:8) Susan, amene zaka 40 zapitazo anayamba kupatula nthawi yoti aziphunzira Baibulo nthawi zonse, akuvomereza kuti poyamba zinali zovuta. Zinali ngati kugwira ntchito yosasangalatsa. Koma ankati akamawerenga kwambiri, m’pamenenso ankasangalala nako kwambiri kuwerengako. Ndipo masiku ano amati akalephera kuphunzira payekha pa chifukwa chinachake, amadandaula. Iye akuti: “Kuphunzira Baibulo kwandithandiza kumudziwa bwino Yehova ngati Atate wanga. Ndikhoza kumukhulupirira, kumudalira, ndi kulankhula naye momasuka m’pemphero. N’zochititsadi nthumanzi kuona momwe Yehova amakondera atumiki ake, momwe amandikondera ineyo pandekha, ndi mmene wandithandizira.” Nafenso tikhoza kupeza chimwemwe chachikulu ngati tisamalira zosowa zathu zauzimu nthawi zonse.
Lamulo la Mulungu Lokhudza Kukunkha
11. Kodi malamulo okhudza kukunkha ankagwira ntchito bwanji?
11 Mbali yachiwiri ya Chilamulo cha Mose imene inasonyeza kuti Mulungu amadera nkhawa anthu ake inali yonena za ufulu wokunkha. Yehova analamula kuti mlimi wa mu Israyeli akakolola mbewu za m’munda mwake, anthu osauka aziloledwa kukunkha zinthu zimene antchito okolola asiya. Alimi sankaloledwa kukolola m’mphepete monse mwa minda yawo, ndipo sankaloledwa kukolola mphesa zotsalira m’munda kapena maolivi otsalira. Mitolo ya zokolola yomwe yaiwalidwa m’munda sinayenera kudzatengedwa. Amenewa anali malamulo achikondi othandiza anthu osauka, alendo, ana amasiye, ndi akazi amasiye. N’zoona kuti anthuwa anafunika kugwira ntchito mwakhama kuti athe kukunkha, koma chifukwa cha malamulo amenewa, akanapewa kupemphapempha.—Levitiko 19:9, 10; Deuteronomo 24:19-22; Salmo 37:25.
12. Kodi lamulo lokhudza kukunkha linapatsa alimi mwayi wotani?
12 Lamulo lokhudza kukunkha silinanene kuti alimi azisiyira anthu ovutika zokolola zochuluka bwanji. Zinali kwa iwo kusiya malo aakulu kapena aang’ono osakololedwa m’mphepete mwa minda yawo. Mwa njira imeneyi, lamuloli linawaphunzitsa kukhala owolowa manja. Linapatsa alimi mwayi wosonyeza kuyamikira kwawo Wowapatsa zokolola, popeza ‘wochitira wosauka chifundo alemekeza [Mlengi wake].’ (Miyambo 14:31) Boazi ndi munthu mmodzi amene anachita zimenezi. Iye mokoma mtima anaonetsetsa kuti Rute, mkazi wamasiye amene anakunkha m’munda mwake, akunkhe zochuluka. Yehova anadalitsa kwambiri Boazi chifukwa cha kuwolowa manja kwake.—Rute 2:15, 16; 4:21, 22; Miyambo 19:17.
13. Kodi lamulo lakale lokhudza kukunkha limatiphunzitsa chiyani?
13 Mfundo imene inali maziko a lamulo lokhudza kukunkha siinasinthe. Yehova amafuna kuti atumiki ake akhale owolowa manja, makamaka kwa anthu ovutika. Tikakhala owolowa manja kwambiri, timalandiranso madalitso ambiri. Yesu anati: “Patsani, ndipo Luka 6:38.
kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m’manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nawo inu.”—14, 15. Kodi tingasonyeze bwanji kuwolowa manja, ndipo zimenezi zingatipindulire bwanji ifeyo ndi anthu amene tawathandizawo?
14 Mtumwi Paulo anatilimbikitsa kuti “tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.” (Agalatiya 6:10) Choncho, tiyenera kudera nkhawa Akristu anzathu kuti alandire thandizo lauzimu akamakumana ndi ziyeso za chikhulupiriro chawo. Koma kodi angafunikirenso thandizo m’njira zina, monga kuwathandiza kupita ku Nyumba ya Ufumu kapena kukawagulira zinthu ku msika? Kodi mu mpingo mwanu muli anthu okalamba, odwala, kapena omwe saatha kutuluka m’nyumba zawo, omwe angayamikire mutapita kukawachezera kapena mutawathandiza m’njira inayake? Ngati timayesetsa kuchitapo kanthu tikadziwa kuti anthu ena akufunika thandizo loterolo, Yehova akhoza kutigwiritsira ntchito kuti ayankhe mapemphero a munthu wovutika. Ngakhale kuti kuthandizana ndi udindo wathu wachikristu, kuchita zimenezi kumapindulitsanso munthu wothandizayo. Kusonyeza olambira anzathu chikondi kumatibweretsera chimwemwe chachikulu, ndipo kumachititsa Yehova kusangalala nafe.—Miyambo 15:29.
15 Njira ina imene Akristu amaonetsera chikondi chenicheni ndiyo kugwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zawo pouza ena zolinga za Mulungu. (Mateyu 28:19, 20) Aliyense amene anakhalapo ndi mwayi wothandiza munthu wina kufika popereka moyo wake kwa Yehova akudziwa kuti mawu otsatirawa amene Yesu ananena, ndi oonadi. Iye anati: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.
Kupewa Kusirira
16, 17. Kodi lamulo lakhumi linaletsa chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani linatero?
16 Mbali yachitatu ya Chilamulo cha Mulungu kwa Aisrayeli imene tikambirane ndi lamulo lakhumi, lomwe linaletsa kusirira. Lamulolo linati: “Usasirire nyumba yake ya mnzako, usasirire mkazi wake wa mnzako, kapena wantchito wake wamwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng’ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.” (Eksodo 20:17) Palibe munthu amene akanaonetsetsa kuti lamulo limeneli likutsatiridwa, popeza palibe amene amatha kuona mumtima mwa munthu wina. Koma lamulo limeneli linakweza Chilamulo pamwamba pa malamulo onse a anthu. Linachititsa Mwiisrayeli aliyense kudziwa kuti adzayankha mwachindunji kwa Yehova, amene amatha kuona zomwe zili mumtima mwa munthu. (1 Samueli 16:7) Ndiponso, lamulo limeneli linafika pa muzu weniweni wa zoipa zambiri zimene anthu amachita.—Yakobo 1:14.
17 Lamulo loletsa kusirira linalimbikitsa anthu a Mulungu kupewa kukonda chuma, umbombo, ndi kudandaula ndi moyo wawo. Linawatetezanso kuti asafune kuba kapena kuchita chiwerewere. Nthawi zonse padzakhala anthu amene ali ndi katundu winawake amene timafuna titakhala naye kapena anthu amene mwanjira inayake akuoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino kuposa ifeyo. Tikapanda kulamulira maganizo athu pazochitika zoterozo, tikhoza kukhala opanda chimwemwe n’kumalakalaka zimene ena ali nazo. Baibulo limati kusirira kumasonyeza “mtima wokanika,” kapena kuti, maganizo oipa. Ndi bwino kupewa mtima woterowo.—Aroma 1:28-30.
18. Kodi ndi mzimu wotani umene uli m’dzikoli masiku ano, ndipo ungatulutse zotsatira zoipa zotani?
18 Mzimu umene uli m’dzikoli masiku ano umalimbikitsa kukonda chuma ndi kupikisana. Potsatsa malonda awo, anthu amalonda amatichititsa kulakalaka zinthu zatsopano ndipo nthawi zambiri uthenga umene amapereka ndi woti sitingakhale osangalala tikapanda kukhala ndi zinthu zimenezo. Umenewu ndiwo mtima umene Chilamulo cha Yehova chinaletsa. Mtima wina wofanana ndi umenewo ndiwo wofuna kuti zinthu zitiyendere bwino m’moyo mwa njira iliyonseyo, ndiponso kudzikundikira chuma. Mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko. Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.”—1 Timoteo 6:9, 10.
19, 20. (a) Kwa munthu wokonda chilamulo cha Yehova, kodi ndi zinthu ziti zimene zilidi zofunika kwambiri? (b) Kodi nkhani yotsatira ifotokoza chiyani?
19 Anthu amene amakonda chilamulo cha Mulungu amadziwa kuopsa kwa mtima wokonda chuma ndipo amatetezedwa ku mtima umenewu. Mwachitsanzo, wamasalmo anapemphera kwa Yehova kuti: “Lingitsani mtima wanga ku mboni zanu, si ku chisiriro ayi. Chilamulo cha pakamwa panu chindikomera koposa golidi ndi siliva zikwizikwi.” (Salmo 119:36, 72) Kukhulupirira kuti mawu amenewa ndi oonadi kungatithandize kuchita zinthu mwanzeru n’kupewa msampha wokonda kwambiri chuma, umbombo, ndi kusakhutiritsidwa ndi moyo wathu. “Kudzipereka kwa Mulungu,” osati kudzikundikira katundu, ndiko kumabweretsa phindu lalikulu koposa zonse.—1 Timoteo 6:6, NW.
20 Mfundo zomwe zinali maziko a Chilamulo chomwe Yehova anapatsa mtundu wakale wa Israyeli n’zothandiza m’masiku athu ovuta ano ngati momwe zinalili pamene Yehova anapereka Chilamulocho kwa Mose. Tikamatsatira kwambiri mfundo zimenezi pamoyo wathu, m’pamenenso tingazimvetse bwino kwambiri, ndipo m’pamenenso tingazikonde kwambiri. Tikatero, m’pamenenso tingakhale achimwemwe kwambiri. Chilamulo chili ndi maphunziro ambiri ofunika kwa ife, ndipo timakumbutsidwa bwino kwambiri za kufunika kwa maphunziro amenewa tikamaona moyo wa anthu otchulidwa m’Baibulo ndi zimene zinawachitikira. Zina mwa zimenezi tiziona mu nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 Mwa mavesi onse 176 a salmo limeneli, ndi mavesi anayi okha amene satchulapo malamulo, maweruzo, chilamulo, malangizo, malemba, mawu, kapena njira za Yehova.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• N’chifukwa chiyani munthu amene analemba Salmo 119 anakonda chilamulo cha Yehova?
• Kodi Akristu angaphunzire chiyani kuchokera ku lamulo lokhudza Sabata?
• Kodi lamulo la Mulungu lokhudza kukunkha lili ndi phindu losatha lotani?
• Kodi lamulo loletsa kusirira limatiteteza bwanji?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 21]
Kodi lamulo lokhudza Sabata linagogomezera chiyani?
[Chithunzi patsamba 23]
Kodi lamulo lokhudza kukunkha limatiphunzitsa chiyani?