Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupeza Choonadi Chenicheni

Kupeza Choonadi Chenicheni

Kupeza Choonadi Chenicheni

PANALI pa December 18, 1810, ndipo kunali kutayamba kuda. Kwinakwake kutali ndi kumwera chakummawa kwa gombe la Scotland, m’nyanja za mafunde, sitima ya nkhondo ya Abritishi yotchedwa HMS Pallas inasochera. Amalinyero anavutika kuti athe kuona nyali za kumtunda zowatsogolera, chifukwa cha mdima ndiponso chipale chofewa chomwe chinali kugwa. Taganizani mmene anamvera ataona nyali n’kulunjikitsa sitima yawo kumene kunali nyalizo. Komabe, n’zachisoni kuti zimenezi sizinali nyali zowatsogolera zomwe ankafuna. Makamaka, unali moto umene anthu ogwira ntchito kumgodi wa laimu womwe unali ku gombelo anayatsa. Sitimayo inagunda miyala ndipo inaswekeratu. Anthu 11 omwe anali m’sitimayo anamira. Imeneyi inali ngozi yoopsa.

Sitima ya Pallas inachita ngozi chifukwa cha kulakwitsa. Komabe, amalinyero nthawi zina ankakumana ndi zoopsa kuposa zimenezi, nyali zachinyengo. Nyali zimenezi zimaikidwa dala kuti zizipusitsa oyendetsa sitima ndipo zimachititsa kuti sitimazo zilunjike ku magombe komwe kunali miyala n’cholinga choti zikasweka abe katundu, linatero buku lakuti Wrecks, Wreckers and Rescuers.

Malembo Opatulika Amene Angathandize Munthu Kupulumuka

Pofufuza choonadi, mumakumana ndi zoopsa zimene zimafanana ndi zija za anthu oyenda panyanja. Mungatsatire zinthu zonyenga, kapena ena angakunamizeni mwadala. Njira iliyonse mwa ziwirizi ingakupezetseni mavuto. Kodi mungatani kuti mudziteteze? Tsimikizani kuti mukufuna choonadi ku malo oyenerera ndiponso odalirika. Kwa zaka zoposa 125, magazini ino yasonyeza kuti Mawu a Mulungu ouziridwa, Baibulo, ndilo gwero lodalirika la choonadi chifukwa chakuti lili ndi “malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso.”​—2 Timoteo 3:15-17.

Komabe, kuti mukhulupirire kuti Baibulo ndi nyali yodalirika imene ingakutsogolereni, muyenera kutsimikizira zimenezi. (Salmo 119:105; Miyambo 14:15) Khalani omasuka kulemba kalata kwa anthu amene amafalitsa magazini ino kuti mudziwe zimene zathandiza anthu mamiliyoni ambiri kukhutira kuti Baibulo ndi louziridwadi ndi Mulungu. Mwachitsanzo, werengani kabuku kakuti Buku la Anthu Onse. * Kabukuka kali ndi mfundo zimene zimasonyeza kuti Baibulo ndi lolondola, lodalirika, ndiponso louziridwa.

Mfundo za Choonadi Zofunika Kwambiri

Kodi zina mwa mfundo zofunika kwambiri za choonadi zimene zimapezeka ‘m’malembo opatulika’ amenewa ndi ziti? Taonani zitsanzo zotsatirazi.

Pali Mulungu Wamphamvuyonse ndi Mlengi mmodzi amene anapanga zinthu zonse. (Genesis 1:1) Tili ndi moyo ‘chifukwa [Mulungu] analenga zonse’ ndipo anatipatsa moyo. (Chivumbulutso 4:11) N’chifukwa chake tiyenera kulambira iye yekha. Mlengi ndiye Gwero lalikulu la choonadi. (Salmo 36:9; Yesaya 30:20, 21; 48:17, 18) Iye ali ndi dzina lakelake limene amafuna kuti tiziligwiritsa ntchito. (Eksodo 3:15) Dzina limenelo, lolembedwa m’zilembo za Chihebri ndipo lomasuliridwa kuti YHWH, limapezeka ka 7,000 m’Baibulo. Kwa zaka zambirimbiri, dzinali lakhala likugwiritsidwa ntchito m’Chichewa kuti “Yehova.”​—Salmo 83:18.

Yehova analenga amuna ndi akazi kuti akhale kosatha m’Paradaiso padziko lapansi pompano. Yehova anapatsa anthu makhalidwe auzimu amene iye mwini ali nawo. Anawapatsa luso ndi mphamvu zowakhozetsa kusangalala ndi moyo wokhutiritsa ndiponso wosatha pano padziko lapansi. (Genesis 1:26-28) Yehova sanafune kuti dziko lapansi likhale poyesera amuna ndi akazi, kapena kuti malo okonzekeretsa amuna ndi akazi kuti kenako akakhale ndi moyo kumwamba monga mizimu, ngati kuti n’kumwamba kokhako kumene angakasangalale kukhala paubwenzi ndi Mulungu.

Panalibe choipa ndi mmene Mulungu analengera anthu. Kuipa kunabwera pamene zolengedwa zina za Mulungu, zaumunthu ndiponso zauzimu, zinagwiritsa ntchito molakwa ufulu wawo wosankha ndi kupandukira Mulungu. (Deuteronomo 32:5) Ndi zimene anachitazo, makolo athu oyambirira anasonyeza ngati kuti ali ndi ufulu wokhazikitsa okha mfundo zodziwira chabwino ndi choipa. (Genesis 2:17; 3:1-5) Zimenezi zinabweretsa imfa kwa anthu onse. (Genesis 3:19; Aroma 5:12) Kuti athetse nkhani zimene zinabuka chifukwa cha kupandukaku, Yehova anaganiza zolola kuipa kwa nthawi yochepa. Koma cholinga chake pa dziko lapansi ndi anthu sichinasinthe. (Yesaya 45:18) Amuna ndi akazi adzakhalabe kosatha m’Paradaiso padziko lapansi lokonzedwa bwino.​—Mateyu 6:10; Chivumbulutso 21:1-5.

Yesu Kristu, si Mulungu Wamphamvuyonse, koma Mwana wa Mulungu. Yesu Kristu mwiniyo anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti: “Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Iye sananene kuti ndi wofanana ndi Mulungu. M’malo mwake anati: “Atate ali wamkulu ndi Ine.”​—Yohane 14:28.

Yesu ali ndi udindo waukulu pa kukwaniritsa cholinga cha Mulungu. Mulungu anatumiza Yesu monga “kuunika ku dziko lapansi, kuti yense wokhulupirira [iye] asakhale mumdima.” (Yohane 12:46) Mogwirizana ndi mtumwi Petro, “palibe chipulumutso mwa wina yense.” (Machitidwe 4:12) Zimenezi n’zoona chifukwa chakuti chipulumutso chathu chimadalira magazi a mtengo wapatali a Kristu. (1 Petro 1:18, 19) Yesu Kristu anapereka moyo wake nsembe ya dipo kuombola anthu ku uchimo umene makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, anadzetsa pa anthu. (Mateyu 20:28; 1 Timoteo 2:6) Ndiponso, Mulungu anagwiritsa ntchito Yesu kuti afotokoze chifuniro Chake.​—Yohane 8:12, 32, 46, 47; 14:6; Machitidwe 26:23.

Mulungu wakhazikitsa Ufumu wa kumwamba, kapena kuti boma, lopangidwa ndi Yesu Kristu ndiponso anthu ena osankhidwa. Nkhani imeneyi imakambidwa mobwerezabwereza m’Baibulo lonse. Mulungu wapatsa boma limeneli udindo woonetsetsa kuti kufuna kwake kuchitike padziko lapansi monga kumwamba. (Mateyu 6:10) Pachiyambi, sichinali cholinga cha Mulungu kuti ena mwa anthu apite kumwamba. Dziko lapansi ndilo kunali kwawo. Koma chifukwa cha kuchimwa kwa munthu, Mulungu anakonza dongosolo latsopano. Anakonza zosankha anthu ‘a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse  . . . kuti akachite ufumu’ ndi Kristu m’boma la kumwamba. (Chivumbulutso 5:9, 10) Ufumu wa m’boma limenelo posachedwapa “udzaphwanya ndi kutha” maulamuliro onse a anthu, amene abweretsa chisoni ndi mavuto kwa anthu.​—Danieli 2:44.

Munthu akamwalira, palibe mbali imene imakhalabe ndi moyo. Mfundo ya choonadi cha m’Baibulo imeneyi imamveketsa bwino zambiri za munthu ndiponso chiyembekezo cha moyo wake. Imathetsanso kusamvana ndiponso mfundo zosocheretsa zimene zasokoneza anthu ponena za mmene akufa alili.

Buku la m’Baibulo la Mlaliki 9:5, 10 limatiuza kuti: “Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi, . . . mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.” Kodi mukudziwa chimene lembali likutanthauza? Palibe mbali ya munthu imene imakhalabe ndi moyo akamwalira. Munthu akamwalira, ‘amabwerera kunthaka.’​—Genesis 3:19.

Anthu amene anamwalira angakhalenso ndi moyo mwa kuuka kwa akufa. Nthawi yochepa imene Mulungu walola kuipa ikadzatha, “onse ali m’manda adzamva mawu [a Yesu], nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.” (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) Anthu akadzauka kwa akufa, adzakhala ndi moyo m’paradaiso padziko lapansi, ndipo moyo wakewo udzakhala umene Mulungu pachiyambi anafuna kuti anthu akhale nawo.

Fufuzani Malemba Mosamala Tsiku ndi Tsiku

Kodi mwaona mmene kudziwa mfundo zofunika za choonadi zimenezi kungakuthandizireni? Nthawi zovuta ndiponso zoopsa zino, kudziwa zimenezi kungakutetezeni ku “zimene ena monama amati ndiko ‘kudziwa zinthu,’” zomwe zimafalitsidwa ndi Satana Mdyerekezi. Iye amadzionetsa ngati “mngelo wa kuunika” ndipo atumiki ake amadzionetsa ngati “atumiki a chilungamo.” (1 Timoteo 6:20, NW; 2 Akorinto 11:13-15) Kudziwa Baibulo molondola kungakutetezeni ku chimene amati ndi choonadi chochokera ku dziko kwa “anzeru ndi akudziwitsa,” amene “akana mawu a Yehova.”​—Mateyu 11:25; Yeremiya 8:9.

Chifukwa chakuti kunali ziphunzitso zosocheretsa zambiri ndi nzeru zaumunthu m’tsiku lake, mtumwi Yohane anachenjeza Akristu oyambirira kuti: ‘Musamakhulupirira mzimu uli wonse, yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu.’ (1 Yohane 4:1) Taganizirani chitsanzo ichi. Ngati mutalandira uthenga umene ungakhudze kwambiri moyo wanu, kodi mungathamangire kuchita zimene uthengawo ukunena chabe chifukwa chakuti ukuoneka kuti ukuchokera ku gwero lodalirika? Ndithudi ayi. Mungayambe kaye mwatsimikiza gwero lake ndiponso kufufuza zimene uthengawo ukunena musanachite zimene mwauzidwazo.

Popereka malangizo ouziridwa ndiponso olembedwa amene ali ndi mfundo za choonadi, Mulungu anachita chotheka kuti inu muchite chimodzimodzi, kuti ‘muyese’ ngati nyali zokutsogolerani zimene mukutsatira, zilidi zenizeni. (1 Atesalonika 5:21) Anthu achidwi a m’nthawi ya atumwi anayamikiridwa chifukwa cha ‘kusanthula m’malembo masiku onse’ kuti atsimikize kuti zimene anali kuphunzirazo zinali zoonadi. (Machitidwe 17:11) Inunso mungachite chimodzimodzi. Lolani Baibulo monga “nyali younikira m’malo a mdima,” likutsogolereni ku chipulumutso. (2 Petro 1:19-21) Mukatero, ‘mudzam’dziwadi Mulungu,’ ndipo mudzapeza choonadi chenicheni.​—Miyambo 2:5.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 4]

Mawu a Mulungu ali ngati nyali

[Chithunzi patsamba 5]

Kodi dzina la Mulungu ndani?

[Chithunzi patsamba 5]

Kodi anthu ali ndi tsogolo lotani?

[Chithunzi patsamba 6]

Kodi Yesu ndi Mulungu Wamphamvuyonse?

[Chithunzi patsamba 6]

Kodi anthu akufa ali kuti?

[Chithunzi patsamba 7]

Kuuka kwa akufa ndi imodzi mwa mfundo zofunika za choonadi zimene Baibulo limaphunzitsa