Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Malangizo Odalirika Opezera Chimwemwe

Malangizo Odalirika Opezera Chimwemwe

Malangizo Odalirika Opezera Chimwemwe

“KUFUNAFUNA Chimwemwe” ndi ufulu wa anthu onse. Amenewo anali maganizo a anthu amene analemba Chikalata cholengeza za ufulu wa dziko la United States of America. Koma kufunafuna chinachake n’kosiyana ndi kuchipeza. Ngakhale kuti achinyamata ambiri amayesetsa kuti adzakhale akatswiri pa zosangalatsa ndi zamasewera, kodi mukudziwapo angati amene akwanitsadi kukhala otchuka ngati mmene ankafunira? Woimba wina wotchuka amene akudziwa bwino mmene zimavutira kuti munthu atchuke pa zoimbaimba anati: “Mwina zinthu sizidzakuyenderani n’komwe.”

Ngati mumaona kuti zinthu zimakhalanso choncho pofuna kupeza chimwemwe, pali chifukwa chabwino choti musatayire mtima. Mukamafunafuna chimwemwe m’njira yoyenerera, mudzachipeza. N’chifukwa chiyani tikutero? Nkhani yapitayi inakambapo za “Mulungu wachimwemwe,” Yehova. (1 Timoteo 1:11, NW) M’Baibulo, Mulungu anapereka malangizo n’cholinga choti mukamafunafuna chimwemwe musagwiritsidwe fuwa lamoto. Yehova angakuthandizeni kuthana ndi zinthu zimene nthawi zambiri zimabweretsa chisoni. Mwachitsanzo, taganizirani momwe iye amakulimbikitsirani munthu amene munali kumukonda akamwalira.

Munthu Amene Munali Kumukonda Akamwalira

Kodi tinganene chabwino chilichonse chokhudza imfa? Imfa imalanda makolo ana, ndipo imalanda ana makolo. Imalekanitsa mabwenzi okondana kwambiri ndipo imachititsa anthu ogwirizana a m’dera limodzi kuona kuti ndi osatetezeka. Wina akamwalira, banja limene linali lachimwemwe likhoza kukhala ndi chisoni chosaneneka.

Simukuchita kufunikira winawake kuti akuuzeni kuti imfa ndi chinthu chomvetsa chisoni. Koma anthu ena savomereza zimenezo ndipo amanena zinthu zosonyeza kuti imfa ndi dalitso. Taganizirani zomwe zinachitika mphepo yamkuntho ya Katrina itakantha gombe la Gulf of Mexico mu August 2005. Pa maliro a munthu wina amene anaphedwa ndi mphepo yamkunthoyi, mtsogoleri wina wachipembedzo anati: “Katrina sanaphe munthuyu. Mulungu wamuitana kuti apite kumwamba.” Panthawi ina, munthu wina wogwira ntchito m’chipatala amene ankaona ngati akutonthoza mtsikana winawake anauza mtsikanayo kuti asadandaule, chifukwa Mulungu watengera mayi ake kumwamba. Mtsikanayo analira kuti: “Chifukwa chiyani? N’chifukwa chiyani wandilanda mayi anga?”

N’zachionekere kuti maganizo olakwika oterowo okhudza imfa nthawi zambiri satonthoza anamfedwa. Chifukwa chiyani? Chifukwa choti maganizo amenewa sanena zoona zenizeni zokhudza imfa. Ndipo kuipa kwina koposa pamenepa n’koti, maganizowa amasonyeza kuti Mulungu amachotsa anthu kwa mabanja awo ndi anzawo amene anali kuwakonda, m’njira yankhanza ndi yopweteka. M’malo mokhala wotonthoza, Mulungu amaoneka ngati woipa amene amabweretsa imfa. Koma Mawu a Mulungu amanena zoona zake zokhudza imfa.

Baibulo limati imfa ndi mdani. Limayerekezera imfa ndi mfumu imene yalamulira anthu. (Aroma 5:17; 1 Akorinto 15:26) Imfa ndi mdani wamphamvu kwambiri moti palibe munthu amene angalimbane nayo, ndipo munthu wokondedwa aliyense amene wamwalira ndi wongowonjezera pa anthu osawerengeka amene atengedwa ndi imfa. Mfundo yoona ya m’Baibulo imeneyi ikufotokoza bwino chisoni ndi kusowa chochita komwe timamva munthu amene tinali kumukonda akamwalira. Imasonyeza kuti kumva choncho n’chinthu chachibadwa. Komabe, kodi Mulungu amagwiritsa ntchito mdani wathu imfa kuti apititse okondedwa athu kumwamba? Tiyeni tilole Baibulo liyankhe funso limeneli.

Lemba la Mlaliki 9:5, 10 limati: “Akufa sadziwa kanthu bi . . . Mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda uli kupitako.” M’manda, akufa sachita kalikonse. Sasuntha, samva, ndiponso saganiza chilichonse. Amakhala ngati ali m’tulo tatikulu. Choncho Baibulo limasonyeza momveka bwino kuti Mulungu satenga okondedwa athu amene amwalira kuti akakhale nawo kumwamba. Imfa imawachititsa kukhala opanda moyo m’manda.

Yesu anasonyeza kuti zimenezi n’zoona atamwalira Lazaro, yemwe anali mnzake. Yesu anayerekezera imfa ndi tulo. Lazaro akanakhala kuti anapita kumwamba kukakhala ndi Mulungu Wamphamvuyonse, sikukanakhala kukoma mtima kuti Yesu amubweretsenso padziko lapansi pano kuti pamapeto pake adzafenso. Nkhani youziridwayo imati kumandako, Yesu ananena ndi mawu okweza kuti: “Lazaro, tuluka.” Nkhani ya m’Baibuloyo imapitiriza kuti: “Ndipo womwalirayo anatuluka.” Lazaro anayambiranso kukhala ndi moyo. Yesu anadziwa kuti Lazaro sanachoke padziko lapansi pano kupita kwina. Anali wakufa m’manda.​—Yohane 11:11-14, 34, 38-44.

Nkhani imene inalembedwa m’Baibuloyi imatithandiza kumvetsa kuti imfa si njira imene Mulungu amagwiritsa ntchito kusamutsira anthu padziko lapansi pano kupita nawo kumwamba. Choncho tikhoza kumukonda Mulungu, podziwa kuti si iyeyo amene watibweretsera chisoni. Tikhozanso kukhulupirira kuti amamvetsa kwambiri chisoni ndi chisokonezo chimene mdani wathu imfa amatibweretsera. Ndiponso mfundo zoona za m’Baibulo zokhudza mmene anthu akufa amakhalira zimasonyeza kuti akufa sazunzika kumoto kapena ku puligatoriyo koma amakhala opanda moyo m’manda. Choncho tikamakumbukira okondedwa athu, sitiyenera kunyansidwa ndi Mulungu kapena kuchita mantha chifukwa chosadziwa kuti okondedwa athuwo ali kuti. Komanso, m’Baibulo Yehova amatilimbikitsa mwa njira inanso.

Chiyembekezo Chimabweretsa Chimwemwe

Malemba amene takambiranawa amanena za chiyembekezo, chomwe ndi chinthu chofunika kuti munthu akhale ndi chimwemwe chenicheni. Mawu akuti “chiyembekezo,” malinga ndi mmene anawagwiritsira ntchito m’Baibulo, amatanthauza kuyembekezera kuti upeza zabwino, popanda kukayikira. Kuti tione mmene chiyembekezo chingabweretsere chimwemwe masiku ano, tiyeni tibwererenso ku nkhani ya mmene Yesu anaukitsira Lazaro.

Pali zifukwa zosachepera ziwiri zimene Yesu anachitira chozizwitsa chimene chija. Chifukwa chimodzi chinali choti achotse chisoni cha Marita, Mariya, ndi anzawo ena. Anthuwa tsopano akanathanso kusangalala chifukwa chokhala limodzi ndi wokondedwa wawo. Koma Yesu anatchulira Marita chifukwa china chachiwiri, chomwe chinali chofunika kwambiri kuposa choyambacho. Anati: “Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?” (Yohane 11:40) Kumbali yomaliza ya vesi limeneli, Baibulo la The New Testament in Modern English, lolembedwa ndi J. B. Phillips, limagwiritsa ntchito mawu akuti “zodabwitsa zimene Mulungu angathe kuchita.” Pomupatsanso Lazaro moyo, Yesu anasonyeza zomwe Yehova Mulungu angathe kuchita, ndi zomwe adzachite m’tsogolo muno. Nazi mfundo zina zofotokoza “zodabwitsa zimene Mulungu angathe kuchita” zimenezi.

Pa Yohane 5:28, 29, Yesu anati: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m’manda [“achikumbutso,” NW] adzamva mawu ake, nadzatulukira.” Zimenezi zikutanthauza kuti akufa onse amene ali m’manda achikumbutso, kuphatikizapo okondedwa athu, adzakhalanso ndi moyo. Lemba la Machitidwe 24:15 limafotokoza mfundo zina zokhudza chochitika chapadera chimenechi. Limati: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” Choncho ngakhale anthu ambiri “osalungama,” omwe ndi anthu ambirimbiri amene sanadziwe ndi kutumikira Yehova, m’tsogolo muno adzakhala ndi mwayi wochita zinthu zosangalatsa Mulungu.

Kodi kuuka kwa akufa kumeneku kudzachitikira kuti? Lemba la Salmo 37:29 limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” Tangoganizirani tanthauzo la mawu amenewa. Mabanja ndi mabwenzi amene analekanitsidwa chifukwa cha imfa adzakumananso padziko lapansi pano. Mukamaganizira zodzakhaliranso limodzi ndi anthu amene munkasangalala kucheza nawo kale, m’pomveka kuti chimwemwe chanu chingadzaze tsaya.

Yehova Akufuna Kuti Mukhale Achimwemwe

Taona njira ziwiri zimene Yehova angakulitsire chimwemwe chanu ngakhale muli ndi mavuto. Choyamba, kudzera m’Baibulo amakupatsani nzeru ndi malangizo amene angakuthandizeni kuthana ndi zovuta. Kuwonjezera pa kutithandiza kulimbana ndi chisoni chimene timakhala nacho chifukwa cha imfa, malangizo a m’Baibulo angatithandizenso kulimbana ndi mavuto azachuma ndi matenda. Angakupatseni mphamvu zoti muthe kulimbana ndi kupanda chilungamo ndi mavuto azandale. Mutagwiritsira ntchito malangizo a m’Baibulo pamoyo wanu, angakuthandizeni kulimbana ndi mavuto ena okhudza inuyo panokha.

Chachiwiri, mwa kuphunzira Baibulo mumapeza chiyembekezo chimene chimaposa chinthu chilichonse chimene anthu angakupatseni. Kuukitsidwa kwa anzanu ndi achibale anu ndi mbali ya chiyembekezo chimene Baibulo limapereka. Lemba la Chivumbulutso 21:3, 4 limafotokoza zambiri pa nkhani imeneyi. Limati: “Mulungu yekha adzakhala [ndi anthu] . . . ; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” Zimenezi zikutanthauza kuti zinthu zonse zomwe zimakubweretserani chisoni pamoyo wanu zidzachotsedwa kwamuyaya. Zimene Baibulo limalonjeza zidzachitikadi, ndipo inuyo mukhoza kudzasangalala nazo zimenezi zikadzakwaniritsidwa. Kungodziwa kuti m’tsogolomu muli zabwino kumapereka mpumulo. Kudziwa kuti munthu ukadzafa sudzazunzika kosatha kumabweretsa chimwemwe.

Mwachitsanzo, taganizirani izi: Zaka zingapo zapitazo, Maria anaona mwamuna wake akufa imfa yopweteka chifukwa cha khansa. Asanayambe n’komwe kuiwala zimenezi, mavuto azachuma anamuchititsa kuti iye ndi ana ake aakazi atatu asamuke m’nyumba yawo ndi kukafuna kwina kokhala. Patatha zaka ziwiri, Maria anazindikira kuti ali ndi khansa. Wachitidwapo maopaleshoni aakulu awiri, ndipo tsiku lililonse amamva ululu woopsa. Ngakhale kuti akukumana ndi mavuto amenewa, iye amaika maganizo ake pa zinthu zabwino moti mpaka amatha kulimbikitsa anthu ena. Kodi amatani kuti akhalebe wachimwemwe?

Maria anati: “Ndikakhala ndi vuto, ndimayesetsa kuti ndisamangoganizira kwambiri za vutolo. Ndimapewa kudzifunsa mafunso ngati akuti: ‘N’chifukwa chiyani zimenezi zinachitikira ineyo? N’chifukwa chiyani ndikuvutika chonchi? N’chifukwa chiyani ndinayamba kudwala?’ Kuganiza zinthu zosalimbikitsa kumathetsa mphamvu. M’malo mwake, mphamvu zanga ndimazigwiritsa ntchito potumikira Yehova ndi kuthandiza anthu ena. Zimenezo zimandibweretsera chimwemwe.”

Kodi chiyembekezo chimamuthandiza bwanji Maria? Iye amadikirira mwachidwi nthawi imene Yehova adzachotse matenda ndi mavuto ena a anthu m’tsogolo muno. Akapita kuchipatala kukalandira chithandizo, amauza chiyembekezo chimenecho anthu ena odwala khansa, amene mwina amakhala opanda chiyembekezo. Kodi chiyembekezo n’chofunika motani kwa Maria? Iye anati: “Nthawi zambiri ndimaganizira zimene Baibulo limanena pa lemba la Ahebri 6:19, pamene Paulo anafotokoza kuti chiyembekezo chili ngati nangula wa moyo. Popanda nangula ameneyo, munthu akhoza kusokonezeka ngati mmene bwato lopanda nangula limatengedwera ndi madzi mu mphepo yamkuntho. Koma ngati wamangiriridwa ku nangula uja, akhoza kukhala wolimba ngakhale azikumana ndi mavuto onga mphepo yamkutho pamoyo wake.” ‘Chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza’ chimathandiza Maria kukhalabe wachimwemwe. Inunso chingakuthandizeni m’njira yomweyo.​—Tito 1:2.

Mwa kuphunzira Baibulo, mukhoza kupeza chimwemwe chenicheni ngakhale muli ndi mavuto. Koma mwina mungakayikire ngati kuchita zimenezi kuli kothandizadi. Mboni za Yehova zidzakhala zokondwa kukusonyezani mfundo za m’Malemba zomwe muyenera kudziwa kuti mukhaledi achimwemwe. Pamene mukudikirira kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo chimene Yehova amapereka, mungakhale mmodzi wa anthu amene anafotokozedwa kuti: “Adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.”​—Yesaya 35:10.

[Chithunzi patsamba 5]

Choonadi cha m’Baibulo chokha n’chimene chingachepetse chisoni

[Chithunzi patsamba 7]

Chiyembekezo chimene Baibulo limapereka choti akufa adzauka chingabweretse chimwemwe