Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anabadwira mu Mtundu Wosankhika wa Mulungu

Anabadwira mu Mtundu Wosankhika wa Mulungu

Anabadwira mu Mtundu Wosankhika wa Mulungu

“Yehova Mulungu wanu anakusankhani, mukhale mtundu wa pa wokha wa iye yekha.”​—DEUTERONOMO 7:6.

1, 2. Kodi ndi zinthu ziti zamphamvu zimene Yehova anachitira anthu ake, ndipo kodi Aisrayeli anakhala pa unansi wotani ndi Mulungu?

MU 1513 B.C.E., Yehova anakhala pa unansi watsopano ndi atumiki ake padziko lapansi. Chaka chimenecho, iye anachititsa manyazi ulamuliro wamphamvu padziko lonse ndi kulanditsa Aisrayeli kuwachotsa mu ukapolo. Atachita zimenezo, anakhala Mpulumutsi wawo ndipo iwo anakhala anthu ake. M’mbuyomo asanawalanditse, Mulungu anauza Mose kuti: “Nena kwa ana a Israyeli, Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aaigupto, ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo aakulu; ndipo ndidzalandira inu mukhale anthu anga, ndipo ndidzakhala Ine Mulungu wanu.”​—Eksodo 6:6, 7; 15:1-7, 11.

2 Atangoyamba ulendo wawo wochoka mu Igupto, sipanatenge nthawi kuti Aisrayeli akhale pa unansi wa pangano ndi Yehova, Mulungu wawo. Kuyambira pamenepo, Yehova anakhala ndi gulu, kapena kuti mtundu umodzi padziko lapansi m’malo mochita zinthu ndi munthu mmodzi, mabanja, kapena mbumba. (Eksodo 19:5, 6; 24:7) Anapatsa anthu ake malamulo amene iwo anali kutsatira posungitsa bata ndi mtendere, ndiponso mbali yaikulu ya malamulowo inakhudza kulambira. Mose anauza anthuwo kuti: “Mtundu waukulu wa anthu ndi uti, wakukhala ndi Mulungu pafupi pawo monga amakhala Yehova Mulungu wathu, pamene pali ponse timaitanira iye? Ndipo mtundu waukulu wa anthu ndi uti, wakukhala nawo malemba ndi maweruzo olungama, akunga chilamulo ichi chonse ndichiika pamaso panu lerolino?”​—Deuteronomo 4:7, 8.

Anabadwira mu Mtundu wa Mboni

3, 4. Kodi chifukwa chachikulu chimene Israyeli anakhalirako monga mtundu chinali chiyani?

3 Patadutsa zaka zambiri, Yehova anakumbutsa Aisrayeli kudzera mwa mneneri wake Yesaya chifukwa chachikulu chimene iwo monga mtundu anakhalirapo. Yesaya anati: “Atero Yehova, amene anakulenga iwe Yakobo, ndi Iye amene anakupanga iwe Israyeli, Usaope, chifukwa ndakuombola iwe, ndakutchula dzina lako, iwe uli wanga. Chifukwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, Woyera wa Israyeli, Mpulumutsi wako. . . . Bwera nawo ana anga aamuna kuchokera kutali, ndi ana anga aakazi kuchokera ku malekezero a dziko lapansi; yense wotchedwa dzina langa, amene ndinam’lenga chifukwa cha ulemerero wanga; ndinamuumba iye; inde, ndinam’panga iye. Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha, . . . anthu amene ndinadzilengera ndekha, kuti aonetse matamando anga.”​—Yesaya 43:1, 3, 6, 7, 10, 21.

4 Pokhala anthu otchedwa ndi dzina la Yehova, Aisrayeli anali kudzakhala mboni za ulamuliro wake pamaso pa amitundu. Anayenera kukhala anthu amene ‘analengedwa chifukwa cha ulemerero wa Yehova.’ Anayeneranso ‘kuonetsa matamando a Yehova,’ kusimba ntchito zake zodabwitsa zimene anachita powalanditsa ndipo mwa kutero, kulemekeza dzina lake loyera. Mwachidule, iwo monga mtundu anayenera kukhala mboni za Yehova.

5. Kodi mtundu wa Israyeli unali wopatulika chifukwa chiyani?

5 Zaka za m’ma 1000 B.C.E., Mfumu Solomo ananena kuti Yehova anali atapanga Israyeli kukhala mtundu wapadera. Popemphera kwa Yehova, iye anati: “Inu munawapatula pa anthu onse a pa dziko lapansi akhale cholowa chanu.” (1 Mafumu 8:53) Ndiponso Aisrayeli, aliyense payekha, anali pa ubwenzi wapadera ndi Yehova. Kalelo, Mose anali atawauza kuti: “Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu . . . , popeza ndinu mtundu wa anthu opatulikira Yehova Mulungu wanu.” (Deuteronomo 14:1, 2) Choncho, ana a Aisrayeli sanafunikire kupereka miyoyo yawo kwa Yehova. Anabadwira mu mtundu wopatulika wa anthu a Mulungu. (Salmo 79:13; 95:7) Mbadwo watsopano uliwonse unaphunzitsidwa malamulo a Yehova ndipo unayenera kuwasunga chifukwa cha pangano limene linali pakati pa Israyeli ndi Yehova.​—Deuteronomo 11:18, 19.

Anali ndi Ufulu Wosankha

6. Kodi Mwisrayeli aliyense payekha anafunikira kusankha chiyani?

6 Ngakhale kuti Aisrayeli anabadwira mu mtundu wopatulika, munthu aliyense anafunikira kusankha yekha kutumikira Mulungu. Iwo asanalowe m’Dziko Lolonjezedwa, Mose anawauza kuti: “Ndichititsa mboni lero kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse inu; ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbewu zanu; kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kum’mamatira iye, pakuti iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka; kuti mukhale m’dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, kuwapatsa ili.” (Deuteronomo 30:19, 20) Choncho, Mwisrayeli aliyense payekha anafunikira kusankha yekha kukonda Yehova, kumvera mawu ake, ndi kum’mamatira. Popeza Aisrayeli anali ndi ufulu wosankha umenewo, anayenera kuvomereza chilichonse chimene chikanachitika chifukwa cha zimene anasankhazo.​—Deuteronomo 30:16-18.

7. Kodi chinachitika n’chiyani mbadwo wa Yoswa utatha kumwalira?

7 Nthawi ya Oweruza imapereka chitsanzo chabwino cha zimene zimachitika anthu akakhala okhulupirika kapena osakhulupirika. Nthawi imeneyi ili pafupi kuyamba, Aisrayeli anatsatira chitsanzo chabwino cha Yoswa ndipo anadalitsidwa. “Anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akuluakulu otsala atafa Yoswa, amene adaona ntchito yaikulu yonse ya Yehova anaichitira Israyeli.” Koma patapita nthawi kuchokera pamene Yoswa anamwalira, ‘panauka mbadwo wina pambuyo pawo; wosadziwa Yehova kapena ntchitoyi adaichitira Israyeli. Ndipo ana a Israyeli anachita choipa pamaso pa Yehova.’ (Oweruza 2:7, 10, 11) Zikuoneka kuti mbadwo wa ana osadziwa zambiri umenewu, sunanyadire cholowa chawo chokhala mtundu wopatulika, umene Yehova Mulungu wawo anauchitira zazikulu m’mbuyomo.​—Salmo 78:3-7, 10, 11.

Kuchita Mogwirizana ndi Kudzipereka Kwawo

8, 9. (a) Kodi ndi dongosolo lotani limene linapatsa Aisrayeli mwayi woonetsa kudzipereka kwawo kwa Yehova? (b) Kodi amene anapereka nsembe zaufulu anapeza phindu lanji?

8 Yehova anapatsa anthu ake mpata wochita mogwirizana ndi kudzipereka kwawo monga mtundu. Mwachitsanzo, Chilamulo chake chinapatsa anthu mwayi wopereka nsembe. Anali kupereka nsembe zina molamulidwa pamene zina anali kupereka mwaufulu. (Ahebri 8:3) Nsembe zotero zinaphatikizapo nsembe zopsereza, nsembe zaufa, ndi nsembe zoyamika ndipo zonse zinali zaufulu. Zinali mphatso zoperekedwa kwa Yehova kuti munthu ayanjidwe ndi kusonyeza kuyamikira.​—Levitiko 7:11-13.

9 Yehova anakondwera ndi nsembe zaufulu zimenezo. Nsembe zopsereza ndi zaufa zinali za “fungo lokoma la kwa Yehova.” (Levitiko 1:9; 2:2) Popereka nsembe yoyamika, magazi ndi mafuta a nyama zinali kuperekedwa kwa Yehova, pamene nyama yake ankadya ndi ansembe ndiponso munthu wopereka nsembeyo. Choncho nsembeyo inali chakudya chophiphiritsa ndipo inasonyeza ubwenzi wamtendere umene unali pakati pa munthuyo ndi Yehova. Chilamulo chinati: “Pamene muphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandiridwe.” (Levitiko 19:5) Ngakhale kuti Aisrayeli onse anali odzipereka kwa Yehova mwa chibadwa, anthu amene anayesetsa kuti kudzipereka kwawo kukhale kwatanthauzo mwa kupereka nsembe zaufulu, ‘analandiridwa’ ndipo anadalitsika kwambiri.​—Malaki 3:10.

10. Kodi Yehova anafotokoza bwanji kusakondwa kwake m’masiku a Yesaya ndi a Malaki?

10 Ngakhale zinali choncho, mtundu wopatulika wa Israyeli unali wosakhulupirika kwa Yehova nthawi zambiri. Yehova, kudzera mwa mneneri wake Yesaya, anawauza kuti: “Iwe sunanditengere Ine zoweta zazing’ono za nsembe zopsereza zako; kapena kundilemekeza ndi nsembe zako. Sindinakutumikiritsa ndi nsembe zaufa.” (Yesaya 43:23) Chinanso n’chakuti, nsembe zimene munthu ankapereka mokakamizika ndiponso osati chifukwa chokonda Mulungu zinali zopanda phindu kwa Yehova. Mwachitsanzo, patadutsa zaka pafupifupi 300 kuchokera nthawi ya Yesaya, kutanthauza masiku a mneneri Malaki, Aisrayeli anapereka nsembe nyama zolemala. N’chifukwa chake Malaki anawauza kuti: “Sindikondwera nanu, ati Yehova wa makamu, ndipo sindidzalandira chopereka m’dzanja lanu. . . . Mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira ku dzanja lanu? ati Yehova.”​—Malaki 1:10, 13; Amosi 5:22.

Mtundu Wopatulika Ukanidwa

11. Kodi Israyeli anapatsidwa mwayi wotani?

11 Panthawi imene Aisrayeli anakhala mtundu wopatulika wa Yehova, iye anawalonjeza kuti: “Ngati mudzamvera mawu anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa chapadera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa; ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika.” (Eksodo 19:5, 6) Mesiya wolonjezedwa anali kudzaonekera pakati pawo n’kuwapatsa mwayi woyambirira woti akhale m’boma la Ufumu wa Mulungu. (Genesis 22:17, 18; 49:10; 2 Samueli 7:12, 16; Luka 1:31-33; Aroma 9:4, 5) Koma ambiri a mtundu wa Israyeli anakhala osakhulupirika pa kudzipereka kwawo. (Mateyu 22:14) Anakana Mesiyayo ndipo mapeto ake, anamupha.​—Machitidwe 7:51-53.

12. Ndi mawu ati a Yesu amene akusonyeza kuti Israyeli, mtundu wopatulika wa Yehova, unakanidwa?

12 Kutatsala masiku ochepa kuti afe, Yesu anauza atsogoleri a chipembedzo cha Chiyuda kuti: “Kodi simunawerenga konse m’malembo, Mwala umene anaukana omanga nyumba Womwewu unakhala mutu wa pangondya: Ichi chinachokera kwa Ambuye, Ndipo chili chozizwitsa m’maso mwathu? Chifukwa chake ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.” (Mateyu 21:42, 43) Posonyeza kuti Yehova anali atawakana monga mtundu wodzipereka kwa Iye, Yesu anati: “Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m’mapiko ake, koma inu simunafuna ayi! Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.”​—Mateyu 23:37, 38.

Mtundu Watsopano Wopatulika

13. Kodi Yehova ananena ulosi woti chiyani m’masiku a Yeremiya?

13 Panthawi ya mneneri Yeremiya, Yehova analosera mbali yatsopano yokhudza anthu ake. Timawerenga kuti: “Taonani, masiku adza, ati Yehova, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israyeli, ndi nyumba ya Yuda; si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo awo tsiku lija ndinawagwira manja kuwatulutsa m’dziko la Aigupto; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyawo, ati Yehova. Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israyeli atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika chilamulo changa m’kati mwawo, ndipo m’mtima mwawo ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, nadzakhala iwo anthu anga.”​—Yeremiya 31:31-33.

14. Kodi mtundu watsopano wopatulika wa Yehova unakhalako liti ndipo maziko a zimenezi n’chiyani? Tchulani mtundu watsopanowo.

14 Maziko a pangano latsopano limeneli anayalidwa Yesu atamwalira ndiponso atapereka mtengo wa magazi ake okhetsedwa kwa Atate wake, mu 33 C.E. (Luka 22:20; Ahebri 9:15, 24-26) Koma, mzimu woyera utatsanulidwa pa Pentekoste mu 33 C.E. ndipo mtundu watsopano wa “Israyeli wa Mulungu” n’kubadwa, pangano latsopano linayamba kugwira ntchito. (Agalatiya 6:16; Aroma 2:28, 29; 9:6; 11:25, 26) Polembera Akristu odzozedwa, mtumwi Petro anati: “Inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa; inu amene kale simunali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu.” (1 Petro 2:9, 10) Unansi wapadera pakati pa Yehova ndi Israyeli wakuthupi unali utatha. Mu 33 C.E., Yehova anasiya kuyanja Israyeli wa padziko lapansi n’kuyamba kuyanja Israyeli wauzimu, mpingo wachikristu, “anthu akupatsa zipatso” za Ufumu wa Mesiya.​—Mateyu 21:43.

Kudzipereka Aliyense Payekha

15. Patsiku la Pentekoste mu 33 C.E., kodi Petro analimbikitsa omvera ake kubatizidwa ubatizo uti?

15 Itadutsa Pentekoste mu 33 C.E., munthu aliyense payekha, Myuda kapena wosakhala Myuda, anafunikira kudzipereka yekha kwa Mulungu ndi kubatizidwa “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera.” * (Mateyu 28:19) Pa Pentekoste, mtumwi Petro anauza anthu omvera, Ayuda ndi anthu otembenukira ku Chiyuda omwe, kuti: “Lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Kristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.” (Machitidwe 2:38) Ayuda amenewo komanso anthu otembenukira ku Chiyuda anafunikira kusonyeza mwa ubatizo wawo kuti sanangopereka miyoyo yawo kwa Yehova komanso kuti analandira Yesu kukhala njira imene Yehova adzakhululukire machimo awo. Anafunika kuvomereza kuti iye ndiye Mkulu wa Ansembe a Yehova ndiponso Mtsogoleri wawo, Mutu wa mpingo wachikristu.​—Akolose 1:13, 14, 18.

16. Masiku a Paulo, kodi zinatani kuti anthu amaganizo abwino​—Ayuda ndi osakhala Ayuda​—akhale mbali ya Israyeli wauzimu?

16 Patapita zaka, mtumwi Paulo anati: “Kuyambira kwa iwo a m’Damasiko, ndi a m’Yerusalemu, ndi m’dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndinalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zoyenera kutembenuka mtima.” (Machitidwe 26:20) Atatsimikiza anthuwo​—Ayuda ndi osakhala Ayuda​—kuti Yesu ndiye Kristu, Mesiya, Paulo anawathandiza kuti adzipereke ndi kubatizidwa. (Machitidwe 16:14, 15, 31-33; 17:3, 4; 18:8) Mwa kutembenukira kwa Mulungu, ophunzira atsopano amenewo anakhala mbali ya Israyeli wauzimu.

17. Kodi ntchito yoika chizindikiro imene yatsala pang’ono kutha ndi iti, ndipo ndi ntchito ina iti imene ikuchitika mofulumira?

17 Panopa, kuikidwa chizindikiro komaliza kwa otsalira a Israyeli wauzimu kuli pafupi. Zimenezi zikachitika, “angelo anayi” amene akugwira mphepo za chiwonongeko cha “chisautso chachikulu” adzalamulidwa kusiya mphepozo. Pakali pano, ntchito yosonkhanitsa a “khamu lalikulu,” amene akuyembekeza kudzakhala padziko lapansi kosatha ikufulumira. “Nkhosa zina” zimenezi mwaufulu zimasankha kukhulupirira “mwazi wa Mwanawankhosa” ndi kubatizidwa posonyeza kudzipereka kwawo kwa Yehova. (Chivumbulutso 7:1-4, 9-15; 22:17; Yohane 10:16; Mateyu 28:19, 20) Pakati pawo pali achinyamata ambiri amene makolo awo ndi Akristu. Ngati inuyo muli wachinyamata wotero, khalani ndi chidwi chowerenga nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

Kubwereza

• N’chifukwa chiyani ana a Aisrayeli sanafunikire kudzipereka okha kwa Yehova?

• Kodi Aisrayeli anasonyeza bwanji kuti akugwirizana ndi kudzipereka kwawo?

• N’chifukwa chiyani Yehova anakana Israyeli amene anali mtundu wake wopatulika, ndipo chinachitika n’chiyani kuti mtundu wina utenge malo ake?

• Kuyambira pa Pentekoste mu 33 C.E., kodi Ayuda ndi osakhala Ayuda anafunikira kuchita chiyani kuti akhale a Israyeli wauzimu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

Ana a Aisrayeli anabadwira mu mtundu wosankhika wa Mulungu

[Chithunzi patsamba 23]

Mwisrayeli aliyense anafunikira kusankha yekha kutumikira Mulungu

[Chithunzi patsamba 23]

Nsembe zaufulu zinapatsa Aisrayeli mwayi woonetsa chikondi chawo pa Yehova

[Chithunzi patsamba 25]

Itadutsa Pentekoste mu 33 C.E., otsatira a Kristu anafunika kudzipereka okha kwa Mulungu ndi kusonyeza zimenezo mwa kubatizidwa