Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene anauza Nikodemo kuti: “Kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera Kumwamba, ndiye Mwana wa munthu”?—Yohane 3:13.
Yesu panthawi imeneyi anali padziko lapansi, ndipo anali asanakwere, kapena kuti, kubwerera kumwamba. Komabe, zimene tikudziwa zokhudza Yesu ndiponso nkhani imene anali kukamba zingatithandize kudziwa tanthauzo la zimene anali kunena.
Yesu ‘anatsika kuchokera kumwamba’ popeza kale ankakhala kudziko la mizimu ndi Atate ake, koma panthawi yoikidwa, moyo wa Mwanayo unasamutsidwira m’mimba mwa Mariya, zomwe zinachititsa kuti Yesu abadwe ngati munthu. (Luka 1:30-35; Agalatiya 4:4; Ahebri 2:9, 14, 17) Pambuyo pa imfa yake, Yesu anadzaukitsidwa monga cholengedwa chauzimu ndipo anapita kukakhalanso ndi Yehova. N’chifukwa chake atatsala pang’ono kuphedwa, Yesu anapemphera kuti: “Atate Inu, lemekezani Ine ndi Inu nokha ndi ulemerero umene ndinali nawo ndi Inu lisanakhale dziko lapansi.”—Yohane 17:5; Aroma 6:4, 9; Ahebri 9:24; 1 Petro 3:18.
Panthawi imene Yesu analankhula ndi Nikodemo, yemwe anali Mfarisi ndi mphunzitsi mu Israyeli, Yesuyo anali asanabwerere kumwamba. Ndiponso palibe munthu wina aliyense amene anafapo n’kukwera kudziko la mizimu, kumwamba. Yesu mwiniwakeyo anati Yohane Mbatizi anali mneneri wa Mulungu wabwino kwambiri, koma ‘wochepa mu Ufumu wa Kumwamba anali wamkulu kwa’ Yohaneyo. (Mateyu 11:11) Ndipo mtumwi Petro anafotokoza kuti ngakhale Mfumu Davide yokhulupirika inafa ndipo inali ikadali m’manda mwake. Davide sanakwere kumwamba. (Machitidwe 2:29, 34) Panali chifukwa chimene anthu amene anafa Yesu asanafe, monga Davide, Yohane Mbatizi, ndi amuna ena okhulupirika, sanapitire kumwamba. Anafa Yesu asanatsegule njira, kapena mwayi woti anthu aziukitsidwira ku moyo wakumwamba. Mtumwi Paulo analemba kuti Yesu, monga kalambulabwalo, anakonza “njira yatsopano ndi yamoyo” yolowera kumwamba.—Ahebri 6:19, 20; 9:24; 10:19, 20.
Popeza Yesu anali asanafe ndi kuukitsidwa, kodi anatanthauza chiyani ponena kwa Nikodemo kuti: “Kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera Kumwamba, ndiye Mwana wa munthu”? (Yohane 3:13) Taganizirani nkhani yomwe Yesu anali kukambirana ndi Nikodemo.
Mtsogoleri wa Ayuda ameneyo atabwera kwa Yesu usiku, Yesu anamuuza kuti: “Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu.” (Yohane 3:3) Nikodemo anamufunsa kuti: ‘Zimenezo zingatheke bwanji? Munthu angabadwe bwanji kachiwiri?’ Iye sanamvetse chiphunzitso cha Mulungu chimenechi chokhudza kukhala mu Ufumu wa Mulungu. Kodi panali njira iliyonse imene akanaphunzirira zimenezi? Kudzera mwa nzeru za anthu sakanatha. Palibe munthu amene akanamuphunzitsa zimenezi chifukwa palibe amene anakhalapo kumwamba kuti athe kufotokoza chilichonse chokhudza kulowa mu Ufumu. Yesu yekha ndi amene anali osiyana ndi ena onse. Iye akanatha kuphunzitsa Nikodemo ndi anthu ena chifukwa anatsika kumwamba ndipo anali woyeneretsedwa kuphunzitsa anthu zinthu zimenezi.
Funso la pavesi limeneli likusonyeza bwino mfundo yofunika kwambiri pophunzira Mawu a Mulungu. Sipomveka kukhumudwa ndi vesi linalake chifukwa choti likuoneka lovuta kumvetsa. Zimene Baibulo limanena pa vesi linalake ziyenera kuyerekezeredwa ndi mbali zina za Baibulo ndipo ziyenera kugwirizana. Komanso, nthawi zambiri zomwe zinali kuchitika m’vesilo, kapena nkhani imene inali kukambidwa, zikhoza kutithandiza kupeza tanthauzo lomveka la vesi lozunguza mutu.