Chikhulupiriro Chake Chimalimbikitsa Ena
Chikhulupiriro Chake Chimalimbikitsa Ena
SILVIA atabadwa mu December 1992, ankaoneka kuti anali mwana wa thanzi labwino. Koma atafika pa msinkhu wa zaka ziwiri, anapezeka ndi matenda enaake osachiritsika omwe amayambitsa mavuto aakulu m’mapapo ndiponso m’mimba. Kuti akhalebe ndi moyo, Silvia amamwa mapilisi 36 tsiku lililonse, kufwenkha mankhwala ena m’mphuno mwake, ndiponso amafunika kum’sinasina. Popeza ndi 25 peresenti yokha ya mapapo ake yomwe imagwira ntchito bwinobwino, anamuika kathanki ka mpweya wa okosijeni komwe amakhala nako nthawi zonse, ngakhale akamayenda.
“N’zodabwitsa kwambiri kuona mmene Silvia amapiririra ndi matendawa,” anatero a Teresa, omwe ndi mayi ake. “Iye ali ndi chikhulupiriro cholimba chifukwa akudziwa bwino Malemba. Chikhulupiriro chimenechi chimam’thandiza kulimbana ndi chisoni komanso nkhawa. Nthawi zonse iye amakumbukira malonjezo a Yehova onena za dziko latsopano, mmene anthu onse odwala adzachiritsidwa.” (Chivumbulutso 21:4) Nthawi zina achibale ake akamam’mvera chisoni, amalimba mtima akaona Silvia akumwetulira. Iye amauza makolo ndi mchimwene wake kuti: “Mavuto athuwa adzatha m’dziko latsopano.”
Silvia amalalikira uthenga wabwino wa Mawu a Mulungu mokhazikika, ndipo anthu omwe amawalalikirawo amatha kuona kuti iye ndi wosangalala. Anthu a mumpingo umene iye amasonkhana, ku zilumba za Canary, amayamikira kwambiri ndemanga zomwe iye amapereka. Pambuyo pa msonkhano uliwonse, Silvia amakonda kutsalira pa Nyumba ya Ufumu n’kumacheza ndi abale ndi alongo. Chifukwa choti iye ndi womasuka ndiponso wochezeka, anthu onse a mumpingowo amam’konda kwambiri.
“Silvia amatiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri,” anatero a Antonio omwe ndi bambo ake. “Ngakhale tili ndi mavuto, moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, ndipo tiyenera kuyamikira mphatso imeneyi.” Monga Silvia, atumiki onse a Mulungu, ana ndi akulu omwe, akudikira mwachidwi nthawi imene “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24.
[Chithunzi patsamba 31]
Silvia akuwerenga Baibulo, ndipo amayi ake atenga kathanki ka okosijeni