Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chimwemwe Chanu N’chochuluka Motani?

Kodi Chimwemwe Chanu N’chochuluka Motani?

Kodi Chimwemwe Chanu N’chochuluka Motani?

INDE, mukhoza kudzifunsa funso lakuti, ‘Kodi chimwemwe changa n’chochuluka motani?’ Asayansi ophunzira za khalidwe la anthu akuyesera kupeza momwe inuyo kapena anthu ena angayankhire funso limenelo, koma ntchito yawo ndi yovuta. Kuyesera kuyeza kuchuluka kwa chimwemwe cha munthu kuli ngati kuyesera kuyeza kuchuluka kwa chikondi chimene mwamuna ali nacho pa mkazi wake kapena kuchuluka kwa chisoni chimene munthu angakhale nacho chifukwa cha imfa ya wachibale wake. N’zovuta kuyeza mmene munthu akumvera mumtima. Komabe, asayansi akudziwa mfundo imodzi yofunika, iyi: Anthu onse akhoza kukhala achimwemwe.

Ngakhale kuti anthu analengedwa m’njira yoti akhoza kukhala achimwemwe, kuchuluka kwa mavuto kwachititsa kuti anthu ambiri akhale opanda chimwemwe. Taganizirani chitsanzo ichi: M’mizinda ina, anthu omwalira ndi Edzi achuluka kwambiri moti manda adzaza. Akuluakulu a boma akufukula manda akale kuti aziikamo anthu amene akumwalira kumene. M’madera ena a ku Africa kuno, ntchito imene anthu ambiri ayamba kugwira ndi yopanga mabokosi a maliro. Ndipo kaya mumakhala kuti, mwaona kuti anthu amene akudwala matenda aakulu ndiponso amene achibale awo ndi anzawo amwalira sakhala achimwemwe.

Nanga bwanji m’mayiko olemera? Zinthu zikasintha, anthu amene sanakonzekere akhoza kuluza chuma chawo chonse mwadzidzidzi. Ku United States, anthu ambiri amene anapuma pantchito ayambiranso ntchito chifukwa choti sakupatsidwa penshoni. Nthawi zambiri, ndalama zimene banja linali nazo zimathera kuchipatala. Mlangizi wina wa zamalamulo anati: “Ndimaona anthu akubwera kuno ali ndi ngongole zambiri komanso ali ndi thanzi lofooka, ndipo zimandimvetsa chisoni kwambiri. Nthawi zambiri ndimafunika kuwauza kuti ‘Mufunikatu kugulitsa nyumba yanu.’” Koma bwanji za anthu amene alibe nkhawa iliyonse ya zachuma? Kodi nawonso akhoza kukhala opanda chimwemwe?

Anthu ena ali ngati wolemba nyimbo wina wotchuka dzina lake Richard Rodgers. Ponena za iyeyu, ena anati: “Ndi anthu ochepa amene anasangalatsa anthu ambiri ngati mmene anachitira iyeyu.” Ngakhale kuti nyimbo zake zinabweretsera anthu ambiri chimwemwe, Richard Rodgers nthawi zonse ankadwala matenda ovutika maganizo. Anakwanitsa kupeza zinthu ziwiri zimene anthu ambiri amafuna, zomwe ndi ndalama ndi kutchuka. Koma kodi anapezanso chimwemwe? Munthu wina wolemba mbiri za anthu anati: “[Rodgers] zinthu zinamuyendera bwino kwambiri pa ntchito yake, anali ndi moyo wapamwamba, ndipo kawiri konse iye limodzi ndi mnzake anapatsidwa mphoto inayake yapadera chifukwa cha luso lawo. Komanso nthawi zambiri anali wopanda chimwemwe ndipo ankadwala matenda ovutika maganizo.”

N’kutheka kuti mwaonapo kuti kuganiza kuti chuma chingabweretse chimwemwe, nthawi zambiri n’kungodzinyenga. Mtolankhani wina wa nkhani zachuma amene analemba nkhani yake mu nyuzipepala ya The Globe and Mail ya ku Toronto, ku Canada, anafotokoza kuti anthu ambiri olemera “amakhala osungulumwa ndiponso amaona kuti moyo wawo ulibe cholinga.” Malinga ndi zimene ananena mlangizi wina wa zachuma, makolo olemera akamapatsa ana awo ndalama ndi mphatso zochuluka, “nthawi zambiri amakhala akuyala maziko oti anawo adzakhale opanda chimwemwe m’tsogolo.”

Kodi Pali Chilichonse Chimene Chingabweretse Chimwemwe?

Kuti chomera chikule bwino, chimafuna dothi labwino, madzi, ndi nyengo yabwino. Mofanana ndi zimenezi, ochita kafukufuku azindikira kuti zinthu zinazake zimabweretsa chimwemwe. Zinthu zake ndi monga thanzi labwino; ntchito yabwino; chakudya, pogona, ndi zovala zokwanira; kukwanitsa kuchita zinthu zimene umalakalaka; ndi kukhala ndi anzako enieni.

Mosakayikira simungatsutse zoti zinthu zimenezi zimathandiziradi kuti munthu akhale wachimwemwe. Koma pali chinthu chinanso chofunika kwambiri. Chinthu chake ndicho kudziwa “Mulungu wachimwemwe,” amene dzina lake ndi Yehova. (1 Timoteo 1:11, NW) Kodi kudziwa zimenezo kumatithandiza bwanji? Yehova ndi Mlengi wathu, ndipo anatilenga m’njira yoti tizitha kukhala achimwemwe. N’zosachita kufunsa kuti amadziwa zinthu zimene zingatichititse kukhaladi achimwemwe. Nkhani yotsatirayi ifotokoza njira imene amagwiritsa ntchito kuti athandize anthu kulikonse ndiponso a moyo uliwonse kukhala ndi chimwemwe chosatha.

[Chithunzi patsamba 4]

Mofanana ndi chomera, chimwemwe chimafuna kuti pakhale zinthu zinazake zoyenerera kuti chikule

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

© Gideon Mendel/​CORBIS