Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Palibenso Njira Yabwino Yomwe Ndikanamalizira Maphunziro Anga Kuposa Imeneyi”

“Palibenso Njira Yabwino Yomwe Ndikanamalizira Maphunziro Anga Kuposa Imeneyi”

“Palibenso Njira Yabwino Yomwe Ndikanamalizira Maphunziro Anga Kuposa Imeneyi”

MPHUNZITSI wa pa sukulu ina ya sekondale ku Spain analemba kuti: “Kwa zaka zoposa 100, Mboni za Yehova zasonyeza mgwirizano weniweni, kuona mtima, ndipo koposa zonse chikhulupiriro cholimba.” Kodi chinam’chititsa mphunzitsiyu, yemwe ndi wokana Mulungu, kuti anene mawu amenewa n’chiyani?

Inali nkhani imene Noemí, wophunzira wa pasukuluyo ndiponso wa Mboni za Yehova analemba. Pamayeso omaliza maphunziro ake, iye anauzidwa kulemba nkhani. Ndiyeno iye anasankha kulemba nkhani ya mutu wakuti “Tinsalu Tapepo mu Ulamuliro wa Nazi.”

N’chifukwa chiyani iye anasankha mutu umenewo? Noemí akulongosola kuti: “Popeza aphunzitsi anafunikira kuona ntchito yanga, ndinaona kuti umenewu ndi mwayi woti ndiwalalikire. Nkhani ya mmene Mboni za Yehova zinakhalira zokhulupirika mu ulamuliro wa Nazi ku Germany, inali itandikhudza mtima. Ndinakhulupirira kuti anthu enanso akaiwerenga achita nayo chidwi.”

Nkhani yomwe Noemí analemba inachititsa chidwi anthu ambiri kuposa mmene iye ankaganizira. Chifukwa cha nkhani imeneyi, iye anapatsidwa mphoto pa October 5, 2002 pampikisano wa m’dziko lawo wofufuza za sayansi ndi za maphunziro a zaumunthu. Amene amasankha anthu opambana pa mpikisano umenewo ndi mapulofesa okwana 20 ochokera m’mayunivesite otchuka a ku Spain.

Amene anapereka mphoto kwa Noemí ndi nduna ya zamaphunziro ya m’dzikolo, a Pilar del Castillo. Noemí anapezerapo mwayi wopereka vidiyokaseti yakuti Jehovah’s Witnesses Stand Firm Against Nazi Assault, kwa ndunayo ndipo inalandira mosangalala.

Nyuzipepala ina ya mumzinda wa Manresa, komwe ndi kwawo kwa Noemí, inalemba nkhani yonena za kupambana kwake pampikisanowo, ndipo inalongosolanso za nkhani yomwe inam’chititsa kupambanako. Ndiyeno mphunzitsi wamkulu wa pa sukuluyo anapempha kuti nkhani yomwe Noemí analembayo idzawerengedwe pa mwambo wokumbukira kuti sukuluyo yatha zaka 75.

“Palibenso njira yabwino yomwe ndikanamalizira maphunziro anga akusekondale kuposa imeneyi,” akutero Noemí. “Ndinasangalala kwambiri nditawerenga mawu omwe aphunzitsi anga, a Jorge Tomás Calot analemba, oyambira lipoti langa:

“‘Ine ndimati kulibe Mulungu, koma ndikufuna n’takhulupirira ndithu kuti kuli Mulungu Wamkulukulu, yemwe amachititsa anthu ake omulambira kukhala ndi “chikondi chenicheni kwa anansi awo.”’”