Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuwonjezeka kwa Mboni Pakati pa Anthu Osiyanasiyana a ku Uganda

Kuwonjezeka kwa Mboni Pakati pa Anthu Osiyanasiyana a ku Uganda

Kuwonjezeka kwa Mboni Pakati pa Anthu Osiyanasiyana a ku Uganda

DZIKO la Uganda ndi lokongola kwambiri. Lili pakati pa mbali yakum’mawa ndi yakumadzulo ya chigwa chachikulu chomwe chili kum’mawa kwa Africa. Dzikoli likupezeka mbali zonse ziwiri za mzera wongoyerekezera umene unagawa dziko lapansi kukhala chigawo chakumpoto ndi chakum’mwera. Lili ndi mapiri, nyanja, mitsinje, zomera zamitundumitundu, ndi zinyama zochititsa chidwi. Lili pa dera lokwera la ku Africa, ndipo lili ndi nyengo yabwino ndi mapiri ochititsa chidwi amene anayala dera lalikulu kwambiri.

Mbali ina ya dziko la Uganda n’kozizira kwambiri moti mpaka madzi amaundana, pamene mbali ina n’kotentha kwambiri. Ndi mayiko ochepa okha amene amakhala ndi nyengo yosiyana kwambiri chonchi. Dzikoli limayambira ku mapiri okutidwa ndi chipale chofewa otchedwa mapiri a Mwezi, kapena kuti mapiri a Ruwenzori kumadzulo, kufika ku chipululu kum’mawa. M’zigwa zake muli njovu, njati, ndi mikango. M’mapiri ndi m’nkhalango mowirira muli mitundu yosiyanasiyana ya anyani akuluakulu ndi mbalame za mitundu yosiyanasiyana yokwana 1,000. Mayiko ambiri a mu Africa amavutika ndi chilala ndi njala, koma dziko la Uganda n’lodala chifukwa lili ndi mitsinje ndi nyanja, monga nyanja ya Victoria, yomwe ndi nyanja yachiwiri kwa nyanja yaikulu kwambiri padziko lonse yokhala ndi madzi opanda mchere. Madzi amene amatulukira kumpoto kwa nyanja ya Victoria amakatsira mu mtsinje wa Nile. N’zosadabwitsa kuti mtsogoleri wina wa dziko la Britain, dzina lake Winston Churchill, anati dziko limeneli ndi “ngale ya Africa”!

‘Ngaleyo’ Ikunyezimira Masiku Ano

Koma chimene chimasangalatsa kwambiri ku Uganda ndi anthu ake. Ndi ochezeka, ochereza alendo, ndiponso kuli mafuko osiyanasiyana. Dzikoli, limene amati n’lachikristu, muli magulu a anthu osiyanasiyana ndi zikhalidwenso zosiyanasiyana. Ngakhale masiku ano, anthuwa ungathe kuwasiyanitsa chifukwa cha miyambo yawo ndi kavalidwe kawo.

Chaposachedwapa, anthu ambiri a ku Uganda ayamba kumvera uthenga wabwino wa m’Baibulo wonena za nthawi imene padziko lapansi padzakhala mtendere wosatha. (Salmo 37:11; Chivumbulutso 21:4) N’zovuta kufikitsa uthenga umenewu kwa anthu onse a m’dziko la Uganda, lomwe n’lalikulu pafupifupi kufanana ndi dziko la Great Britain.

Kuyambira ndi chiyambi chochepa pamene munthu woyamba wa m’dzikoli anabatizidwa m’nyanja ya Victoria mu 1955 monga Mboni ya Yehova yodzipereka, “wamng’ono” anasanduka chikwi mu 1992. Kuyambira pamenepo, pakhala kuwonjezeka kokhakokha. Zimenezi zikugwirizana ndi mawu a Mulungu olimbikitsa akuti: “Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthawi yake.”​—Yesaya 60:22.

Kuthana ndi Vuto Losiyana Zinenero

Chingelezi ndicho chinenero chaboma ndipo chimagwiritsidwa ntchito kwambiri, makamaka m’masukulu, komabe si chinenero choyamwira cha anthu ambiri a ku Uganda. Choncho, pofuna kuuza anthu uthenga wabwino, Mboni za Yehova zimagwiritsanso ntchito zinenero zina zikuluzikulu. Zimenezi n’zothandiza, chifukwa choti anthu oposa 80 pa anthu 100 alionse m’dzikoli, momwe muli anthu 25 miliyoni, amakhala kumidzi kapena m’matawuni aang’ono. M’madera amenewa anthu amalankhulitsana m’chinenero chawo choyamwira. Kufikira anthu olankhula zinenero zimenezi ndi kuwakhutiritsa mwauzimu kumafuna khama lalikulu.

Ngakhale ndi choncho, Mboni za Yehova zayesetsa kukwanitsa zimenezi mwa kulalikira kwa anthuwo m’chinenero chawo ndi kutulutsa mabuku ofotokoza za m’Baibulo m’zinenero zosiyanasiyana. Ku ofesi ya nthambi ku Kampala, lomwe ndi likulu la dzikoli, kuli magulu omasulira mabuku m’zinenero zinayi: Chiacholi, Chilukonzo, Chiluganda, ndi Chirunyankore. Ndiponso, ku misonkhano yadera yachikristu yomwe yachitika m’zinenero zosiyanasiyana m’dziko lonseli kwakhala kukubwera anthu ambiri zedi, oposa kuwirikiza kawiri chiwerengero cha Mboni za Yehova ku Uganda. Zimenezi zikusonyeza bwino kuti ntchito yoyesetsa kulalikira anthu olankhula zinenero zosiyanasiyana ikuchititsa kuti pakhale kuwonjezeka kwamsanga kwauzimu. Koma si zokhazi zimene zikuchititsa kuwonjezeka kumeneku.

Apainiya Akutsogolera Ntchito Yolalikira

Mipingo imachirikiza mosangalala ntchito yapadera ya chaka ndi chaka ya miyezi pafupifupi itatu, pamene amakalalikira ku madera akutali. (Machitidwe 16:9) Apainiya achinyamata achangu, kapena kuti alaliki a nthawi zonse, amene akumka nawonjezereka, ndi amene akutsogolera ntchito imeneyi. Amapita ku madera akutali, kumene nthawi zina uthenga wabwino umakhala woti sunalalikidweko.

Mboni ziwiri zinaikidwa kukhala apainiya apadera kwa miyezi itatu ku Bushenyi, yomwe ndi tawuni yaing’ono kumadzulo kwa Uganda. Iwo limodzi ndi Mboni imodzi yokha ya Yehova yomwe inali kukhala m’deralo, anagwira ntchito yolalikira ndi kukonza misonkhano yachikristu. Pomatha mwezi, apainiya awiriwo anali kuchititsa maphunziro a Baibulo nthawi zonse ndi anthu 40, ndipo 17 mwa amenewa anayamba kubwera ku misonkhano ya Mboni za Yehova. Apainiyawo anati: “Anthu ena amene tinawasiyira kabuku kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? * anabwera kunyumba kwathu patatha masiku ochepa atanyamula mapepala angapo. Pa mapepalawo analembapo mayankho a mafunso a m’kabukuka. Ankafuna kudziwa ngati mayankho awowo anali olondola.” Lero, m’tawuni imeneyi muli mpingo womwe uli ndi Nyumba ya Ufumu yakeyake.

Apainiya awiri anapita kudera lina kumadzulo kwa Uganda kumene uthenga wabwino unali usanalalikidweko. Analemba kuti: “Anthu kuno alidi ndi ludzu la choonadi cha m’Baibulo. Pa miyezi itatu imene takhala kuno, tayambitsa ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo 86.” Sipanapite nthawi yaitali kuti kudera limenelo akhazikitseko kagulu ka Mboni.

Antchito Enanso Achangu M’munda

Pakati pa apainiya achanguwa pali ena amene atumikira kwa zaka zingapo. Patrick asanakhale wa Mboni za Yehova, ankaimba chida chinachake chokhala ngati chitoliro mu bandi ya asilikali apandege a Idi Amin, mtsogoleri wa dziko la Uganda. Patrick anabatizidwa mu 1983 ndipo patatha miyezi sikisi chibatizidwireni, anakhala mtumiki wa nthawi zonse. Panopa Patrick ndi woyang’anira woyendayenda, ndipo amayendera ndi kulimbikitsa mipingo.

Margaret anabatizidwa mu 1962. Ngakhale kuti ali ndi zaka za m’ma 70 ndipo amavutika kuyenda chifukwa chodwala mwendo, amatha maola 70 mwezi uliwonse akuuza anansi ake uthenga wa chiyembekezo wochokera m’Baibulo. Amaika mabuku pa benchi panja pa nyumba yake ndipo amacheza ndi munthu aliyense wodutsa amene akufuna kumva uthenga wabwino wa dziko latsopano lamtendere.

Simon, mlimi wa kum’mawa kwa dziko la Uganda anakhala akufunafuna choonadi kwa zaka 16. Ndiyeno mu 1995, anapeza mabuku ena ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Zomwe anawerenga zinamuchititsa kufuna kudziwa zambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu ndi cholinga chabwino kwambiri cha Yehova chokhudza dziko lapansi. Ku Kamuli komwe ankakhala kunalibe Mboni, choncho Simon anayenda ulendo wa makilomita pafupifupi 140 kupita ku Kampala kuti akafunefune Mbonizo. Lero, m’mudzi wawo muli mpingo.

“Takhazikika Kuno”

Monga mmene zilili m’madera ena a ku Africa kuno, anthu ambiri amayembekezera gulu lachipembedzo kukhala ndi malo abwino opempherera. Limeneli linali vuto lalikulu kwa mipingo ina ya Mboni za Yehova, chifukwa inalibe ndalama zoti ingamangire Nyumba ya Ufumu yabwino. Abalewo anachita kulephera kuthokoza pamene kumapeto kwa chaka cha 1999, padziko lonse lapansi panakhazikitsidwa dongosolo lomanga Nyumba za Ufumu mwachangu. Pa zaka zisanu zotsatira, Nyumba za Ufumu 40 zinamangidwa ku Uganda. Masiku ano, pafupifupi mipingo yonse ili ndi Nyumba ya Ufumu yawoyawo yooneka bwino. Uthenga umene ntchito yomangayi ikupereka kwa anthu okhala m’madera amenewo ndi woti “Takhazikika kuno.” Zimenezi zathandizira kuti Mboni zichuluke.

Mpingo wina waung’ono kumpoto kwa Uganda unkachitira misonkhano pansi pa mitengo ya mango ya masamba ambiri. Utapeza malo, ntchito inagwirika mofulumira. Abale omanga, limodzi ndi Mboni za m’deralo, anayamba kumanga Nyumba ya Ufumu. Munthu wina amene kale anali wandale wotchuka m’deralo anachita chidwi ndi ntchitoyo. Anauza abalewo kuti akhoza kumachitira misonkhano m’galaja mwake mpaka Nyumba ya Ufumuyo idzathe kumangidwa. Anavomeranso kuti aziphunzira Baibulo ndi mmodzi mwa anthu omangawo. Tsopano ndi wofalitsa wobatizidwa wachangu, ndipo ndi wosangalala kulambirira Yehova m’Nyumba ya Ufumu yokongolayo.

Pa malo ena pamene panali kumangidwa Nyumba ya Ufumu kum’mwera chakum’mawa kwa dzikoli, munthu wina wodziwa ntchito yomanga anakhudzidwa kwambiri ndi mzimu waubwenzi, chikondi ndi mgwirizano umene anaona pakati pa abalewo moti anadzipereka kuti athandize nawo pantchitoyo. Chakumapeto kwa ntchitoyo, anagwira nawo ntchito usiku wonse kuti m’mawa wotsatira Nyumba ya Ufumuyo ikhale itatha kuti iperekedwe kwa Mulungu. Iye anati: “Ndinu nokha amene mumakondanadi, osati kukondana ndi mawu okha.”

Mboni Zikuchulukabe, Ngakhale Pali Mavuto

Popeza magawo atsopano akulalikidwa ku Uganda, chiwerengero cha Mboni chikukwera nthawi zonse, ndipo anthu ambiri achidwi akusonkhana m’mipingo. Komabe, vuto limene panopa likudetsa nkhawa ndi lokhudza anthu ambiri othawa kwawo amene athawira ku Uganda. Nkhondo zapachiweniweni m’mayiko oyandikana nawo zakhudzanso anthu a Yehova. Mboni zomwe zili m’misasa ya anthu othawa kwawo zasonyeza chikhulupiriro cholimba mwa Yehova. Munthu wina amene anali ndi udindo wapamwamba m’dziko lapafupi ndi Uganda, amene anazunzapo Mboni pamene zinali zoletsedwa m’dziko lakwawolo, anafotokoza za moyo wabwino umene anali nawo kale. Ataphunzira Baibulo mu msasa wina wa anthu othawa kwawo n’kukhala Mboni, iye anati: “Chuma ndi udindo wapamwamba m’dzikoli zilibe phindu lenileni. Ngakhale kuti panopa ndine wosauka ndiponso ndikudwala, moyo wanga sunakhalepo wabwino ngati mmene ulili panopa. Ndamudziwa Yehova, ndipo ndimathokoza mwayi womwe ndili nawo wopemphera kwa iye. Kuwonjezera pa kukhala ndi chiyembekezo cholimba cha m’tsogolo, ndikudziwa chifukwa chomwe tikuzunzikira ndi mavuto masiku ano. Choncho ndili ndi mtendere wa mumtima womwe sindinakhalepo nawo.”

Pali mawu oti ngati uzika ndodo madzulo m’dothi la ku Uganda, lomwe ndi lachonde kwambiri, pofika m’mawa imakhala itamera mizu. Kuwonjezeka kwauzimu komwe kukuchitika m’dzikoli kukusonyeza kuti dothi lauzimu nalonso n’lachonde kwambiri. Tikuthokoza Yehova Mulungu chifukwa chopereka nthawi yoti anthu enanso osiyanasiyana a ku Uganda aphunzire za Ufumu. Yesu anati Ufumuwu ndi wamtengo wosayerekezeka mofanana ndi “ngale imodzi ya mtengo wapatali.” Anthu ambiri a ku Uganda akufika pomvetsetsa zimenezo.​—Mateyu 13:45, 46.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mapu patsamba 8]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

SUDAN

UGANDA

Mtsinje wa Nile

Kamuli

Tororo

Kampala

Bushenyi

Nyanja ya Victoria

KENYA

TANZANIA

RWANDA

[Chithunzi patsamba 9]

Atatu mwa apainiya ambiri achangu

[Chithunzi patsamba 10]

Patrick

[Chithunzi patsamba 10]

Margaret

[Chithunzi patsamba 10]

Simon

[Chithunzi patsamba 10]

Msonkhano wachigawo ku Tororo

[Mawu a Chithunzi patsamba 8]

Background: © Uganda Tourist Board