Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamata, Sankhani Kutumikira Yehova

Achinyamata, Sankhani Kutumikira Yehova

Achinyamata, Sankhani Kutumikira Yehova

“Mudzisankhire lero amene mudzam’tumikira.”​—YOSWA 24:15.

1, 2. Kodi m’Matchalitchi Achikristu mwachitika maubatizo otani olakwika?

“MUZIDIKIRA kaye kuti [ana] azikhala Akristu atadziwa Kristu.” Amene analemba mawu amenewa ndi Tertullian, cha kumapeto kwa zaka za m’ma 100 C.E. Anali kutsutsa ubatizo wa makanda, umene unayamba kukhazikika m’Chikristu champatuko m’masiku akewo. Potsutsa mfundo ya Tertullian ndiponso Baibulo, Bambo wa Tchalitchi Augustine anati, ubatizo umachotsa litsiro la uchimo woyambirira ndiponso anati makanda amene amamwalira asanabatizidwe amapita ku helo. Kukhulupirira zimenezi kunalimbikitsa mchitidwe wobatiza makanda mwamsanga akangobadwa.

2 M’Matchalitchi Achikristu ambiri amabatizabe makanda mpaka pano. Kale, olamulira ndi atsogoleri a zipembedzo a m’mayiko amene amati ndi achikristu anali kubatiza anthu “akunja” mokakamiza. Koma ubatizo wa makanda ndi ubatizo wokakamiza wa anthu amene ndi achikulire si wa m’Baibulo ayi.

Masiku Ano Munthu Sabadwa Ali Wodzipereka

3, 4. Kodi n’chiyani chimene chingathandize ana amene makolo awo ndi odzipereka kuti adzipereke mwa kufuna kwawo?

3 Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amaona ana aang’ono kukhala oyera ngakhale ngati kholo limodzi ndi limene lili Mkristu wokhulupirika. (1 Akorinto 7:14) Kodi ndiye kuti ana ngati amenewo ndi atumiki odzipereka a Yehova chifukwa cha zimenezi? Ayi. Koma ngakhale zili choncho, ana oleredwa ndi makolo odzipereka kwa Yehova amalandira maphunziro amene angathandize anawo kudzipereka okha kwa Yehova. Mfumu Solomo yanzeru inalemba kuti: “Mwananga, sunga malangizo a atate wako, usasiye malamulo a mako. . . . Adzakutsogolera ulikuyenda, ndi kukudikira uli m’tulo. Ndi kulankhula nawe utauka. Pakuti malangizo ndi nyali, malamulo ndi kuunika; ndi zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo.”​—Miyambo 6:20-23.

4 Malangizo amene makolo achikristu amapereka angateteze ana, malinga ngati anawo awatsatira. Solomo ananenanso kuti: “Mwana wanzeru akondweretsa atate; koma mwana wopusa amvetsa amake chisoni.” “Tamvera tsopano, mwananga, utenge nzeru, ulunjikitse mtima wako m’njiramo.” (Miyambo 10:1; 23:19) Inde, kuti mupindule ndi chiphunzitso cha makolo anu, ana inu muyenera kulandira mwaufulu malangizo, uphungu, ndi chilango. Simunabadwe anzeru, koma ‘mungatenge nzeru,’ kapena kuti mungakhale anzeru ndi kutsatira “njira ya moyo” mwa kufuna kwanu.

Kodi Chilangizo N’chiyani?

5. Kodi Paulo anapereka uphungu wotani kwa ana ndi atate?

5 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi n’chabwino. Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko. Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.”​—Aefeso 6:1-4.

6, 7. Kodi kulera ana “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye” kumafuna chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi sizitanthauza kuti makolowo akupotoza ana awo?

6 Kodi makolo achikristu akamalera ana awo “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye,” amakhala akupotoza anawo? Ayi. Kodi ndi munthu wanji amene angadzudzule makolo chifukwa chophunzitsa ana awo zimene makolowo akuona kuti n’zabwino ndipo n’zothandiza anawo kukhala ndi khalidwe labwino? Palibe amene amadzudzula anthu okana Mulungu chifukwa chophunzitsa ana awo kuti kulibe Mulungu. Akatolika amakhulupirira kuti ndi udindo wawo kulera ana awo mogwirizana ndi Chikatolika, ndipo sadzudzulidwa chifukwa chochita zimenezo. N’chimodzimodzinso Mboni za Yehova. Izo siziyenera kuimbidwa mlandu wopotoza ana maganizo zikamalera ana awo kuti akhale ndi maganizo a Yehova pa mfundo zazikulu za choonadi ndi za makhalidwe abwino.

7 Malinga ndi buku lakuti Theological Dictionary of the New Testament, mawu a Chigiriki oyambirira omwe anawamasulira kuti “chilangizo” pa Aefeso 6:4 amanena za kaphunzitsidwe kamene “cholinga chake ndi kukonza maganizo, kukonza zolakwika, kuthandiza munthu kuti akhale ndi mtima wokonda zauzimu.” Nanga bwanji ngati wachinyamata wina, anzake akum’nyengerera kuti asamamvere zimene makolo ake akum’phunzitsa, ndipo iye akutsatira zimene anzakewo akumuuza? Kodi tingati ndani amene akum’potoza? Makolo ake kapena anzake? Ngati anzakewo akum’nyengerera kuti ayambe kumwa mankhwala osokoneza bongo, kumwa mowa mwauchidakwa, kapena kuchita chiwerewere, kodi chingakhale chanzeru kudzudzula makolo a mwanayo chifukwa chakuti iwo akuyesa kukonza maganizo ake ndi kum’thandiza kuona mavuto amene angakumane nawo chifukwa cha khalidwe loipalo?

8. Kodi chinachitika n’chiyani kuti Timoteo ‘atsimikize mtima’ n’kukhulupirira?

8 Mtumwi Paulo analembera Timoteo wachinyamata kuti: “Ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziwa amene adakuphunzitsa; ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Kristu Yesu.” (2 Timoteo 3:14, 15) Kuyambira Timoteo ali wakhanda, mayi ake ndi agogo ake anayesetsa kum’thandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba mwa Mulungu chimene maziko ake anali kudziwa Malemba Opatulika. (Machitidwe 16:1; 2 Timoteo 1:5) Kenako, iwo atakhala Akristu, sanakakamize Timoteo kukhulupirira koma ‘anam’tsimikizira’ mwa kupereka zifukwa zomveka za m’Malemba amene iwo anali kuwadziwa.

Yehova Akufuna Kuti Musankhe

9. (a) Kodi Yehova anazilemekeza bwanji zolengedwa zake, ndipo n’chifukwa chiyani anatero? (b) Kodi Mwana wobadwa yekha wa Mulungu anagwiritsa ntchito bwanji ufulu wake wosankha?

9 Yehova akanafuna, akanapanga anthu ngati nyama, kuti azichita chifuniro chake mwachibadwa ndi kuti asamathe kusankha okha zochita. Koma sanatero. M’malo mwake, anawalemekeza mwa kuwapatsa ufulu wosankha. Mulungu wathu amafuna kuti ena azimumvera mwa kufuna kwawo. Amasangalala akamaona zolengedwa zake, achikulire ndi ana omwe, zikum’tumikira chifukwa chomukonda. Mwana wake wobadwa yekha amagonjera chifuniro cha Mulungu chifukwa chokonda Mulunguyo, ndipo iye ndi chitsanzo chabwino kwambiri. Za Mwanayo, Yehova anati: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera.” (Mateyu 3:17) Mwana woyamba kubadwa ameneyu anati kwa Atate wake: “Kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali m’kati mwa mtima mwanga.”​—Salmo 40:8; Ahebri 10:9, 10.

10. Kodi chofunika n’chiyani kuti kutumikira Yehova kukhale kovomerezeka?

10 Yehova amafuna kuti amene akum’tumikira motsogoleredwa ndi Mwana wake, azigonjera chifuniro Chake mwa kufuna kwawo ngati mmene Mwanayo amachitira. Wamasalmo polosera, anaimba kuti: “Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: m’moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha, muli nawo mame a ubwana wanu.” (Salmo 110:3) Gulu lonse la Yehova, mbali ya kumwamba ndiponso ya padziko lapansi, limagonjera chifuniro cha Mulungu chifukwa chomukonda, ndipo limayendera zimenezi.

11. Kodi achinyamata amene aleredwa ndi makolo odzipereka ayenera kusankha okha kuchita chiyani?

11 Choncho, inu achinyamata mudziwe kuti makolo anu kapena akulu achikristu mumpingo sangakukakamizeni kuti mubatizidwe. Inuyo muyenera kufuna nokha kutumikira Yehova. Kale, Yoswa anauza Aisrayeli kuti: ‘Tumikirani [Yehova] ndi mtima wangwiro ndi woona . . . Mudzisankhire lero amene mudzam’tumikira.’ (Yoswa 24:14-22) N’chimodzimodzinso inuyo. Muyenera kusankha nokha kudzipereka kwa Yehova ndi kugwiritsa ntchito moyo wanu kuchita chifuniro chake.

Senzani Udindo Wanu

12. (a) Ngakhale kuti makolo angaphunzitse ana awo, kodi n’chiyani chimene iwo sangachitire ana awowo? (b) Kodi ndi liti pamene mwana amakhala ndi udindo woyankha kwa Yehova pa zosankha zimene amapanga?

12 Nthawi imafika pamene ananu mumasiya kukhala otetezeka chifukwa cha kukhulupirika kwa makolo anu. (1 Akorinto 7:14) Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Kwa iye amene adziwa kuchita bwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo.” (Yakobo 4:17) N’zosatheka kuti makolo atumikire Mulungu chifukwa cha ana awo kapena ana kutumikira Mulungu chifukwa cha makolo awo. (Ezekieli 18:20) Kodi mwaphunzira za Yehova ndi zolinga zake? Kodi mwafika pa msinkhu woti mukumvetsa zimene mwaphunzira ndipo mungakhale pa ubwenzi wanuwanu ndi iye? Ngati mwatero, kodi si pake kuganiza kuti Mulungu akuona kuti mutha kusankha nokha kum’tumikira?

13. Kodi ndi mafunso ati amene achinyamata osabatizidwa angachite bwino kudzifunsa?

13 Kodi ndinu wachinyamata wosabatizidwa amene mukuleredwa ndi makolo opembedza, ndipo mumafika pamisonkhano yachikristu, ngakhale kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu? Ngati ndi choncho, dzifunseni moona mtima kuti: ‘N’chifukwa chiyani ndikuchita zimenezi? Kodi ndimapita kumisonkhano ndi kukalalikira chifukwa chakuti makolo anga amafuna kuti ndizichita zimenezi kapena chifukwa chakuti ndikufuna kukondweretsa Yehova?’ Kodi mwazindikira “chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro”?​—Aroma 12:2.

N’chifukwa Chiyani Mukuchedwa Kubatizidwa?

14. Kodi ndi zitsanzo ziti za m’Baibulo zimene zikusonyeza kuti m’posafunika kuchedwa kwambiri kubatizidwa?

14 “Chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?” Mwaitiopiya amene anafunsa Filipo zimenezi anali atangophunzira kuti Yesu ndiye Mesiya. Koma Malemba amene Mwaitiopiyayo anadziwa anali okwanira kum’thandiza kuzindikira kuti sanayenere kuzengereza kunena poyera kuti kuyambira pamenepo adzatumikira Yehova mumpingo wachikristu, ndipo zimenezo zinam’sangalatsa kwambiri. (Machitidwe 8:26-39) Nayenso mayi wina dzina lake Lidiya, anachita zofananazo. Ameneyu mtima wake unatseguka “kuti amvere zimene anazinena Paulo,” ndipo “anabatizidwa” pomwepo, iye ndi a pabanja pake. (Machitidwe 16:14, 15) Ndiponso, mdindo wa ndende ku Filipi anamvetsera kwa Paulo ndi Sila pamene iwo “anamuuza iye mawu a Ambuye,” ndipo ‘anabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pake.’ (Machitidwe 16:25-34) Choncho, ngati mukudziwa mfundo zofunika zokhudza Yehova ndi zolinga zake, ndipo mukufuna ndi mtima wonse kuchita chifuniro chake, komanso ngati muli ndi mbiri yabwino mumpingo ndiponso mumafika pamisonkhano mokhulupirika ndi kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu, n’chifukwa chiyani mukuchedwa kubatizidwa?​—Mateyu 28:19, 20.

15, 16. (a) Kodi ndi maganizo olakwika ati amene amalepheretsa achinyamata ena kubatizidwa? (b) N’chifukwa chiyani kudzipereka ndi kubatizidwa kungateteze achinyamata?

15 Kodi mwina mukuzengereza kuchita mbali yofunika kwambiri imeneyi chifukwa choopa kuti mudzafunsidwa mukalakwa? Ngati ndi zimene mukuopa, taganizani izi: Kodi mungakane kutenga laisensi yoyendetsera galimoto chabe chifukwa chakuti mukuopa kuti tsiku lina mungadzachite ngozi? Iyayi! Ndiye musachedwe kubatizidwa ngati mukuyenerera. Ngati mwapereka moyo wanu kwa Yehova ndipo mwavomera kuchita chifuniro chake, zidzakuthandizani kuyesetsa ndi mtima wonse kupewa cholakwa. (Afilipi 4:13) Achinyamatanu, musaganize kuti mwa kuchedwa kubatizidwa mukupewa mlandu. Mukafika pa msinkhu woyenera kusenza nokha udindo, mumayamba kuyankha mlandu kwa Yehova chifukwa cha zimene mukuchita, kaya ndinu wobatizidwa kapena ayi.​—Aroma 14:11, 12.

16 Mboni zambiri padziko lonse lapansi zikuona kuti kusankha kwawo kubatizidwa pamene zinali zachinyamata kunazithandiza kwambiri. Mwachitsanzo, taganizani za munthu wina wa Mboni wa zaka 23 kumadzulo kwa Ulaya. Iye amakumbukira kuti kubatizidwa ali ndi zaka 13 kunam’limbikitsa kukhala wosamala ndiponso kupewa kutengeka ndi “zilakolako za unyamata.” (2 Timoteo 2:22) Ali mwana, cholinga chake chinali kukhala mtumiki wa nthawi zonse. Tikunena pano, akusangalala kutumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova. Madalitso ochuluka akudikirira achinyamata onse, ngakhale inuyo, amene mukusankha kutumikira Yehova.

17. Kodi ndi mbali ziti zimene tifunika kudziwitsa “chifuniro cha Ambuye”?

17 Tikadzipereka ndi kubatizidwa, timayamba kumaganiza za chifuniro cha Yehova pa zonse zimene tikuchita pa moyo wathu. Kuti tikhale okhulupirika pa kudzipereka kwathu, m’pofunika kuombola nthawi. Kodi tingachite bwanji zimenezo? Tingatero mwa kupatula nthawi imene tikanaigwiritsa ntchito pa zinthu zopanda phindu n’kuigwiritsa ntchito pa kuphunzira Baibulo mwakhama, kufika pamisonkhano mokhulupirika, ndi kulalikira mwachangu ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’ (Aefeso 5:15, 16; Mateyu 24:14) Kudzipereka kwathu kwa Yehova ndiponso kukhala kwathu ndi mtima wofuna kuchita chifuniro chake, zimatithandiza pa moyo wathu m’mbali zonse, kuphatikizapo pa nthawi yopuma, pa nkhani ya kudya ndi kumwa, ndi nyimbo zimene timamvetsera. Bwanji osasankha zosangalatsa zimene mungathe kukhala nazo mpaka muyaya? Mboni zambiri zachinyamata komanso zosangalala zingakuuzeni kuti pali njira zambiri zabwino zimene mungasangalalire popanda kudutsa malire a “chifuniro cha Ambuye.”​—Aefeso 5:17-19.

“Tidzamuka Nanu”

18. Kodi achinyamata ayenera kudzifunsa kuti chiyani?

18 Kuyambira mu 1513 B.C.E. mpaka pa Pentekoste mu 33 C.E., Yehova anali ndi gulu la anthu padziko lapansi limene anasankha kuti lizimulambira ndi kukhala mboni zake. (Yesaya 43:12) Ana a Aisrayeli anabadwira mu mtundu umenewo. Kuyambira pa Pentekoste, Yehova wakhala ndi “mtundu” watsopano padziko lapansi. Mtunduwo ndi Israyeli wauzimu, “anthu a dzina lake.” (1 Petro 2:9, 10; Machitidwe 15:14; Agalatiya 6:16) Mtumwi Paulo ananena kuti Kristu anadziyeretsera yekha “anthu [kuti] akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.” (Tito 2:14) Zili kwa inu achinyamata kupeza nokha kumene anthu amenewo akupezeka. Ndani masiku ano amene amapanga “mtundu wolungama, umene uchita zoonadi,” umatsatira mfundo za m’Baibulo, ndiwo Mboni zokhulupirika za Yehova, ndipo umalalikira kuti Ufumu wake ndi wokhawo umene anthu onse ayenera kuyang’anako? (Yesaya 26:2-4) Taonani zimene amatchita Matchalitchi Achikristu ndi zipembedzo zina, ndipo yerekezani khalidwe lawo ndi zimene Baibulo limafuna kwa atumiki oona a Mulungu.

19. Kodi anthu mamiliyoni padziko lonse lapansi atsimikiza zoti chiyani?

19 Anthu mamiliyoni padziko lonse lapansi, kuphatikizapo achinyamata ambiri, atsimikiza kuti otsalira odzozedwa a Mboni za Yehova ndiwo “mtundu wolungama.” Anthuwo amauza Aisrayeli auzimu kuti: “Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.” (Zekariya 8:23) Tikukhulupirira kuti achinyamatanu musankha kukhala pakati pa anthu a Mulungu, ndipo tikupempherera zimenezi. Mukatero, ndiye kuti ‘mwasankha moyo.’ Inde, moyo wosatha m’dziko latsopano la Yehova.​—Deuteronomo 30:15-20; 2 Petro 3:11-13.

Kubwereza

• Kodi chilangizo chimatanthauza chiyani?

• Kodi ndi utumiki wotani umene Yehova amavomereza?

• Kodi achinyamata onse oleredwa ndi makolo odzipereka afunikira kusankha chiyani?

• N’chifukwa chiyani ubatizo sufunika kuuchedwetsa?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 26]

Kodi mudzamvera ndani?

[Chithunzi patsamba 28]

Kodi kudzipereka ndi kubatizidwa kungakutetezeni bwanji?

[Chithunzi patsamba 29]

Kodi chimene chimakuletsani inu kubatizidwa n’chiyani?