Kodi TV ndi Njira Yabwino Yolerera Ana?
Kodi TV ndi Njira Yabwino Yolerera Ana?
NTHAWI zina kusiya ana anu akuonerera TV inu n’kumagwira ntchito zanu kumaoneka ngati njira yothandiza. Koma kodi zimenezi zingakhudze bwanji ana anu?
Nyuzipepala ya The New York Times inati: “Ngakhale ana ang’onoang’ono amatengera zinthu zokhudza mtima zomwe amaona pa TV.” Pa kafukufuku winawake waposachedwapa, ana a chaka chimodzi anaonetsedwa zithunzi zinazake kwa kanthawi kochepa pa TV. Ankawaonetsa zithunzi za mzimayi akusewera ndi chidole m’njira zosiyanasiyana. Nyuzipepalayo inati: “Mzimayiyo akamaopa chidole chinachake, anawo sankafuna kuchiseweretsa ndipo nthawi zambiri ankaoneka ankhawa, ankachita tsinya, ankaipitsa nkhope, kapena ankalira. Mkaziyo akamasangalala kwambiri ndi chidolecho, anawo nthawi zambiri ankafuna kusewera nacho.”
N’zachionekere kuti TV imakhudza ana. Nanga kodi pakapita nthawi imawakhudza motani anawo? Dr. Naoki Kataoka, pulofesa wa matenda a ana pa koleji yophunzitsa zachipatala ya Kawasaki mu mzinda wa Kurashiki, ku Japan, waonapo ana ambiri amene amangokhala phe osalankhula ndipo pankhope pawo sipasonyeza chilichonse. Onsewa anali oti anakhala akuonerera TV kapena mavidiyo kwa nthawi yaitali. Panali mwana wina wamwamuna wa zaka ziwiri amene sankatha kucheza ndi anthu ndipo sankadziwa mawu ambiri. Ankaonerera mavidiyo kuyambira m’mawa mpaka madzulo tsiku lililonse kuyambira ali ndi chaka chimodzi. Mayi ake analangizidwa ndi dokotalayu kuti asiye kumuonetsa mavidiyo ndipo ayambe kumasewera naye. Atayamba kuchita zimenezi m’pamene mnyamatayu, pang’ono ndi pang’ono, anayamba kudziwa mawu ambiri. Indedi, makolo ayenera kuchitira limodzi zinthu ndi ana awo.
Yehova Mulungu, amene anayambitsa banja, anasonyeza bwino amene ali woyenera kwambiri kuchitira zinthu limodzi ndi ana. Kalelo anauza anthu ake kuti: “[Mawu a Mulungu ] muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” (Deuteronomo 6:7) Makolo, osati TV, ndi amene angaphunzitse bwino kwambiri ana. Mwa zonena zawo ndi chitsanzo chawo, angawaphunzitse “njira” yawo.—Miyambo 22:6.